Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Yesu Ndi Chitsanzo Chabwino Kwambiri

Yesu Ndi Chitsanzo Chabwino Kwambiri

Yesu Ndi Chitsanzo Chabwino Kwambiri

KODI mumafuna mutakhala munthu wabwino komanso wosangalala? Mtumwi Petulo anafotokoza mmene tingachitire zimenezi. Iye analemba kuti: “Khristu anavutika chifukwa cha inu, kukusiyirani chitsanzo kuti mutsatire mapazi ake mosamalitsa.” (1 Petulo 2:21) Yesu Khristu anachita zinthu zambiri ali padziko lapansi zomwe zingatithandize kwambiri. Tikaphunzira za Yesu ndi kumutsatira pamoyo wathu, tingathe kukhala osangalala ndiponso amakhalidwe abwino. Tsopano tiyeni tione ena mwa makhalidwe amene munthu woposa onse ameneyu anali nawo ndiponso tione mmene kutsanzira makhalidwe amenewa kungatithandizire.

Yesu sankachita zinthu monyanyira. Ngakhale kuti Yesu ananena kuti “alibiretu poti n’kutsamiritsa mutu wake,” iye sankakhala moyo wodzimana zinthu ndipo sankalimbikitsa ena kukhala ndi moyo wotere. (Mateyo 8:20) Nthawi zina Yesu ankapita ku mapwando. (Luka 5:29) Pazinthu zodabwitsa zimene anachita, choyamba chinali kusintha madzi kukhala vinyo wabwino kwambiri paphwando laukwati. (Yohane 2:1-11) Zimenezi zimasonyeza kuti iye sanali munthu wodana ndi kusangalala kapena munthu wokonda moyo wodzimana. (Yohane 2:1-11) Komabe, Yesu ananena momveka bwino kuti chofunika kwambiri kwa iyeyo chinali kuchita chifuniro cha atate wake. Iye anati: “Chakudya changa ndicho kuchita chifuniro cha iye amene anandituma ine ndi kutsiriza ntchito yake.”​—Yohane 4:34.

Kodi inuyo munayamba mwafatsapo n’kuganizira bwinobwino zimene mungachite kuti chuma chisamasokoneze zinthu zauzimu pamoyo wanu?

Yesu anali wochezeka. Baibulo limasonyeza kuti Yesu anali munthu wochezeka ndiponso wansangala. Anthu akabwera ndi mavuto awo kapena kudzamufunsa mafunso amene akuwavutitsa, iye sankakhumudwa nawo. Nthawi ina Yesu anazunguliridwa ndi khamu la anthu, ndipo mayi wina amene anali atadwala nthenda inayake kwa zaka 12 anakhudza chovala cha Yesu pofuna kuchiritsidwa. Iye sanam’kalipire mayiyo ngakhale kuti ena ankaona kuti zimene anachitazo kunali kusamvera malamulo. Koma mwachifundo Yesu anati: “Mwanawe, chikhulupiriro chako chakuchiritsa.” (Maliko 5:25-34) Ananso ankamasuka kucheza naye, popanda kuopa chilichonse. (Maliko 10:13-16) Akamacheza ndi ophunzira ake sankawabisira chilichonse ndipo ankacheza nawo ngati anzake. Ndipo ophunzirawo ankamasuka naye monga mnzawo weniweni.​—Maliko 6:30-32.

Nanga bwanji inuyo? Kodi anthu amamasuka nanu?

Ankachitira ena chifundo. Yesu ankaganiziranso anthu ena pa mavuto awo ndi nkhawa zawo, ndipo kenako ankawathandiza. Mtumwi Yohane anafotokoza kuti Yesu ataona Mariya akulira chifukwa cha imfa ya m’bale wake Lazaro, Yesuyo “anadzuma povutika mu mtima ndi kumva chisoni” ndipo “anagwetsa misozi.” Anthu oona zimenezi anadziwa kuti Yesu ankakonda kwambiri banja limeneli, moti sanachite manyazi kulira pagulu. Ndipotu Yesu anasonyeza chifundo chachikulu poukitsa mnzakeyo.​—Yohane 11:33-44.

Panthawi ina, munthu wina wodwala nthenda yoopsa ya khate, yomwe inam’chititsa kuti azikhala kwayekha, anam’pempha Yesu kuti: “Ambuye, mukangofuna, mukhoza kundiyeretsa.” Yesu anam’yankha molimbikitsa kwambiri. Baibulo limati: “Anatambasula dzanja lake namukhudza, nati: “Ndikufuna. Khala woyera.” (Mateyo 8:2, 3) Sikuti Yesu ankachiritsa anthu kuti angokwaniritsa ulosi. Iye ankafunadi kuwathandiza. Chilichonse chimene iye ankachita chinali chogwirizana ndi imodzi mwa mfundo zake zodziwika kwambiri yakuti: “Zimene mukufuna kuti anthu akuchitireni, inuyo muwachitire zimenezo.”​—Luka 6:31.

