Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

N’chifukwa Chiyani Amandiikira Malamulo Ambirimbiri?

N’chifukwa Chiyani Amandiikira Malamulo Ambirimbiri?

 Zimene Achinyamata Amadzifunsa

N’chifukwa Chiyani Amandiikira Malamulo Ambirimbiri?

“Nthawi imene anandiuza kuti ndizifika panyumba siinkandisangalatsa! Zinkandikwiyitsa chifukwa anthu ena ankaloledwa kufika panyumba mochedwa kusiyana ndi ine.”—Anatero Allen.

“N’zokwiyitsa kwambiri kufunsidwa za aliyense amene wakuimbira foni kapena amene iweyo wamuimbira. Ndimaona kuti amandichitira zinthu ngati ndine khanda!”—Anatero Elizabeth.

KODI mumaona kuti ndinu woponderezedwa chifukwa cha malamulo a panyumba panu? Kodi munayamba mwayesapo kuzemba panyumba kapena kunamiza makolo anu pa zimene mwachita? Ngati ndi choncho, mungamve ngati mmene anamvera mtsikana wina amene anati makolo ake ndi okhwimitsa zinthu kwambiri, ndipo anati: ‘Ndimachita kusowa popumira!’

Malamulo a panyumba ndi zinthu zimene makolo anu kapena amene akukuyang’anirani amakuuzani kuti muzichita, kapena musamachite. Malamulo amenewa angaphatikizepo zoyenera kuchita ponena za ntchito yanu ya kusukulu yolembera panyumba, ntchito za pakhomo, ndi nthawi yoti muzifika panyumba, komanso malamulo okhudza nthawi imene mungagwiritse ntchito foni, TV, kapena kompyuta. Malamulo ena angakhale okhudza zinthu zoti muzichita mukakhala kuti simuli panyumba ndipo angaphatikizepo khalidwe lanu la kusukulu ndiponso mmene mungasankhire anzanu ocheza nawo.

Kawirikawiri achinyamata ambiri amaphwanya malamulo a makolo. Pafupifupi achinyamata awiri mwa atatu alionse amene anafunsidwapo mafunso pa kafukufuku wina, ananena kuti analangidwapo chifukwa chophwanya malamulo a panyumba. Zimenezi zikutanthauza kuti kuphwanya malamulo apanyumba n’kumene kuli chifukwa chofala kwambiri chimene ana amalangidwira.

Achinyamata ambiri amadziwa ndithu kuti malamulo ena n’ngofunika kuti zinthu ziyende bwino. Koma ngati malamulo a panyumba alidi ofunika, n’chifukwa chiyani ena mwa iwo amakhala osasangalatsa? Ndipo ngati mukuona kuti mukuponderezedwa ndi malamulo a makolo anu, kodi mpumulo mungaupeze motani?

“Siine Khanda”!

“Kodi ndingachite chiyani kuti makolo anga adziwe kuti siine khanda, ndipo ayenera kundipatsa ufulu monga munthu wamkulu?” anafunsa choncho mtsikana wina dzina lake Emily. Kodi inuyo munamvapo choncho? Mofanana ndi Emily, inunso mungaipidwe ndi malamulo enaake chifukwa choganiza kuti akukuchitirani zinthu ngati ndinu mwana wa khanda. N’zoona kuti mwina makolo anu sakuganiza  choncho. Mosakayikira, iwo amaona kuti malamulowo n’ngofunika kuti akutetezeni ndi kukuthandizani kukonzekera udindo wanu wam’tsogolo mukadzakula.

Ngakhale mutakhala ndi ufulu wochulukirapo, mungaonebe kuti malamulo a panyumba panu sakusintha inuyo mukamakula. Zimenezi zingakhale zopweteka makamaka ngati azing’ono anu kapena azikulu anu akuoneka kuti amapatsidwa ufulu wochulukirapo. Mtsikana wina dzina lake Marcy anati: “Ndili ndi zaka 17, ndipo anandiikira lamulo loti ndizifika panyumba kunja kusanade kwambiri. Ndikangolakwitsa chinthu chilichonse, amandiuza kuti ndisayende, koma pamene mchimwene wanga anali msinkhu wangawu, sanapatsidwe nthawi iliyonse yoti azifikira panyumba, ndiponso sankam’letsa kuyenda akalakwitsa zinthu.” Pokumbukira zomwe zinkachitika pamene anali asanakwanitse zaka 20, Matthew ponena za mchemwali wake ndi asuweni ake aakazi anati: “Atsikanawo ankalekereredwa ngakhale alakwe chotani!”

