Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Amasangalala Ngakhale Kuti Sachita Khirisimasi

Amasangalala Ngakhale Kuti Sachita Khirisimasi

PALI Akhristu ambiri amene sakondwerera Khirisimasi. Kodi iwo amaona kuti akumanidwa kanthu kena? Kodi ana awo amasirira akaona anzawo akusangalala pa Khirisimasi? Taonani zimene a Mboni za Yehova osiyanasiyana ananena pa nkhaniyi.

Kukumbukira Yesu Khristu: “Ndisanakhale wa Mboni za Yehova ndinkangopita kutchalitchi pa Khirisimasi ndi pa Isitala pokha. Komanso ngakhale ndinkapita pa nthawiyi, sindinkaganiza za Yesu Khristu. Panopa sindikondwereranso Khirisimasi koma ndimapita kumisonkhano ya mpingo kawiri mlungu uliwonse komanso ndimaphunzitsa ena zimene Baibulo limanena zokhudza Yesu.”—EVE, AUSTRALIA.

Kupatsana mphatso: “Ndimasangalala kwambiri munthu akandipatsa mphatso pa nthawi yomwe sindikuyembekezera. Ndimakondanso kuwapangira anthu makadi ndi zithunzi chifukwa zimachititsa kuti anthuwo komanso ineyo tisangalale.”—REUBEN, NORTHERN IRELAND.

Kuthandiza osowa: “Timakonda kuwaphikira chakudya anthu amene akudwala. Nthawi zina timawapatsanso maluwa, keke kapena mphatso inayake ndipo iwo amasangalala. Zimenezi zimatisangalatsa chifukwa timatha kuzichita nthawi iliyonse osati pa Khirisimasi pokha.”—EMILY, AUSTRALIA.

Kukachezera achibale: “Tikakumana pachibale pathu, ana athu amadziwana ndi amalume awo, azakhali, agogo komanso asuwani awo ndipo zimakhala zosangalatsa kwambiri. Popeza timadziwa kuti tingathe kukachezera achibale nthawi iliyonse osati pa Khirisimasi pokha, sitipanikizika ndipo achibale athu amadziwa kuti timawachezera chifukwa chowakonda.”—WENDY, CAYMAN ISLANDS.

Kukhala mwamtendere: “Pa nthawi ya Khirisimasi anthu amakhala otanganidwa kwambiri moti sakhalanso ndi nthawi yoganizira zimene angachite kuti azikhala mwamtendere ndi ena. Koma ineyo ndinaphunzira zimene Baibulo limalonjeza zokhudza anthu, choncho zimenezi zimandipangitsa kukhala ndi mtendere wamumtima. Tsopano ndimaona kuti ana anga ali ndi tsogolo labwino.”—SANDRA, SPAIN.