Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Oyenerera Kulandira Ufumu

Oyenerera Kulandira Ufumu

Oyenerera Kulandira Ufumu

“Zimenezi ndi umboni wa chiweruzo cholungama cha Mulungu, ndipo chifukwa cha izi muyesedwa oyenerera ufumu wa Mulungu.”​—2 ATES. 1:5.

1, 2. Kodi cholinga cha Mulungu ndi chiyani pankhani ya kuweruza, ndipo ndani adzakhala woweruza?

CHA m’ma 50 C.E., mtumwi Paulo anali ku Atene. Atawawidwa mtima poona mafano paliponse, anakakamizika kupereka umboni mogwira mtima. Pomaliza ulaliki wake, analankhula mawu amene ayenera kuti anachititsa chidwi anthu akunja omwe anali kumvetsera. Iye anati: “Tsopano [Mulungu] akuuza anthu kwina kulikonse kuti onse alape. Pakuti wakhazikitsa tsiku limene akufuna kudzaweruza m’chilungamo dziko lapansi kumene kuli anthu, kudzera mwa munthu amene iye wamuika. Ndipo wapereka chitsimikizo kwa anthu onse mwa kumuukitsa kwa akufa.”​—Mac. 17:30, 31.

2 Nkhani yakuti Mulungu wakhazikitsa tsiku loweruza anthu si yamasewera. Ku Atene, Paulo sanatchule munthu amene adzapereka chiweruzo chimenechi koma ife tikudziwa kuti ndi Yesu Khristu yemwe anaukitsidwa. Chiweruzo chimene Yesu adzapereka chidzakhala moyo kapena imfa.

3. N’chifukwa chiyani Yehova anachita pangano ndi Abulahamu, ndipo ndani ali ndi udindo wapadera pokwaniritsa panganolo?

3 Tsiku la Chiweruzo limenelo lidzakhala la zaka 1,000. Yesu ndi amene adzayang’anira tsikulo m’dzina la Yehova chifukwa chakuti iye ndi Mfumu ya Ufumu wa Mulungu, koma sadzakhala yekha. Yehova amasankha anthu ena kuti akalamulire ndiponso kuweruza limodzi ndi Yesu patsiku limenelo la zaka 1,000. (Yerekezerani ndi Luka 22:29, 30.) Zaka pafupifupi 4,000 zapitazo, Yehova anayala maziko a Tsiku la Chiweruzo limenelo pamene anachita pangano ndi Abulahamu, mtumiki wake wokhulupirika. (Werengani Genesis 22:17, 18.) Zikuoneka kuti pangano limenelo linachitika mu 1943 B.C.E. N’zodziwikiratu kuti Abulahamu sanamvetse bwinobwino mmene panganolo lidzakhudzira anthu onse. Koma ife lero tikuona kuti malinga ndi mfundo za panganolo, mbewu ya Abulahamu ili ndi udindo wapadera pokwaniritsa cholinga cha Mulungu choweruza anthu onse.

4, 5. (a) Kodi mbali yoyamba ya mbewu ya Abulahamu ndani, ndipo iye anati chiyani za Ufumu? (b) Kodi mwayi wokhala ndi chiyembekezo chokalamulira mu Ufumu unayamba kuperekedwa liti?

4 Yesu ndi amene anakhala mbali yoyamba ya mbewu ya Abulahamu, ndipo mu 29 C.E. anadzozedwa ndi mzimu woyera kukhala Mesiya wolonjezedwa, kapena kuti Khristu. (Agal. 3:16) Kenako kwa zaka zitatu ndi theka, Yesu analalikira uthenga wabwino wa Ufumu kwa Ayuda. Yohane Mbatizi atagwidwa, Yesu anasonyeza kuti anthu ena adzakhala ndi chiyembekezo cholamulira mu Ufumuwo. Iye anati: “Kuyambira m’masiku a Yohane Mbatizi mpaka tsopano anthu akulimbikira kupeza mwayi wokalowa ufumu wa kumwamba, ndipo amene akulimbikira mwachamuna akuupeza.”​—Mat. 11:12.

