Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Chifukwa Chake Iye Ali Wofunika Kwambiri

Chifukwa Chake Iye Ali Wofunika Kwambiri

 Chifukwa Chake Iye Ali Wofunika Kwambiri

KWA zaka 2000 tsopano, anthu akhala akuchita chidwi kwambiri ndi kubadwa kwa Yesu. Monga mmene Luka, dokotala wa m’nthawi ya atumwi analembera, namwali wotchedwa Mariya anauzidwa ndi mngelo kuti: “Mvetsera! Udzakhala ndi pathupi nudzabereka mwana wamwamuna, ndipo udzam’patse dzina lakuti Yesu.” Kodi mngeloyo anabweretsa uthenga wotani wonena za Yesu? “Ameneyu adzakhala wamkulu nadzatchedwa Mwana wa Wam’mwambamwamba. Adzalamulira monga mfumu” ndipo “ufumu wake sudzatha konse.”—Luka 1:31-33.

Ndithudi zimenezo n’zimene anthu akufunikira, wolamulira wolungama amene adzalamulire dziko lonse mwachikondi! Inde, kale kwambiri Yesu asanabadwe, Baibulo linaneneratu kuti: “Kwa ife mwana wakhanda wabadwa, kwa ife mwana wamwamuna wapatsidwa; ndipo boma lidzakhala pa phewa lake. Ndipo adzamutcha dzina lake . . . Atate Wosatha, Kalonga wa Mtendere. Za kuwonjezera boma lake ndi mtendere sizidzatha.”—Yesaya 9:6, 7, New International Version.

Boma lolungama komanso lamtendere lidzakhala losangalatsa kwambiri! Koma taonani kuti boma limeneli linanenedweratu kuti lidzakhala pa phewa la kalonga, yemwe ndi “Kalonga wa Mtendere,” zomwe zikusonyeza kuti Mfumu ya chilengedwe chonse, yomwe ndi Mulungu Wamphamvuyonse, idzapereka ulamuliro kwa Mwana Wake. N’chifukwa chake, mobwerezabwereza Yesu anatchula boma limeneli, limene iye adzakhale Wolamulira wake kuti “Ufumu wa Mulungu.”—Luka 9:27, 60, 62.

Atangoyamba kumene utumiki wake, Yesu ananena kuti: “Ndiyenera kukalengeza uthenga wabwino wa ufumu wa Mulungu, chifukwa ndizo anandituma kudzachita.” (Luka 4:43) Yesu anaphunzitsa ngakhale ophunzira ake kupempherera Ufumu wa Mulungu kuti ubwere. (Mateyo 6:9, 10) Magazini yotchedwa Christianity and Crisis inati, “Ufumu unali mutu waukulu wa chiphunzitso cha [Yesu].” Inawonjezeranso kuti: “Palibe nkhani ina imene inali m’maganizo ake kapena imene inali yofunika kwambiri mu uthenga wake kuposa Ufumuwu. Ufumu umenewu umatchulidwa nthawi zoposa 100 mu nkhani za m’Mauthenga Abwino.”

Mafunso Ofunika Kuwaganizira

Kodi inuyo mukuganiza kuti Yesu ndi wotani lerolino? Nthawi zambiri, makamaka pa nyengo ino ya chaka, iye amajambulidwa monga khanda lomwe lagonekedwa modyera ng’ombe. Ndipo n’zoona kuti kwa kanthawi kochepa iye anakhalapodi khanda. (Luka 2:15-20) Koma kodi iye ayenera kukumbukiridwa makamaka monga khanda? Taganizani, N’chifukwa  chiyani Yesu anabadwa monga munthu? Kodi iye anali ndani kwenikweni?

