Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kukachezera Achibale

Kukachezera Achibale

“Taonani! Ndi zabwino komanso zosangalatsa kwambiri abale akakhala pamodzi mogwirizana!”—SALIMO 133:1.

Chifukwa chimene ena amakondwerera Khirisimasi.

Popeza kuti Aisiraeli onse anachokera kwa Yakobo kapena kuti Isiraeli, iwo anali “abale” chifukwa anali a banja limodzi. Zinkakhala “zabwino komanso zosangalatsa kwambiri” akakumana pamodzi pa nthawi ya zikondwerero ku Yerusalemu. Masiku anonso mabanja ambiri amayembekezera kuchezerana ndi kusangalala limodzi pa nthawi ya Khirisimasi.

Pamene pagona vuto.

Buku lina linafotokoza kuti: “Popeza anthu apachibale amakhala kuti atha chaka chonse asanakumane, akakumana pa Khirisimasi amayamba kukambirana nkhani zapamtundu ndipo nthawi zambiri m’malo moti asangalale pa nthawiyi ena amakhumudwitsana.”—Encyclopedia of Christmas and New Year’s Celebrations.

Mfundo za m’Baibulo zimene zingakuthandizeni.

‘Bwezerani makolo ndi agogo anu zowayenerera.’ (1 Timoteyo 5:4) Ngati n’zotheka, muyenera kumakaona achibale anu nthawi ndi nthawi. Ngati achibale anu amakhala kutali kwambiri, mukhoza kumalankhula nawobe kawirikawiri powalembera kalata, kuwaimbira foni komanso kuwatumizira imelo kapena kucheza nawo pa Intaneti. Ngati mutamachita zimenezi nthawi zonse, zingakuthandizeni kuti muzichepetsa kusemphana maganizo.

“M’chikondi chanu ndi mmene muli malo ochepa . . . futukulani mtima wanu.” (2 Akorinto 6:12, 13) Achibale amene amachezerana kamodzi pa chaka sagwirizana kwenikweni komanso sadziwana bwino. Izi zimachitika makamaka kwa ana. Ana ena amaona kuti zimene iwo amakonda n’zosiyana kwambiri ndi zimene agogo awo kapena achibale awo amakonda. Choncho muyenera kulimbikitsa ana anu kuti adziwane ndi achibale osiyanasiyana kuphatikizapo agogo awo, komanso azicheza nawo. * Ana amene amakonda kucheza ndi okalamba amakhala achifundo komanso amalemekeza anthu ena amene ali aakulu kuposa iwowo.

Mawu onenedwa pa nthawi yoyenera ndi abwino kwambiri.” (Miyambo 15:23) Kodi mungatani kuti kusemphana maganizo kapena nkhani zina zisawononge ubale wanu? Njira ina ndi kusankha “nthawi yoyenera” yokambirana nkhani zimene mwasemphana maganizo. Ngati pachibale panu mumalankhulana nthawi zonse simudzavutika kukambirana nkhani zimene mwasemphana popanda kukhumudwitsana. Zimenezi zidzathandiza kuti muzisangalala mukakumana.

^ ndime 9 Onani nkhani yakuti, “Kodi N’chifukwa Chiyani Ndiyenera Kudziwana ndi Agogo Anga?” mu Galamukani! ya May 8, 2001 ndi yakuti, “Kodi Nditani Kuti Ubale Wanga ndi Agogo Ulimbe?” mu Galamukani! ya June 8, 2001. Magaziniwa ndi ofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.