5 Chochititsa chidwi ndi chakuti, asanalankhule za anthu ‘opeza’ Ufumu wa kumwamba, Yesu anati: “Ndithu ndikukuuzani anthu inu, Mwa onse obadwa mwa akazi, sanabadwepo wamkulu woposa Yohane Mbatizi; koma munthu amene ali wocheperapo mu ufumu wa kumwamba ndi wamkulu kuposa iyeyu.” (Mat. 11:11) Chifukwa chiyani ananena zimenezi? Ananena zimenezi chifukwa chakuti mwayi wokhala ndi chiyembekezo chokalamulira mu Ufumu, unali usanayambe kuperekedwa kwa anthu okhulupirika mpaka pamene mzimu woyera unatsanulidwa pa Pentekosite wa mu 33 C.E. Nthawi imeneyo, Yohane Mbatizi anali atamwalira kale.​—Mac. 2:1-4.

Mbewu ya Abulahamu Imayesedwa Yolungama

6, 7. (a) Kodi mbewu ya Abulahamu inali kudzachuluka “monga nyenyezi za kumwamba” m’lingaliro lotani? (b) Kodi Abulahamu analandira dalitso lotani, nanga mbewu yake ikulandiranso dalitso lofanana lotani?

6 Abulahamu anauzidwa kuti mbewu yake idzachuluka “monga nyenyezi za kumwamba” ndi mchenga wa m’mphepete mwa nyanja. (Gen. 13:16; 22:17) Apa zikusonyeza kuti m’nthawi ya Abulahamu, zinali zosatheka kwa anthu kudziwa chiwerengero cha amene adzapanga mbewu imeneyi. Koma patapita nthawi, chiwerengero cha mbewu yake yauzimu chinavumbulidwa. Kuwonjezera pa Yesu, padzakhalanso anthu ena 144,000.​—Chiv. 7:4; 14:1.

7 Pofotokoza chikhulupiriro cha Abulahamu, Mawu a Mulungu amati: “[Abulahamu] anakhulupirira Yehova, ndipo kunayesedwa kwa iye chilungamo.” (Gen. 15:5, 6) Kunena zoona, palibe munthu amene kulungama kwake kungakhale kwangwiro. (Yak. 3:2) Ngakhale zili choncho, Yehova anachita ndi Abulahamu ngati kuti anali munthu wolungama mpaka anamutcha bwenzi lake chifukwa Abulahamuyo anali ndi chikhulupiriro chachikulu. (Yes. 41:8) Anthu amene ndi mbewu yauzimu ya Abulahamu limodzi ndi Yesu amayesedwanso olungama, ndipo chifukwa cha zimenezi amadalitsidwa kwambiri kuposa Abulahamu.

8. Kodi anthu amene ndi mbewu ya Abulahamu amalandira madalitso otani?

8 Akhristu odzozedwa amayesedwa olungama chifukwa chakuti amakhulupirira nsembe ya dipo ya Yesu. (Aroma 3:24, 28) Yehova amawaona kuti ndi omasuka ku uchimo ndipo n’chifukwa chake amawadzoza ndi mzimu woyera kukhala ana auzimu a Mulungu, kapena kuti abale a Yesu Khristu. (Yoh. 1:12, 13) Iwo amalowa m’pangano latsopano ndi kukhala mtundu watsopano wa “Isiraeli wa Mulungu.” (Agal. 6:16; Luka 22:20) Umenewutu ndi mwayi waukulu! Chifukwa cha zimene Mulungu amawachitirazi, Akhristu odzozedwa sayembekezera kukhala ndi moyo wosatha padziko lapansi pano. Iwo amalolera kusiya chiyembekezo chimenechi kuti akalandire chisangalalo chosasimbika chokakhala ndi Yesu pa Tsiku la Chiweruzo ndi kulamulira limodzi naye kumwamba.​—Werengani Aroma 8:17.

9, 10. (a) Kodi Akhristu anadzozedwa liti koyamba ndi mzimu woyera, ndipo anali kudzakumana ndi zotani? (b) Kodi Akhristu odzozedwa analandira thandizo lotani?