Kodi Mungakonde Kukhala Opanda Malamulo?

N’zomveka kuti mungafune kukhala ndi moyo wosalamuliridwa ndi makolo anu. Koma kodi n’zoona kuti zinthu zingakuyendereni bwino kwambiri popanda malamulo a makolo? Mwina inuyo mukudziwa achinyamata ena a msinkhu wanu amene amafika panyumba nthawi imene akufuna, amavala zilizonse zimene akufuna, ndipo amapita ndi anzawo kulikonse pa nthawi iliyonse imene akufuna. Mwina makolo awo ndi otanganidwa kwambiri moti sadziwa zimene ana awo akuchita. Mulimonsemo, kulera ana m’njira yotereyi kwaoneka kuti sikwabwino. (Miyambo 29:15) Kusowa chikondi kumene mukukuona m’dzikoli kukuchitika chifukwa choti dziko ladzadza ndi anthu odzikonda, ndipo ambiri mwa anthu amenewa anakulira m’mabanja olekerera zinthu.—2 Timoteyo 3:1-5.

Tsiku lina m’tsogolo muno simungadzaganize kuti kukhala opanda malamulo apanyumba n’kwabwino. Taganizirani zimene anapeza pa kafukufuku winawake wofunsa azimayi achitsikana amene anakulira m’mabanja olekerera zinthu kapena osayang’aniridwa ndi makolo. Poganizira za moyo wawo wa m’mbuyo, palibe aliyense wa iwo amene ananena kuti kulekereredwako kunali kwabwino. M’malo mwake, iwo anakuona kuti ndi umboni woti makolo awo sankawakonda kapena analephera udindo wawo.

M’malo mosirira achinyamata amene amaloledwa kuchita zilizonse zimene akufuna, yesani kuona malamulo a makolo anu monga umboni wotsimikizira kuti amakukondani ndiponso amakusamalirani. Pokuikirani malire oyenerera, iwo amakhala akutsanzira Yehova Mulungu, amene amanena kwa anthu ake kuti: “Ine ndidzakulangiza ndi kuphunzitsa iwe za njira ukayendayo; ndidzakupangira ndi diso langa lakuyang’ana iwe.”—Salmo 32:8.

 Komabe, mwina panopa malamulowo angaoneke ngati okhwima kwambiri. Ngati mukuona choncho, taonani njira zina zimene zingakuthandizeni kuti muzisangalala ndi moyo kunyumba.

Kulankhulana Kwabwino

Kaya mukufuna ufulu wochuluka kapena mukungofuna kuti musamadandaule kwambiri ndi kuchepa kwa ufulu wanu, mfundo yofunika ndiyo kulankhulana kwabwino. Ena anganene kuti, ‘Koma ndayesetsa kulankhula ndi makolo anga, komabe sizikuthandiza!’ Ngati mumamva choncho, dzifunseni kuti, ‘Kodi ndikufunika kumalankhula bwino?’ Kulankhulana ndi chida chofunika kwambiri chimene chingakuthandizeni kuti (1) mupatsidwe zimene mukufuna kapena (2) mumvetse bwino chifukwa chake akukukanizani zimene mukufunazo. Ndithudi, ngati mukufuna kuti azikupatsani ufulu woyenera munthu wamkulu, m’pofunikanso kwambiri kuti mukhale ndi luso lotha kulankhula monga munthu wokhwima maganizo.

Phunzirani kuupeza mtima. Baibulo limati: “Chitsiru chivumbulutsa mkwiyo wake wonse; koma wanzeru auletsa nautontholetsa.” (Miyambo 29:11) Kulankhulana kwabwino sikuti ndi kudandaula kokhakokha. Mukamadandaula nthawi zonse, makolo angakudzudzuleninso! Choncho pewani kunyinyirika, kukwiya, ndi kunyanyala. Ngakhale zinthu zisakusangalatseni, musamenyetse chitseko mokwiya kapena kumenyetsa mapazi pansi m’nyumba makolo anu akakuletsani kuchita zinthu zinazake. Kusonyeza khalidwe lokwiya chonchi mwina kungachitse kuti makolo anu akuwonjezereni malamulo ena, osati ufulu.

