Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Nditavutika kwa Zaka Zambiri, Ndinapeza Ufulu Weniweni

Nditavutika kwa Zaka Zambiri, Ndinapeza Ufulu Weniweni

“Palibe aliyense amene wapempha kuti mumasulidwe, choncho inu mukhalabe m’ndende muno.” Woyang’anira ndende wina ndi amene ananena monyodola mawu amenewa. Kodi n’chiyani chinachititsa kuti banja lathu lochokera ku Russia, lomwe linali lolimbikira ntchito komanso lamtendere, litsekeredwe m’ndende ku North Korea mu 1950, zaka zisanu nkhondo yachiwiri ya padziko lonse itatha?

NDINABADWA m’chaka cha 1924, m’mudzi winawake wotchedwa Shmakovka umene uli kum’mawa kwenikweni kwa Russia. Mudzi umenewu uli m’malire ndi dziko la China.

Tsiku lina bambo ndi azichimwene anga aakulu anatengedwa ndi gulu linalake la zigawenga ndipo sanabwererenso. Popeza m’banja mwathu tinalipo ana ambirimbiri, zimenezi zinachititsa kuti udindo wonse wodyetsa anafe ukhale ndi mayi anga. Bambo ena amene tinkakhala nawo pafupi anadzipereka kuti atenge anafe kukatisiya kumalo ena osamalira ana amasiye a tchalitchi cha Orthodox ndipo kumeneko anakanena kuti mayi athu anatithawa.

Mayi anagwirizana ndi zimene bamboyu anachita chifukwa anaona kuti sakanatha kutisamalira ndipo tikanafa ndi njala. Tsopano ndili ndi zaka zopitirira 80 ndipo ndimayamikira kuti mayi anatitumiza kumalo osungirako ana amasiye. Ndikuona kuti zimenezi zinachititsa kuti tisafe ndi njala. Komabe pena ndimadzimvera chisoni kuti mayi athu anakatisiya kumalowa iwo ali moyo.

Mu 1941, ndinasamukira ku Korea ndipo kumeneko ndinakwatirana ndi mwamuna wina wokoma mtima wa ku Russia, dzina lake Ivan. Mwana wathu woyamba wamkazi, dzina lake Olya, anabadwa mu 1942 mumzinda wa Seoul ku Korea. Wachiwiri, ndi wamwamuna, dzina lake Kolya ndipo anabadwiranso komweko mu 1945. Mng’ono wake, Zhora anabadwa mu 1948. Mwamuna wanga ankayang’anira sitolo yathu ndipo ine ndinkasoka. Popeza mumzinda umene tinkakhala munali anthu ambiri olankhula Chijapanizi, ana athu ankalankhula chinenerochi ngakhale kuti kunyumba tinkakonda kulankhula Chirasha. Ngakhale kuti mumzinda wa Seoul munkapezeka anthu a ku Russia, America komanso a ku Korea, tinkakhala mwamtendere mpaka m’chaka cha 1950. Anthu onsewa anali makasitomala athu chifukwa ankakonda kugula zinthu m’sitolo yathu.

Mzinda Wathu Unalandidwa ndi Asilikali a North Korea

Mu 1950, zinthu zinasintha mwadzidzidzi. Asilikali a ku North Korea analanda mzinda wa Seoul. Ife tinalephera kuthawa choncho tinamangidwa limodzi ndi anthu enanso ochokera m’mayiko ena. Kwa zaka zitatu ndi hafu tinkayenda limodzi ndi akaidi a ku Britain, Russia, America ndi France ndipo tinayenda m’madera osiyanasiyana ku North Korea. Ankatiika paliponse pamene apeza malo ndipo nthawi zambiri tinkafunika kupewa mabomba kuti asatiphulikire.

