Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi N’zotheka Kukhala ndi Mtendere M’dziko la Mavutoli?

Kodi N’zotheka Kukhala ndi Mtendere M’dziko la Mavutoli?

Kodi N’zotheka Kukhala ndi Mtendere M’dziko la Mavutoli?

KODI inuyo muli pamtendere? Anthu ambiri sali pamtendere chifukwa akukhala m’madera amene mukuchitika nkhondo, mavuto a zandale kapenanso zauchigawenga. Mwina inuyo simukukumana ndi mavuto ngati amenewa, koma mukuvutika chifukwa cha anthu ophwanya malamulo, mukuchitiridwa nkhanza, mwinanso mumasemphana maganizo ndi anzanu amene mumagwira nawo ntchito kapena oyandikana nawo nyumba. Ndiponso m’mabanja ambiri mulibe mtendere chifukwa amangokhalira kukangana.

Anthu ambiri amafuna atakhala ndi mtendere wamumtima ndipo amaufunafuna m’zipembedzo, m’makalasi ophunzitsa anthu kusinkhasinkha kapenanso pochita masewera olimbitsa thupi. Ena amaganiza kuti angapeze mtendere ngati atapita kutchuti, atakakwera mapiri, atakayenda m’nkhalango kapena atapita kukaona malo ena a zinthu zachilengedwe. Koma ngakhale anthuwo ataona kuti apezadi mtendere, n’kupita kwa nthawi, amazindikira kuti mtenderewo ndi wosakhalitsa komanso si weniweni.

Ndiyeno kodi mtendere weniweni tingaupeze kuti? Tingaupeze kwa Mlengi wathu, Yehova Mulungu, chifukwa Baibulo limati iye ndi “Mulungu amene amapatsa mtendere.” (Aroma 15:33) Mu ulamuliro wa Ufumu wake, umene ukubwera posachedwapa, anthu adzakhala “ndi mtendere wochuluka.” (Salmo 72:7; Mateyo 6:9, 10) Mtendere umenewu udzakhala woposa mtendere umene anthu amakhala nawo magulu omenyana akasayinirana mapangano a mtendere. Zili choncho chifukwa chakuti mapangano a mtendere amenewa amangothetsa kumenyana kwa nthawi yochepa chabe. Koma mtendere wa Mulungu udzathetsa zonse zimene zimalimbikitsa nkhondo ndiponso mikangano. Ndipotu anthu onse sadzaphunziranso nkhondo koma adzakhala pamtendere weniweni.​—Salmo 46:8, 9.

Pamene mukuyembekezera mtendere weniweni umenewu, kodi panopa mungatani kuti mukhale ndi mtendere wamumtima? Kodi pali chilichonse chimene mungachite kuti mukhale pamtendere umenewu m’dziko lamavutoli? N’zosangalatsa kudziwa kuti Baibulo limatithandiza kupeza mtenderewu. Taonani malangizo omwe ali m’kalata imene mtumwi Paulo analembera Akhristu a ku Filipi. Tikukupemphani kuti muwerenge Afilipi 4:4-13, m’Baibulo lanu.

“Mtendere wa Mulungu”

Mu vesi 7 timawerenga kuti: “Mtendere wa Mulungu wopambana luntha lonse la kulingalira, udzateteza mitima yanu ndi maganizo anu mwa Khristu Yesu.” Munthu sangapeze mtendere umenewu chifukwa chongosinkhasinkha kapena chifukwa chosintha khalidwe lake. Koma umachokera kwa Mulungu ndipo umakhala weniweni “wopambana luntha lonse la kulingalira.” Mtenderewu umaposa nkhawa zathu zonse, nzeru zathu ngakhalenso maganizo athu. Nthawi zina tingaone ngati mavuto athu sadzatha, koma mtendere wa Mulungu ungatipatse chiyembekezo chodalirika chakuti tsiku lina adzatha.

Anthu sangathe kuchita zimenezi, koma “zinthu zonse n’zotheka ndi Mulungu.” (Maliko 10:27) Kukhulupirira kwambiri Mulungu kungatithandize kuti tisamade nkhawa. Mwachitsanzo, tiyerekezere kuti mwana wina anali ndi mayi ake kumsika ndipo wasochera. Mwanayo akudziwa kuti zimene ayenera kuchita n’kufufuza mayi ake, chifukwa akapanda kutero zinthu sizingamuyendere bwino. Mofanana ndi mwanayo, ifenso tingakhale ndi chikhulupiriro choti Mulungu adzatiteteza, adzatitonthoza ndiponso adzathetsa mavuto athu onse.