Kodi inunso mumachitira ena chifundo?

Yesu anali womvetsa zinthu. Ngakhale kuti anali munthu wopanda tchimo ngakhale pang’ono, Yesu sankayembekezera kuti ena azichita zinthu mosalakwitsa ndiponso sankachita zinthu zodzionetsera. Iye ankachita zinthu mwanzeru. Panthawi ina mayi “amene anali wodziwika mu mzindawo monga wochimwa,” anasonyeza chikhulupiriro chake ndiponso kuyamikira posambitsa mapazi a Yesu ndi misozi yake. Yesu anam’lola kuchita zimenezi, ngakhale kuti mwininyumbayo ankaona kuti mayiyo anali munthu wamakhalidwe oipa. Koma podziwa kuti mayiyo anachita zimenezi moona mtima, Yesu sanam’dzudzule ngakhale kuti anali munthu wochimwa. M’malomwake iye anati: “Chikhulupiriro chako chakupulumutsa; pita mu mtendere.” N’zosakayikitsa kwenikweni kuti chifukwa cha zimene Yesu anachitazi, n’kutheka kuti mayiyo anasiya makhalidwe ake oipa.​—Luka 7:37-50.

Kodi inuyo mumadziwika kuti ndinu munthu wokonda kuyamikira ena ndiponso wosafulumira kuwadzudzula?

Anali wosakondera ndiponso ankalemekeza ena. Yesu ankakonda kwambiri wophunzira wake Yohane, mwina chifukwa chakuti ankagwirizana pa zinthu zambiri kapena chifukwa choti anali pachibale. * Komabe, iye sankachita zinthu momukondera. (Yohane 13:23) Ndipotu Yohane ndi m’bale wake Yakobe atapempha Yesu kuti adzawapatse udindo wapamwamba mu Ufumu wa Mulungu, Yesu anati: “Kunena zokhala kudzanja langa lamanja kapena kumanzere kwanga, si ine wopereka mwayi umenewo.”​—Maliko 10:35-40.

Yesu nthawi zonse ankachita zinthu molemekeza anthu ena. Iye analibe maganizo atsankho amene anthu ambiri anali nawo panthawiyo. Mwachitsanzo, anthu ambiri ankaona kuti akazi ndi otsika powayerekezera ndi amuna. Koma Yesu ankawapatsa akazi ulemu wawo. Munthu woyamba amene Yesu anamuuzako kuti iye ndi Mesiya anali mkazi yemwenso anali Msamariya osati Myuda. Ayuda ankaona Asamariya ngati anthu onyozeka kwambiri moti sankawapatsa moni n’komwe. (Yohane 4:7-26) Ndipo akazi ndiwo anali anthu oyamba kukhala ndi mwayi woona Yesu atangoukitsidwa kumene.​—Mateyo 28:9, 10.

Kodi inuyo mumakonda anthu mosaganizira mtundu wawo, chinenero chawo, dziko lawo kapena zoti ndi akazi kapena amuna?

Anali mwana wolimbikira ntchito ndiponso ankathandiza abale ake. Zikuoneka kuti bambo ake omulera, a Yosefe, anamwalira Yesuyo adakali wamng’ono. Motero n’kutheka kuti Yesu ankagwira ntchito ya ukalipentala kuti athandize mayi ake ndi abale ake. (Maliko 6:3) Atatsala pang’ono kufa, iye anasiya udindo wosamalira mayi ake m’manja mwa wophunzira wake Yohane.​—Yohane 19:26, 27.

Potsanzira Yesu, kodi zilipo zimene inuyo mungachite kuti muthandize anthu m’banja lanu?

Yesu ankakondadi anzake. Yesu anali bwenzi labwino kwambiri. Anzake akalakwitsa zinthu,iye ankapitirizabe kuwakonda, ngakhale iwo achite zimenezi mobwerezabwereza. Nthawi zina ophunzira ake ankachita zinthu zosam’sangalatsa, koma iye anasonyeza kuti analidi mnzawo weniweni. Ankaganizira kwambiri makhalidwe awo abwino m’malo mowakayikira. (Maliko 9:33-35; Luka 22:24-27) Iye sankakakamiza ena kumvera mfundo zake, koma ankawalola kuti nawonso anene maganizo awo.​—Mateyo 16:13-15.

Ndipo mfundo yaikulu ndi yakuti Yesu ankakonda anzake. (Yohane 13:1) Kodi chikondi chake chinali chachikulu bwanji? Iye anati: “Palibe amene ali ndi chikondi choposa ichi, chakuti wina n’kupereka moyo wake chifukwa cha mabwenzi ake.” (Yohane 15:13) Kodi pali munthu aliyense amene angapatse anzake chinthu chamtengo wapatali ngati chimenechi?

Kodi mumapitirizabe kukonda anzanu ngakhale atakukhumudwitsani?