Nthawi zina, tinkakhala m’nyumba zotenthera bwino ndipo ankatipatsa chakudya chokwanira. Komabe nthawi zambiri ndipo tinkagona pamalo ozizira kwambiri m’nyumba zimene eniake anathawamo. Akaidi ambiri anafa chifukwa cha kuperewera kwa zakudya m’thupi komanso chifukwa chokhala m’malo osasamalidwa. Zinkandikhudza kwambiri ndikaona mmene ana anga ankavutikira. Ku North Korea, nyengo yozizira imayamba mwamsanga. Ndikukumbukira kuti nthawi zambiri ndinkatenthetsa miyala usiku wonse n’kumaiika pafupi ndi ana anga kuti azimva kutentha.

Ikafika nthawi yotentha, anthu ena m’dzikoli, ankatiuza za zakudya zina zam’tchire monga bowa, anyezi, mphesa komanso zipatso zinazake. Kunena zoona anthu amenewa sankatichitira nkhanza, ankangotimvera chisoni. Ndinaphunzira kugwira achule n’cholinga choti ndiziwonjezera chakudya chochepa chimene ankatipatsa.  Ndinkamva chisoni kwambiri kumva ana anga akulirira achule.

M’chaka china, m’mwezi wa October, anatilamula kuti tisamukire m’tawuni ya Manp’o ndipo anatiuza kuti apereka ngolo zoti zinyamule akaidi omwe ankadwala komanso ana aang’ono. Olya ndi bambo ake anayenda pansi limodzi ndi gulu lina. Ine ndi ana anga ena aja tinadikira kwa masiku angapo kuti ngolo zifike kudzatitenga. Patapita nthawi ngolo zija zinafikadi.

Akaidi omwe ankadwala ankangowaunjika m’ngolomo ngati matumba a chimanga. Zinali zinthu zomvetsa chisoni kwambiri zoti sungafune kuyang’ana kawiri. Ndinabereka Zhora kumbuyo ndipo ndinayesetsa kumukweza Kolya m’ngolo koma iye anayamba kulira kuti: “Amama, musandisiye ndikufuna kuyenda ndi inu.”

Kolya anapitiriza kulira ndipo anandigwira siketi. Pa ulendo wathuwu, womwe unatenga masiku ambiri, akaidi ochuluka anawomberedwa. Akhwangwala ambirimbiri ankadya mitembo ya akaidi imene inkangosiidwa m’njira. Kenako tinafika m’tawuni ya Manp’o ndipo tinasangalala kukumananso ndi Olya ndi bambo ake. Tinakumbatirana komanso kulira chifukwa cha chisangalalo. Usiku wa tsiku limeneli sindinagone ndipo ndinkangokhalira kutenthetsa miyala n’kumaiika pafupi ndi ana anga kuti azimva kutentha. Ndinasangalala kwambiri kuona kuti tsopano ndinali ndi ana anga onse omwe ndinkatha kuwasamalira pamodzi.

Mu 1953 tinayamba kukhala pafupi ndi malire a dziko la North Korea ndi South Korea, ndipo zinthu zinayamba kuyendako bwino. Tinalandira mayunifolomu atsopano, nsapato, buledi komanso mabisiketi. Patapita nthawi pang’ono akaidi a ku Britain anamasulidwa ndipo kenako akaidi a ku France nawonso anamasulidwa. Koma ife sitinali nzika za dziko lililonse choncho akaidi onse atamasulidwa, tinatsala tokha. Tinkangolira ndipo tinkalephera ndi kudya komwe. Pa nthawi imeneyi ndi pamene woyang’anira ndende anatiuza mawu opweteka amene ali koyambirira kwa nkhani ino.

Moyo Unasintha Titapita ku America

Mosayembekezereka anatipititsa ku South Korea. Kumeneko asilikali a ku America  anatifunsa mafunso ndipo anatilola kuti tipite ku America. Tinakwera sitima kupita ku San Francisco ku California ndipo kumeneko tinathandizidwa ndi bungwe lina lachifundo. Kenako tinasamukira ku Virginia, ndipo anthu amene tinakumana nawo kumeneko anatithandiza kupeza zochita. Patapita nthawi tinasamukira ku Maryland komwe tinakakhazikika.

