Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kufufuza Zolakwa Kunandidziwitsa Choonadi

Kufufuza Zolakwa Kunandidziwitsa Choonadi

 Kufufuza Zolakwa Kunandidziwitsa Choonadi

Yosimbidwa ndi R. Stuart Marshall

“Ife sitilankhula ndi a Mboni za Yehova chifukwa amagwiritsa ntchito Baibulo,” anatero wansembe wachikatolika. Yankho lake linandidabwitsa chifukwa ndinali nditam’pempha kuti asonyeze mkazi wanga umboni wakuti zimene a Mboni za Yehova amaphunzitsa ndi zolakwika. Ndinaganiza zophunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova kuti ndizimusonyeza ndekha kuti zimene amaphunzitsa n’zolakwika.

PANTHAWI imeneyi ndinali ndi zaka 43 ndipo ndinayamba kutsutsa zomwe Mboni za Yehova zimaphunzitsa. Ndinkachita zimenezi pogwiritsa ntchito maphunziro anga a zaumulungu ndiponso luso langa lofotokoza bwino mfundo. Ndaphunzira sukulu zachikatolika mpaka ku koleji. Ngakhale kuti mu 1969 ndinapeza digiri ya kayendetsedwe ka zachuma komanso ndinachita maphunziro a nzeru za anthu ndi zaumulungu, sindinaphunzirepo zilizonse zochokera m’Baibulo.

Nditamaliza maphunziro a kukoleji ndinakwatira Mkatolika mnzanga dzina lake Patricia McGinn. Tonse tinapitiriza maphunziro pa yunivesite ya Stanford ndipo tinalandira madigiri apamwamba. Mwana wathu Stuart anabadwa mu 1977 ndipo kenako tinasamukira ku Sacramento, mu mzinda wa California, ku United States. Ndipo kwa zaka 23, ndinagwira ntchito muofesi yaboma yofufuza kayendetsedwe ka ndalama za boma pamaphunziro. Ndinali wolimbikira ntchito ndipo zinthu zinkandiyendera bwino. Ndinkasangalala kwambiri kulera mwana wathu. Mkazi wanga anali kundithandiza kwambiri ndipo inenso ndinkamuthandiza.

Kupeza Mayankho ndi Ndalama Zochepa

Mwana wathu ali ndi zaka ziwiri, mkazi wanga anapeza Baibulo kwa Mboni za Yehova ndipo anayamba kuphunzira nawo. Anabatizidwa patapita zaka zitatu. Ndinkaona kuti Mboni za Yehova zinkaganiza moperewera pankhani za tchuti ndi kuika magazi komabe nkhani zina ankazifotokoza mogwira mtima. Koma zochititsa chidwi n’zakuti ndinatchula za Mboni za Yehova nditapemphedwa kufotokoza maganizo anga pamsonkhano wa akuluakulu aboma opanga malamulo a zamaphunziro mu 1987.

Akuluakulu a payunivesite ya California ankafuna ndalama kuti apikisane ndi mizinda ina kuti apeze ntchito inayake ya ndalama zokwana madola 6 biliyoni. Ntchito imeneyi inali yopanga chipangizo chachikulu cha sayansi. Ndinafotokoza kuti ndibwino kuti ntchito imeneyi isachitike chifukwa boma silidzapeza phindu lililonse. Chifukwa cha zimenezi akuluakulu a payunivesiteyi anaitanitsa akatswiri awiri a sayansi kuti afotokozere akuluakulu a boma maganizo awo pankhaniyi. Aliyense anafotokoza mmene chipangizo chimenechi chidzathandizire asayansi pamaphunziro awo. Mmodzi  ananena kuti chipangizochi chidzawathandiza kupeza mayankho a mafunso okhudza mmene chilengedwe chinayambira. Ndipo winayo ananena kuti chipangizochi chidzathandiza anthu kudziwa mmene moyo unayambira padziko lapansi.

Kenako yemwe anali mkulu wa msonkhanowo anandifunsa kuti:

“Kodi ukuganiza kuti 6 biliyoni ndi ndalama zochuluka kuti tipeze mayankho a mafunsowa?”

Ndinayankha kuti: “Ndi zoona kuti mafunso amenewa ndi ofunika kwambiri. Koma a Mboni za Yehova amabwera kunyumba kwanga Loweruka lililonse ndipo amandigawira magazini amene angayankhenso mafunso amenewa. Amapereka magazini amenewa pamtengo wa masenti okwana 25 okha. Ndipo ndikukhulupirira kuti mayankho amene tingapeze mwa kupereka ndalama yochepa imeneyi ndi olondola kuposa omwe tingadzapeze tikapanga chipangizo cha ndalama zokwana madola 6 biliyoni.”

Aliyense yemwe anali pamsonkhanowo, kuphatikizapo akatswiri asayansi aja, anaseka kwambiri. Ngakhale kuti boma linaperekabe ndalama zogwirira ntchitoyo, palibe amene anatsutsa mfundo yangayi.

