Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Yang’anirani ‘Luso Lanu la Kuphunzitsa’

Yang’anirani ‘Luso Lanu la Kuphunzitsa’

 Yang’anirani ‘Luso Lanu la Kuphunzitsa’

“Lalika mawu, . . . dzudzula, tsutsa, dandaulira, ndi kuleza mtima konse, ndi luso la kuphunzitsa.”​—2 TIM. 4:2.

1. Kodi Yesu anawalamulira chiyani ophunzira ake, ndipo anapereka chitsanzo chotani?

NGAKHALE kuti Yesu ali pa dziko lapansi anachita ntchito zodabwitsa zochiritsa anthu, anali kudziwika kwambiri monga mphunzitsi osati wochiritsa kapena wochita zozizwitsa. (Maliko 12:19; 13:1) Yesu anaika patsogolo ntchito yolalikira uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu, ndipo otsatira ake masiku ano amateronso. Akhristu alamulidwa kupitiriza ntchito yopanga ophunzira mwa kuphunzitsa anthu kuti asunge zinthu zonse zimene Yesu anawalamulira.​—Mat. 28:19, 20.

2. Kodi tiyenera kuchita chiyani kuti tikwaniritse ntchito yathu yolalikira?

2 Kuti tikwaniritse ntchito yathu yopanga ophunzira, sitifunikira kusiya kukulitsa luso lathu la kuphunzitsa. Polembera kalata mlaliki mnzake Timoteyo, mtumwi Paulo anasonyeza kufunika kwa luso limeneli. Iye anati: “Udziyang’anire wekha mosalekeza, ndi kusamalanso zimene umaphunzitsa. Pitiriza kuchita zimenezi, pakuti potero, udzadzipulumutsa iwe mwini ndi aja okumvera iwe.” (1 Tim. 4:16) Kuphunzitsa kumene Paulo anali kunena pano sikungothandiza munthu kudziwa zinthu ayi. Akhristu odziwa kuphunzitsa amafika anthu pamtima ndipo amawalimbikitsa kusintha moyo wawo. Zimenezo zimafuna luso. Nanga tingachite chiyani kuti tikhale ndi “luso la kuphunzitsa” pouza ena uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu?​—2 Tim. 4:2.

 Zimene Zingatithandize Kukhala ndi “Luso la Kuphunzitsa”

3, 4. (a) Kodi tiyenera kuchita chiyani kuti tikhale ndi “luso la kuphunzitsa”? (b) Kodi Sukulu ya Utumiki wa Mulungu imatithandiza bwanji kukhala aphunzitsi ogwira mtima?

3 Pofotokoza mawu akuti “luso,” dikishonale ina imanena kuti munthu “amapeza luso mwa kuphunzira, kuchita zimene waphunzira, kapena kuonerera ena akamachita zinthuzo.” Kuti tikhale aphunzitsi ogwira mtima a uthenga wabwino, tiyenera kutsatira njira zitatu zonsezi. Timamvetsa nkhani imene tikuphunzitsa ngati tinayamba tapemphera ndi kuiphunzira patokha. (Werengani Salmo 119:27, 34) Atumiki aluso akamaphunzitsa ife tikuonerera, timaphunzirapo ndi kutengera kaphunzitsidwe kawoko. Ndipo tikamayesetsa nthawi zonse kuchita zimene tikuphunzira, timakulitsa luso lathu.​—Luka 6:40; 1 Tim. 4:13-15.

