Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

‘Ine Yehova Mulungu Wanu Ndine Woyera’

‘Ine Yehova Mulungu Wanu Ndine Woyera’

Yandikirani Mulungu

‘Ine Yehova Mulungu Wanu Ndine Woyera’

Levitiko Chaputala 19

BAIBULO limati: “Woyera, woyera, woyera ndiye Yehova Mulungu.” (Chivumbulutso 4:8) Mawu amenewa akutanthauza kuti Yehova ndi wosadetsedwa ngakhale pang’ono ndipo sangachite tchimo kapena kudetsedwa ndi uchimo wina uliwonse. Koma kodi zimenezi zikutanthauza kuti anthu opanda ungwirofe sitingathe kukhala naye paubwenzi? Ayi. Tiyeni tikambirane mawu opezeka m’chaputala 19 cha Levitiko, omwe akusonyeza kuti n’zotheka kukhala paubwenzi Mulungu.

Yehova anauza Mose kuti ‘anene ndi khamu lonse la ana a Isiraeli’ zimene munthu wina aliyense anayenera kuchita. Kodi Mulungu anamuuza Mose kuti anene zotani kwa Aisiraeli? Iye anati: “Nuti nawo, ‘Muzikhala oyera; pakuti ine . . . Yehova Mulungu wanu, ndine woyera.’” (Vesi 2) Choncho, munthu aliyense anafunika kukhala woyera. Ponena kuti “muzikhala oyera,” Mulungu anali kupereka lamulo osati pempho. Kodi zimenezi zikutanthauza kuti iye ankafuna kuti anthu azichita zinthu zimene sangathe?

Yehova anatchula zoti iye ndi woyera, osati n’cholinga choti anthu akhale oyera mofanana naye ndendende, koma ankafuna kuwasonyeza chifukwa chimene anaperekera lamulolo. Choncho, Yehova sanauze Aisiraeli kuti akhale oyera mofanana ndi iye chifukwa zimenezo n’zosatheka. Aliyense sangafanane ndi Yehova chifukwa iye ndi ‘Woyera Koposa.’ (Miyambo 30:3) Komabe, popeza kuti iye ndi woyera, amafuna kuti anthu amene amam’lambira aziyesetsa mwakhama kuti akhale oyera. Kodi anthu ayenera kuchita chiyani kuti akhale oyera?

Atapereka lamulo lakuti Aisiraeli akhale oyera, Yehova anauza Mose kuti afotokozere anthuwo zimene angachite kuti akhale oyera. Aliyense anafunika kumvera malangizo okhudza makhalidwe abwino monga: Kulemekeza makolo ndiponso anthu achikulire (vesi 3, 32) kuchitira chifundo anthu ogontha, osaona ndiponso ovutika (vesi 9, 10, 14); kukhala oona mtima komanso opanda tsankho (11-13, 15, 35, 36); ndiponso kukonda olambira anzawo monga mmene ankadzikondera. (Vesi 18) Kutsatira malamulo amenewa kukanathandiza aliyense ‘kukhala wopatulika kwa Mulungu wake.’​—Numeri 15:40.

Lamulo loti anthu azikhala oyera likutithandiza kumvetsa mmene Yehova Mulungu amaganizira ndiponso zimene amafuna kuti anthu azichita. Pamenepa tikuphunzirapo kuti n’zotheka kukhala paubwenzi ndi Mulungu ngati tikuyesetsa mwakhama kutsatira malangizo ake, omwe amafotokoza zimene tingachite kuti tikhale oyera. (1 Petulo 1:15, 16) Kuchita zimenezi kungatithandize kukhala ndi moyo wosangalala kwambiri.​—Yesaya 48:17.

Lamuloli likusonyezanso kuti Yehova amakhulupirira anthu amene amam’lambira. Iye sayembekezera kuti tizichita zimene sitingakwanitse. (Salmo 103:13, 14) Anatilenga m’chifaniziro chake ndipo amadziwa kuti tingathe kukhala oyera, koma osati mofanana ndendende ndi iyeyo. (Genesis 1:26) Sitikukayika kuti zimenezi zikulimbikitsani kuti muphunzire zambiri zokhudza zimene mungachite kuti mukhale paubwenzi ndi Yehova, yemwe ndi Mulungu woyera.

[Chithunzi patsamba 9]

Munthu aliyense angathe kukhala oyera