Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Baibulo Limasintha Anthu

Baibulo Limasintha Anthu

Baibulo Limasintha Anthu

N’chifukwa chiyani mayi wina yemwe anakhumudwitsidwapo ndi chipembedzo, n’kusiya kupemphera, tsopano akuthera nthawi yake yambiri akuphunzitsa ena za Mulungu? Nanga n’chiyani chinathandiza bambo wina wokonda masewera achiwawa kuti asinthe, n’kuyamba kukonda mtendere? Kodi n’chiyani chimene chinathandiza munthu wina yemwe ankakonda kugwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo, kuledzera ndiponso ndewu kuti asinthe moyo wake? Werengani nkhaniyi kuti mumve zimene anthuwa ananena.

ZA MUNTHUYU

DZINA: PENELOPE TOPLICESCU

ZAKA: 40

DZIKO: AUSTRALIA

POYAMBA: ANAKHUMUDWITSIDWA NDI CHIPEMBEDZO

KALE LANGA: Ndinabadwira mu mzinda wa Sydney, m’dziko la Australia. Koma ndili ndi zaka ziwiri, tinasamukira ku New Guinea. Kwa zaka pafupifupi ziwiri, tinakhala mu mzinda wa Rabaul ndipo kenako tinasamukira pachilumba cha Bougainville. M’masiku amenewo, m’dziko la New Guinea munalibe TV, choncho ineyo ndi mchimwene wanga tinkakonda kupita kukasambira ndiponso kukaona malo osiyanasiyana.

Nditatsala pang’ono kukwanitsa zaka 10, ndinayamba kukonda kupemphera. Mayi anga anali a Katolika ndipo anandiuza kuti ndiyambe kupita ku kalasi yomwe sisitere wina ankaphunzitsa Baibulo. Motero, ndinakhala wa Katolika ndipo nditakwanitsa zaka 10 ndinabatizidwa.

Kenako, tinabwerera ku Australia koma ndili ndi zaka 13, ndinayamba kukayikira zimene tinkaphunzira kutchalitchi. Panthawi yomwe ndinali ku sekondale, ndinkaphunzira mbiri yakale ndipo ndinkakonda kukambirana ndi bambo anga za chiyambi cha chipembedzo ndiponso za nkhani za m’Baibulo zimene tinkakhulupirira kuti zinali nthano chabe. Kenako, ndinachoka mu mpingo wa Katolika.

Ndili ndi zaka 16, makolo anga anasiyana ukwati ndipo anafe tinakhala ndi mayi athu. Koma chifukwa choti ankavutika kutisamalira, ineyo ndinachoka n’kukakhala ndi bambo omwe panthawiyi anali ndi mkazi wina. Koma mchimwene wanga anapitirizabe kukhala ndi amayi, omwe kenako anasamukira m’dera lina. Zimenezi zinachititsa kuti ndiziwasowa kwambiri. Panapita zaka ziwiri kuti ndiyambenso kugwirizana ndi mayi anga. Kenako ndinayamba makhalidwe oipa monga kuledzera, kugwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo ndiponso kupita ku malo a zisangalalo. Patapita nthawi, ndinasiya sukulu n’kupeza ntchito. Ndipo m’zaka zanga zonse zaunyamata, ndinkakhala moyo wotayirira kwambiri.

Ndili ndi zaka 25, ndinayambiranso kuchita chidwi ndi Baibulo. Ndinayamba ntchito ina ndipo kuntchitoko ndinakumana ndi mtsikana wina wakhalidwe labwino dzina lake Liene. Mtsikanayu anali waulemu kwambiri kwa bwana wake ngakhale kuti bwanayo ankamuchitira nkhanza. Nditam’funsa kuti n’chifukwa chiyani sankayankha bwanayo mwamwano, iye anandiuza kuti ankaphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova, choncho ankatsatira mfundo za Baibulo pamoyo wake. Kenaka Liene anandiuza kuti azindiphunzitsa Baibulo. Koma chifukwa choti sindinamumvetse bwino, ndinaganiza kuti mu ola limodzi lokha, andiphunzitsa mfundo zonse za m’Baibulo zimene iye ankazidziwa. Tsiku limenelo, Liene anatha maola atatu akuyankha mafunso anga okhudza Baibulo. Ndipo ine ndinasangalala kwambiri chifukwa anandiyankha mafunso onse pogwiritsa ntchito malemba a m’Baibulo.