4 Yehova ndiye Mlangizi wathu Wamkulu. Iye, kudzera m’mbali ya padziko lapansi ya gulu lake, amapereka malangizo kwa atumiki ake, osonyeza mmene iwo angakwaniritsire ntchito yawo yolalikira. (Yes. 30:20, 21) Amachita zimenezi kudzera mu Sukulu ya Utumiki wa Mulungu imene mpingo uliwonse umakhala nayo mlungu ndi mlungu. Cholinga cha sukuluyi ndicho kuthandiza onse amene analembetsa kuti alengeze Ufumu wa Mulungu mogwira mtima. Pasukuluyi, buku lalikulu limene amaphunzira ndi Baibulo. Mawu a Yehova ouziridwa amatiuza zimene tiyenera kuphunzitsa. Ndiponso amatisonyeza kaphunzitsidwe koyenera ndi kogwira mtima. Sukulu ya Utumiki wa Mulungu imatikumbutsa kuti titha kukhala aphunzitsi aluso ngati tiphunzitsa zimene Mawu a Mulungu amanena, tifunsa mafunso ogwira mtima, tiphunzitsa m’njira yosavuta kumva ndiponso ngati tisonyeza chikondi ndi chidwi mwa anthu ena. Tiyeni tikambirane mfundo zimenezi iliyonse payokha. Kenako tikambirana zimene tingachite kuti timufike pa mtima wophunzira wathu.

Phunzitsani Zimene Mawu a Mulungu Amanena

5. Kodi zimene tikuphunzitsa tiyenera kuzitenga kuti, ndipo chifukwa chiyani?

5 Yesu, mphunzitsi waluso kuposa anthu onse, anaphunzitsa zimene Malemba amanena. (Mat. 21:13; Yoh. 6:45; 8:17) Iye analankhula m’dzina la amene anamutumayo osati m’dzina lake. (Yoh. 7:16-18) Ife timatengera chitsanzo chake. Choncho zimene timalankhula, kaya ndi mu utumiki wa khomo ndi khomo kapena paphunziro la Baibulo la panyumba, ziyenera kuchokera m’Mawu a Mulungu. (2 Tim. 3:16, 17) Ngakhale nzeru zathu zichuluke bwanji, sizingakhale ndi mphamvu pamunthu yofanana ndi imene Malemba ouziridwa angakhale nayo. Baibulotu ndi lamphamvu. Kaya mfundo imene tikuyesa kumuthandiza kumvetsa wophunzira wathu ikhale yotani, njira yabwino koposa yomuthandizira ndi kumuuza kuti awerenge zimene Malemba amanena.​—Werengani Aheberi 4:12.

6. Kodi mphunzitsi ayenera kuchita chiyani kuti athandize wophunzira kumvetsetsa zimene akuphunzira?

6 Apa sitikunena kuti mphunzitsi wachikhristu asamakonzekere phunziro la Baibulo la panyumba. M’malo mwake, ayenera kuganizira bwino pasadakhale malemba amene iye kapena wophunzirayo adzawerenga paphunziro la Baibulolo. Ndi bwino kuwerenga malemba amene pakuchokera zikhulupiriro zathu. M’pofunikanso  kuthandiza wophunzira kumvetsa lemba lililonse limene wawerenga.​—1 Akor. 14:8, 9.

Funsani Mafunso Ogwira Mtima

7. N’chifukwa chiyani kuphunzitsa mwa kufunsa mafunso kumakhala kogwira mtima?

7 Mphunzitsi akamafunsa mafunso mwaluso, amathandiza wophunzira kuganiza ndipo amamufika pa mtima. Choncho m’malo mouza wophunzira wanu zimene malemba akutanthauza, m’pempheni kuti akufotokozereni. Nthawi zina pangafunike funso kapena mafunso owonjezera kuti muthandize wophunzira kumvetsa bwino mfundo. Mukamaphunzitsa munthu mwanjira imeneyi, mumachita zinthu ziwiri. Mumamuthandiza kumvetsa zifukwa zotsimikizira mfundozo komanso kuzikhulupirira.​—Mat. 17:24-26; Luka 10:36, 37.