Sitinkadziwa zinthu zambiri moti titaona chipangizo china chimene amasesera pakalapeti tinadabwa kwambiri chifukwa tinali tisanachionepo. Monga alendo m’dzikoli, tinkagwira ntchito mwakhama. Koma zinkandikhumudwitsa kwambiri ndikaona anthu ochita bwino akupezerapo mwayi wodyera masuku pamutu alendo. Titangofika m’derali, tinakumana ndi wansembe wina wa Orthodox ndipo anatiuza kuti: “M’dziko lino mukhoza kulemera mosavuta. Koma kuti zimenezo zitheke, muzipewa kucheza ndi anthu ochokera m’dziko lanu.” Ndinadabwa kwambiri ndi mawu amenewa ndipo ndinadzifunsa kuti, ‘Kodi kuthandizana n’kulakwa?’

M’chaka cha 1970 munthu wina wa Mboni za Yehova, dzina lake Bernie Battleman, anafika kunyumba kwathu kudzakambirana nafe mfundo za m’Baibulo. Iye anali wosapita m’mbali polankhula monga mmenenso ife tinalili. Tinacheza kwa nthawi yaitali. Popeza ndinakulira pamalo osungira ana amasiye a tchalitchi cha Orthodox, ndinaloweza ziphunzitso zonse za tchalitchichi. Koma ndinalibe Baibulo ndipo ndinali ndisanaganizepo kuti ndi lofunika kukhala nalo. Wa Mboniyo anatibweretsera Baibulo ndipo anatiuza kuti: “Ndakupatsani Baibuloli chifukwa ndimakukondani.” Iye anatithandizanso kuti tidziwane ndi wa Mboni wina wochokera ku Belarus, dzina lake Ben, yemwe anali wolankhula Chirasha kuti tiziphunzira naye Baibulo.

Ben ndi mkazi wake ankagwiritsa ntchito Baibulo kuyankha mafunso anga ndipo iwo ankachita zimenezi mokoma mtima. Komabe ineyo ndinkaona kuti a Mboni anapotoza malemba m’Baibulo lawo. Ndinakwiya kwambiri nditaona kuti m’mabuku awo amanena kuti Mariya analinso ndi ana ena kuwonjezera pa Yesu, pomwe tchalitchi chathu chinkatiphunzitsa kuti mwana wa Mariya anali Yesu yekha.

Ndinaimbira foni mnzanga wina wa ku Poland ndipo ndinamuuza kuti andiwerengere lemba la Mateyu 13:55, 56 kuchokera m’Baibulo lake lachipolishi. Ndinadabwa kwambiri atawerenga kuti Yesu analidi ndi azichimwene ake. Mnzangayo nayenso anaimbira mnzake wina yemwe ankagwira ntchito kulaibulale ina mumzinda wa Washington, D.C. kuti aone vesili m’Mabaibulo osiyanasiyana omwe anali mulaibulaleyo. Iye ananena kuti Mabaibulo onse akunena zomwezo, kuti Yesu anali ndi azichimwene ndiponso azichemwali.

Ndinalinso ndi mafunso ena ambiri monga akuti, n’chifukwa chiyani ana amafa? N’chiyani chimachititsa kuti mayiko azimenyana? Nanga n’chifukwa  chiyani anthu, ngakhale olankhula chinenero chofanana, sagwirizana? Mayankho a m’Baibulo a mafunso amenewa anandichititsa chidwi kwambiri. Ndinaphunzira kuti si cholinga cha Mulungu kuti anthu azivutika. Ndinasangalala zedi nditadziwa kuti anthu amene anafa pa nkhondo ndidzawaonanso. M’kupita kwa nthawi ndinayamba kukonda kwambiri Yehova.

Tsiku lina ndinaima pafupi ndi zithunzi za Mariya ndi Yesu, ndipo ndinayamba kupemphera kwa Mulungu kuti athandize mwana wanga wamwamuna amene anali atangobwera kumene kuchokera kunkhondo ku Vietnam ndipo ankavutika kwambiri maganizo. Koma ndinakumbukira kuti ndiyenera kupemphera kwa Yehova Mulungu basi osati kugwiritsa ntchito chinthu chilichonse. Nthawi yomweyo ndinang’amba zithunzizi ndipo ndinaona kuti zilibe phindu lililonse. Zithunzi zimenezi ndinazigula kutchalitchi kwathu koma tsiku limeneli ndinazitaya.

