Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 Kalata Yochokera ku Benin

Koma Ndikwanitsadi?

Koma Ndikwanitsadi?

IKAKHALA nyengo yotentha, ku Benin, kumene ndi kumadzulo kwa Africa, dzuwa limayamba kutentha kudakali m’mawa. Nthawi zambiri kukacha, sulephera kumva kafungo ka zakudya monga mpunga wophika ndi zina zotero. Umaona azimayi ambiri atadendekera katundu pamitu yawo. Kumamvekanso phokoso la anthu akuseka komanso akunenerera malonda.

Ana atationa, anayamba kuimba kanyimbo kawo n’kumavina. Iwo ankakuwa kuti, azungu! azungu! ndipo kenako anatiuza kuti tiwapatse ndalama chifukwa choti avina. Koma panali mnyamata mmodzi amene sankaimba nawo. Kenako mnyamatayu anayamba kunditsatira n’kumandilankhula ndi manja. Ndili ku America, ndinaphunzira chinenero chamanja cha ku America, koma ku Benin amalankhula Chifulenchi.

Ndinayesetsa kumuuza dzina langa m’chinenero chamanja. Nditatero mnyamatayu anamwetulira. Nthawi yomweyo anandigwira dzanja n’kuyamba kupita nane kwawo. Nditafika kumeneko ndinapeza kuti amakhala m’kanyumba kachipinda chimodzi ndipo anthu ambiri a m’derali amakhala m’nyumba zoterezi. Achibale ake atationa anabwera pafupi. Onse ankalankhula chinenero chamanja. Ndinayamba kuda nkhawa kuti ndilankhula nawo bwanji anthu amenewa. Ndinayesetsa kuwauza dzina langa m’chinenero chamanja ndipo kenako ndinawalembera papepala kuwauza kuti ndine mmishonale ndipo ndimaphunzira ndi anthu Baibulo. Ndinawalemberanso kuti ndidzabweranso nthawi ina kudzawachezera. Panabweranso anthu ena akumva amene ankakhala nyumba zapafupi ndipo onsewo anasangalala. Koma ndinayamba kudzifunsa kuti, ‘Koma ndikwanitsadi kuwaphunzitsa Baibulo anthu amenewa?’

Nditabwerera kunyumba, ndinayamba kuganiza kuti zingakhale bwino patapezeka munthu wina woti awathandize kudziwa zimene Mulungu analonjeza monga zoti: “Makutu a anthu ogontha adzayamba kumva.” (Yesaya 35:5) Ndinafufuza kuti ndidziwe chiwerengero cha anthu osamva amene ali m’dzikoli. Ndinapeza kuti kafukufuku waposachedwapa anasonyeza kuti ku Benin kuli anthu osamva okwana 12,000. Mtima wanga unakhala m’malo nditamva kuti anthu osamva a m’dzikoli amaphunzitsidwa chinenero chamanja cha ku America osati chachifulenchi. Koma ndinamva chisoni kwambiri nditamva kuti palibe wa Mboni za Yehova aliyense amene amadziwa chinenero chamanja cha ku America. Ndinauza mayi wina wa Mboni kuti: “Zikanakhala bwino munthu wina wodziwa chinenero chamanja akanabwera kuno kudzawaphunzitsa anthuwa.” Koma iye anandiyankha kuti: “Inuyo simulipo, athandizeni.” Ananenadi zoona. Ndinaitanitsa buku lothandiza kuphunzira chinenero chamanja cha ku America komanso ma DVD amene amapangidwa ndi Mboni za Yehova. Pemphero langa  linayankhidwa pamene wa Mboni wina wodziwa chinenero chamanja cha ku America anabwera m’dzikoli kuchokera ku Cameroon.

Anthu ambiri anamva zoti ndikuphunzira chinenero chamanja. Anthu ena anandiuza kuti ndikaonane ndi munthu wina wosamva, dzina lake Brice, yemwe anali ndi shopu yazopentapenta. Shopuyi inapangidwa ndi masamba a mtengo wakanjedza ndipo pa nyengo yotentha inkazizira bwino. Chifukwa choti nthawi zambiri akafuna kupukuta mabulashi ake, ankapukutira kumakoma a shopuyi, makomawa anali ndi mitundu yosiyanasiyana ya penti. Nditafika, iye anandipatsa kampando ndipo nayenso anakhala pampando n’kumadikira kuti ndifotokoze zimene ndabwerera. Ndinaika DVD kuti iye aone zimene ndabwerera ndipo anayandikira pafupi kuti azitha kuona bwinobwino. Atayamba kuonera, anandiuza m’chinenero chamanja kuti akumva zimene ankaonazo. Panabweranso ana ambiri akuderali ndipo ankasuzumira kuti aone. Mwana wina anafuula kuti: “N’chifukwa chiyani anthuwa akuonera filimu yopanda mawu?”

Nthawi iliyonse imene ndapita kwa Brice, kunkabwera anthu ambiri kudzaonera DVD. Posapita nthawi Brice ndiponso anthu ena anayamba kusonkhana ndi Mboni za Yehova. Popeza kuti ndinkawamasulira zimene zikunenedwa, zinapangitsa kuti ndichidziwe bwino chinenero chamanjachi. Pamene gululi linakula, ena anayamba kumachita kunditsatira kuti ndiwaphunzitse. Mwachitsanzo, tsiku lina galimoto yanga inkalira modabwitsa chifukwa cha maenje amene ndinaponda pomwe ndinkapewa kuti ndisagunde mbuzi ndi nkhumba. Kenako ndinamva phokoso kumbuyo kwa galimoto yanga. Ndinaganiza kuti mwina galimoto yanga yawonongeka. Koma nditayang’ana, ndinaona kuti anali munthu wina wosalankhula amene ankandithamangira n’kumamenya kumbuyo kwa galimotoyo pofuna kundiimitsa.

Timagulu ta chinenero chamanja cha ku America tinakhazikitsidwa m’mizinda inanso. Pamene anakonza zoti pamisonkhano ikuluikulu pazimasuliridwa nkhani m’chinenero chamanja, ineyo ndinali mmodzi mwa anthu amene anasankhidwa kuti azimasulira. Tsiku loyamba nditafika papulatifomu, n’kumadikirira kuti wokamba nkhani ayambe kulankhula, ndinayamba kukumbukira zimene ndinkaganiza nditangoyamba kumene ntchito yanga yaumishonale. Nthawi zonse ndinkaganiza kuti, ‘Monga mmishonale, kodi ndi zinthu zinanso ziti zimene ndingachite ku Africa kuno?’ Choncho nditayang’ana omverawo ndinaona kuti tsopano ndapeza yankho la funso langali. ‘Monga mmishonale, ndiyenera kuthandizanso anthu osamva.’ Masiku ano sindimadzifunsanso kuti, ‘Koma ndikwanitsadi?’