Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kukumbukira Yesu Khristu

Kukumbukira Yesu Khristu

“Muzichita zimenezi pondikumbukira.”​—LUKA 22:19.

Chifukwa chimene ena amakondwerera Khirisimasi.

Anthu ambiri amati pa Khirisimasi amakumbukira kubadwa kwa Yesu.

Pamene pagona vuto.

Zochitika zambiri za pa Khirisimasi, kuphatikizapo nyimbo, sizigwirizana kwenikweni ndi zimene Yesu Khristu anaphunzitsa. Anthu ambiri amene amasangalala pa Khirisimasi satsatira mfundo zimene Yesu anaphunzitsa kapenanso sakhulupirira n’komwe zoti iye anakhalako. Masiku ano, nyengo ya Khirisimasi ikafika anthu ambiri amaona kuti ndi nthawi yogulitsa malonda m’malo mokumbukira Yesu.

Mfundo za m’Baibulo zimene zingakuthandizeni.

“Mwana wa munthu sanabwere kudzatumikiridwa, koma . . . kudzapereka moyo wake dipo kuwombola anthu ambiri.” (Maliko 10:45) N’zodziwikiratu kuti Yesu analankhula mawu a palemba la Luka 22:19, omwe ali poyambirira pa nkhaniyi, pa usiku woti afa mawa osati pa tsiku limene anabadwa. Usiku umene analankhula mawu amenewa anayambitsanso mwambo wokumbukira imfa yake. Komano kodi n’chifukwa chiyani Yesu anafuna kuti otsatira ake azikumbukira imfa yake osati kubadwa kwake? Chifukwa choti nsembe ya dipo la Yesu imathandiza anthu omvera kuti adzapeze moyo wosatha. Baibulo limati: “Malipiro a uchimo ndi imfa, koma mphatso imene Mulungu amapereka ndi moyo wosatha kudzera mwa Khristu Yesu Ambuye wathu.” (Aroma 6:23) Choncho, chaka chilichonse otsatira a Yesu Khristu amamukumbukira monga “mpulumutsi wa dziko” osati monga khanda lobadwa kumene.—Yohane 4:42.

“Khristu anavutika chifukwa cha inu, ndipo anakusiyirani chitsanzo kuti mutsatire mapazi ake mosamala kwambiri.” (1 Petulo 2:21) Muyenera kuphunzira zimene Yesu anachita komanso kuyesetsa kumutsanzira ndipo zimenezi ndi zimene zingasonyeze kuti mumamulemekeza komanso kumukumbukira. Muyeneranso kuganizira kwambiri mmene Yesu anasonyezera kuti anali wachifundo, woleza mtima komanso wolimba mtima pochita zoyenera. Pezani njira zimene mungamutsanzirire pa moyo wanu.

“Ufumu wa dziko wakhala ufumu wa Ambuye wathu ndi wa Khristu wake. Iye adzalamulira monga mfumu kwamuyaya.” (Chivumbulutso 11:15) Mukamakumbukira Yesu Khristu muziganizira zimene iye akuchita panopa. Yesu akulamulira kumwamba monga Mfumu. Ponena za iye Mawu a Mulungu analosera kuti: “Adzaweruza mwachilungamo anthu onyozeka ndipo adzadzudzula anthu mowongoka mtima, pothandiza ofatsa a padziko lapansi.” (Yesaya 11:4) Wolamulira wamphamvu, osati mwana wakhanda, ndi amene angaweruze komanso kudzudzula anthu mwachilungamo.