Zinali zovuta kwambiri kuti ndisiye chipembedzo chimene ndinakulira. Koma ndinaona kuti zimene Baibulo limaphunzitsa n’zofunika kuposa chilichonse. Patatha chaka chimodzi ine, mwana wanga komanso mwamuna wanga tinapita kwa wansembe wathu. Ndinatenga kope limene ndinalembamo mafunso a m’Baibulo komanso mavesi ogwirizana ndi mafunsowo. Pamene ndinkawerenga mavesiwo, wansembeyo anapukusa mutu n’kunena kuti: “Inutu mwataika.” Iye anatiuza kuti tisadzapitenso kunyumba kwake.

Zimenezi zinathandiza kwambiri mwana wanga Olya chifukwa zinam’pangitsa kufuna kudziwa zambiri zimene Baibulo limaphunzitsa. Nayenso anayamba kufufuza mayankho a m’Baibulo pa nkhani zosiyanasiyana komanso anayamba kupita kumisonkhano ya Mboni za Yehova. Ine ndinabatizidwa mu 1972, ndipo Olya anabatizidwa chaka chotsatira.

Mfundo Imene Banja Lathu Linkayendera

Mfundo imene banja lathu linkayendera ndi yakuti chapitachapita, tiyenera kuiwala zakale. Choncho tinkatha kuyamba kuchita zinthu zatsopano, ngati taona kuti zinthuzo n’zoyenera. Ine ndi mwana wanga titayamba kukonda kwambiri Mulungu, tinaona kuti ndi bwino kuti tiziphunzitsa anthu zimene tinkaphunzira m’Baibulo. Komabe chifukwa choti ndimalankhula mosapita m’mbali komanso mosanyengerera, nthawi zina zimenezi zinkabweretsa mavuto ndikamalalikira, moti pankafunika munthu wina woti akonze zimene ndalankhulazo kuti munthu amene ndikumulalikirayo asakhumudwe. Koma m’kupita kwa nthawi, ndinaphunzira kulankhula bwino ndi anthu osiyanasiyana amene mofanana ndi ine, ankafuna kudziwa zimene angachite kuti akhale ndi moyo wabwino.

Kenako ine ndi mwana wanga tinayamba kuganiza kuti malamulo oletsa kupita ku Russia akadzasintha, tidzapita ku Russia kukathandiza anthu kuphunzira za Mulungu. Choncho malamulowa atasinthadi cha koyambirira kwa zaka za m’ma 1990, Olya anakwaniritsadi zimene tinkalakalakazi. Anapita ku Russia ndipo kwa zaka 14 anatumikira kumeneko monga mtumiki wa nthawi zonse. Iye anaphunzitsa Baibulo anthu ambiri komanso anathandiza nawo kumasulira m’Chirasha mabuku othandiza anthu kuphunzira Baibulo. Pa nthawiyi ankatumikira kumaofesi a Mboni za Yehova ku Russia.

Panopa ndimangokhala pabedi chifukwa chodwaladwala koma ana anga amayesetsa kundisamalira. Ndikuyamikira Mulungu kuti pambuyo povutika kwa zaka zambiri, ndinaphunzira choonadi cha m’Baibulo chomwe chinandithandiza kuti ndikhale ndi moyo wosangalala. Panopa ndazindikira kuti mawu a m’Baibulo a Davide yemwe anali m’busa ndi oona. Mawuwa amati: “[Mulungu] amandiyendetsa m’malo opumira a madzi ambiri. Amatsitsimula moyo wanga. Amanditsogolera m’tinjira tachilungamo chifukwa cha dzina lake.”—Salimo 23:2, 3. *

^ ndime 29 Maria Kilin anamwalira pa March 1, 2010 pamene nkhaniyi inkakonzedwa kuti ilembedwe.