Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Nyumba Zabwino kwa Aliyense Pomalizira Pake

Nyumba Zabwino kwa Aliyense Pomalizira Pake

Nyumba Zabwino kwa Aliyense Pomalizira Pake

KUNJA kwa mzinda wa Nairobi ku Kenya, kuli malo okongola kwambiri a United Nations otchedwa Gigiri omwe ndi aakulu maekala 140, ndipo ndi otetezedwa bwino ndiponso n’kumene kuli likulu loona za nyumba la UN-HABITAT. Malo amenewa ndi chizindikiro chosonyeza mgwirizano wa mayiko onse ofuna kuthetsa vuto la kusowa nyumba la padziko lonse. Mukamayenda m’kasewu kotchedwa Gigiri Nature Trail, kamene kali m’mudziwo, mumaona umboni wa zimene zingachitike ngati mayiko ataikira mtima kwambiri ndiponso ngati atapereka thandizo lokwanira bwino la ndalama. Malo amenewa omwe poyamba anali tchire lokhalokha, anawakonza bwinobwino n’kuwasandutsa malo okongola ndi osangalatsa kumene anthu ogwirako ntchito ndiponso alendo amasangalalirako.

Koma makilomita ochepa chabe kuchokera pamalowa, pali mudzi umene ukukula mofulumira kwambiri wa nyumba za zisakasa umene wangoyambika posachedwapa. Imeneyi ndi mbali yochepa chabe yosonyeza mmene ntchito yothana ndi vuto la kusowa kwa nyumba ilili yovuta. Nyumba za m’mudziwu zomwe n’zomanga ndi matope, mitengo, ndi malata azitini n’zazikulu pafupifupi mamita folo mu litali, mamita folo mu lifupi, ndiponso za makoma otalikanso mamita folo. Tinjira todutsa m’kati mwa mudziwu timanunkha kwambiri chifukwa cha madzi oipa amene amataya. Anthu a m’mudzi umenewu amalipira madzi ndi ndalama zopitirira maulendo faifi poyerekezera ndi anthu a ku United States. Anthu pafupifupi 40,000 amene amakhala m’mudziwu ndi a zaka zapakati pa 20 ndi 40. Anthu amenewa sikuti ndi aulesi ayi. Iwo anabwera kumeneku n’cholinga chodzafuna ntchito mu mzinda wa Nairobi umene uli chapafupi.

Mosiyana kwambiri ndi zimenezi, atsogoleri a mayiko amadzakumana m’dera lomweli m’malo abwino, ndi okongola kudzakambirana za tsogolo la abambo, amayi, ndi ana omwe akuvutika koma akukhala chapafupi pomwepo. Zimene ananena mlembi wamkulu wa bungwe la United Nations ndi zoona komanso n’zogwetsa ulesi. Iye anati, “dziko lili ndi zonse zofunika, luso, ndi mphamvu” zoti likhoza kuthandizira kutukulira miyoyo ya anthu ovutika amene akukhala m’zisakasa. Ndiyeno kuti zimenezi zitheke, kodi pakufunika kuchitanji? A Annan anamaliza ndi kunena kuti: “Ndikukhulupirira kuti . . . anthu onse amene amagwira nawo ntchitoyi akhoza kusiya mzimu wosasamala za ena ndiponso kupanda chidwi kwa atsogoleri andale zomwe ndi zinthu zimene zakhala zikulepheretsa kuti ntchitoyi ipite patsogolo.”

Koma kodi zimene ananenazo n’zodalirika motani? Kodi pangafunike chiyani kuti athandize atsogoleri andale onse kusiya dyera ndiyeno n’kugwirizana pa zinthu zomwe zingakhale zothandiza kwa aliyense? Koma pali Winawake amene ali ndi zonse zofunika, luso, ndiponso mphamvu zothetsera vuto limene lilipoli. Ndipo chosangalatsanso n’chakuti ndi woganizira ena ndiponso ndi wofunitsitsa kuchitapo kanthu. Ndipotu boma lake linaika kale ndondomeko ya pulogalamu imene idzathetseratu vuto la padziko lonse la kusowa nyumba.

Pulogalamu Yatsopano Yomanga Nyumba

Mlengi wathu, Yehova Mulungu, amafotokoza zimene akufuna kuchita kudzera m’Baibulo. Akulonjeza kuti: ‘Ndikulenga kumwamba kwatsopano ndi dziko lapansi latsopano.’ (Yesaya 65:17) Zimenezi zidzasintha zinthu kwambiri. Boma latsopano la “kumwamba” limeneli lidzachita zimene maboma a anthu sangakwanitse. Ufumu wa Mulungu kapena kuti boma, udzapereka moyo wabwino, chitetezo, ndiponso ulemu kwa munthu wina aliyense amene adzapanga nawo dziko lapansi latsopano. Poyamba, Yesaya anauzidwa kuti anthu amene adzakhale m’dziko lapansi latsopano adzasonkhanitsidwa m’nthawi ya “masiku otsiriza.” (Yesaya 2:1-4) Zimenezi zikutanthauza kuti kusintha kumeneku kuli pafupi kwambiri.—Mateyu 24:3-14; 2 Timoteo 3:1-5.