Patapita nthawi, ndinayamba kuona kuti ndinkafunikira kuthetsa vuto limene linali m’banja mwathu. Nditakambirana ndi mkazi wanga kwa zaka 6 pa nkhani ya Baibulo ndi Mboni za Yehova, ndinakhumudwa kwambiri kuona kuti ankafuna kuthera nthawi yambiri mu ntchito yawo yolalikira. Ndipo kuti achite zimenezi ankafunika kuchepetsa nthawi yake yogwira ntchito. Zinkandikhumudwitsa kwambiri kuona kuti munthu wabwinobwino ngati iyeyo anali ndi zolinga ngati zimenezi. Ndipo zinkaoneka kuti palibe chomwe ndingachite kuti asinthe maganizo ake.

Kenako ndinaganiza zopempha thandizo kwa katswiri wina wolidziwa bwino Baibulo kuti amuthandize kuona kulakwika kwa zimene Mboni za Yehova zimaphunzitsa poyerekezera ndi zimene Baibulo limanena. Ndinaona kuti akangomusonyeza kuti chiphunzitso chawo chinachake ndi cholakwika ndiye kuti iye adzayamba kukayikira zonse zimene amaphunzitsa. Ndinaona kuti ndikatere ndiye kuti ndamutha. Choncho ndinaitana wansembe wachikatolika wa mpingo umene ine ndi mkazi wanga tinkapemphera poyamba. Ndipo zokambirana zathu zinatha ndi mawu amene ali kumayambiriro kwa nkhani ino aja. Wansembeyo atakana kulankhula ndi mkazi wanga, ndinaona kuti ndiyenera kufufuza ndekha zolakwazo ndi kumufotokozera Patricia, ngakhale kuti zimenezi zikananditengera nthawi yaitali.

Ndinayamba Kufufuza Zolakwa

Maulosi a m’Baibulo ndi amene ankandisangalatsa kwambiri pamene ndinkaphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova. Ndinawerenga m’buku lolembedwa ndi mneneri Yesaya nkhani yonena za kugwa kwa Babulo yomwe inalembedwa kutatsala zaka 200 kuti zinthuzo zichitike. Ulosiwo  unatchulanso kuti Koresi ndi amene adzagonjetse Babulo ndipo unafotokoza kuti adzapatutsa madzi a mu mtsinje wa Firate kuti agonjetse mzindawo. (Yesaya 44:27–45:4) Ndisanawerenge zimenezi ndinali nditaphunzira za kugwa kwa mzinda wa Babulo pa phunziro lina lokhudza luso limene anthu amagwiritsa ntchito pomenya nkhondo. Ndinaphunziranso kuti mneneri Danieli anali ataneneratu kudakali zaka zoposa 200 kuti mfumu yamphamvu ya Girisi ikadzamwalira, ufumu wake udzagawanika n’kukhala maufumu aang’ono anayi. (Danieli 8:21, 22) Nkhani imeneyi inandikumbutsa mbiri ya Alesandro Wamkulu imene ndinaphunzira kusukulu. Mwa kufufuza umboni wa m’mabuku ena, ndinapeza kuti mabuku a m’Baibulo amenewa analembedwadi zinthuzo zisanachitike.

Kuphunzira ndi Mboni za Yehova kunandithandiza kukhulupirira kwambiri kuti Baibulo ndi Mawu a Mulungu. Ndipo zimenezi sindinaziphunzire zaka zonse zomwe ndinkachita maphunziro a zaumulungu ku makoleji achikatolika. Chifukwa cha zimene ndinaphunzira, ndinadzipereka kwa Yehova kuti ndikhale mmodzi wa Mboni zake. (Yesaya 43:10) Ndinabatizidwa mu 1991, patangodutsa zaka ziwiri kuchokera pamene ndinakambirana ndi wansembe uja. Ndipo mwana wathu anabatizidwa chaka chotsatira.

Tinasintha zolinga za banja lathu chifukwa cha zimene tinaphunzira. Nditangobatizidwa tinakonza zoti pakatha zaka 5, mkazi wanga adzasiye ntchito yophunzitsa ku yunivesite. Pamene azidzasiya ntchitoyi mkazi wanga adzakhala ali ndi zaka 50. Iye ankafuna kuyamba upainiya umene panthawi imeneyo umafunika kuti munthu azikwanitsa maola 1,000 pachaka kapena maola pafupifupi 83 pamwezi akuthandiza anthu kuphunzira Baibulo. Pofika m’chaka cha 1994, iye anali atachepetsa nthawi imene amagwira ntchito kuti ayambe upainiya. Zolinga zanga zoyambirira zinali kuwonjezera utumiki, kuthandiza pampingo ndiponso kudzipereka pantchito yowerengera ndalama za ntchito yomanga Nyumba za Ufumu m’dera lathu.

Nthawi zina kuntchito ndinkakhala ndi mwayi wokambirana ndi anthu nkhani za m’Baibulo. Kuntchito kwathu kunabwera katswiri wina woona za kayendedwe ka zachuma yemwe anali Mboni yofooka chifukwa chokayikira mfundo zina za m’Baibulo. Ndinasangalala kumuthandiza mwauzimu. Ndipo atabwerera kwawo anayamba upainiya.

