Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

“Kodi Mumakondwerera Tsiku la Agogo Aakazi?”

“Kodi Mumakondwerera Tsiku la Agogo Aakazi?”

 “Kodi Mumakondwerera Tsiku la Agogo Aakazi?”

TSIKU lina m’mawa m’nyengo yachisanu, mtsikana wina wa ku Poland wa zaka 16, dzina lake Natalia akudikira sitima, atolankhani awiri a nyuzipepala inayake yakwawoko anamupeza ndi kum’funsa kuti, “Kodi umakondwerera Tsiku la Agogo Aakazi?”

Ku Poland, masiku okumbukira agogo aakazi, agogo aamuna, amayi, ndi aphunzitsi n’ngapadera kwambiri. Nthawi zambiri ana aang’ono amakondwerera Tsiku la Agogo Aakazi, ndi Tsiku la Agogo Aamuna, polemba makadi, pamene ana okulirapo amapereka mphatso kapena maluwa kwa agogo awo.

Atangofunsidwa funso limeneli, Natalia anasowa chonena. Koma atapemphera kaye chamumtima, anawauza atolankhaniwo kuti, “Ndine wa Mboni za Yehova, ndipo sindikondwerera Tsiku la Agogo Aakazi.” Atolankhaniwo anaoneka odabwa kwambiri. Natalia anangomwetulira n’kunena kuti: “Ndimakhala ndi agogo anga aakazi, ndipo nditha kuwabweretsera maluwa, kulankhula nawo ndi kuwathokoza chifukwa cha kukoma mtima kwawo tsiku lililonse. Ndiye n’kumawakumbukiriranji kamodzi kokha pachaka?”

Mawu ozama amenewa anachititsa chidwi atolankhaniwo monganso mmene inuyo mungachitire nawo chidwi. Nyuzipepala ya m’mawa mwake, inali ndi chithunzi cha Natalia ndi mawu amene ananena.

Kodi chitsanzo chimenechi chikukuchititsani kudzifunsa ngati muli okonzeka kuyankha mafunso okhudza chikhulupiriro komanso khalidwe lanu, makamaka ngati mutafunsidwa mwadzidzidzi? Onse amene amalambira Mulungu m’choonadi ayenera kuyesetsa kum’lemekeza mwa kukhala okonzeka ndi ofunitsitsa kufotokoza chikhulupiriro chawo nthawi iliyonse imene angafunikire kutero.—1 Petulo 3:15.