Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kupulumuka ku Msampha wa Kumwa Mowa Mopitirira Muyeso

Kupulumuka ku Msampha wa Kumwa Mowa Mopitirira Muyeso

 Kupulumuka ku Msampha wa Kumwa Mowa Mopitirira Muyeso

“Bambo anga anali chidakwa, ndipo inenso ndinakhala chidakwa. Pamene ndimafika zaka 12 n’kuti nditayamba kale kumwa. Mmene ndimakwatira, n’kuti ndikuledzera tsiku lililonse. Ndinali munthu wachiwawa; moti apolisi samati abwera liti kudzateteza banja langa. Thanzi langa silinalinso bwino ayi. Mowa unandiyambitsa matenda ochucha magazi m’mimba omwe ndinatsala pang’ono kufa nawo. Kenako ndinayamba kudwala matenda ouma chiwindi ndiponso kutha magazi m’thupi. Ndinalowa nawo m’magulu othandiza anthu kudzithandiza okha kuti mwina ndingasiye kumwa, koma sizinathandize. Ndinkangoona ngati kuti ndagwidwa mu msampha ndipo ndikukanika kuchokamo.”—ANATERO VÍCTOR, * WA KU ARGENTINA.

NKHANI ngati zimenezi zimakambidwa kawirikawiri ndi anthu amene agwidwa mu msampha womwa mowa. Monga Víctor, iwo amadziona kuti agwidwa mu msampha moti sangathenso kuchokamo. Kodi mavuto amene mowa umabweretsa n’ngotheka kuthana nawo kapena kuwapewa kumene? Ngati ndi choncho, zingatheke bwanji?

Kuzindikira Vutolo

Choyamba, pamafunika kuti munthu amene amamwayo ndiponso anthu amene amakhala naye azindikire kuti munthuyo ali ndi vuto. Uchidakwa ndi mbali yochepa chabe ya vuto lalikulu limene munthu womwa mowayo ali nalo. Kuti munthu afike pokhala chidakwa zimatenga nthawi yaitali, ndipo mwina m’mbuyomo akhoza kukhala kuti ankamwa mwachikatikati. Ndipo chodabwitsa n’chakuti anthu ambiri amene amachititsa ngozi, ziwawa, komanso mavuto ena ambiri chifukwa cha mowa, si anthu amene ali zidakwa. Tamvani zimene ananena a bungwe la World Health Organization (WHO). Iwo anati: ‘Njira yabwino yochepetsera mavuto amene amachitika m’dzikoli chifukwa chomwa mowa, ndiyo kuyesa kuchepetsa kamwedwe ka anthu amene amamwa mowa mwachikatikati m’malo molimbana ndi zidakwa.’ Kodi kamwedwe kanu kamapitirira mulingo wovomerezeka ndi azaumoyo? Kodi mumamwa koma mukukonzekera kuchita zinazake zofunika kuti mukhale atcheru kwambiri? Kodi kamwedwe kanu kakubweretsa mavuto m’banja mwanu kapena kuntchito? Ngati mwazindikira kuti kamwedwe kanu sikali bwino, ndiye kuti chinthu chabwino koposa chimene mungachite ndicho kuchepetsa kamwedweko moyenerera kuti mupewe mavuto amene angabwere m’tsogolo. Munthu akangoti wafika pokhala chidakwa, kusintha kumakhala kovuta kwambiri.

Vuto la anthu ambiri amene amamwa mowa mopitirira muyeso ndilo kukana kuti ali ndi vuto. Iwo amanena kuti: “Ndimamwa monga mmene aliyense amamwera” kapena “Ndimatha kusiya kumwa panthawi iliyonse imene ndafuna.” Konstantin wa ku Russia anati: “Ngakhale kuti mowa unatsala pang’ono kundipha, sindinkaona ngati kuti ndafika pauchidakwa, chotero panalibe chilichonse chimene ndimachita kuti ndisiye.” Ndipo Marek wa ku Poland anati: “Ndinakhala ndikuyesetsa maulendo ambirimbiri kuti ndisiye kumwa,  koma ndinkakana kuvomera kuti ndine chidakwa. Ndinkawachepetsa kwambiri mavuto obwera chifukwa cha mowa.”

Kodi munthu angathandizidwe bwanji kuzindikira kuti ali ndi vuto lakumwa, kuti pambuyo pake achitepo kanthu? Choyamba, munthuyo ayenera kuvomereza kuti mavuto amene akukumana nawo akubwera chifukwa cha kumwa mowa mopitirira muyeso ndiponso kuti ngati atasiya kumwa zingamuthandize kuti akhale ndi moyo wabwino. Monga mmene linafotokozera buku lotchedwa La Revue du Praticien—Médecine Générale, munthu ayenera kusintha maganizo ake, kuchoka poganiza kuti “ndimamwa chifukwa chakuti mkazi wanga anathetsa banja ndiponso chifukwa choti ntchito inandithera,” n’kuyamba kuganiza kuti “mkazi wanga anathetsa banja ndiponso ntchito inandithera chifukwa chomwa mowa.”