8. Kodi tingachite chiyani kuti tidziwe zimene zili mu mtima mwa wophunzira?

8 Mabuku athu amagwiritsa ntchito mafunso ndi mayankho monga njira yophunzirira. Mosakayika, anthu ambiri amene mumaphunzira nawo Baibulo savutika kuyankha mafunso osindikizidwa. Amangoyang’ana pa ndime zakezo ndi kupeza yankho. Koma mphunzitsi wozindikira sangokhutira ndi mayankho olondola amene wophunzirayo wapereka. Mwachitsanzo, wophunzira atha kufotokoza bwinobwino zimene Baibulo limanena pa nkhani ya dama. (1 Akor. 6:18) Komabe, mafunso ofunsidwa mwaluso angavumbule maganizo enieni amene wophunzirayo ali nawo pankhaniyo. N’chifukwa chake mphunzitsi ayenera kufunsa mafunso monga awa: “N’chifukwa chiyani Baibulo limaletsa anthu kugonana ngati sali pa banja? Kodi lamulo limene Mulungu anaperekali mumaliona bwanji? Kodi mukuganiza kuti pali ubwino uliwonse ngati munthu atsatira mfundo za makhalidwe abwino zimene Mulungu wapereka?” Mmene wophunzirayo angayankhire mafunso ngati amenewa, zingasonyeze zimene zilidi mu mtima mwake.​—Werengani Mateyo 16:13-17.

Phunzitsani M’njira Yosavuta Kumva

9. Kodi tiyenera kukumbukira chiyani tikamaphunzitsa mfundo za m’Malemba?

9 Mfundo zambiri za choonadi zimene zili m’Mawu a Mulungu si zovuta kumva kwenikweni. Ngakhale zili choncho, zingatheke kuti anthu amene tikuphunzira nawo Baibulo asokonezeka ndi ziphunzitso zonyenga kuzipembedzo zawo. Udindo wathu monga aphunzitsi ndi wophunzitsa Baibulo m’njira yosavuta kumva. Aphunzitsi ogwira mtima amafotokoza mfundo momveka, molondola ndiponso m’njira yosavuta kumva. Tikatsatira mfundo imeneyi, sitingacholowanitse mfundo za choonadi zomwe ndi zosavuta kumva. Pewani kufotokoza mfundo zambirimbiri. Sitifunikira kukambirana mbali iliyonse ya lemba limene tawerenga. Tiyenera kukambirana mbali yokhayo yomwe ikuthandiza kumveketsa mfundo imene tikukambirana. Wophunzirayo adzayamba kumvetsa mfundo zozama za choonadi cha m’Malemba akamapita patsogolo.​—Aheb. 5:13, 14.

10. Kodi ndi zinthu ziti zimene zimatithandiza kudziwa kuchuluka kwa mfundo zimene tingaphunzire pa phunziro la Baibulo?

10 Kodi ndi mfundo zochuluka bwanji zimene tiyenera kuphunzira pa ulendo umodzi? Apa m’pofunika kuzindikira. Luso logwira zinthu  ndiponso mpata, zimene wophunzira ndi mphunzitsi ali nazo, zimasiyana. Koma tizikumbukira nthawi zonse kuti cholinga chathu monga aphunzitsi ndi kuthandiza wophunzira kukhala ndi chikhulupiriro cholimba. N’chifukwa chake tiyenera kumupatsa nthawi yokwanira yowerenga, kumvetsa ndi kuvomereza mfundo za choonadi za m’Mawu a Mulungu. Sitiphunzira naye mfundo zochuluka kwambiri zoti sangathe kuzimvetsa. Komabe, timaonetsetsa kuti phunzirolo likuyenda. Wophunzira akangomvetsa mfundoyo, timapita pa mfundo yotsatira.​—Akol. 2:6, 7.

11. Ponena za kaphunzitsidwe kathu, kodi mtumwi Paulo akutiphunzitsa chiyani?

11 Polankhula ndi atsopano, mtumwi Paulo anafotokoza uthenga wabwino m’njira yosavuta kumva. Ngakhale kuti iye anali wophunzira kwambiri, sanalankhule mawu ovuta kumva. (Werengani 1 Akorinto 2:1, 2.) Chifukwa chakuti choonadi cha m’Malemba ndi chosavuta kumva, anthu okonda choonadi amakopeka. Munthu safunikira kukhala wophunzira kwambiri kuti amvetse choonadi.​—Mat. 11:25; Mac. 4:13; 1 Akor. 1:26, 27.

