Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Zodzoladzola Zimene Anthu Akale Ankagwiritsa Ntchito Podzikongoletsa

Zodzoladzola Zimene Anthu Akale Ankagwiritsa Ntchito Podzikongoletsa

Akazi akamaliza kusamba, ankadzola mafuta onunkhira. Akatero ankatsegula bokosi limene munkakhala timabotolo topangidwa ndi galasi, minyanga ya njovu, zigoba za nkhono kapena miyala. M’timabotoloti munkakhala mafuta odzikongoletsera a basamu, sinamoni, lubani, uchi, mule ndi zina zotero.

M’bokosimo munkakhalanso zinthu zina monga timasupuni komanso timbale tolowa ndi tosalowa. Akazi ankagwiritsa ntchito zinthu zimenezi kusakaniza zodzikongoletsera zimene akufuna kudzola pa tsikulo. Akatero ankadziyang’anira pagalasi kuti aonetsetse kuti atsatira zonse zofunika podzola mafutawa.

ZIKUONEKA kuti kuyambira kale kwambiri, akazi amakonda kudzikongoletsa ndi zinthu zosiyanasiyana kuti azioneka bwino. Zinthu monga zolembedwa pamanda akale, zojambula m’makoma komanso tiziboliboli timene ankaika pakhoma zimasonyeza kuti anthu ambiri a ku Mesopotamia ndi Iguputo ankagwiritsa ntchito zodzikongoletsera. Panalinso zithunzi zosonyeza akazi a ku Iguputo atakongoletsa maso awo n’kumaoneka ngati kamtedza ka zipatso za amondi ndipo zithunzi zimenezi zinali zokongola kwambiri.

Nanga bwanji akazi achiisiraeli, kodi nawonso ankadzikongoletsa? Ngati ankadzikongoletsa, kodi ankagwiritsa ntchito zinthu ziti? Ku Isiraeli sikunapezeke zinthu monga zolembedwa pamanda akale ndiponso zojambula m’makoma zimene zingatithandize kudziwa zimene Aisiraeli akale ankagwiritsa ntchito podzikongoletsa. Komabe nkhani zina za m’Baibulo komanso zinthu zimene zinafukulidwa pansi ku Isiraeli zingatithandize kudziwa zodzikongoletsera zimene iwo ankagwiritsa ntchito.

Zinthu Zomwe Ankagwiritsa Ntchito

Pali zinthu zambirimbiri zomwe zinafukulidwa ku Isiraeli zimene zimasonyeza kuti Aisiraeli ankagwiritsa ntchito mafuta onunkhira komanso zodzikongoletsera zina. Zina mwa zinthu zimenezi ndi monga timbale tolowa kapena tosalowa timene ankaperera ndiponso kusakanizira zodzoladzola, timabotolo ta mafuta onunkhira tooneka ngati karoti, mabotolo a alabasitala ndi magalasi odziyang’anira. Anapezanso sipuni ya m’nyanga wa njovu ndipo pachogwirira chake panajambulidwa masamba akanjedza. Mbali ina ya chogwiriracho anajambulapo mutu wa mzimayi utazunguliridwa ndi nkhunda.

Zikuoneka kuti anthu olemera ankakonda kusunga zodzikongoletsera zawo m’zigoba za nkhono. Ku Iguputo ndi ku Kanani anapezakonso timasipuni ting’onoting’ono togwiritsa ntchito podzikongoletsa taminyanga ya njovu kapena mitengo. Timasipuniti tinkaoneka ngati kamtsikana kakusambira ndipo tina tinkakhala tamaonekedwe osiyanasiyana. Zinthu zonsezi ndi umboni wosonyeza kuti akazi a pa nthawiyo ankagwiritsira ntchito zinthu zodzikongoletsera.