Buku lotchedwa Encarta Yearbook la mu 1996 linafunsa kuti: “Kodi Yesu anali Mwana wa Mulungu, Mesiya wolonjezedwa m’Baibulo la Chiheberi? Kapena kodi iye anali munthu wosiyana ndi anthu wamba, koma munthube basi?” Mafunso amenewa ndi ofunika kuwaganizira kwambiri. Chifukwa chiyani? Chifukwa moyo wathu weniweni ndiponso chimwemwe chathu, zimadalira pa mmene timaonera Yesu ndi mmene timachitira zinthu kwa iye. “Iye wokhulupirira mwa Mwanayo ali nawo moyo wosatha,” limatero Baibulo, koma “wosamvera Mwanayo sadzauona moyowu.”—Yohane 3:36.

Sanali Munthu Wamba

Pambuyo polongosola zimene Yesu anachita ku kachisi wa ku Yerusalemu ali ndi zaka 12, Baibulo limati iye anabwerera kunyumba kwawo pamodzi ndi Mariya ndi mwamuna wake Yosefe, ndipo “[Yesu] anapitiriza kuwamvera.” (Luka 2:51, 52) Koma Yesu atakula, zinaonekeratu kuti sanali munthu wamba.

Yesu atatontholetsa namondwe, mnzake wina pochita mantha anafuula kuti: “Kodi ameneyu ndani?” (Maliko 4:41) Patapita nthawi, Yesu anabweretsedwa kwa bwanamkubwa wa Chiroma, Pontiyo Pilato pa milandu yom’namizira. Atakhutira kuti Yesu anali wosalakwa ndiponso pochita chidwi ndi mmene Yesu anadzisungira ulemu pamaso pa anthu ankhanza ndi opanda chilungamowo, Pilato anasonyeza Yesu kwa khamulo atagoma naye, n’kufuula kuti: “Taonani! Mwamunatu ameneyu!” Koma Ayuda anayankha kuti: “Tili ndi chilamulo ife, ndipo malinga ndi chilamulocho iyeyu ayenera kufa, chifukwa akudziyesa yekha mwana wa Mulungu.”—Yohane 19:4-7.

Atamva anthuwo akumutchula Yesu kuti “mwana wa Mulungu,” Pilato anachita mantha kwambiri. Pilato analinso atalandira uthenga wochokera kwa mkazi wake wonena za maloto okhudza Yesu amene mkaziyo analota, ndipo mkazi wakeyo anam’tchula Yesu kuti “munthu wolungamayu.” (Mateyo 27:19) Choncho, Pilato anadzifunsa kuti Yesu anali ndani kwenikweni. Ngakhale ankadziwa kuti Yesu amachokera ku Galileya, Pilato anafunsa kuti: “Kodi umachokera kuti?” Yesu atakana kuyankha, kukambiranako kunathera pomwepo.—Yohane 19:9, 10.

N’zachidziwikire kuti Yesu anali munthu, koma anali wosiyana ndi ena onse chifukwa anakhalapo munthu wauzimu, yemwe ankadziwika kumwamba ndi dzina loti Mawu. Ndiyeno, m’njira yodabwitsa, moyo wake unasamutsidwira m’mimba mwa Mariya. Mtumwi Yohane anachitira umboni kuti: “Mawu ameneyo anakhala ndi thupi la nyama nakhala pakati pathu.”—Yohane 1:1, 2, 14, 18; Chivumbulutso 3:14.

Chifukwa Chake Mulungu Anatumiza Mwana Wake

Adamu woyamba anachimwa asanabereke ana. Mngelo wopanduka, amene pambuyo pake anatchedwa Mdyerekezi ndi Satana, anachititsa  Adamu kusamvera Mulungu. Chifukwa cha zimenezi, Adamu anataya mwayi wake wokhala Mwana wa Mulungu, monga mmene Mulungu anamuuziratu kuti adzatero akapanda kumvera. Choncho Adamu anakolola zimene anafesa. Sanakhalenso wangwiro, anakalamba, ndipo kenako anafa.—Genesis 2:15-17; 3:17-19; Chivumbulutso 12:9.

Polongosola za mmene kusamvera kwa Adamu kwakhudzira ife tonse mbadwa zake, Baibulo limati: “Uchimo unalowera m’dziko kudzera mwa munthu mmodzi [Adamu], ndi imfa mwa uchimo, imfayo nifalikira kwa anthu onse chifukwa onse anachimwa.” (Aroma 5:12) N’zomvetsa chisoni kuti tonse tinatengera uchimo wa kholo lathu Adamu, ndi zotsatirapo zake zoipa, zomwe ndi ukalamba ndi imfa.—Yobu 14:4; Aroma 3:23.

