Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 Yandikirani Mulungu

Kodi Dzina Lanu Lili ‘M’buku la Chikumbutso’ la Mulungu?

Kodi Dzina Lanu Lili ‘M’buku la Chikumbutso’ la Mulungu?

KODI Yehova amaona zimene atumiki ake amachita pofuna kumukondweretsa? Inde amaona. Komanso sikuti iye amangodziwa mawu omutamanda ndi zinthu zabwino zimene iwo amachita pomutumikira. Iye amaonanso ngakhale zimene atumiki ake amaganiza zokhudza iyeyo. Koma chofunikanso kwambiri n’choti Yehova sadzaiwala anthu ake komanso zomwe anachita pomutumikira. Kodi tingatsimikize bwanji zimenezi? Yankho likupezeka m’mawu amene mneneri Malaki analemba.—Werengani Malaki 3:16.

Malaki anali mneneri m’zaka za m’ma 400 B.C.E. ndipo pa nthawiyi mu Isiraeli, kulambira mafano kunali ponseponse komanso anthu anali ndi makhalidwe oipa. Ansembe anasiya kugwira ntchito yawo komanso anthu ankachita zinthu zosalemekeza Mulungu monga zamatsenga, chigololo komanso chinyengo. (Malaki 2:8; 3:5) Koma ngakhale zinali chonchi, panali Aisiraeli ena amene anapitirizabe kukhala okhulupirika. Kodi anthu amenewa ankachita chiyani?

Malaki anati: “Anthu oopa Yehova analankhulana.” Kuopa Yehova ndi khalidwe labwino. Apa Malaki ankanena za Aisiraeli amene ankalemekeza Mulungu ndipo ankaopa kumukhumudwitsa. Komanso onani kuti anthu oopa Mulunguwa ‘ankalankhulana aliyense ndi mnzake.’ N’zodziwikiratu kuti anthuwa ankalankhula zabwino zokhudza Yehova komanso ankalimbikitsana kuti asafooke n’kutengera makhalidwe a anthu oipa.

Aisiraeli okhulupirikawa anasonyeza kuopa Yehova m’njira inanso yofunika kwambiri. Iwo “anali kuganizira za dzina lake.” Baibulo lina linamasulira mawu amenewa kuti “ankalemekeza dzina lake.” Aisiraeli amenewa ankalemekeza Yehova osati ndi zimene ankalankhula zokha, koma ndi zimenenso ankaganiza. M’mitima yawo ankayamikira komanso kuganizira kwambiri za Yehova ndi dzina lake lalikulu. Kodi Yehova ankaona zimene iwo ankachitazi?

Malaki anati: “Yehova anatchera khutu ndi kumvetsera.” Ali kumwamba, Yehova ankamva mawu onse omutamanda amene atumiki akewa ankalankhulana. Iye ankadziwanso zimene anthu akewa ankaganiza m’mitima yawo. (Salimo 94:11) Yehova atadziwa zimene iwo ankaganizazo anachitapo kanthu.

Malaki ananenanso kuti: “Buku la chikumbutso linayamba kulembedwa pamaso pake.” Buku limeneli likutanthauza mbiri ya anthu onse amene atumikira Yehova mokhulupirika. Onani kuti bukuli likutchedwa “buku la chikumbutso.” * Zimenezi zikutanthauza kuti Yehova saiwala atumiki ake okhulupirika komanso zabwino zonse zimene iwowo amaganiza, kulankhula komanso kuchita pomutamanda. Yehova amawakumbukira anthu amenewa n’cholinga choti adzawapatse moyo wosatha. *Salimo 37:29.

N’zolimbikitsa kwambiri kudziwa kuti Yehova amaona zonse zimene timachita pomutumikira. Mawu a pa Malaki 3:16 ayenera kutipangitsa kuganizira bwino mmene ubwenzi wathu ndi Yehova ulili. Tingachite bwino kudzifunsa kuti: ‘Kodi ineyo dzina langa lili “m’buku la chikumbutso” la Mulungu?’ Likhoza kukhalamo ngati tsiku lililonse timachita, kulankhula komanso kuganiza zinthu zimene zingapangitse kuti Yehova adzatikumbukire.

Mavesi amene mungawerenge mu December:

Nahumu 1-3Malaki 1-4

^ ndime 6 Mawu achiheberi omwe anamasuliridwa kuti “chikumbutso” amatanthauza zambiri osati kungokumbukira zinthu zinazake. Amatanthauzanso kuchita zinazake chifukwa cha zimene wakumbukirazo.

^ ndime 6 Kuti mudziwe zambiri za lonjezo la Mulungu la moyo wosatha, werengani mutu 3 m’buku lakuti Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.