Liene atamaliza kundiphunzitsa Baibulo tsiku limenelo, ndinayamba ulendo wobwerera kunyumba. Koma ndimakumbukira kuti ndinakwiya kwambiri chifukwa ndinkaona kuti Mulungu wandithandiza mochedwa kuti ndidziwe choonadi cha Baibulo. Ndinkadziwa kuti Mboni za Yehova ndi anthu a makhalidwe abwino koma ndinkaona kuti ineyo sindingakwanitse kusintha makhalidwe anga oipa. Komanso ndinkaona kuti sindingakwanitse kulalikira khomo ndi khomo ngati mmene Mboni zimachitira. Ndinapitirizabe kuphunzira Baibulo ndi Mboni koma ndinkangofuna kuwapezera zifukwa n’cholinga choti ndisiye kuphunzira. Koma patapita nthawi ndinalephera kuwapezera chifukwa chilichonse.

MMENE BAIBULO LASINTHIRA MOYO WANGA: Nditayamba kuphunzira mfundo zambiri za m’Baibulo zokhudza makhalidwe abwino, chikumbumtima changa chinayamba kundivuta kwambiri, motero ndinasiya kugwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo. Koma kenako ndinasamukira kudziko lina ndipo ndili kumeneko, ndinayambiranso kuledzera komanso kupita kumalo a zisangalalo. Ndinkayesetsa ndithu kutsatira mfundo za m’Baibulo koma ndinkapezeka kuti ndayambiranso khalidwe langa loipa lija. Zikatero, mwamanyazi ndinkagwada pansi n’kupemphera kwa Yehova, koma chikumbumtima chinkandivutabe.

Mtima wanga unakhala m’malo nditaphunzira mmene Yehova anasonyezera chifundo kwa Mfumu Davide ndi Bateseba atachita tchimo lalikulu. Davide atadzudzulidwa, anasonyeza kulimba mtima povomereza tchimo lake m’malo modziikira kumbuyo. Ndiponso iye anavomereza modzichepetsa kulandira chilango. (2 Samueli 12:1-13) Nthawi iliyonse ndikachita tchimo ndinkakumbukira nkhaniyi, ndipo zimenezi zinandithandiza kuti ndisamaope kupempha Yehova kuti andikhululukire. Kenako ndinaona kuti ndibwino kuti ndizipemphera ndisanachite tchimo m’malo momapemphera nditachita kale tchimolo, ndipo zimenezi zinandithandiza kwambiri.

PHINDU LIMENE NDAPEZA: Ndinali munthu wosachedwa kupsa mtima, koma lemba la Aefeso 4:29-31 landithandiza kupewa makhalidwe oipa monga ‘kupsa mtima ndiponso mkwiyo.’ Ndinaphunzira kuugwira mtima ndiponso kupewa kulankhula zosayenera. Komanso malangizo a Yesu akuti “mukati Inde akhaledi Inde, ndipo mukati Ayi akhaledi Ayi,” andithandiza kwambiri kuti ndikhale munthu woona mtima.​—Mateyo 5:37.

Poyamba mayi anga sankagwirizana ndi zoti ndiziphunzira Baibulo ndiponso kusonkhana ndi Mboni za Yehova. Koma tsiku lina anandiuza kuti akusangalala ndi khalidwe langa. Iwo anandiuza kuti, “Ndikudziwa kuti tsopano ndiwe munthu wabwino chifukwa cha zimene waphunzira zokhudza Yehova, osati chifukwa cha mmene tinakulerera.” Ndinasangalala kwambiri kumva mayi anga akunena mawu amenewa.

Panopa ndikuona kuti moyo wanga uli ndi cholinga ndiponso ndi watanthauzo. Pa zaka 9 zapitazi, ineyo pamodzi ndi mwamuna wanga takhala tikuchita utumiki wanthawi zonse. Ndimapita kolalikira khomo ndi khomo ndipo ndimaona kuti ntchito imeneyi ndi yofunika kwambiri kuposa ntchito zonse zimene ndagwirapo.

ZA MUNTHUYU

DZINA: DENIS BUSIGIN

ZAKA: 30

DZIKO: RUSSIA

POYAMBA: ANKAKONDA MASEWERA A KARATE

KALE LANGA: Ndinabadwira mu mzinda wa Perm’ koma ndinakulira mu mzinda wa Furmanov, womwe uli m’chigawo cha Ivanovo ku Russia ndipo uli ndi anthu pafupifupi 40,000. Mzindawu ndi wokongola kwambiri ndipo muli mitengo yochititsa chidwi yomwe imaoneka yachikasu ndiponso yofiira m’nthawi yachilimwe. Mu mzindawu munkachitika zachiwawa kawirikawiri m’zaka za m’ma 1980 ndiponso 1990. Banja lathu linali losauka kwambiri ndipo tinkakhala mopanikizana m’kanyumba ka chipinda chimodzi.