Ngati mukufuna kuthandiza munthu amene ndi chidakwa kuti ayambe kuganiza mwanjira imeneyi, mungachite bwino kutsatira mfundo zotsatirazi: Mvetserani mwatcheru, m’funseni mafunso amene angamuthandize kufotokoza momasuka maganizo ake ndiponso mmene akumvera, sonyezani kuti ndinu munthu wachifundo, zimene zingamuthandize kuzindikira kuti mukumumvetsa, mulimbikitseni ngakhale ngati pali kusintha kochepa chabe, pewani maganizo oweruza kapena kuchita zinthu zimene zingamulepheretse kufotokoza zakukhosi kwake ndiponso kufuna thandizo. Kungakhalenso kothandiza kwambiri kum’pempha kuti alembe m’ndandanda wa mayankho a mafunso awa: Kodi chingachitike n’chiyani ngati nditapitiriza kumwa mowa? ndi Kodi chingachitike n’chiyani ngati nditasiya kumwa mowa?

Kufunafuna Thandizo

Munthu akayamba kumwa mowa mopitirira muyeso, sizitanthauza kuti basi watha ntchito kapena kuti palibenso chilichonse chimene angachite. Ndipo ena amatha kusiya paokha popanda wina kuwathandiza. Komabe, anthu omwe ndi zidakwa angafunike thandizo la dokotala kuti asiye. * Kwa anthu ena, kuchita kuyendera kupita kuchipatala kukapeza thandizo kumatha kukhala kothandiza, koma ngati mavuto obwera chifukwa chosiya mowa akula, ndiye kuti kugonekedwa m’chipatala kungakhale kothandiza. Mavuto oyambirira obwera chifukwa chosiya kumwa akatha, mwina pambuyo pa masiku awiri kufika asanu, angakupatseni mankhwala oti muzikamwa ochepetsa chilakolako chofuna mowa ndiponso okuthandizani kuti musakamwenso.

Sikuti mabungwe opereka thandizo amathandiza kuthetseratu mavuto onse obwera chifukwa cha uchidakwa. Mankhwala amene angakupatseni amakhala thandizo lakanthawi chabe osati lochiziratu. Alain wa ku France, analandirapo thandizo losiyanasiyana maulendo angapo. Iye anati: “Ndinkangoti ndikachoka kuchipatala, nthawi yomweyo ndinkayambiranso kumwa chifukwa ndinali kukachezanso ndi anzanga omwe ndinkamwa nawo. Kwenikweni, ndinganene kuti ndinalibe cholinga chenicheni chofuna kusiya.”

Kupeza Zolowa M’malo

Anthu ambiri amalephera kusiya mowa chifukwa akasiya amaona ngati tsopano alibe chochita, zomwe tikhoza kuziyerekezera ndi kusiyana ndi bwenzi la pamtima. Vasiliy, wa ku Russia anati: “Nthawi zonse ndinkangoganiza zomwa mowa. Ngati tsiku ladutsa osamwa, ndinkangoona kuti palibe chimene ndachita tsiku limenelo.” Munthu amene ndi chidakwa amaona kuti zinthu zina zonse n’zosafunika kwenikweni poziyerekezera ndi chilakolako chake chofuna kumwa mowa. Jerzy wa ku Poland anati: “Ntchito yanga yaikulu pamoyo inali kumwa ndi kufunafuna ndalama zoti ndikamwere.” Choncho, ndi bwino kuti munthu amene wasiya kumwa mowa apeze chochita china m’moyo kuti apitirizebe kukhala wosamwa.

Buku limene lili ndi malangizo kwa anthu amene akuyesa kusintha kamwedwe kawo ka mowa lofalitsidwa ndi a bungwe la WHO limafotokoza kufunika kochita zinthu zina zaphindu kuti munthu apewe kuyambiranso kumwa. Mfundo imene anaitchula monga chitsanzo ndiyo kuchita zinthu zachipembedzo.

Kukhala wotanganidwa ndi zinthu zauzimu kukhoza kum’thandiza munthu kuthetsa chilakolako cha mowa chimene amakhala nacho. Mwachitsanzo, Alain anayamba kuphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova paulendo wake wachitatu wokhala m’ndende chifukwa cha zimene anachita atamwa mowa. Iye anati: “Kuphunzira Baibulo kunandipatsa cholinga m’moyo ndipo kunandithandiza kuti ndisayambirenso kumwa  mowa. Cholinga changa sichinali kungofuna kusiya kumwa mowa ayi, koma kusangalatsa Yehova.”