Chochititsanso chidwi n’chakuti, m’mawu amene analembedwa m’mavesi ena a Yesaya chaputala 65, Mulungu ananena molunjika kuti aliyense m’nthawi imeneyo adzakhala ndi nyumba yake. Iye anati: “Ndipo iwo adzamanga nyumba ndi kukhalamo . . . Iwo sadzamanga, ndi wina kukhalamo.” (Yesaya 65:21, 22) Tangoganizani kukhala ndi nyumba ndiponso kukhala m’malo abwino kwambiri ndi otetezeka m’paradaiso wosangalatsa! Kodi ndani amene sangafune kukhala moyo wotere? Koma kodi mungatsimikize motani kuti zimene Mulungu akulonjezazi n’zoona?

Lonjezo Limene Mungalikhulupirire

Mulungu atalenga Adamu ndi Hava, sikuti anawaika m’malo onyansa. M’malo mwake, anawaika m’munda wa Edene, malo okongola kwambiri okhala ndi mpweya wabwino ndi madzi okwanira ndiponso chakudya. (Genesis 2:8-15) Adamu anauzidwa “kudzaza dziko lapansi” koma osati mpaka kusowa poponda. (Genesis 1:28) Kuchokera pachiyambi pomwe, Mulungu anafuna kuti aliyense m’mundamo azisangalala ndi mtendere, umodzi, ndiponso ndi zinthu zina zambiri zabwinozabwino.

Koma patapita nthawi, m’tsiku la Nowa, anthu anadzaza ndi chiwawa ndi chiwerewere, choncho, “dziko lapansi linavunda pamaso pa Mulungu.” (Genesis 6:11, 12) Kodi Mulungu anangosiyirira khalidwe loipali? Ayi. Anachitapo kanthu mwamsanga. Anasesa dziko lonse lapansi ndi Chigumula ali ndi zolinga ziwiri. Choyamba chinali chifukwa cha dzina lake ndipo chachiwiri chinali chifukwa cha munthu wolungama Nowa pamodzi ndi ana ake. Ndiyeno pamene Nowa anatuluka m’chingalawa ndi kuyambiranso moyo watsopano, anauzidwanso kachiwiri kuti amwazikane ndipo ‘achuluke, adzaze dziko lapansi.’—Genesis 9:1.

Kenakonso, Mulungu anapereka kwa Aisrayeli cholowa chimene analonjeza kholo lawo Abrahamu. Dziko Lolonjezedwa limenelo analifotokoza kuti linali ‘dziko labwino . . . dziko loyenda mkaka ndi uchi.’ (Eksodo 3:8) Koma chifukwa cha kusamvera kwawo, Aisrayeli anakhala akuzungulira m’chipululu kwa zaka 40 opanda malo okhazikika okhala. Koma Mulungu pofuna kukwaniritsa mawu ake, anawapatsa dziko loti akhalemo. Mawu ake ouziridwa amafotokoza kuti: “Yehova anawapatsa mpumulo pozungulira ponse . . . Sikadasowa kanthu konse ka zinthu zokoma zonse Yehova adazinenera nyumba ya Israyeli; zidachitika zonse.”—Yoswa 21:43-45.

Aliyense Adzakhala ndi Nyumba Yake

N’zoonekeratu kuti mawu a Yehova a m’chaputala 65 cha buku la Yesaya sali malonjezo opanda pake. Monga Mlengi wa zinthu zonse, iye ali ndi mphamvu zochita chilichonse chimene akufuna kuti ayeretse dziko lapansili n’kukwaniritsa chifuno chake chimene anali nacho poyambirira. (Yesaya 40:26, 28; 55:10, 11) Kuwonjezeranso pamenepa, Baibulo limatitsimikizira kuti zimenezi n’zimene iye akufuna kuti azichite. (Salmo 72:12, 13) M’mbuyomu anapereka nyumba zabwino kwa anthu olungama, ndipo n’zimene azichitenso posachedwapa.