Thandizani Ophunzira Kuzindikira Phindu la Zimene Akuphunzira

12, 13. Kodi n’chiyani chingalimbikitse wophunzira kuchita zimene akuphunzira? Perekani chitsanzo.

12 Kuti tikhale mphunzitsi waluso, zimene tikuphunzitsa ziyenera kumufika pa mtima wophunzirayo. Iye ayenera kumvetsa mmene mfundozo zikumukhudzira, phindu lake ndiponso mmene angakhalire ndi moyo wabwino ngati atsatira Malemba.​—Yes. 48:17, 18.

13 Mwachitsanzo, tingakhale tikukambirana lemba la Aheberi 10:24, 25, limene limalimbikitsa Akhristu kusonkhana ndi okhulupirira anzawo kuti alimbikitsane mwa Malemba ndi kuyanjana mwachikondi. Ngati wophunzirayo sanayambebe kufika pa misonkhano ya mpingo, tingamufotokozere mwachidule mmene misonkhanoyo imachitikira ndi zimene timaphunzira kumeneko. Tingamuuze kuti ife timalambira Mulungu pamisonkhano ya mpingo ndi kuti imatithandiza kwambiri. Kenako tingapemphe wophunzirayo kupezekapo. Iye azilabadira malamulo a m’Malemba, chifukwa chakuti akufuna kumvera Yehova osati kusangalatsa munthu amene akuphunzira naye.​—Agal. 6:4, 5.

14, 15. (a) Kodi wophunzira Baibulo angaphunzire chiyani za Yehova? (b) Kodi kudziwa makhalidwe a Mulungu kungamuthandize bwanji wophunzira Baibulo?

14 Phindu lalikulu limene ophunzira amapeza pophunzira Baibulo ndiponso kugwiritsa ntchito mfundo zake, ndi lakuti amafika podziwa mmene Yehova alili ndi kuyamba kumukonda. (Yes. 42:8) Sikuti iye wangokhala Atate wachikondi, Mlengi ndiponso Mwini chilengedwe chonse basi. Koma amathandizanso anthu amene amamukonda ndi kumutumikira kudziwa makhalidwe ake ndiponso mphamvu zake. (Werengani Eksodo 34:6, 7.) Nthawi itakwana yakuti Mose atulutse mtundu wa Isiraeli mu ukapolo ku Iguputo, Yehova anadzidziwikitsa ndi mawu akuti: “Ndidzakhala amene ndidzafune kukhala.” (Eks. 3:13-15, NW) Zimenezi zinatanthauza kuti Yehova adzakhala aliyense amene akufunikira kuti akwaniritse zolinga zake pa anthu ake osankhika. Choncho Aisiraeli anafika pozindikira udindo wosiyanasiyana umene Yehova amakhala nawo monga Mpulumutsi, Wankhondo, Wopatsa ndiponso Wokwaniritsa malonjezo ake.​—Eks. 15:2, 3; 16:2-5; Yos. 23:14.

15 Pamoyo wawo, ophunzira athu sangathe kulandira thandizo la Yehova mozizwitsa ngati mmene zinalili ndi Mose. Ngakhale zili choncho, chikhulupiriro chawo chikamakula ndipo akayamba kukonda kwambiri zimene akuphunzira ndi kuzigwiritsa ntchito, iwo mosakayika adzaona kuti afunika kudalira Yehova kuti awathandize kukhala olimba mtima, awapatse nzeru ndi kuwatsogolera. Akamachita zimenezo, iwonso adzafika podziwa Yehova monga Phungu wanzeru ndi wodalirika, Mtetezi wawo ndi Wowapatsa zinthu zonse zofunika pamoyo mosaumira.​—Sal. 55:22; 63:7; Miy. 3:5, 6.

Asonyezeni Chikondi ndi Chidwi

16. Kodi n’chifukwa chiyani luso lachibadwa siliyenera kukhala vuto lalikulu pamene tikufuna kukhala mphunzitsi wogwira mtima?

