Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mumakhulupirira Kuti Musanabadwe Munakhalapo ndi Moyo Kwinakwake?

Kodi Mumakhulupirira Kuti Musanabadwe Munakhalapo ndi Moyo Kwinakwake?

“Munthu akafa amabadwanso chinthu china. Anthu amene ali ndi moyo panopa analipo kale kwinakwake ndipo atafa kumeneko anadzabadwanso. Mizimu ya anthu imapitirizabe kukhala ndi moyo anthuwo akamwalira.”—PLATO, KATSWIRI WA NZERU ZA ANTHU WA KU GREECE, 400 B.C.E., ANAGWIRA MAWU A “SOCRATES.”

“Ngakhale kuti mzimu si thupi, sungathe kukhala pawokha popanda thupi. Choncho thupi likamafa, umatulukamo n’kukalowa m’thupi la munthu wina pamene munthuyo akubadwa.”—GIORDANO BRUNO, KATSWIRI WA NZERU ZA ANTHU WA KU ITALY, 1500 C.E.

“Munthu samafa. Amangooneka ngati wafa . . . koma amakhala ali bwinobwino, kungoti amapitiriza kukhala ndi moyo m’thupi lina ndipo akamaona zinthu m’dzikoli amangoona ngati akuzionera pawindo chifukwa amakhala atabadwanso ndi thupi lina.”—RALPH WALDO EMERSON, WOLEMBA NKHANI NDI NDAKATULO WA KU AMERICA, 1800 C.E.

KODI munayamba mwadzifunsapo kuti munali kuti poyamba? Kapena kodi munaganizapo kuti mwina musanabadwe munakhalapo ndi moyo kwinakwake? Anthu ambiri amakhala ndi maganizo amenewa. Kuyambira kalekale anthu osiyanasiyana akhala akudzifunsa mafunso oterewa. Pofufuza mayankho a mafunsowa, anthu ena anayamba kukhulupirira kuti munthu akamwalira amakabadwanso kwinakwake. Iwo amakhulupirira kuti munthu akafa, “mzimu” wake umatuluka m’thupi lake n’kukabadwanso mwa munthu, nyama kapena chomera ndipo zimenezi zimachitika mobwerezabwereza.

 Ngakhale kuti anthu ena amakhulupirira zimenezi, kodi ndi zoonadi kuti munthu akamwalira amakabadwanso kwinakwake? Kodi Mawu a Mulungu, Baibulo, amati chiyani pa nkhaniyi? Komabe, tiyeni tikambirane kaye mmene chikhulupiriro chimenechi chinayambira.

Kodi Chikhulupiriro Chakuti Munthu Akamwalira Amakabadwanso Kwina Chinayamba Bwanji?

Akatswiri a mbiri yakale komanso akatswiri a maphunziro amanena kuti anthu a mumzinda wa Babulo, umene unamangidwa zaka 2,000 Khristu asanabadwe, anayamba kukhulupirira kuti munthu ali ndi mzimu umene suufa munthuyo akamwalira. Munthu wina, dzina lake Morris Jastrow, Jr., analemba m’buku lake kuti, “Akatswiri a maphunziro a zachipembedzo a ku Babulo ndiwo anayambitsa chikhulupiriro choti munthu akamwalira mzimu wake suufa.” Morris analembanso kuti Ababulo ankaona kuti: “Imfa ndi njira yopita ku moyo wina. Iwo anayambitsa chikhulupiriro chimenechi chifukwa chakuti sankakhulupirira kuti munthu akamwalira, mzimu wakenso umafa.”—The Religion of Babylonia and Assyria.

Ababulo atayamba kukhulupirira zimenezi, kenako anthu enanso m’madera osiyanasiyana padziko lapansi anayambanso kukhulupirira kuti munthu akafa amakabadwanso kwina. Mwachitsanzo, akatswiri a nzeru za anthu a ku India anayamba kukhulupirira kuti zochita za munthu zimakhudza mmene munthuyo adzakhalire akadzabadwanso kwina. Nawonso akatswiri a nzeru za anthu a ku Greece anayamba kukhulupirira kuti munthu akafa amakabadwanso kwina ndipo zimenezi zinachititsa kuti chikhulupirirochi chifalikire.

M’nthawi yathu ino, anthu ambiri a kumayiko a azungu anayamba kuchita chidwi ndi chikhulupiriro chimenechi. Anthu otchuka komanso achinyamata ndi amene akukopeka kwambiri ndi chikhulupirirochi. Masiku ano pali mabuku ambiri komanso Mawebusaiti amene amafotokoza za anthu amene amati anali ndi moyo kwinakwake asanabadwe moyo uno. M’mayiko ambiri muli madokotala amene amagonetsa anthu n’cholinga choti adziwe zimene amati zinamuchitikira munthuyo asanabadwe moyo uno. Iwo amachita zimenezi poyesa kufufuza zimene zili mu ubongo wa anthuwo ndipo amafuna kuona mmene zimenezo zikukhudzira thanzi komanso khalidwe la anthuwo panopa.

Kodi N’zoona Kuti Munthu Akafa Amakabadwanso Kwina?

Ngakhale kuti chikhulupiriro chakuti munthu akafa amakabadwanso kwinakwake chinayamba kalekale, m’pofunika kudziwa ngati chili choona. Komanso Akhristu ayenera kudziwa ngati chikhulupiriro chimenechi n’chogwirizana ndi zimene Baibulo limanena. (Yohane 17:17) Popeza Mlengi wathu, Yehova Mulungu, ndi amene anayambitsa moyo ndiponso ndi “Woulula zinsinsi,” iye amatiuza zinthu zokhudza moyo komanso imfa zimene akanapanda kutiuza sitikanazidziwa. Choncho tili ndi chikhulupiro choti Mawu ake, Baibulo, angatithandize kupeza yankho pa nkhaniyi.—Danieli 2:28; Machitidwe 17:28.