Zodzikongoletsera Zopaka M’maso

Baibulo limati mwana wina wamkazi wa Yobu dzina lake linali “Kereni-hapuki.” Dzina limeneli m’Chiheberi limatanthauza “Nyanga ya Utoto Wakuda,” ndipo limeneli linali bokosi lomwe ankasungiramo zodzoladzola za m’maso. (Yobu 42:14) N’kutheka kuti anam’patsa dzina limeneli chifukwa choti anali wokongola. Koma n’kuthekanso kuti zimenezi zikungosonyeza kuti anthu pa nthawiyo ankagwiritsa ntchito zodzikongoletsera.

N’zochititsa chidwi kuti nthawi zambiri Baibulo likamanena za kupaka zodzikongoletsa m’maso, limanena za akazi osakhulupirika monga  Mfumukazi Yezebeli ndiponso Yerusalemu wosakhulupirika amene mneneri Yeremiya ndi Ezekieli anafotokoza kuti zochita zake zinali ngati za mkazi wachigololo. (2 Mafumu 9:30; Yeremiya 4:30; Ezekieli 23:40) Mogwirizana ndi zinthu zambiri zagalasi kapena zamiyala zokhala ndi tizipangizo togwiritsa ntchito podzikongoletsa m’maso zomwe zinafukulidwa, zikuoneka kuti akazi opanduka ambiri achiisiraeli, makamaka a m’mabanja achifumu ndi olemera, ankadzikongoletsa mopitirira muyezo.

Mafuta Onunkhira Amene Ankagwiritsa Ntchito Polambira ndi pa Zinthu Zina

Kuyambira kale anthu a ku Isiraeli ankapanga komanso kugwiritsa ntchito mafuta onunkhira opangidwa ndi maolivi. M’buku la m’Baibulo la Ekisodo muli ndondomeko ya kapangidwe ka mafuta onunkhira amene ansembe ankagwiritsa ntchito pakachisi. Mafutawa ankapangidwa posakaniza sinamoni, mule ndi zomera zina zonunkhira bwino. (Ekisodo 30:22-25) Ku Yerusalemu, anthu ofukula zinthu apeza malo amene akukhulupirira kuti m’nthawi ya atumwi, ankapangirako mafuta onunkhira ogwiritsa ntchito pakachisi. Komanso m’Baibulo  muli mavesi osiyanasiyana amene amanena za mafuta onunkhira amene ankagwiritsidwa ntchito polambira ndiponso pa zinthu zina.—2 Mbiri 16:14; Luka 7:37-46; 23:56.

Ku Isiraeli madzi anali osowa, choncho anthu ankagwiritsa ntchito kwambiri mafuta onunkhira ngati zinthu zowathandiza kukhala aukhondo. Ankadzola mafuta osati pongofuna kuteteza thupi lawo ku nyengo yotentha, koma pofunanso kudzikongoletsa. (Rute 3:3; 2 Samueli 12:20) Mtsikana wachiyuda dzina lake Esitere asanakaonekere kwa Mfumu Ahasiwero, anamudzoza kaye mafuta a mule kwa miyezi 6 ndi a basamu kwa miyezi inanso 6.—Esitere 2:12.

Mafuta onunkhira anali odula mofanana ndi siliva ndi golide. Pamene mfumukazi ya ku Seba inapita kukaona Mfumu Solomo, inamupititsira mphatso zagolide, miyala ya mtengo wapatali ndi mafuta a basamu. (1 Mafumu 10:2, 10) China mwa chuma chimene Mfumu Hezekiya inaonetsa anthu a ku Babulo amene anabwera kunyumba kwake, chinali “mafuta a basamu, mafuta abwino,” siliva, golide komanso zida zankhondo.—Yesaya 39:1, 2.