Mu 1995, ndinapezeka pamsonkhano wapadera wa akuluakulu a boma opanga malamulo a zamaphunziro. Ndipo cholinga cha msonkhanowu chinali kukambirana za kafukufuku yemwe ndalama zake zinkachokera kuboma. Mkulu wa msonkhanowo anafunsa woimira boma mmene ntchito yomanga chipangizo chachikulu cha sayansi chija ikuyendera. Iye anayankha kuti ntchitoyo inaperekedwa kwa akuluakulu a ku Texas koma siinamalizidwe pa zifukwa zitatu. Choyamba, ntchitoyo isanayambe, ndalama zomwe zinkafunika zinali zitawonjezeka kuchoka pa 6 biliyoni kufika pa 9 biliyoni. Chachiwiri, boma linkafuna kugwiritsa ntchito ndalamazo pantchito ina, makamaka pa nkhondo ya ku Iraq ya mu 1991. Ndipo chifukwa chachitatu chinali choti anaona kuti akhoza kupeza mayankho a mafunso onena za moyo kwa Mboni za Yehova ndi ndalama zochepa zokwana masenti 25 okha. Apa ndinaona kuti mawu amene ndinalankhula pamsonkhano woyamba aja akhala akubwerezedwa ndi anthu ambiri ndipo tsopano amabwerezedwanso pamsonkhano umenewu.

Aliyense atayamba kuseka, akuluakulu ena pamsonkhanopo anandiyang’ana. Kenako ndinawauza kuti: “Tsopano mungapeze mayankho amenewa kwaulere mwa kungowerenga mabuku ndi magazini athu.”

Tinayamba Kukhala Moyo Wosangalala

Mkazi wanga atapuma pantchito, tinakonza zoti nanenso ndidzapume pantchito pakatha zaka 5. Ndinayamba kufufuza kumene ndingapeze ntchito ya maola ochepa chifukwa ndinkafuna kuti ndizithera nthawi yambiri ndikuphunzitsa anthu Baibulo. Mosayembekezereka, kuntchito kwathu anandilola kuti ndizigwira ntchito maola ochepa. Ndipo mu 1998, nanenso ndinayamba upainiya.

Tsiku lina m’mawa, ine ndi mkazi wanga tikukonzekera kupita muutumiki, tinalandira foni kuchokera ku ofesi ya nthambi ya Mboni za Yehova ya ku United States yomwe ili ku Brooklyn, mu mzinda wa New York. Anandifunsa ngati ndingakonde kukathandiza pantchito inayake ku Brooklyn. Nthawi yomweyo ndinavomera ndipo tinakatumikira kwa miyezi 18 ku likulu la padziko  lonse la Mboni za Yehova. Chifukwa cha zimenezi ndinapuma mwamsanga pantchito kuti tikagwire ntchitoyo. Titamaliza ntchito imeneyi, tinadzipereka kukagwira ntchito yomanga Nyumba ya Msonkhano ya Mboni za Yehova ku Fairfield, ku California. Tinagulitsa nyumba yathu ya ku Sacramento ndipo tinasamukira mu nyumba ina yaing’ono ku Palo Alto. Tinapeza madalitso enanso ambiri chifukwa chopuma pantchito mwamsanga. Kuchokera nthawi imeneyi tatumikira pantchito zosiyanasiyana ku maofesi a nthambi a Mboni za Yehova ku Nigeria, South Africa, Canada, Britain, ndi ku Germany.

Mofanana ndi Mboni zimene zinatithandiza kuphunzira choonadi, ine ndi mkazi wanga tikusangalalanso kuthandiza ena kudziwa choonadi cha m’Baibulo. Ndikuona kuti pamaphunziro onse apamwamba, maphunziro a Yehova ndi amene ali opindulitsa kwambiri. Maphunziro ake amasiyana ndi maphunziro ena onse chifukwa amakhudza nkhani zambiri ndipo mfundo zake zimafotokozedwa bwino kwambiri. Yehova waphunzitsa Mboni zake kuti zizitha kuphunzitsa anthu choonadi cha m’Baibulo mowafika pamtima. Zimenezi n’zimene zimandichititsa kuti ndipitirizebe kuphunzira. Tsopano ine ndi mkazi wanga tikuthokoza kwambiri chifukwa cha moyo umene tili nawo ndiponso mwayi wapadera wogwiritsa ntchito maphunziro athu kutumikira Mfumu ya chilengedwe chonse, Yehova Mulungu.

[Mawu Otsindika patsamba 27]

Maulosi a m’Baibulo ndi amene ankandisangalatsa kwambiri pamene ndinkaphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova

[Chithunzi patsamba 27]

Ndili ndi Patricia tsiku la ukwati wathu

[Chithunzi patsamba 29]

Timasangalala kuthandiza ena kuphunzira choonadi cha m’Baibulo