Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kukhala Mwamtendere

Kukhala Mwamtendere

“Ulemerero kwa Mulungu kumwambamwamba, ndipo pansi pano mtendere pakati pa anthu amene iye amakondwera nawo.”​—LUKA 2:14.

Chifukwa chimene ena amakondwerera Khirisimasi.

Chaka chilichonse papa komanso atsogoleri ena azipembedzo amalalikira uthenga wonena za mtendere. Iwo amakhala ndi chikhulupiriro choti nthawi ya Khirisimasi ikhala ya mtendere mogwirizana ndi mawu amene angelo analengeza akuti: “Mtendere pakati pa anthu amene iye amakondwera nawo.” Ena pa nthawiyi amapita kukaona malo osiyanasiyana achipembedzo.

Pamene pagona vuto.

Mtendere umene umakhalapo pa nthawi ya Khirisimasi umangokhala wakanthawi kochepa. Mwachitsanzo, mu December 1914, pa nthawi imene ku Ulaya kunkachitika nkhondo yoyamba ya padziko lonse, asilikali a dziko la Britain ndi la Germany anasonkhana pamodzi kukondwerera Khirisimasi. Iwo anadya, kumwa ndiponso kusutira limodzi. Komanso pa tsikuli, anasewerera limodzi mpira. Komabe iwo anangogwirizana tsiku limodzi lokhali. M’kalata imene msilikali wina wa Britain analembera msilikali wa Germany, iye anati: “Lero tili pa mtendere, koma mawa tikhala adani chifukwa aliyense akhala akumenyera nkhondo dziko lake.”

Mfundo za m’Baibulo zimene zingakuthandizeni.

“Kwa ife kwabadwa mwana. . . . Iye adzapatsidwa dzina lakuti . . . Kalonga Wamtendere. Ulamuliro wake wangati wa kalonga udzafika kutali ndipo mtendere sudzatha.” (Yesaya 9:6, 7) Ulosi umenewu wonena za Yesu Khristu ndi wolimbikitsa kwambiri. Yesu sanabadwe padziko lapansi n’cholinga chakuti anthu azikhala pa mtendere kamodzi kokha pa chaka. Monga Wolamulira wa kumwamba, iye adzabweretsa padzikoli mtendere weniweni womwe sudzatha.

“Mukhale mu mtendere chifukwa cha ine [Yesu]. M’dzikomu mukumana ndi masautso, koma limbani mtima. Ndaligonjetsa dziko ine.” (Yohane 16:33) Masiku anonso Yesu amathandiza otsatira ake kuti azikhala mwamtendere. N’zoona kuti Akhristu amakumana ndi mavuto. Komabe kudzera m’Baibulo, iwo aphunzira chifukwa chake padzikoli pali mavuto komanso aphunzira mmene Yesu adzabweretsere mtendere wosatha. Zimenezi zimawathandiza kukhala ndi mtendere wamumtima.

Chifukwa choti a Mboni za Yehova amatsatira mawu a Yesu, iwo amakhala mwamtendere ngakhale kuti ndi osiyana mayiko, mitundu, khungu komanso zinenero. Tikukulimbikitsani kuti mudzapite ku Nyumba ya Ufumu kuti mukaone nokha zimenezi. Mofanana ndi anthu ambiri, nanunso mudzavomereza kuti Mboni za Yehova zimakhala pa mtendere nthawi zonse kusiyana ndi mtendere umene anthu amakhala nawo pa nthawi ya Khirisimasi yokha.

A Mboni za Yehova amakhala mwamtendere ngakhale kuti ndi osiyana khungu komanso zinenero. Tikukulimbikitsani kuti mudzapite ku Nyumba ya Ufumu kuti mukaone nokha zimenezi