Anali wolimba mtima. Sikuti Yesu anali munthu wofooka ngati mmene zithunzi zina za Yesu zimasonyezera. Mauthenga abwino amasonyeza kuti iye anali munthu wamphamvu. Kawiri konse, Yesu anathamangitsa anthu omwe ankagula ndiponso kugulitsa malonda m’kachisi. (Maliko 11:15-17; Yohane 2:14-17) Gulu la anthu limene linkafunafuna “Yesu Mnazareti” litafika, iye analimba mtima n’kudziulula kuti munthuyo ndi iyeyo, ndipo pofuna kuteteza ophunzira ake, iye anauza gululo kuti: “Ndakuuzani kuti ndine amene. Choncho ngati mukufuna ine, alekeni awa apite.” (Yohane 18:4-9) Motero n’zosadabwitsa kuti Pontiyo Pilato anagoma poona kulimba mtima kwa Yesu ngakhale kuti anali atamangidwa ndiponso anthu ankamuchitira zachipongwe. Iye anati: “Taonani! Mwamunatu ameneyu!”​—Yohane 19:4, 5.

Kodi nanunso mumachita zinthu mosakayikakayika ndiponso molimba mtima?

Makhalidwe apadera ngati amenewa ndiponso ena ambiri amachititsa Yesu kukhala chitsanzo chabwino kwambiri kwa ifeyo choyenera kutsatira. Ngati titatengera makhalidwe amenewa, tidzakhala anthu abwino ndiponso osangalala. N’chifukwa chake mtumwi Petulo analimbikitsa Akhristu kuti azitsatira mapazi a Yesu mosamalitsa. Kodi inuyo mumayesetsa kuchita zimenezo?

Yesu Anaperekanso Moyo Wake

Sikuti Yesu anali chitsanzo chabwino chabe. Iye anati: “Ine ndine njira ndi choonadi ndi moyo. Palibe amene amafika kwa Atate osadzera mwa ine.” (Yohane 14:6) Kuwonjezera pa kutidziwitsa choonadi cha Mulungu, n’kutsegula njira yoti tithe kumuyandikira, Yesu anatsegulanso njira yoti anthu okhulupirika adzapeze moyo wosatha.​—Yohane 3:16.

Pofotokoza chifukwa chachikulu chimene anabwerera padziko lapansi, Yesu anati: “Mwana wa munthu sanabwere kudzatumikiridwa, koma kudzatumikira ndi kudzapereka moyo wake dipo kuwombola anthu ambiri.” (Mateyo 20:28) Chifukwa chopereka moyo wake nsembe, Yesu anatsegula njira yoti anthu adzapeze moyo wosatha. Kodi ifeyo, aliyense payekha, tiyenera kuchita chiyani kuti tidzapeze madalitso amenewo? Yesu anafotokoza kuti: “Moyo wosatha adzaupeza akamaphunzira ndi kudziwa za inu, Mulungu yekha woona, ndi za Yesu Khristu, amene inu munam’tuma.”​—Yohane 17:3.

Choncho, kuphunzira za Yesu, kutengera chitsanzo chake ndiponso kukhulupirira nsembe yake n’zofunika kwambiri kuti tidzapeze moyo wosatha. Tikukulimbikitsani kupatula nthawi yoti muphunzire Baibulo, lomwe lingakuthandizeni kudziwa zambiri zokhudza Yesu ndiponso kuti mutsatire chitsanzo chake. *

Kudziwa za moyo wa Yesu kumatithandiza kuona khalidwe limene tiyenera kukhala nalo. Imfa yake ingathe kutipulumutsa ku uchimo ndi imfa imene ndi mphotho ya uchimo. (Aroma 6:23) Ndipotu n’zosatheka kukhala moyo wosangalatsa popanda kutsatira chitsanzo cha Yesu Khristu. Choncho musalole kuti kutanganidwa ndiponso nkhawa zikutayitseni mwayi woganizira ndiponso kutsatira mosamalitsa chitsanzo cha Yesu Khristu, yemwe ndi munthu woposa onse amene anakhalapo.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 12 Mayi ake a Yohane anali a Salome ndipo zikuoneka kuti iwowa ndi Mariya mayi a Yesu, anali munthu ndi mng’ono wake. Yerekezerani Mateyo 27:55, 56 ndi Maliko 15:40 komanso Yohane 19:25.

^ ndime 26 Kuti mudziwe zambiri zokhudza moyo wa Yesu padziko lapansi, werengani buku la Munthu Wamkulu Woposa Onse Amene Anakhalako, lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.

[Bokosi/​Zithunzi patsamba 7]

▪ Yesu anali wosakondera ndiponso ankalemekeza ena

▪ Anakonda ophunzira ake mpaka mapeto

▪ Anali wolimba mtima

Kodi inuyo mumayesetsa kutsatira mapazi a Yesu?

[Zithunzi patsamba 5]

Yesu sankachita zinthu monyanyira . . .

anali wochezeka . . .

wachifundo