9 Pa Pentekosite wa mu 33 C.E., kagulu ka anthu okhulupirika kanapatsidwa mwayi wokhala pakati pa anthu amene adzalamulira ndi Yesu pa Tsiku la Chiweruzo. Ophunzira a Yesu okwanira pafupifupi 120, anabatizidwa ndi mzimu woyera ndipo anakhala Akhristu oyambirira kudzozedwa. Koma chimenecho chinali chiyambi chabe. Zili choncho chifukwa chakuti kuyambira nthawi imeneyi, iwo anayenera kukhalabe okhulupirika kwa Yehova ngakhale atayesedwa ndi Satana m’njira zosiyanasiyana. Iwo anafunikira kukhalabe okhulupirika mpaka imfa kuti akalandire kolona wa moyo wakumwamba.​—Chiv. 2:10.

10 Kuti zimenezi zitheke, Yehova anapatsa Akhristu odzozedwawo malangizo ndi chilimbikitso chimene anafunikira, kudzera mwa Mawu ake ndiponso mpingo wachikhristu. Mwachitsanzo, mtumwi Paulo analembera Akhristu odzozedwa a ku Tesalonika kuti: “Tinali kudandaulira aliyense wa inu, monga tate amachitira kwa ana ake, kukutonthozani ndi kuchitira umboni kwa inu. Inde, kuti mupitirize kuyenda moyenera Mulungu amene akukuitanani ku ufumu wake ndi ulemerero.”​—1 Ates. 2:11, 12.

11. Kodi ndi zinthu zotani zimene Yehova analembera anthu a m’gulu la “Isiraeli wa Mulungu”?

11 Patadutsa zaka zambiri kuchokera pamene anthu oyambirira a mpingo wa Akhristu odzozedwa anasankhidwa, Yehova anaona kuti ndi bwino kulemba ndi kusunga mbiri ya utumiki wa Yesu wa padziko lapansi. Anaonetsetsanso kuti analemba ndi kusunga mbiri ya zochita zake ndi Akhristu odzozedwa ndiponso uphungu umene anali kuwapatsa. Motero Yehova anawonjezera Malemba Achigiriki Achikhristu pa Malemba Achiheberi omwe analipo kale. Ndipo malemba onsewa anali ouziridwa. Poyamba, Malemba Achiheberi analembedwera mtundu wa Isiraeli wakuthupi panthawi imene iwo anali pa ubale wapadera ndi Mulungu. Malemba Achigiriki Achikhristu analembedwera makamaka “Isiraeli wa Mulungu,” kutanthauza anthu odzozedwa kukhala abale ake a Khristu ndi ana auzimu a Mulungu. Koma zimenezi sizikutanthauza kuti anthu amene sanali Aisiraeli sakanapindula kwambiri pophunzira Malemba Achiheberi. Chimodzimodzinso Akhristu amene si odzozedwa ndi mzimu woyera. Iwonso amapindula kwambiri pophunzira Malemba Achigiriki Achikhristu ndi kutsatira uphungu wake.​—Werengani 2 Timoteyo 3:15-17.

12. Kodi Paulo anawakumbutsa chiyani Akhristu odzozedwa?

12 Akhristu oyambirira anayesedwa olungama ndi kudzozedwa ndi mzimu woyera kuti akalandire cholowa chawo chakumwamba. Kudzozedwa kwawo sikunawakweze kukhala mafumu pa Akhristu anzawo odzozedwa padziko lapansi. Zikuoneka kuti Akhristu ena oyambirira anaiwala mfundo imeneyi ndipo anayamba kufuna kuti azipatsidwa ulemu wosayenera pakati pa abale awo mumpingo. N’chifukwa chake Paulo anafunsa kuti: “Kodi anthu inu mwakhuta kale eti? Mwalemera kale, si choncho? Kodi mwayamba kale kulamulira monga mafumu, popanda ife? Ndipo ndikanakondadi mukanayamba kulamuliradi monga mafumu, kuti ifenso tilamulire limodzi nanu monga mafumu.” (1 Akor. 4:8) Choncho, Paulo anakumbutsa odzozedwa a m’nthawi yake kuti: “Sikuti ndife olamulira chikhulupiriro chanu, koma ndife antchito anzanu kuti mukhale ndi chimwemwe.”​—2 Akor. 1:24.