Yesetsani kumvetsa cholinga cha makolo anu. Tracy, mtsikana wachikhristu amene wakulira m’banja la kholo limodzi, anaona kuti mfundo imeneyi ndi yothandiza. Iye anati: “Ndimadzifunsa kuti, ‘Kodi ndi cholinga chotani chimene mayi anga akufuna kukwaniritsa pondiikira malamulowa?’ Akufuna kundithandiza kuti ndikhale munthu wolongosoka.” (Miyambo 3:1, 2) Kuyesa kumvetsa zinthu koteroko kungakuthandizeni kufotokoza bwino maganizo anu kwa makolo anu. Mwachitsanzo, tiyerekezere kuti makolo anu akukukanizani kupita ku macheza enaake. M’malo mokakamira, mungawafunse kuti, “Kodi mungandilole kupita limodzi ndi mnzanga wamkulu, wokhwima maganizo komanso wodalirika?” Nthawi zonse, sikuti makolo anu azingovomereza zilizonse zomwe mukupempha ayi; koma mukamvetsa nkhawa zawo, mukhoza kuwauza maganizo amene angawavomereze.

Chitani zoti makolo anu azikukhulupirirani. Kuchita zinthu zoti makolo anu azikukhulupirirani kuli ngati kuika ndalama kubanki. Mungatenge ndalama zogwirizana ndi zimene munaikako kale. Angakulipiritseni faini ngati mutatengako ndalama zoposa zimene munaika ku buku lanu, ndipo ngati mutamachita zimenezi mobwerezabwereza, angakutsekereni buku lanu la kubanki. Kupatsidwa ufulu wowonjezereka kuli ngati kutenga ndalama kubanki; mudzapatsidwa ufulu woterowo ngati mwasonyeza kuti akhoza kukukhulupirirani.

Musamayembekezere zinthu zoti sizingatheke. Makolo ali ndi udindo wotetezera bwino ana awo. N’chifukwa chake Baibulo limanena za “malangizo a atate wako” ndi “malamulo a mako.” (Miyambo 6:20) Komabe, musaganize kuti malamulo a panyumba adzakuwonongerani moyo wanu. M’malo mwake, mukamagonjera udindo wa makolo anu, Yehova akulonjeza kuti, m’tsogolo muno ‘zinthu zidzakuyenderani bwino’!—Aefeso 6:1-3.

Nkhani zina zakuti “Zimene Achinyamata Amafunsa,“ mungazipeze pa adiresi yathu ya pa Intaneti ya www.jw.org.

ZOTI MUGANIZIRE

▪ Kodi ndi malamulo ati amene amakuvutani kwambiri kuwamvera?

▪ Ndi mfundo ziti m’nkhani ino zimene zikuthandizeni kutsatira mosavuta malamulo a makolo?

▪ Kodi mungatani kuti makolo anu azikukhulupirirani kwambiri?

[Bokosi/Zithunzi patsamba 11]

Mukaphwanya Lamulo

Zochitika zotsatirazi mwina zakuchitikiranipo kambirimbiri: Mwafika panyumba mochedwa, simunagwire ntchito yanu ya pakhomo, kapena mwalankhula pa foni nthawi yaitali kuposa imene mumaloledwa. Ndipo tsopano muli pamaso pa makolo anu! Kodi mungatani kuti zinthu zisaipe kwambiri?

Nenani zoona. Imeneyi sinthawi yoti muname. Lankhulani moona mtima ndiponso mosatalikitsa nkhani. (Miyambo 28:13) Kupeka nkhani kungachititse kuti makolo anu asadzakukhulupirireninso. Pewani kulungamitsa kapena kuchepetsa zomwe mwachitazo. Nthawi zonse kumbukirani kuti, “mayankhidwe ofatsa abweza mkwiyo.”—Miyambo 15:1.

Pepesani. Kusonyeza kuti mukumva chisoni chifukwa choti mwakhumudwitsa makolo anu, kapena chifukwa choti mwawawonjezera ntchito ina yapadera, n’koyenera ndipo kungawachititse kuti akupatseni chilango chofewerapo. (1 Samueli 25:24) Komabe, chisoni chanu chikhaledi chenicheni.

Vomerezani chilango. Mwina chinthu choyamba chimene mungachite chingakhale kukana chilango, makamaka ngati chikuoneka kuti sichoyenera. (Miyambo 20:3) Komatu, kuvomereza zotsatirapo za zochita zathu n’chizindikiro cha kukhwima maganizo. (Agalatiya 6:7) Chinthu chabwino chimene mungachite n’kuyesetsa kumachita zinthu zoti makolo anu ayambenso kukukhulupirirani.

[Chithunzi patsamba 12]

Yesetsani kumvetsa nkhawa za makolo anu