Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

2. Liwerengeni Muli ndi Maganizo Oyenera

2. Liwerengeni Muli ndi Maganizo Oyenera

Zimene Mungachite Kuti Muzimvetsa Baibulo

2. Liwerengeni Muli ndi Maganizo Oyenera

Kodi mnzanu anakuuzanipo zoipa za munthu winawake amene simukumudziwa? Pamene munakumana ndi munthuyo, kodi zimene munauzidwazo zinakulepheretsani kuona makhalidwe abwino a munthuyo? Zimenezi zingachitikenso ndi Baibulo.

MTUMWI Paulo anachenjeza za zimene zingachitike ngati tingawerenge Baibulo tili ndi maganizo osayenera. Ponena za Ayuda a m’nthawi yake, Paulo analemba kuti: “Ndikuwachitira umboni kuti ndi okangalika potumikira Mulungu; koma mosam’dziwa molondola.”​—Aroma 10:2.

Ena mwa Ayuda amenewa sankafuna kuvomereza choonadi chokhudza Mesiya chimene Malemba Achiheberi amafotokoza. Panali umboni wa m’Malemba woonekeratu woti Yesu wa ku Nazarete anali Mesiya. Komabe, maganizo olakwika omwe anthu ambiri anali nawo okhudza Mesiya anawalepheretsa kumvetsa Mawu a Mulungu.

Kodi tikuphunzirapo chiyani pamenepa? Tiyenera kuwerenga Baibulo tili ndi maganizo oyenera. Kuwerenga Baibulo tili ndi maganizo olakwika kungatilepheretse kumvetsa choonadi.

Mwachitsanzo, pulofesa wina wa maphunziro a zachipembedzo wa ku North Carolina, ku America, anafotokoza kuti, “m’Baibulo muli nzeru za anthu zokhazokha ndipo mfundo zake zambiri zimatsutsana komanso sizingathandize anthu ngakhale pang’ono.” Choncho, ngati munthu akuwerenga Baibulo ali ndi maganizo oti lili ndi “nzeru za anthu,” ndiye kuti sangatsatire mfundo za m’Baibulo zimene sakugwirizana nazo.

Mosiyana ndi zimenezi, Mawu a Mulungu amatilimbikitsa kuti tiziwerenga Baibulo mwakhama. Ponena za Akhristu a ku Bereya a m’nthawi ya Paulo, Malemba amati: “Iwowa analandira mawuwo ndi chidwi chachikulu kwambiri. Anali kufufuza Malemba mosamala tsiku ndi tsiku kuti aone ngati zinthuzo zinalidi choncho.” (Machitidwe 17:11) Mofanana ndi anthu amenewa, inunso muyenera kupewa maganizo olakwika alionse amene angapangitse kuti musamvetse bwino Baibulo. Choncho, yesetsani kuwerenga Baibulo muli ndi maganizo oyenera kuti mumvetse uthenga wochititsa chidwi wa Mulungu.