Kukwaniritsa Chiwerengero Chimene Chinaloseredwa

13. Kodi kuitanidwa kwa odzozedwa kunayenda bwanji chaka cha 33 C.E. chitadutsa?

13 Akhristu odzozedwa okwanira 144,000 sanasankhidwe onse m’nthawi ya atumwi. Odzozedwawo anapitiriza kuitanidwa m’nthawi yonse imene atumwi anali ndi moyo. Zikuoneka kuti pambuyo pake ndi anthu ochepa amene anayamba kuitanidwa. Ndipo zimenezi zinapitiriza m’zaka zonse zotsatira mpaka m’nthawi yathu ino. (Mat. 28:20) Ndiyeno Yesu atayamba kulamulira mu 1914, zinthu zinayamba kuchitika mofulumira.

14, 15. Kodi chachitika n’chiyani m’nthawi yathu pankhani yoitana odzozedwa?

14 Choyamba, Yesu anayeretsa kumwamba kuchotsako onse otsutsa ulamuliro wa Mulungu. (Werengani Chivumbulutso 12:10, 12.) Kenako anayamba kusonkhanitsa otsalira a anthu a m’boma la Ufumu wake kuti akwanitse chiwerengero cha 144,000. Zikuoneka kuti cha m’ma 1935, ntchitoyi inali itagwirika ndithu ndipo ambiri amene analabadira pamene ntchito yolalikira inali kuchitika, analibe chikhumbo chopita kumwamba. Mzimu sunali kuwachitira umboni kuti iwo anali ana a Mulungu. (Yerekezerani ndi Aroma 8:16.) Koma iwo anazindikira kuti anali a “nkhosa zina,” amene ali ndi chiyembekezo chokhala ndi moyo wosatha m’paradaiso padziko lapansi. (Yoh. 10:16) Choncho chaka cha 1935 chitadutsa, cholinga chachikulu cha ntchito yolalikira chinali chosonkhanitsa “khamu lalikulu” limene mtumwi Yohane anaona m’masomphenya, ndipo lidzapulumuka “chisautso chachikulu.”​—Chiv. 7:9, 10, 14.

15 Ngakhale zili choncho, anthu angapo aitanidwa kukhala ndi chiyembekezo chopita kumwamba kwa zaka zonsezi kuyambira m’ma 1930. Chifukwa chiyani? Nthawi zina, zingakhale chifukwa chakuti anthuwo analowa m’malo mwa ena amene poyamba anaitanidwa koma sanakhale okhulupirika. (Yerekezerani ndi Chivumbulutso 3:16.) Paulo analankhulanso za anzake ena amene anasiya choonadi. (Afil. 3:17-19) Kodi Yehova angaitane anthu otani kuti alowe m’malo mwawo? Pajatu nkhani yosankha ili m’manja mwake. Ngakhale zili choncho, n’zomveka kuti sangaitane anthu amene angotembenuka kumene, koma anthu amene akhala okhulupirika kwa nthawi yaitali mofanana ndi ophunzira amene Yesu analankhula nawo poyambitsa mwambo wa Chikumbutso. *​—Luka 22:28.