Mafuta ena ochepa onunkhira ankapangidwa kuchokera ku maluwa osiyanasiyana, zipatso, masamba, utomoni komanso makungwa a mitengo. Baibulo limatchula zina mwa zomera zimene zinkagwiritsidwa ntchito popanga mafuta onunkhira monga mitengo ya aloye, basamu, bedola, kalamasi, kasiya, sinamoni, lubani, mule, maluwa a safironi komanso mitengo ya nado. Zina mwa zinthu zimenezi zinkapezeka ku Isiraeli komweko ndipo zinkamera m’mbali mwa mtsinje wa Yorodano. Koma zina zinkachokera kumayiko ena monga India ndi kum’mwera kwa Arabia.

Mafuta a Basamu Otchulidwa M’Baibulo

Mafuta a basamu amatchulidwa m’Baibulo pa nkhani za Mfumukazi Esitere, mfumukazi ya ku Seba ndiponso Mfumu Hezekiya monga taonera pamwambapa. Mu 1988 anthu anapeza kabotolo kakang’ono ka mafuta kuphanga lina pafupi ndi dera lotchedwa Qumran limene lili m’mbali mwa nyanja ya Dead Sea. Akatswiri ambiri ananenapo zosiyanasiyana zokhudza kabotolo kameneka. Ena akuganiza kuti kabotoloka n’kamafuta omaliza a basamu otchulidwa m’Baibulo. Komabe akatswiriwa sanapeze mfundo yotsimikizika pa nkhaniyi. Alimi akhala akuyesetsa kuti apezenso mbewu ya basamu wotchulidwa m’Baibulo ameneyu.

Zikuoneka kuti mitengo imene ankapangira mafuta a basamu otchulidwa m’Baibulo inkalimidwa m’dera lotchedwa En-gedi. Akatswiri ofukula zinthu zakale anapeza ng’anjo, mabotolo, zinthu zina zachitsulo ndi mafuta zosonyeza kuti zinapangidwa cha m’ma 500 B.C.E. Zinthuzi zinali zofanana ndi zimene zinkagwiritsidwa ntchito m’madera ena popanga mafuta onunkhira. Akatswiri ambiri amaphunziro amakhulupirira kuti mitengo imene ankapangira basamu inkachokera ku Arabia kapena ku Africa. Kafungo konunkhira kamene kankakhala m’mafutawa ndi kochokera ku madzi a mitengo. Mafuta a basamu anali odula kwambiri moti anthu sankaulula njira zimene ankagwiritsa ntchito polima mitengo komanso popanga mafutawa.

Mafuta a basamu ankagwiritsidwanso ntchito pa nkhani zandale. Mwachitsanzo, malinga ndi wolemba mbiri wina dzina lake Josephus, Mark Antony anapereka munda wake wa mitengo yopangira mafuta a basamu kwa Mfumukazi Cleopatra ya ku Iguputo ngati mphatso. Komanso wolemba mbiri wina wa ku Roma, dzina lake Pliny, ananena kuti pa nkhondo ya Ayuda yolimbana ndi Aroma, Ayudawo ankafuna kuwononga mitengo ya basamu, n’cholinga chakuti Aroma asaitenge.

Choncho nkhani za m’Baibulo ndiponso zimene akatswiri ofukula zinthu zakale apeza, zimatithandiza kudziwa zinthu zodzikongoletsera zomwe anthu akale ankagwiritsira ntchito. Baibulo sililetsa kugwiritsa ntchito mafuta onunkhira komanso zinthu zina zodzikongoletsera. Koma limatiuza kuti zinthu zimenezi siziyenera kugwiritsidwa ntchito mopitirira muyezo komanso munthu sayenera kumangoganizira zodzikongoletsa nthawi zonse. (1 Timoteyo 2:9) Mtumwi Petulo analemba kuti chinthu ‘chamtengo wapatali pamaso pa Mulungu’ ndi “mzimu wabata ndi wofatsa.” Popeza kuti masiku anonso anthu ambiri amakonda kugwiritsa ntchito zinthu zodzikongoletsera zosiyanasiyana, malangizo amenewa ndi ofunika kwambiri kwa akazi achikhristu, azimayi ndi atsikana omwe.—1 Petulo 3:3, 4.