Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Mavuto a Kumwa Mowa Mopitirira Muyeso

Mavuto a Kumwa Mowa Mopitirira Muyeso

 Mavuto a Kumwa Mowa Mopitirira Muyeso

KUMWA zakumwa zoledzeretsa kuli ndi zotsatirapo ziwiri. Choyamba ndi chisangalalo, ndipo chachiwiri ndi chisoni. Baibulo limanena kuti kumwa mowa moyenera kumakondweretsa mtima wa munthu. (Salmo 104:15) Komanso, Baibulo lomwelo limachenjeza kuti kumwa mowa mopitirira muyeso kungativulaze kapena kutipha kumene, monga mmene imalumira njoka ya ululu wakupha. (Miyambo 23:31, 32) Tsopano tiyeni tione mavuto amene amabwera chifukwa chomwa mowa mopitirira muyeso.

“Loweruka, dalaivala woledzera anagunda mayi wazaka 25 pamodzi ndi mwana wake wamwamuna wa zaka ziwiri . . . Mayiyo, amene anali ndi pakati pa miyezi isanu ndi umodzi anamwalira Lamlungu. Mwana wakeyo, amene wavulala kwambiri m’mutu, ali mwakayakaya,” inatero nyuzipepala yotchedwa Le Monde. Chomvetsa chisoni n’chakuti, nkhani zoterezi sizachilendo. Mwina mukudziwapo munthu wina amene anali nawo pa ngozi imene inachitika chifukwa chomwa mowa mopitirira muyeso. Chaka chilichonse, anthu ambirimbiri amaphedwa kapena kuvulala pa ngozi za pamsewu zochitika chifukwa cha madalaivala oledzera.

Imfa

Padziko lonse lapansi, kumwa mowa mopitirira muyeso kumabweretsa mavuto osaneneka pa thanzi ndi moyo wa anthu. Ku France, kumwa mowa mopitirira muyeso kuli pamalo achitatu pa zinthu zimene zimapha anthu kwambiri, ndipo kumapha anthu oposa 50,000 pachaka. Ziwiri zoyambirira ndi matenda a khansa ndi matenda a mtima. Ena amafa nthawi yomweyo atangotha kumwa pamene ena amafa ndi matenda obwera chifukwa cha mowawo. Lipoti la Unduna wa Zaumoyo ku France linafotokoza kuti, “chiwerengero chimenechi chingafanane ndi chiwerengero cha anthu amene angamafe ndege ziwiri kapena zitatu zikuluzikulu zonyamula anthu zitamagwa mlungu uliwonse.”

Amene makamaka amafa kwambiri chifukwa cha mowa ndi achinyamata. Malingana ndi lipoti la World Health Organization limene linafalitsidwa mu 2001, akuti mowa ndi umene umapha anyamata ambiri a zaka zapakati pa 15 ndi 29 ku Ulaya. Akuti posachedwapa m’tsogolo muno m’mayiko ena a kummawa kwa Ulaya, kumwa mowa mopitirira muyeso kuzipha mnyamata mmodzi pa anyamata atatu alionse kumeneko.

Chiwawa ndi Kugwirira Akazi

Mowa umachititsanso munthu kuchita zinthu zachiwawa. Munthu akamwa mowa, angamalephere kudziletsa, manyazi angamuthere ndiponso angamalephere kumvetsetsa zochita za ena zimene zikhoza kum’pangitsa kuyamba kuchita zachiwawa.

Anthu ochuluka amene amachita zachiwawa panyumba ndiponso kugwirira akazi, nthawi zambiri amachita zimenezi chifukwa cha mowa. Kafukufuku amene anachitika ku France anasonyeza kuti akaidi ambiri amene anawapeza ndi milandu ya kugwirira kapena kuchitira akazi zachipongwe anachita zimenezo atamwa mowa. Magazini ya Polityka inati kafukufuku amene anachitika ku Poland, anasonyeza kuti akazi 75 mwa akazi 100 alionse amene amuna awo amamwa mowa mwauchidakwa amachitidwa zachiwawa. Bungwe la American Medical Association, Council on Scientific Affairs litachita kafukufuku linati, “chifukwa chomwa mowa mopitirira muyeso, anthu a msinkhu uliwonse amatha kuphedwa mosavuta komanso anthu amene amakhala ndi zidakwa amakhala pangozi yoti akhoza kuphedwa mosavuta.”

 Kubwezera Chitukuko M’mbuyo

Tikawerengera ndalama zimene dziko limawononga popereka chithandizo chamankhwala, inshuwalansi, ndiponso chifukwa cha kusagwira ntchito kwa anthu chifukwa cha ngozi, matenda, ndi imfa zosayembekezereka, timaona kuti kumwa mowa mopitirira muyeso kumabwezera chitukuko m’mbuyo kwambiri. Ku Ireland komwe kuli anthu 4 miliyoni, akuti kumwa mowa mopitirira muyeso kumawonongetsa ndalama zokwana pafupifupi madola wani biliyoni pachaka. Nyuzipepala ya The Irish Times inagwira mawu munthu wina amene anati, ndalama zimenezi n’zofanana ndi “ndalama zimene angagwiritse ntchito kumangira chipatala, sitediyamu, ndi kugulira ndege nduna iliyonse chaka ndi chaka.” Mu 1998, nyuzipepala ya Mainichi Daily News inanena kuti ndalama zimene zimawonongedwa chifukwa cha kumwa mowa kwambiri ku Japan, ndi “zoposa 6 thililiyoni yen [madola 55 biliyoni] pa chaka.” Lipoti lopita ku nyumba ya malamulo ya ku United States linati: “Ndalama zimene zinawonongedwa chifukwa cha kumwa mowa mopitirira muyeso mu 1998 mokha, zinali pafupifupi madola 184.6 biliyoni, zimene mongoyerekezera akanati agawire munthu aliyense wokhala mu United States m’chaka chimenechi, ndiye kuti aliyense akanalandira madola pafupifupi 638.” Ndiyeno palinso mavuto a kusokonezeka maganizo chifukwa cha kutha kwa mabanja kapena kufa kwa wina m’banja, ndiponso kulephera kupitiriza maphunziro kapena kugwira ntchito.

Mavuto amene dziko limakumana nawo chifukwa chomwa mowa mopitirira muyeso n’ngoonekeratu. Kodi kamwedwe kanu ka mowa kakuopseza thanzi lanu kapenanso la ena? Funso limeneli liyankhidwa m’nkhani yotsatirayi.