16. Ponena za odzozedwa, kodi ndife oyamikira chiyani, ndipo tili ndi chikhulupiriro chotani?

16 Komabe zikuoneka kuti pa anthu amene akuitanidwa kukhala ndi chiyembekezo chopita kumwamba kuyambira m’ma 1930, si onse amene amalowa m’malo mwa anthu amene apanduka. Zikuoneka kuti Yehova waonetsetsa kuti tikhalebe ndi Akhristu odzozedwa pakati pathu m’masiku ano onse otsiriza a dongosolo lino la zinthu mpaka “Babulo Wamkulu” atawonongedwa. * (Chiv. 17:5) Ndipo tili ndi chikhulupiriro chakuti chiwerengero chonse cha anthu 144,000 chidzakwanira panthawi yoikika ya Yehova ndipo m’kupita kwa nthawi anthu onsewa adzayamba kulamulira m’boma la Ufumuwo. Tikukhulupiriranso Mawu a ulosi onena kuti khamu lalikulu lonselo limene likukulirakulira, lidzakhalabe lokhulupirika. Posachedwapa ‘lidzatuluka m’chisautso chachikulu’ chimene chidzabwera pa dziko la Satana ndipo mosangalala lidzalowa m’dziko latsopano la Mulungu.

Boma la Kumwamba la Mulungu Latsala Pang’ono Kukwanira

17. Malinga ndi kunena kwa 1 Atesalonika 4:15-17 ndi Chivumbulutso 6:9-11, n’chiyani chachitikira Akhristu odzozedwa amene anamwalira ali okhulupirika?

17 Kuyambira mu 33 C.E., Akhristu odzozedwa ambirimbiri asonyeza chikhulupiriro cholimba ndipo apirira mokhulupirika mpaka imfa. Amenewa ayenerera kale kulandira Ufumu ndipo zikuoneka kuti kuchokera ku mayambiriro kwa nthawi ya kukhalapo kwa Khristu, iwo alandira mphoto yawo.​—Werengani 1 Atesalonika 4:15-17; Chivumbulutso 6:9-11.

18. (a) Kodi odzozedwa amene akali pa dziko lapansi amakhulupirira kuti chiyani? (b) Kodi a nkhosa zina amaona motani abale awo odzozedwa?

18 Odzozedwa amene akali pa dziko lapansi amakhulupirira ndi mtima wonse kuti akakhalabe okhulupirika, adzalandira mphoto yawo posachedwapa. Anthu ambirimbiri a nkhosa zina akamaganizira za chikhulupiriro cha abale awo odzozedwa, amagwirizana ndi mawu a mtumwi Paulo amene pofotokoza za abale odzozedwa a ku Tesalonika, anati: “Ifeyo timakunyadirani ku mipingo ya Mulungu chifukwa cha chipiriro ndi chikhulupiriro chanu pokumana ndi mazunzo, ndi masautso onse amene mukulimbana nawo. Zimenezi ndi umboni wa chiweruzo cholungama cha Mulungu, ndipo chifukwa cha izi muyesedwa oyenerera ufumu wa Mulungu, umenedi mukuuvutikira.” (2 Ates. 1:3-5) Panthawi iliyonse imene wodzozedwa womaliza adzamwalira pa dziko lapansi, boma la kumwamba la Mulungu lidzakwanira. Kudzakhala kusangalala kwadzaoneni kumwamba ndi padziko lapansi.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 15 Onani Nsanja ya Olonda ya March 1, 1992, tsamba 20, ndime 17.

^ ndime 16 Onani “Mafunso Ochokera kwa Owerenga” mu Nsanja ya Olonda ya May 1, 2007.

Kodi Mungafotokoze?

• Kodi Mulungu anamuuza chiyani Abulahamu zokhudza Tsiku la Chiweruzo?

• N’chifukwa chiyani Abulahamu anayesedwa wolungama?

• Kodi kuyesedwa olungama kwa anthu a mbewu ya Abulahamu kumawapatsa mwayi wotani?

• Kodi Akhristu onse akutsimikiza za chiyani?

[Mafunso]

[Chithunzi patsamba 20]

Yesu analimbikitsa otsatira ake kulimbikira kuti apeze Ufumu

[Chithunzi patsamba 21]

Pa Pentekosite wa mu 33 C.E., Yehova anayamba kusankha anthu amene ndi mbali yachiwiri ya mbewu ya Abulahamu

[Chithunzi patsamba 23]

A nkhosa zina amayamikira kukhala limodzi ndi Akhristu odzozedwa m’masiku otsiriza ano