Anthu ambiri omwe amalambira Yehova amaona kuti mtendere wa Mulungu umawathandiza pa nthawi imene akukumana ndi mayesero aakulu. Mwachitsanzo, taganizirani za mayi wina dzina lake Nadine, amene anali woyembekezera koma anapita padera. Iye anafotokoza kuti: “Zinkandivuta kuuza ena mmene ndinkamvera ndipo nthawi zonse ndinkangodzilimbitsa kuti anthu aziona ngati ndikusangalala, koma mkati mwa mtima ndinali wachisoni kwambiri. Pafupifupi tsiku lililonse ndinkapemphera kwa Yehova kuti andithandize. Ndaona kuti pemphero lili ndi mphamvu kwambiri chifukwa ndinkati ndikasowa mtendere wamumtima, ndikangopemphera, mtima wanga unkakhala m’malo.”

Mtendere wa Mulungu Umateteza Maganizo ndi Mtima Wanu

Tiyeni tionenso lemba la Afilipi 4:7. Lembali limafotokoza kuti mtendere wa Mulungu udzateteza mitima yathu ndiponso maganizo athu. Mofanana ndi mmene mlonda amatetezera katundu, mtendere wa Mulungu udzateteza mtima wathu kuti tisayambe kukonda chuma, tisamade nkhawa ndi zinthu zosafunika ndiponso kuti tisayambe kuganizira zinthu zoipa. Taonani chitsanzo chotsatirachi.

Anthu ochuluka m’dziko lamavutoli amakhulupirira kuti munthu ayenera kukhala ndi chuma chambiri kuti akhale wosangalala ndiponso kuti akhale ndi mtendere wamumtima. Potsatira malangizo a akatswiri a zachuma, munthu angayambe kuchita bizinesi inayake. Koma kodi zimenezi zingam’thandizedi kuti akhale ndi mtendere wamumtima? N’zokayikitsa, chifukwa tsiku ndi tsiku amakhala ndi nkhawa poganizira mmene angapezere katundu ndiponso kumene angakam’gulitse. Ndipo iye angakhalenso ndi nkhawa kwambiri ngati chuma sichikuyenda bwino chifukwa zingakhudze bizinesi yakeyo. N’zoona kuti Baibulo sililetsa anthu kuchita malonda koma limapereka malangizo abwino kwambiri pankhani yokhudza ndalama. Limati: “Wokonda siliva sadzakhuta siliva; ngakhale wokonda chuma sadzakhuta phindu; ichinso ndi chabe. Tulo ta munthu wogwira ntchito n’tabwino, ngakhale adya pang’ono ngakhale zambiri; koma kukhuta kwa wolemera sikum’gonetsa tulo.”​—Mlaliki 5:10, 12.

Lemba la Afilipi 4:7 limamaliza n’kunena kuti mtendere wa Mulungu umateteza mitima ndiponso maganizo athu “mwa Khristu Yesu.” Kodi pali kugwirizana kotani pakati pa Khristu Yesu ndi mtendere wa Mulungu? Yesu ali ndi udindo waukulu pokwaniritsa cholinga cha Mulungu. Iye anapereka moyo wake n’cholinga chotimasula ku uchimo ndi imfa. (Yohane 3:16) Ndiponso Yesu anaikidwa kukhala Mfumu ya Ufumu wa Mulungu ndipo kudziwa zimenezi kungatithandize kwambiri kukhala ndi mtendere wamumtima. Kodi zingatheke bwanji?

Mulungu amatikhululukira tikalapa machimo athu ndi mtima wonse ndiponso tikam’pempha kuti atikhululukire kudzera mu nsembe ya Yesu. Zimenezi zimachititsa kuti tikhale ndi mtendere wamumtima. (Machitidwe 3:19) Tizikumbukira kuti panthawi ino n’zosatheka kukhala opanda mavuto chifukwa Ufumu wa Khristu sunabwere. Kukumbukira zimenezi kudzatithandiza kupewa moyo wosaganizira za mtsogolo. (1 Timoteyo 6:19) N’zoona kuti sitingakhale opanda mavuto koma timatonthozedwa tikamakumbukira kuti posachedwapa tidzakhala ndi moyo wopanda mavuto.

Zimene Mungachite Kuti Mukhale ndi Mtendere wa Mulungu

Kodi mungatani kuti mukhale ndi mtendere wa Mulungu? Zina mwa mfundo zothandiza mungazipeze pa lemba la Afilipi 4:4, 5, pomwe timawerenga kuti: “Nthawi zonse kondwerani mwa Ambuye. Ndibwerezanso, Kondwerani! Kulolera kwanu kudziwike kwa anthu onse. Ambuye ali pafupi.” Paulo analemba mawu amenewa ali m’ndende, atamangidwa popanda chifukwa. (Afilipi 1:13) M’malo momangodandaula chifukwa chomangidwa wosalakwa, Paulo analimbikitsa Akhristu anzake kuti azikondwera mwa Ambuye. Iye ankasangalala, osati chifukwa cha mmene zinthu zinalili pamoyo wake, koma chifukwa cha ubwenzi wake ndi Mulungu. Ifenso tiyenera kusangalala potumikira Mulungu ngakhale kuti tikukumana ndi mavuto. Tikadziwa bwino Yehova n’kumayesetsa kuchita chifuniro chake, tidzasangalala kwambiri pomutumikira. Zimenezi zidzatithandiza kuti tikhale ndi mtendere wamumtima.