Kuthana ndi Vuto Loyambiranso Kumwa

Alangizi a anthu amene amamwa mowa mopitirira muyeso, amafotokoza za ubwino wothandiza ndi kulimbikitsa anthu amene asiya uchidakwa. Ambiri amakhala oti banja linawathera ndiponso alibe mabwenzi chifukwa cha khalidwe lawo loipali. Chifukwa chokhala okha, akhoza kuyamba kuvutika maganizo ndiponso mwina kudzipha kumene. Buku la malangizo limene talitchula kale lija limapereka malangizo otsatirawa kwa anthu amene akuthandiza munthu amene ali ndi vuto lomwa mowa: “Yesetsani kuti musamuimbe mlandu munthu amene mukumuthandizayo ngakhale ngati mutanyansidwa kapena kukhumudwa ndi zochita zake. Kumbukirani kuti kusintha chizolowezi si nkhani yophweka ayi. Masiku ena angachite bwino ndipo masiku ena sangachite bwino. Kumulimbikitsa ndiponso kumuthandiza kuti azingomwa pang’ono kapena kusiyiratu kumwa ndiponso malangizo ena n’zofunika.”

Hilario amene anakhala akumwa mowa kwa zaka 30 anati: “Chimene chinandithandiza chinali chikondi ndiponso chisamaliro cha mabwenzi anga a mu mpingo wathu wa Mboni za Yehova. Nthawi zambiri ndinkayambiranso kumwa, koma mabwenzi anga amumpingo sankandithawa, ndipo anali kundilimbikitsa ndiponso kundipatsa malangizo apanthawi yake a m’Baibulo.”

Ngati mukulimbana ndi kusiya kumwa mowa, kumbukirani kuti mungayembekezere kuti nthawi zina muziyambiranso kumwa ndipo zimenezi muyenera kuziona ngati mbali ya kuyesayesa kwanu kusiya kumwa. Musataye mtima! Fufuzani ndi kupeza chimene chinakupangitsani kuti mumwenso, ndipo gwiritsani ntchito zimene mwapezazo kuti zikuthandizeni kudzapewa kumwa m’tsogolo. Dziwani zinthu zimene zimakuyambitsani kufuna kumwa. Kodi kapena kungakhale kusowa chochita, kuvutika maganizo, kusungulumwa, mikangano, nkhawa, kapena zochitika kapenanso malo amene anthu ena amamwera mowa? Ngati ndi choncho, pewani zinthu zimenezi! Jerzy, amene zinamutengera zaka ziwiri kuti asiyiretu kumwa mowa anati: “Ndinaphunzira kuzindikira ndiponso kutulukira zinthu zimene zikhoza kundipangitsa kuti ndimwe. Panopa ndimapewa chilichonse chimene chingandiyambitsenso kumwa. Sindiyandikira malo amene anthu amamwera mowa. Sindidya chilichonse chimene asakaniza ndi mowa, ndipo ndimapewanso ngakhale zodzoladzola kapena mankhwala amene pokonza amaphatikizako mowa. Sindiyang’ananso zithunzi zilizonse zotsatsira malonda a mowa.” Ambiri aona kuti kupemphera kwa Mulungu kuti awapatse ‘mphamvu’ yoposa yachibadwa chakhala chinthu chothandiza kwambiri kuti asayambirenso kumwa.—2 Akorinto 4:7; Afilipi 4:6, 7.

Kumasuka

Ngakhale kuti vutoli likhoza kumapitirirabe, n’zotheka kuti munthu achoke mu msampha wa uchidakwa. Anthu onse amene tawatchula mu nkhani ino, anakwanitsa kusiya uchidakwa. Tsopano ali ndi thanzi labwino ndipo akuimba lokoma limodzi ndi mabanja awo ndiponso kuntchito kwawo. Alain anati: “Tsopano ndamasuka ku msampha wauchidakwa.” Konstantin ananena kuti: “Kudziwa Yehova kwateteza banja langa. Tsopano ndili ndi cholinga m’moyo. Kuti ndikhale wachimwemwe sizikudaliranso kumwa mowa.” Víctor anathirirapo ndemanga kuti: “Ndimadziona monga munthu amene wamasuka. Ulemu wanga wabwereranso.”

Munthu akhoza kusintha, kaya vuto lake likhale loti akhoza kuchita ngozi chifukwa chomwa mowa kwambiri, kapena wafika poti akuvutika chifukwa chomwa mowa mopitirira muyeso, kapenanso wafika pokhala chidakwa. Ngati kamwedwe kanu kakukubweretserani mavuto, musachedwe kuchitapo kanthu. Kuchita zimenezi kungathandize inuyo ndiponso anthu amene amakukondani.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 2 Mayina ena asinthidwa.

^ ndime 10 Kuli zipatala ndiponso mabungwe ambirimbiri amene angakuthandizeni. Mboni za Yehova sizilangiza anthu kuti atsatire njira yakutiyakuti yolandirira thandizo. M’pofunika kusamala kuti munthu asadzilowetse mu zochitika zimene zili zosemphana ndi mfundo za m’Malemba. Aliyense ayenera kudzisankhira yekha thandizo limene angafunikire akaganizira mfundo zonse zofunika.

[Chithunzi patsamba 10]

Kuvomereza vuto lanu ndiye chiyambi cholithetsera

[Chithunzi patsamba 11]

Ambiri amafunika thandizo la dokotala kuti asiye kumwa mowa

[Chithunzi patsamba 12]

Pemphero lingakuthandizeni

[Chithunzi patsamba 12]

Mukhoza kukana!