Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kuthandiza Osowa

Kuthandiza Osowa

“Wa diso labwino adzadalitsidwa, chifukwa amapereka chakudya chake kwa munthu wonyozeka.”—MIYAMBO 22:9.

Chifukwa chimene ena amakondwerera Khirisimasi.

Popeza Yesu ankachiritsa odwala komanso kuthandiza osauka ndi ovutika, anthu ena amafuna kutengera chitsanzo chake. Iwo amaona kuti nthawi yabwino kuchita zimenezi ndi pa nyengo ya Khirisimasi pamene mabungwe ambiri othandiza osowa amalimbikitsa anthu kuti apereke zinthu zothandizira osowa.

Pamene pagona vuto.

Pa nthawi ya holide anthu ambiri amatanganidwa ndi kugula zinthu, kusangalala komanso kukachezera anzawo ndi achibale. Zinthu zimenezi zimachititsa kuti asakhale ndi nthawi, mphamvu kapenanso ndalama zoti angathandizire osauka kapena zoti apereke ku mabungwe othandiza osowa.

Mfundo za m’Baibulo zimene zingakuthandizeni.

“Usalephere kuchitira zabwino anthu amene akufunikira zabwinozo, pamene dzanja lako lingathe kuchita zimenezo.” (Miyambo 3:27) Anthu osauka ndi ovutika safunika thandizo nthawi ya Khirisimasi yokha. Ngati mukuona kuti munthu wina akufunika thandizo ndipo inuyo mungathe kumuthandiza, kodi ndi bwino kudikira kuti mudzamuthandize nthawi ya Khirisimasi? Mulungu angakudalitseni chifukwa cha kukoma mtima kwanu ndiponso chifundo chimene mungasonyeze nthawi iliyonse, osati pa Khirisimasi pokha.

“Tsiku lililonse loyamba la mlungu, aliyense wa inu aziika kenakake pambali kunyumba kwake malinga ndi mmene zinthu zikuyendera pa moyo wake.” (1 Akorinto 16:2) Mtumwi Paulo anapereka malangizo amenewa kwa Akhristu oyambirira amene ankafuna kuthandiza osowa. Kodi nanunso nthawi zonse ‘mungamaike pambali’ ndalama zina n’cholinga choti muzizipereka kwa anthu osauka kapena ku bungwe limene lingazigwiritse ntchito bwino? Zimenezi zingachititse kuti muzithandiza osowa popanda kulowa m’ngongole.

“Musaiwale kuchita zabwino ndi kugawana zinthu ndi ena, pakuti nsembe zotero Mulungu amakondwera nazo.” (Aheberi 13:16) Onani kuti lembali likusonyeza kuti kuwonjezera pa “kugawana zinthu ndi ena,” sitiyenera kuiwala “kuchita zabwino.” Mwachitsanzo, makolo abwino amaphunzitsa ana awo kuti azithandiza okalamba pa ntchito zosiyanasiyana, kulimbikitsa odwala pokawaona kapena kuwaimbira foni komanso kuti azikonda ana anzawo osauka ndi olumala. Zimenezi zingathandize kuti ana aphunzire kukhala okoma mtima ndi owolowa manja nthawi zonse, osati pa Khirisimasi pokha.

Makolo abwino amaphunzitsa ana awo kuti azithandiza okalamba, odwala komanso ana anzawo ovutika. Zimenezi zingathandize kuti ana aphunzire kukhala okoma mtima ndi owolowa manja nthawi zonse, osati pa Khirisimasi pokha