16 Ngati mukuona kuti inu sindinu mphunzitsi  waluso, musataye mtima. Yehova ndi Yesu akuyang’anira ntchito yophunzitsa anthu imene ikuchitika pa dziko lonse. (Mac. 1:7, 8; Chiv. 14:6) Iwo angadalitse khama lathu kuti mawu athu akhudze anthu a mtima wabwino. (Yoh. 6:44) Ngati mphunzitsi amakondadi wophunzira wake, chikondicho chimathandiza pamene luso lachibadwa la mphunzitsiyo likuperewera. Mtumwi Paulo anasonyeza kuti iye anamvetsa kuti anthu amene akuphunzitsidwa afunika kukondedwa.​—Werengani 1 Atesalonika 2:7, 8.

17. Kodi tingasonyeze bwanji chidwi chenicheni kwa wophunzira Baibulo aliyense?

17 Tingasonyezenso chidwi chenicheni kwa wophunzira Baibulo aliyense mwa kupeza nthawi yomudziwa bwino. Tikamaphunzira naye mfundo za m’Malemba, tingathe kudziwa mmene akuchitira zinthu pamoyo wake. Tingaone kuti wayamba kale kugwiritsa ntchito pamoyo wake mfundo zina zimene waphunzira m’Baibulo. M’mbali zina, mwina angafunikirebe kusintha. Ngati paphunziro la Baibulo lililonse timuthandiza wophunzirayo kuona mmene angagwiritsire ntchito zimene akuphunzira pamoyo wake, chimenecho ndiye chikondi ndipo iye angathe kukhala wophunzira weniweni wa Khristu.

18. Kodi n’chifukwa chiyani m’pofunika kupemphera ndi wophunzira wathu ndiponso kumupempherera?

18 Chofunika koposa, tiyenera kupemphera ndi wophunzira wathu ndiponso kumupempherera. Iye ayenera kuona kuti ife tikufuna kumuthandiza kudziwa bwino Mlengi wake, kukhala bwenzi la pamtima la Mulungu ndiponso kupindula ndi malangizo ake. (Werengani Salmo 25:4, 5.) Tikamapemphera kuti Yehova azimudalitsa pamene iye akuyesetsa kutsatira zimene akuphunzira, wophunzira angaone kuti afunika kukhala ‘wochita zimene mawu amanena.’ (Yak. 1:22) Ndipo wophunzirayo akamamvetsera mapemphero athu ochokera pansi pa mtima, iyenso amaphunzira kupemphera. Zimasangalatsa kwambiri kuthandiza ophunzira Baibulo kukhala pa ubale ndi Yehova.

19. Kodi tidzakambirana chiyani m’nkhani yotsatira?

19 N’zolimbikitsa kudziwa kuti Mboni zoposa 6,500,000 padziko lonse zikuyesetsa kukhala ndi “luso la kuphunzitsa.” Zikuchita zimenezi pofuna kuthandiza anthu amtima wabwino kusunga zinthu zonse zimene Yesu analamulira. Kodi ntchito yathu yolalikira ikubala zipatso zotani? Tidzakambirana yankho la funsoli m’nkhani yotsatira.

Kodi Mukukumbukira?

• N’chifukwa chiyani Akhristu ayenera kukhala ndi “luso la kuphunzitsa”?

• Kodi tiyenera kugwiritsa ntchito njira ziti kuti kuphunzitsa kwathu kukhale kogwira mtima?

• Kodi ndi chiyani chingathandize ngati tilibe luso lachibadwa la kuphunzitsa?

[Mafunso]

[Chithunzi patsamba 9]

Kodi munalembetsa mu Sukulu ya Utumiki wa Mulungu?

[Chithunzi patsamba 10]

N’chifukwa chiyani mufunika kuuza wophunzira wanu kuwerenga m’Baibulo?

[Chithunzi patsamba 12]

Pempherani ndi wophunzira wanu ndipo mupempherereni