Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 Phunzirani Zimene Mawu a Mulungu Amanena

N’chifukwa Chiyani Mulungu Anatumiza Yesu Padziko Lapansi?

N’chifukwa Chiyani Mulungu Anatumiza Yesu Padziko Lapansi?

khani ino ili ndi mafunso amene mwina mumafuna mutadziwa mayankho ake ndipo ikusonyeza mavesi a m’Baibulo amene mungapezeko mayankhowo. A Mboni za Yehova ndi okonzeka kukambirana nanu mafunso amenewa.

1. Kodi Yesu anali kuti Mulungu asanamutumize padziko lapansi pano?

Yesu anali kumwamba asanabadwe ku Betelehemu. Iye ndi amene anayambirira kulengedwa ndipo ndi yekhayo amene Mulungu anamulenga mwachindunji. Choncho mpake kuti amatchedwa Mwana wobadwa yekha wa Mulungu. Pa nthawi imene anali kumwamba, Mulungu ankamugwiritsa ntchito monga womulankhulira wake. N’chifukwa chake amatchedwanso kuti Mawu. Iye anathandizanso Mulungu polenga zinthu zina zonse. (Yohane 1:2, 3, 14) Yesu anakhala ndi Mulungu kumwamba kwa zaka zambirimbiri anthu asanalengedwe.—Werengani Mika 5:2; Yohane 17:5.

2. Kodi Mulungu anatumiza bwanji Mwana wake padziko lapansi?

Yehova anagwiritsa ntchito mzimu woyera kusamutsa moyo wa Yesu kumwamba n’kuuika m’mimba mwa Mariya. Choncho Mariya anabereka Yesu ngakhale kuti sanagone ndi mwamuna aliyense. Angelo anauza abusa za kubadwa kwa Yesu ndipo abusawo anali ali kutchire akuyang’anira nkhosa zawo usiku. (Luka 2:8-12) Choncho Yesu sanabadwe m’nyengo yozizira koma ayenera kuti anabadwa koyambirira kwa October pamene nyengo ya kuderali imakhala yotentha. Kenako Mariya ndi mwamuna wake Yosefe anatenga Yesu n’kupita naye kwawo ku Nazareti ndipo Yesu anakulira kumeneko. Yosefe ankasamalira Yesu monga mwana wake wopeza.—Werengani Mateyu 1:18-23.

Pamene Yesu anali ndi zaka 30, anabatizidwa ndipo Mulungu analengeza kuti Yesuyo ndi Mwana wake. Kenako Yesu anayamba kugwira ntchito imene Mulungu anamutuma.—Werengani Mateyu 3:16, 17.

 3. Kodi n’chifukwa chiyani Mulungu anatumiza Yesu padziko lapansi pano?

Mulungu anatumiza Yesu kuti adzaphunzitse anthu choonadi. Yesu anaphunzitsa anthu za Ufumu wa Mulungu, womwe ndi boma limene lidzabweretse mtendere padziko lonse lapansi. Iye anaphunzitsanso anthu kuti angathe kudzakhala ndi moyo wosatha. (Yohane 4:14; 18:36, 37) Yesu anathandizanso anthu kudziwa zimene angachite kuti akhale osangalala. (Mateyu 5:3; 6:19-21) Ankaphunzitsa anthu powapatsa chitsanzo cha mmene angachitire zinthu kuti asangalatse Mulungu. Mwachitsanzo, iye anasonyeza mmene munthu angachitire zofuna za Mulungu ngakhale pa nthawi yovuta. Pamene anthu anamuchitira zoipa iye sanabwezere.—Werengani 1 Petulo 2:21-24.

Yesu anaphunzitsanso otsatira ake kukhala ndi chikondi chololera kuvutikira ena. Iye anali kumwamba ndi Atate wake ndipo ankagwira ntchito zosiyanasiyana zapamwamba, koma modzichepetsa anamvera Atate wake n’kubwera padziko lapansi pano kudzakhala limodzi ndi anthu. Choncho palibe amene angatipatse chitsanzo cha chikondi kuposa mmene Yesu anachitira.—Werengani Yohane 15:12, 13; Afilipi 2:5-8.

4. Kodi imfa ya Yesu inakwaniritsa chiyani?

Chifukwa china chimene Mulungu anatumizira Yesu padziko lapansi chinali choti adzatifere chifukwa cha machimo athu. (Yohane 3:16) Anthu tonse ndife ochimwa chifukwa choti ndife opanda ungwiro. N’chifukwa chake timadwala komanso kufa. Koma munthu woyamba, Adamu anali wangwiro. Iye anali wosachimwa ndipo akanamvera Mulungu, sakanafa kapena kudwala. Koma chifukwa chosamvera, anakhala wochimwa komanso wopanda ungwiro. Anthufe tinatengera uchimo kuchokera kwa Adamu ndipo uchimowo unabweretsa imfa.—Werengani Aroma 5:12; 6:23.

Popeza Yesu anali munthu wangwiro, sanafe chifukwa cha machimo ake. Iye anafa chifukwa cha machimo athu. Imfa ya Yesu inachititsa kuti anthu okhulupirika adzapeze moyo wosatha ndipo Mulungu adzawadalitsa kwambiri.—Werengani 1 Petulo 3:18.