Kumasulidwa ku zotsatirapo zauchimo kukanatheka mwa kukhala ndi tate wangwiro basi, amene sanatengere nawo uchimo ndi zotsatirapo zake zoipa. Taonani mmene tate watsopanoyo, wofanana ndi Adamu wangwiro, anaperekedwera.

Panaperekedwa Munthu Woyenera

“Kalonga wa Mtendere” wolonjezedwayo, ngati mukukumbukira, amatchedwanso “Atate Wosatha.” (NIV) Kubadwa kwake monga munthu kunanenedweratu motere: “Namwali adzatenga pathupi ndipo adzabereka mwana wamwamuna.” (Yesaya 7:14; Mateyo 1:20-23, NIV) Yesu analibe atate womubereka, monganso mmene munthu woyambirira, Adamu analili. Pofotokoza za mzera wobadwira wa Yesu mpaka kufika poyambirira pa mibadwo ya anthu, wolemba mbiri ya Baibulo Luka anasonyeza kuti Adamu anakhalapo monga “mwana wa Mulungu.” (Luka 3:38) Koma monga mmene taonera, Adamu anataya mwayi wokhala mwana wa Mulungu, iye mwini ndi ana ake omwe. Choncho, tingati tonse tikufunika atate wangwiro, wofanana ndi mmene Adamu analili atangolengedwa kumene.

Mulungu anatumiza Mwana wake kuchokera kumwamba kuti akhale Adamu watsopanoyo, kulowa m’malo mwa Adamu woyamba uja. Baibulo limati: “‘Munthu woyambirira, Adamu, anakhala munthu wamoyo.’ Adamu womalizira anakhala mzimu wopatsa moyo. Munthu woyambayo anachokera padziko lapansi ndipo anapangidwa ndi fumbi; wachiwiriyo anachokera kumwamba.” (1 Akorinto 15:45, 47) Yesu, “Adamu womalizira,” ali ngati “Adamu woyambirira” chifukwa choti anali munthu wangwiro, wokhoza kubereka ana angwiro, amene akanatha kukhala ndi moyo wosatha komanso wangwiro pa dziko lapansi.—Salmo 37:29; Chivumbulutso 21:3, 4.

Yesu, yemwe analibe ana, anakhalabe wokhulupirika kwa Mulungu mpaka imfa yake, ngakhale kuti anayesedwa m’njira zosiyanasiyana ndi Satana. Moyo wangwiro ndi wokhulupirika umene Yesu anautaya, kapena kuupereka nsembe, umatchedwa dipo. Baibulo limafotokoza kuti: “Tinamasulidwa [ku uchimo ndi imfa zomwe tinatengera kwa Adamu] ndi dipo la magazi [a Yesu].” Ndipo limanenanso kuti: “Monga mwa kusamvera kwa [Adamu] ambiri anakhala ochimwa, momwemonso kudzera mwa kumvera kwa [Yesu] ambiri adzakhala olungama.”—Aefeso 1:7; Aroma 5:18, 19; Mateyo 20:28.

Tikakhulupirira Yesu, iye adzakhala kwa ife “Atate Wosatha” ndi “Mpulumutsi” wathu. Iye adzakhala Kalonga wolamulira bwino kwambiri, pamene adzakhale Wolamulira wa Ufumu wa Atate wake. Tiyeni tsopano tione mmene zinthu zidzakhalire mu ulamuliro umenewo, ndiponso nthawi imene tingayembekezere kukwaniritsidwa kwa madalitso osangalatsa amenewa.—Luka 2:8-11.

[Zithunzi patsamba 5]

Kodi inuyo mumaganiza kuti Yesu ndi wotani lerolino?

[Chithunzi patsamba 6]

N’chifukwa chiyani Yesu amatchedwa “Adamu womalizira”?