Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 Phunzitsani Ana Anu

Yotamu Anakhalabe Wokhulupirika Bambo Ake Atasiya Kutumikira Yehova

Yotamu Anakhalabe Wokhulupirika Bambo Ake Atasiya Kutumikira Yehova

BAMBO kapena mayi akasiya kutumikira Yehova Mulungu, zimakhala zovuta kwa mwana. Tiye tikambirane zimene zinachitikira Yotamu. Tiona mavuto amene iye anakumana nawo ali mwana.

Uziya, yemwe anali bambo ake a Yotamu, anali mfumu ya Yuda. Iye anali ndi mphamvu m’dzikolo kuposa aliyense. Poyamba Uziya anali mfumu yabwino kwa zaka zambiri ngakhale pa nthawi imene Yotamu anali asanabadwe. Koma kenako, Yotamu ali mwana, Uziya anayamba kunyada ndipo anasiya kutsatira Chilamulo cha Mulungu. Choncho Mulungu anamulanga ndi matenda oopsa akhate. Kodi ukudziwa zomwe Yotamu anachita zimenezi zitachitika? *

Zinali zovuta kwa Yotamu kuti akhalebe wokhulupirika kwa Yehova, Uziya bambo ake, atasiya kukhala wokhulupirika. Koma iye anapitirizabe kutumikira Yehova. Mwina mayi ake, dzina lawo a Yerusa, ndi amene anamuthandiza.

Kodi iweyo ungatani bambo ako kapena mayi ako atasiya kutumikira Yehova? Zimenezitu zingakhale zovuta kwambiri, si choncho?— Komabe sikulakwa kuganiza kuti zimenezi zingachitike. Umboni wakuti sikulakwa kuganiza zimenezi ndi zomwe Davide analemba m’Baibulo.

Jese, yemwe anali bambo ake a Davide, anali munthu wabwino kwambiri. Iye ankatumikira Yehova ndipo n’zodziwikiratu kuti Davide ankawakonda bambo akewa. Koma Davide anaphunzira kukonda kwambiri Yehova kuposa mmene ankakondera bambo ake. Tiye tione chifukwa chake tikutero.

 Tsegula Baibulo lako tiwerenge lemba la Salimo 27:10. Davide analemba kuti: “Ngakhale bambo anga ndi mayi anga atandisiya, Yehova adzanditenga.” Lembali likusonyeza kuti Davide ankaona kuti ngakhale bambo ake kapena mayi ake akanasiya kutumikira Yehova, iyeyo akanapitirizabe kumutumikira.

Kodi iweyo ungapitirize kutumikira Yehova bambo kapena mayi ako atasiya kumutumikira?— Uyenera kudzifunsa funso limeneli chifukwa ndi logwirizana ndi lamulo lalikulu la m’Baibulo. Lamuloli ndi lakuti: “Uzikonda Yehova Mulungu wako ndi mtima wako wonse, moyo wako wonse, ndi maganizo ako onse.”

Lamulo limeneli limatanthauza kuti tiyenera kukhalabe okhulupirika kwa Yehova ngakhale pamene zinthu zavuta. Kodi ukuganiza kuti ndi ndani yemwe amafuna kuti tisiye kutumikira Yehova?— Ndi Satana Mdyerekezi, yemwe ndi mdani wa Mulungu. Yesu ananena kuti Satana ndi “wolamulira wa dzikoli.” Baibulo limanenanso kuti iye ndi “mulungu wa nthawi ino.” Koma kodi tiyenera kuopa Satana?

Ayi, sitiyenera kumuopa. Tiyenera kukumbukira kuti Yehova ndi wamphamvu kwambiri kuposa Satana. Tikakhulupirira Yehova, iye adzatiteteza. Werenga m’Baibulo lako kuti uone mmene Yehova anatetezera Davide kwa Goliyati yemwe anali chiphona chochititsa mantha. Iwenso Yehova angakuteteze ngati utakhalabe wokhulupirika kwa iye.

^ ndime 4 Ngati mukuwerenga nkhaniyi ndi mwana, mukapeza mzera muime kaye ndi kumulimbikitsa kuti anenepo maganizo ake.