Tingapeze mosavuta zimene Mulungu amanena pa nkhani imeneyi ngati titaphunzira zimene Baibulo limaphunzitsa. Mwachitsanzo, pa Genesis 3:19 pali mawu amene Mulungu anauza Adamu, Adamuyo ndi Hava atachimwa. Mulungu anati: “Udzadya chakudya kuchokera m’thukuta la nkhope yako mpaka utabwerera kunthaka, pakuti n’kumene unatengedwa. Popeza ndiwe fumbi, kufumbiko udzabwerera.” Popeza Mulungu analenga Adamu kuchokera kufumbi, mawu akewa anali osavuta kumva. Choncho munthu akamwalira, sikuti amakabadwanso kwina koma amathera pomwepo. * Monga mmene zilili kuti kutentha n’kosiyana ndi kuzizira ndipo kuwala n’kosiyana ndi mdima, n’chimodzimodzinso moyo ndi imfa n’zosiyana. Munthu akafa ndiye kuti salinso ndi moyo. Zimenezitu n’zosavuta kumvetsa.

Choncho payenera kukhala zinthu zina zimene zimachititsa anthu ena kuganiza kuti akukumbukira zomwe amati zinawachitikira poyamba asanabadwe moyo uno. Zinthu monga zotsatira za mankhwala amene munthu wamwa, zinthu zoipa zimene zinachitika pa moyo wa munthu kapenanso mmene ubongo umagwirira ntchito, zingayambitse zinthu zimene ngakhale madokotala sanazimvetsebe. Maloto komanso zinthu zimene timaona ngati zikuchitikadi zochokera mu ubongo wathu, womwe muli zinthu zambirimbiri, zingamaoneke ngati zenizeni. Nthawi zinanso ziwanda zimapanga zinthu zamatsenga zimene zimachititsa kuti zinthu zoti sizingachitike, zizioneka ngati zachitikadi.—1 Samueli 28:7-19.

Mwachibadwa palibe munthu amene amafuna kufa,  koma aliyense amafuna kudziwa za tsogolo lake. Koma kodi n’chifukwa chiyani anthufe sitifuna kufa? N’zochititsa chidwi kuti Baibulo limanena za Mlengi kuti: “Anapatsa anthu mtima wofuna kukhala ndi moyo mpaka kalekale.” (Mlaliki 3:11) Choncho n’chifukwa chake anthu safuna kufa ndipo amafuna kukhala ndi moyo kwamuyaya.

Ngati Mlengi wathu, Yehova Mulungu, anatipatsa mtima wofuna kukhala ndi moyo mpaka kalekale, ndiye kuti anayenera kutiuzanso zimene tingachite kuti zimenezi zitheke. Baibulo limatiuza kuti Mlengi adzadalitsa anthu omvera powapatsa moyo wosatha m’paradaiso padziko lapansi. Mulungu anauza Mfumu Davide kulemba kuti: “Olungama adzalandira dziko lapansi, ndipo adzakhala mmenemo kwamuyaya.” (Salimo 37:29) Mfundo ya m’Baibulo imene imagwirizana ndi cholinga cha Mulungu choti anthu adzakhale kosatha, ndi yakuti akufa adzauka.—Machitidwe 24:15; 1 Akorinto 15:16-19.

Akufa Adzaukadi

M’Baibulo muli nkhani za anthu 8 amene anaukitsidwa n’kukhalanso ndi moyo padziko lapansi ndipo anthu ambiri anaona zimenezi. * Anthu amenewa anaukitsidwa, osati anachita kubadwanso kuchokera ku moyo wina. Anthuwa ataukitsidwa, abale komanso mabwenzi awo anawazindikira mosavuta. Palibe achibale amene anapita n’kumakafunafuna tiana tobadwa kumene tam’dera lawo kapena takutali kuti aone ngati tianato tinali abale awo amene anamwalira.—Yohane 11:43-45.

N’zolimbikitsa kudziwa kuti Mawu a Mulungu amasonyeza kuti anthu ambiri amene anamwalira adzaukitsidwa m’dziko limene Mulungu walonjeza. Dziko limeneli libwera posachedwapa ndipo lidzalowa m’malo mwa dziko loipali. (2 Petulo 3:13, 14) Yehova Mulungu akukumbukira anthu ambirimbiri amene anamwalira ndiponso zonse zokhudza anthuwo. Izi zili choncho chifukwa iye amatha kudziwa mayina a nyenyezi zonse. (Salimo 147:4; Chivumbulutso 20:13) Yehova akadzaukitsa anthu onse amene anamwalira m’mibadwo yosiyanasiyana, anthuwo adzatha kudziwa achibale awo komanso azigogo awo. Zimenezitu n’zosangalatsa kwambiri.

^ ndime 13 Kuti mudziwe zambiri, werengani mutu 6 wakuti “Kodi Akufa Ali Kuti?” m’buku lakuti Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.

^ ndime 18 Nkhani za anthu 8 amenewa zimapezeka pa 1 Mafumu 17:17-24; 2 Mafumu 4:32-37; 13:20, 21; Luka 7:11-17; 8:40-56; Yohane 11:38-44 ndi Machitidwe 9:36-42; 20:7-12. Mukamawerenga nkhani zimenezi, muona kuti panali anthu amene anaona anthuwa akuukitsidwa. Munthu wa 9 amene anaukitsidwa anali Yesu Khristu.—Yohane 20:1-18.