Komanso tikulimbikitsidwa kukhala oganiza bwino chifukwa zimenezi zidzatithandiza kuti tisamayembekezere kuchita zinthu zimene sitingathe. Timadziwa kuti ndife opanda ungwiro ndipo sitingachite chilichonse mosalakwitsa. Choncho tisamadandaule kwambiri mpaka kusowa tulo poganizira zimene tingachite kuti tizichita zinthu mosalakwitsa kapena tizichita bwino zinthu kuposa aliyense. Komanso tisamayembekezere kuti ena azichita zinthu mosalakwitsa ndiponso tisamapse mtima anthu ena akatilakwira. Mawu a Chigiriki amene anawamasulira kuti “kuganiza bwino” amatanthauzanso “kulolera.” Tikakhala ololera pa zokonda za ena, timapewa mikangano imene sikhala ndi phindu lililonse chifukwa imachititsa kuti tisakhale pamtendere ndi anthu ena komanso tizisowa mtendere wamumtima.

Mawu ena a pa Afilipi 4:5 akuti, “Ambuye ali pafupi,” angaoneke ngati sakugwirizana ndi nkhaniyi. Koma mawuwa akusonyeza kuti posachedwapa Mulungu adzachotsa dongosolo la zinthu loipa lino ndipo Ufumu wake udzabweretsa dongosolo la zinthu latsopano. Komabe, ngakhale masiku ano, Mulungu amakhala pafupi ndi wina aliyense amene akuyesetsa kuti akhale naye paubwenzi. (Machitidwe 17:27; Yakobe 4:8) vesi 6 likusonyeza kuti kudziwa mfundo yakuti Mulungu ali nafe pafupi, kumatithandiza kukhala osangalala, oganiza bwino ndiponso kuti tisamadandaule ndi mavuto athu kapenanso tisamade nkhawa ndi za mtsogolo.

Komanso, mavesi 6 ndi 7 akusonyeza kuti pemphero limatithandiza kukhala ndi mtendere wa Mulungu. Koma anthu ena amaganiza kuti pemphero n’lofanana ndi kungosinkhasinkha basi moti kupemphera mwa njira iliyonse kungawathandize kukhala ndi mtendere wamumtima. Mosiyana ndi zimenezi, Baibulo limasonyeza mmene tingalankhulire moyenera ndi Yehova. Limatiuza kuti tingamuuze zakukhosi kwathu ngati mmene mwana amalankhulirana mwachikondi ndi makolo ake akamawauza zinthu zomwe zimamusangalatsa ndiponso zimene zimamudetsa nkhawa. Ndipo n’zolimbikitsa kwambiri kudziwa kuti tingauze Atate wathu wakumwamba “chilichonse” chimene chili mumtima mwathu.

Vesi 8 likutilimbikitsa kuganizira kwambiri zinthu zabwino. Komabe, kungoganizira zinthu zabwino sikokwanira. Monga mmene vesi 9 likusonyezera, tiyeneranso kutsatira malangizo abwino kwambiri a m’Baibulo. Ndipo tikamachita zimenezi tidzakhala ndi chikumbumtima choyera.

Monga mmene taonera, n’zotheka kukhala ndi mtendere wamumtima. Mtenderewu umachokera kwa Yehova Mulungu, ndipo amaupereka kwa anthu amene akuyesetsa kutsatira malangizo ake kuti akhale naye paubwenzi. Inuyo mukhoza kudziwa zimene Mulungu akufuna kuti muzichita ngati mutamawerenga Mawu ake, omwe ndi Baibulo. Ngakhale kuti kutsatira malangizo a m’Baibulo kumakhala kovuta nthawi zina, m’pofunika kuchita khama chifukwa mukatsatira malangizowa, “Mulungu wa mtendere adzakhala nanu.”​—Afilipi 4:9.

[Mawu Otsindika patsamba 10]

“Mtendere wa Mulungu . . . udzateteza mitima yanu.”​AFILIPI 4:7

[Mawu Otsindika patsamba 12]

N’zolimbikitsa kwambiri kudziwa kuti tingauze Mulungu “chilichonse”