Ndipo pamene Mwana wake Yesu Kristu anabwera padziko lapansi, anaphunzitsa ophunzira ake kupempherera ‘chifuno cha Mulungu kuchitika, monga kumwamba, chomwecho pansi pano.’ (Mateyu 6:10) Iye anasonyeza kuti dziko lapansi lidzakhala paradaiso. (Luka 23:43) Taganizirani tanthauzo la zimenezi. Zimenezi zikutanthauza kuti sikudzakhalanso midzi ya nyumba za zisakasa, midzi yopanda chilolezo, anthu kugona m’misewu, kapenanso anthu kuthamangitsidwa pa malo. Imeneyi idzakhaladi nthawi yosangalatsa zedi! Mu ulamuliro wa Ufumu wa Mulungu, aliyense adzakhala ndi nyumba yakeyake yokhalitsa.

[Bokosi/Chithunzi patsamba 26]

MMENE AISRAYELI AMAMANGIRA NYUMBA KALE

Zikuoneka kuti Aisrayeli, mofanana ndi Akanani, amene anakhalako Aisrayeliwo asanakhaleko, ankakonda kumanga nyumba za miyala chifukwa chakuti nyumba zimenezi zimakhala zolimba kwambiri kuposa nyumba zina ndiponso zimawateteza kwa adani. (Yesaya 9:10; Amosi 5:11) Komabe, m’malo a m’zidikha amagwiritsa ntchito zidina zosawotcha kapena zowotcha kumangira nyumba zokhalamo. Madenga ambiri a nyumba zawo amakhala afulati, ndipo nthawi zina amamanga kachipinda pamwamba pakepo. Nthawi zambiri, pabwalo la nyumbazi pamakhala uvuni ndipo nthawi zina pamakhalanso chitsime.—2 Samueli 17:18.

Chilamulo cha Mose chinali ndi malamulo ambiri okhudza nyumba, ndipo mbali yofunika kwambiri ya Chilamulocho inali yokhudza chitetezo. Padenga lomwe ndi lafulati anali kumangapo kampanda kakafupi kuzungulira denga lonselo pofuna kupewa ngozi. Lamulo la khumi linali kuchenjeza Aisrayeli kuti asasirire nyumba ya mnzawo. Komanso amene wagulitsa nyumba yake, anali ndi ufulu woigulanso pakapita nthawi.—Eksodo 20:17; Levitiko 25:29-33; Deuteronomo 22:8.

Mu Israyeli, nyumba imagwiranso ntchito monga malo ofunika kwambiri operekeramo malangizo auzimu. Azibambo anali kuuzidwa mosapita m’mbali kuti ayenera kuphunzitsa ana awo malamulo a Mulungu pamene akukhala m’nyumba zawo, ndiponso kuti m’nyumbazo simunayenera kupezeka zinthu zokhudzana ndi kupembedza mafano.—Deuteronomo 6:6, 7; 7:26.

[Chithunzi]

Mu Israyeli wakale, nyumba zinkagwiritsidwa ntchito kuchitira zinthu zauzimu, monga Madyerero a Misasa

[Bokosi/Chithunzi patsamba 28]

NYUMBA ZOYAMBIRIRA

Baibulo silinena chilichonse chokhudza munthu woyambirira Adamu, kuti ankakhala m’nyumba. Koma lemba la Genesis 4:17 limanena kuti Kaini “anamanga mudzi, nautcha dzina lake la mudziwo monga dzina la mwana wake, Enoke.” Sikuti mudzi umenewu unali wolimba kwambiri poyerekezera ndi mizinda ya m’nthawi yathu ino. Koma nkhaniyi sinafotokoze mtundu wa nyumba zimene anamanga. Mwinamwake mudzi wonsewo unamangidwa ndi anthu a m’banja la Kaini okhaokha basi.

M’nthawi zakale anthu ankakonda kukhala m’mahema. Yabala yemwe anali mmodzi wa mbumba za Kaini amatchedwa kuti “ndiye atate wawo wa iwo okhala m’mahema, akuweta ng’ombe.” (Genesis 4:20) N’zodziwikiratu kuti, mahema anali osavuta kuzika ndiponso osavuta kuyenda nawo.

M’kupita kwa nthawi, midzi yambiri imene inali itayamba kutukuka munayamba kumangidwa nyumba zapamwamba. Mwachitsanzo, mu mzinda wa Uri, kumene nthawi inayake kholo lakale Abramu (Abrahamu) anakhalako, zotsalira za nyumba zakalekale zimenezi zimasonyeza kuti anthu ena ankakhala m’nyumba zabwino, zopaka pulasitala ndiponso laimu zomwe zinali ndi zipinda 13 kapena 14. Nyumba ngati zimenezi ziyenera kuti zinali nyumba zosiririka m’nthawi imeneyo.

[Chithunzi pamasamba 24, 25]

Mulungu akulonjeza nyumba zotetezeka kwa anthu olungama