Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kuthandiza Akaidi Kusintha M’ndende za ku Mexico

Kuthandiza Akaidi Kusintha M’ndende za ku Mexico

 Kuthandiza Akaidi Kusintha M’ndende za ku Mexico

Yolembedwa ndi wolemba Galamukani! ku Mexico

NTHAWI zina timauzidwa kuti kuthandiza anthu a makhalidwe oipa kusintha n’chifukwa chomveka choikira zigawenga m’ndende. Komabe, kutsekera zigawenga m’ndende pakokha sikungasinthe khalidwe la munthu. Cholinga chofuna kusintha chiyenera kuchokera mu mtima ndi m’maganizo a munthuyo, ndiyeno munthuyo ayenera kulapa moonadi ndi kufunitsitsa kusiya khalidwe lake loipa. M’ndende zambiri padziko lonse lapansi, akaidi ambiri asintha modabwitsa chifukwa cha ntchito yophunzitsa Baibulo ya Mboni za Yehova. Tiyeni tione mmene ntchito imeneyi ikuyendera ku Mexico.

Ku Mexico, Mboni za Yehova zimapita ku ndende zokwana 150, kukaphunzitsa akaidi kuwerenga Baibulo, mfundo za makhalidwe abwino, ndi ziphunzitso za m’Baibulo. Mwachitsanzo, ku ndende ya ku Ciudad Juárez ku Chihuahua, atumiki a Mboni za Yehova amalalikira nthawi zonse kwa akaidi pafupifupi 1,200. Akaidiwo amalemekeza kwambiri atumiki amenewa ndipo amawateteza ngati pachitika chipwirikiti. Nthawi ina, kunabuka chisokonezo m’ndende imeneyi, koma akaidi ena ovuta kwambiri anakhazikitsa bata kuti Mboni zituluke ndi kuti zisavulazidwe.

Galamukani! ya May 8, 2001, yomwe inali ndi mutu wakuti “Kodi Akaidi Angatheke Kuwasintha?” inachititsa chidwi akaidi ndi oyang’anira ndende ambiri. M’ndende ya ku San Luis Río Colorado ku Sonora, Mboni 12 zinagawira magazini amenewa okwana 2,149.

Akaidi achidwi akapezeka, Mboni za Yehova zimabwererako mlungu ndi mlungu kukawaphunzitsa Baibulo m’magulumagulu ndi kukachititsa misonkhano. Kodi ntchito yophunzitsa Baibulo imeneyi yathandiza bwanji kusintha akaidi?

Akaidi Akhala Atumiki Achikristu

Pofika zaka 20, Jorge anali atayamba kale moyo wauchigawenga. Atagwira ukaidi kwa zaka 13 m’ndende ya ku Islas Marías, anamasulidwa. Koma posakhalitsa, anayambiranso moyo wauchigawenga. Anali kuzembetsa mankhwala osokoneza bongo. Anayamba kugwira ntchito yopha anthu motumidwa, ndipo anapha anthu 32. Atamangidwanso, maloya ake anamuuza kuti mabwana ake akale anali okonzeka kulipira ndalama zambiri kuti amutulutse m’ndende. Mabwana akewo ankafuna kuti amutulutse m’ndende kuti akawapherenso munthu wina. Koma panthawi imeneyi, Jorge anali kuphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova. Anali atapita patsogolo mwauzimu mpakana kubatizidwa ndi kukhala mlaliki wa nthawi zonse m’ndende momwemo. Kodi akanalola kumasulidwa ndi kukatumikiranso atsogoleri azigawenga amenewa kapena akanasankha kukhalabe m’ndende ndi kutumikira Yehova? Jorge ananena kuti: “Ndasankha kukhalabe m’ndende ndi kulandira chilango pa zolakwa zanga. Tsopano ndikutumikira Yehova Mulungu, Ambuye Mfumu.” Jorge anapitirizabe kukhala wokhulupirika kwa Mulungu ndipo anafa ali ndi  chikhulupiriro cha kuuka kwa akufa. Anzake achikristu anati: “Jorge ‘anazindikira choonadi ndipo choonadi chinam’masula.’”—Yohane 8:32.

