Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Sanakayikire Malonjezo a Mulungu

Sanakayikire Malonjezo a Mulungu

Zoti Achinyamata Achite

Sanakayikire Malonjezo a Mulungu

Malangizo: Chitani zotsatirazi muli pamalo opanda phokoso. Pamene mukuwerenga mavesiwo, yerekezerani kuti nkhaniyo ikuchitika inuyo muli pomwepo. Yesani kuona m’maganizo mwanu zimene zikuchitika. Mukhale ngati mukumva zimene anthuwo akulankhula. Yesani kumva mmene anthu a m’nkhaniyi akumvera.

ONANI NKHANIYI BWINOBWINO.​—WERENGANI GENESIS 12:1-4; 18:1-15; 21:1-5; 22:15-18.

Kodi mukuganiza kuti Abulahamu anamva bwanji, atalonjezedwa ndi Mulungu kuti adzakhala tate wa “mbewu” imene idzadalitsa mitundu yonse ya padziko lapansi?

․․․․․

Kodi mukuganiza kuti alendo atatu otchulidwa pa Genesis 18:2 ankaoneka bwanji?

․․․․․

Kodi inuyo mukuganiza kuti zinthu zomwe zatchulidwa pa Genesis 18:6-8 zinachitika bwanji? (Musaiwale kuti panthawi imeneyi Abulahamu anali ndi zaka pafupifupi 100.)

․․․․․

FUFUZANI MOZAMA.

Kodi panadutsa nthawi yotalika motani kuchokera pamene Yehova analonjeza Abulahamu kuti adzakhala ndi mwana, kufika panthawi imene Isake anabadwa? (Werenganinso Genesis 12:4 ndi 21:5.)

․․․․․

Panthawi imene Abulahamu ankayembekezera kuti malonjezo amene anauzidwa akwaniritsidwe, kodi Yehova anatani pofuna kumutsimikizira kuti malonjezowo adzakwaniritsidwadi? (Werengani Genesis 12:7; 13:14-17; 15:1-5, 12-21; 17:1, 2, 7, 8, 15, 16.)

․․․․․

Kodi Yehova anachita chiyani kwa Abulahamu pamene Abulahamuyo anasonyeza kuti akukayikira zoti adzakhala ndi mwana? (Werenganinso Genesis 15:3-5, 12-21.)

․․․․․

Kodi Yehova anakhala akuvumbula motani zinthu zina zokhudza “mbewu” imeneyo?

․․․․․

GWIRITSANI NTCHITO ZIMENE MWAPHUNZIRA. LEMBANI ZIMENE MWAPHUNZIRA PONENA ZA . . .

Kufunika kokhulupirira malonjezo a Mulungu.

․․․․․

Mmene Yehova amafotokozera chifuniro chake mwapang’onopang’ono.

․․․․․

M’NKHANIYI, KODI NDI MFUNDO ZITI ZIMENE ZAKUSANGALATSANI KWAMBIRI NDIPO N’CHIFUKWA CHIYANI?

․․․․․