Ndili ndi zaka 7, ndinayamba kuphunzira karate ndipo ndinkakonda kwambiri masewerawa. Nthawi zambiri ndinkapezeka ku malo ochitira masewerawa, choncho anzanga onse analinso okonda masewera. Ndili ndi zaka 15, ndinalandira mphoto ya lamba wofiira, yemwe amasonyeza ulemu wapadera pamasewerawa ndipo patapita chaka, ndinapatsidwanso lamba wakhofi. Ndinasankhidwa kuti ndikhale m’gulu la akatswiri a masewera a karate lomwe linachita nawo mipikisano m’dziko lathu lomwelo komanso m’mayiko a ku Asia ndiponso ku Ulaya. Zinkaoneka kuti ndili ndi tsogolo labwino kwabasi koma ndili ndi zaka 17, moyo wanga unasintha kwambiri.

Ineyo ndi azinzanga tinapalamula mlandu ndipo anatimanga, n’kutilamula kuti tikakhale m’ndende zaka ziwiri. Moyo wa kundende unali wovuta kwambiri, komabe kundendeko n’kumene ndinaona Baibulo kwa nthawi yoyamba. Ndinawerenga mabuku a Genesis, Masalmo ndiponso mabuku a m’Chipangano Chatsopano. Mpaka ndinafika poloweza pemphero la Atate Wathu ndipo tsiku lililonse ndinkapemphera pempheroli mokweza ndisanagone chifukwa ndinkaganiza kuti kuchita zimenezi kungandithandize.

M’chaka cha 2000, ndinatulutsidwa m’ndende, koma ndinkaona kuti palibe chilichonse chimene ndingachite pamoyo wanga. Kenako ndinayamba kugwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo. Patapita nthawi yochepa, mayi anga anamwalira ndipo zimenezi zinandikhudza kwambiri chifukwa ndinkawakonda. Komabe ndinayesetsa kusiya mankhwala osokoneza bongo ndipo ndinayambiranso kupita kumalo ochitira masewera a karate. Kenako, ndinasamukira mu mzinda wa Ivanovo ndipo ndinayamba ntchito m’sitolo ina yogulitsa zakudya. Bwana wa m’sitoloyo anali wa Mboni za Yehova ndipo anandifotokozera mfundo za choonadi cha m’Baibulo. Ndiyeno, iye anakonza zoti munthu wina wa Mboni azindiphunzitsa nane Baibulo nthawi zonse.

MMENE BAIBULO LASINTHIRA MOYO WANGA: Pophunzira Baibulo, ndinakhudzidwa mtima kwambiri kumva kuti cholinga cha Mulungu ndi chakuti dziko lapansili likhale paradaiso. Choncho ndinkafunitsitsa kuti nanenso ndidzayenerere kupeza nawo madalitso amenewa. Posapita nthawi, ndinazindikira kuti Yehova Mulungu amafuna kuti anthu azitsatira mfundo zake zapamwamba za makhalidwe abwino. Poyamba ndinkangoganizira za ine ndekha basi. Koma ndinaphunzira kuti Yehova amafuna kuti ndiziganiziranso anthu ena ndiponso kuti ndiziyesetsa kukhala ndi makhalidwe abwino monga chifundo ndiponso kukonda mtendere.

Nditaganizira mwakuya kwambiri zimene Yehova wandichitira, monga kupereka Mwana wake nsembe kuti machimo anga akhululukidwe, ndinayesetsa kusintha moyo wanga. Mwachitsanzo, nditawerenga lemba la Salmo 11:5 ndinaona kuti Yehova amadana ndi chiwawa. Choncho, ndinasiya kuonera ma pulogalamu a pa TV a chiwawa ndiponso olimbikitsa chidani. Motero ndinasiya kuchita masewera achiwawa, ngakhale kuti kuchita zimenezi kunali kovuta kwambiri. Mfundo imene ili pa lemba la 1 Akorinto 15:33 inandithandiza kuzindikira kuti timatengera khalidwe la anthu omwe timacheza nawo. Mfundo imeneyi ndi yoona chifukwa ineyo ndinaikidwa m’ndende chifukwa cha anthu omwe ndinkacheza nawo. Choncho, ndinasiya kucheza ndi anthu okonda za chiwawa.

PHINDU LIMENE NDAPEZA: Panopo ndine munthu woona mtima chifukwa choti ndimapita kumisonkhano ya Mboni za Yehova ndiponso chifukwa choti ndimaphunzira Baibulo. Mwachitsanzo, pa lemba la Aheberi 13:5 ndinaphunzirapo kuti ndiyenera kukhutira ndi zimene ndili nazo ndiponso ndiyenera kupewa kukondetsa ndalama. Ndipo kutsatira malangizo amenewa kwandithandiza kusiya khalidwe lokonda kunama ndiponso kuba.