David, yemwe anamulamula kuti akhale m’ndende zaka 110 chifukwa cha kupezeka ndi milandu ya kupha, kusowetsa anthu, ndi kuba, anatsekeredwa m’ndende ku mbali ya chitetezo chokhwima yokonzedwera zigawenga zoopsa zedi. Komano, chifukwa cha mmene wasinthira khalidwe lake kuchokera pamene anayamba kuphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova, anamupatsa chilolezo chapadera chotuluka kuchoka kumbali imeneyi ndi kupita ku misonkhano ku mbali ina ya ndendeyi moperekezedwa ndi woyang’anira akaidi. Moyo wake wasintha kwambiri chifukwa chotsatira malangizo a Baibulo, kotero kuti panopa amalalikira ndipo akuphunzitsa Baibulo akaidi anzake eyiti m’ndende momwemo. Ngakhale banja lake lachita chidwi kuona momwe wasinthira kotero kuti amapita ku ndendeko ndi cholinga chakuti azikawaphunzitsa Baibulo. David akuti: “Sinditopa kuthokoza Yehova pondipatsa ufulu mwauzimu.”

Chifukwa cha maphunziro a Baibulo amene Mboni za Yehova zikuchititsa, akaidi 175 amene asintha khalidwe lawo m’ndende 79 za ku Mexico, tsopano ndi ovomerezedwa kugwira ntchito yolalikira, ndipo 80 mwa iwo anabatizidwa. Amachititsa maphunziro a Baibulo okwana 703 ndi akaidi anzawo. Ndipo akaidi 900 amapezeka pamisonkhano yachikristu yomwe imachitikira m’ndende zimenezi.

Akuluakulu a Ndende Akuyamikira

Akuluakulu a ndende akuyamikira ntchito imene Mboni za Yehova zikuchita. Mwachitsanzo, m’chaka cha 2002, akuluakulu a ndende ya ku Tekax ku Yucatán, anapereka satifiketi yothokoza kudzipereka kwa Mboni za Yehova ndi “ntchito yabwino yothandiza akaidi” yomwe Mbonizi zikuchita.

Pamene Mboni zinkayamba ntchito yophunzitsa akaidi m’ndende imeneyi, zikamachita misonkhano yawo pankakhala oyang’anira akaidi ambiri amene ankawapenyetsetsa. Komano, m’kupita kwa nthawi, akaidi amenewa anasintha khalidwe lawo, ndipo owayang’anira awo anayamba kuwapatsa ulemu, moti m’malo motumiza oyang’anira ambirimbiri kukawalondera, amatumiza mmodzi yekha basi.

Ndende ya ku Ciudad Juárez ili ndi Nyumba ya Ufumu yakeyake. Anawalola kulowetsa m’ndendemo zipangizo zofunikira kuti akonze nyumba ya zitsulo zokhazokha yomwe sinali kugwiritsidwa ntchito kukhala nyumba yolambiriramo. Akaidi obatizidwa 13 ndi akaidi enanso omwe ankaphunzira Baibulo ndi akaidi amenewa ndiwo anagwira ntchito yonseyi. Nyumba ya Ufumu imeneyi ili ndi zida zokuzira mawu, zimbudzi, mipando yangati ya m’nyumba yoonetseramo kanema, ndipo mutha kukwana anthu 100. Anthu pafupifupi 50 amafika ku misonkhano yonse isanu ya mlungu ndi mlungu.

Ndithudi, akaidi atha kusintha akaphunzira Baibulo. Mofanana ndi mfumu yachiyuda Manase, yomwe itachita machimo aakulu kwambiri n’kugwidwa kukhala m’kaidi ku Babulo, inalapa n’kupempha Mulungu kuti aikhululukire, nawonso akaidi masiku ano angasinthe khalidwe lawo n’kukhala anthu oopa Mulungu.—2 Mbiri 33:12, 13.

[Chithunzi pamasamba 30, 31]

Ubatizo m’ndende

[Chithunzi pamasamba 30, 31]

Atumiki a nthawi zonse ndi alangizi awo pa Sukulu ya Utumiki wa Upainiya m’ndende