Ineyo ndimakonda kucheza ndi anthu, koma ndakhala ndikuona anthu okondana akudana chifukwa cha dyera kapena kuopa kukhumudwitsa ena. N’zoona kuti Mboni za Yehova ndi anthu opanda ungwiro, koma ndimaona kuti iwo amalemekeza kwambiri mfundo za Mulungu za makhalidwe abwino ndiponso amayesetsa kutsatira malangizo othandiza kukhala bwino ndi ena. Ndipo ineyo ndapeza anthu abwino ocheza nawo m’gulu la Mboni za Yehova.

Panopo sindikudziwa kuti moyo wanga ukanakhala wotani zikanakhala kuti sinditsatira mfundo za choonadi cha m’Baibulo pamoyo wanga. Mwina bwenzi ndili kabwerebwere kundende kapena bwenzi ndili wovuta kwambiri. Tsopano ndili ndi mkazi wabwino ndiponso ana awiri aamuna. Ineyo ndi banja langa timasangalala kuphunzitsa anthu choonadi chokhudza Mulungu.

ZA MUNTHUYU

DZINA: JOSÉ CARLOS PEREIRA DA SILVA

ZAKA: 31

DZIKO: BRAZIL

POYAMBA: ANALI WANDEWU

KALE LANGA: Ndinabadwira m’tauni yauve kwambiri yotchedwa Americana yomwe ili mu mzinda wa São Paulo. Tinalibe madzi akumwa abwino, zimbudzi ndiponso m’malo abwino otaya zinyalala. Dera limeneli linali lotchuka ndi anthu ovuta ndiponso okonda zachiwawa.

Choncho ineyo ndinakulanso monga munthu wokonda zachiwawa ndiponso ndewu. Nthawi zambiri ndinkakonda kumenyana ndi anthu m’misewu ndipo chifukwa cha zimenezi anthu ankandiopa kwambiri. Kavalidwe ndi kaonekedwe kanga kankasonyeza kuti ndinali munthu woopsa. Ndiponso ndinkamwa mowa kwambiri ndipo nthawi zambiri ndinkachita kukomoka nawo. Komanso ndinkagwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo monganso mmene azichimwene anga ankachitira. Ndipotu mchimwene wanga wina anafa chifukwa cha mankhwala osokoneza bongo.

MMENE BAIBULO LASINTHIRA MOYO WANGA: Tsiku lina ndinakumana ndi a Mboni za Yehova ndipo anandisonyeza m’Baibulo kuti Mulungu adzakonza dziko lapansi kuti likhale paradaiso. (Luka 23:42, 43; Chivumbulutso 21:3, 4) Ndinaphunziranso kuti anthu akufa sadziwa kanthu kalikonse, choncho Mulungu salanga anthu ku Gehena. (Mlaliki 9:5, 6) Mtima wanga unakhala pansi nditamva zimenezi ndipo zimene ndinaphunzira zokhudza Mulungu zinandithandiza kuti ndiyesetse kwambiri kusintha moyo wanga. Koma sizinali zophweka kuti ndisiye kugwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo, uchidakwa, ndewu ndiponso kutukwana.

Komabe, mawu a mtumwi Paulo opezeka pa lemba la 1 Akorinto 6:9-11 anandilimbikitsa kwambiri. Lembali limasonyeza kuti poyamba, Akhristu ena a m’nthawi ya atumwi ankachita makhalidwe amenewa. Koma nkhaniyi imanenanso kuti: “Ndipo ena mwa inu munali otero. Koma mwasambitsidwa kukhala oyera, mwapatulidwa, mwayesedwa olungama m’dzina la Ambuye wathu Yesu Khristu, komanso ndi mzimu wa Mulungu wathu.” Mawu amenewa anandithandiza kuona kuti zinali zotheka kuti inenso ndisinthe moyo wanga n’cholinga choti ndisangalatse Mulungu.

Nditayamba kusonkhana ndi a Mboni za Yehova, ndinaona kuti amachitadi zimene anthu olambira Mulungu amayenera kuchita. Iwo amadziwa kuti kale ndinali munthu wachiwawa ndiponso woopsa, komabe amandilandira mwansangala ndipo amasangalala kucheza nane.

PHINDU LIMENE NDAPEZA: Zikanakhala kuti sindinaphunzire Baibulo n’kusintha moyo wanga, mwina bwenzi pano nditamwalira kalekale. M’malomwake ndine wosangalala chifukwa ndathandiza mchimwene wanga wina kuphunzira Baibulo ndiponso kusiya kugwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo. Komanso ndalimbikitsa abale anga ena kuti ayambe kuphunzira Baibulo. Ndikuthokoza kwambiri Mulungu chifukwa wandilola kudzipereka kwa iye ndiponso chifukwa choti amasamala kwambiri za ife.

[Mawu Otsindika patsamba 24]

“Ndinaona kuti ndibwino kuti ndizipemphera ndisanachite tchimo m’malo momapemphera nditachita kale tchimolo, ndipo zimenezi zinandithandiza kwambiri”