Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

“Wochenjera Asamalira Mayendedwe Ake”

“Wochenjera Asamalira Mayendedwe Ake”

“Wochenjera Asamalira Mayendedwe Ake”

MUNTHU wochenjera n’ngochita zinthu moyenera, wanzeru, woganiza bwino ndiponso wozindikira. Sachita zinthu mwachinyengo kapena mwaumambala. Miyambo 13:16 imati: “Yense wochenjera amachita mwanzeru.” Inde, kukhala wochenjera kapena kuti wanzeru, n’kofunika kwambiri.

Kodi tingasonyeze bwanji kuchenjera pamoyo wathu wa tsiku ndi tsiku? Tingasonyeze motani kuti ndife ochenjera pa zosankha zathu, mmene timachitira zinthu ndi ena, ndi zimene timachita pa zochitika zosiyanasiyana? Kodi anthu anzeru amapeza mphoto zanji? Nanga amapewa mavuto otani? Mfumu Solomo ya dziko lakale la Israyeli ikutipatsa mayankho ogwira mtima pa mafunsowa pamene tikuwerenga Miyambo 14:12-25. *

Sankhani Zochita Zanu Mwanzeru

Kuti tizisankha zinthu mwanzeru ndiponso kuti zinthu zizitiyendera bwino, tiyenera kudziwa kusiyanitsa chabwino ndi choipa. Komabe Baibulo limachenjeza kuti: “Ilipo njira yooneka kwa mwamuna ngati yoongoka; koma matsiriziro ake ndi njira za imfa.” (Miyambo 14:12) Chotero, tiyenera kuphunzira kusiyanitsa zimene zimaoneka ngati zoyenera ndi zimene zilidi zoyenera. Mawu akuti “njira za ifa,” akusonyeza kuti pali njira zambiri zosocheretsa. Taonani zinthu zina zimene tiyenera kusamala nazo ndi kuzipewa.

Anthu olemera ndiponso otchuka m’dzikoli kawirikawiri amaoneka aulemu wawo ndiponso osiririka. Chifukwa cha kutchuka ndi kulemera kwawo, njira zawo zingaoneke ngati zoyenera. Koma kodi ambiri mwa anthu amenewa amagwiritsa ntchito njira zotani kuti akhale olemera kapena otchuka? Kodi nthawi zonse njira zawo ndi zachilungamo ndi zoyenera? Ndiyeno pali anthu ena amene amasonyeza changu chosiririka pa zikhulupiriro za zipembedzo zawo. Koma kodi kuona mtima kwawoko ndi umboni wakuti zikhulupiriro zawozo ndi zoona?​—Aroma 10:2, 3.

Njira ina ingaoneke ngati yolondola chifukwa cha kudzinyenga tokha. Kusankha zochita potsatira zimene ifeyo tikuganiza kuti n’zolondola, ndiko kudalira mtima wathu womwe uli wonyenga. (Yeremiya 17:9) Ngati chikumbumtima chathu sichinaphunzitsidwe, chingatipangitse kuona njira yolakwika ngati yabwino. Ndiye kodi n’chiyani chimene chingatithandize kusankha njira yoyenera?

Kuti tizitha “kusiyanitsa chabwino ndi choipa,” tiyenera kumaphunzira mwakhama patokha choonadi chozama cha m’Mawu a Mulungu. Kuwonjezera apo, tiyenera kuphunzira kusiyanitsa chabwino ndi choipa mwa “kuchita nazo,” kutanthauza kugwiritsa ntchito mfundo za m’Baibulo. (Ahebri 5:14) Tiyenera kukhala osamala kuti njira yooneka ngati yolondola isatipatutse pa ‘njira yopapatiza yakumuka nayo kumoyo.’​—Mateyu 7:13, 14.

Pamene ‘Mtima Umawawa’

Kodi tingakhale achimwemwe pamene tilibe mtendere mumtima? Kodi kuseka ndi kuchita zosangalatsa kumachepetsa ululu wa mumtima? Kodi ndi chinthu chanzeru kumamwa mowa kwambiri, kapena mankhwala osokoneza bongo, kayanso kuyamba moyo wachiwerewere kuti munthu uiwale mavuto? Yankho ndi lakuti ayi. “Ngakhale m’kuseka mtima uwawa.”​Miyambo 14:13a.

Kuseka kungathe kubisa ululu koma osati kuuchotsa. “Kanthu kalikonse kali ndi nthawi yake,” limatero Baibulo. Zoona, pali “mphindi yakugwa misozi ndi mphindi yakuseka; mphindi yakulira ndi mphindi yakuvina.” (Mlaliki 3:1, 4) Ngati tikupitiriza kuvutika maganizo, tiyenera kuyesetsa kuthetsa vutolo. Tingafunsire nzeru ngati kuli kofunika. (Miyambo 24:6) * Kuseka ndiponso kuchita zosangalatsa n’kofunika, koma kuli ndi malire ake. Potichenjeza za kuipa kwa zosangalatsa zosayenera ndi kukonda zosangalatsa kwambiri, Solomo anati: “Matsiriziro a chiphwete ndi chisoni.”​Miyambo 14:13b.

Kodi Wosakhulupirira ndi Wabwino Amakhuta Motani?

Mfumu Solomo inapitiriza kuti: “Wobwerera m’mbuyo m’mtima adzakhuta njira zache; koma munthu wabwino adzakhuta za mwa iye yekha.” (Miyambo 14:14) Kodi munthu “wobwerera m’mbuyo m’mtima” kapena kuti wosakhulupirira ndi munthu wabwino amakhuta motani zipatso za ntchito zawo?

Munthu wopanda chikhulupiriro saganizira za Mulungu pa zochita zake. Chotero iye saona kuti kuchita zoyenera pamaso pa Yehova n’kofunika. (1 Petro 4:3-5) Munthu wotero amakhutira ndi zotsatira za moyo wake wokonda chuma. (Salmo 144:11-15a) Koma munthu wabwino, amakonda kuchita zokondweretsa Mulungu. Amatsatira miyezo yolungama ya Mulungu pa zochita zake zonse. Munthu wotero amakhala wokhutira podziwa kuti Yehova ndi Mulungu wake ndipo amakhala ndi chimwemwe chachikulu chifukwa chotumikira Wam’mwambamwamba.​—Salmo 144:15b.

‘Osamakhulupirira Mawu Aliwonse’

Posiyanitsa njira za anthu achibwana ndi anzeru, Solomo anati: “Wachibwana akhulupirira mawu onse; koma wochenjera asamalira mayendedwe ake.” (Miyambo 14:15) Munthu wanzeru sachita zinthu m’chimbulimbuli. M’malo mokhulupirira chilichonse chimene wamva kapena kungotsatira maganizo a ena, iye amaganizira zochita zake mwanzeru. Amayamba kaye wafufuza zinthu bwinobwino n’kusankha chochita mwanzeru.

Mwachitsanzo, taganizirani funso lakuti, “Kodi kuli Mulungu?” Wachibwana amangotsatira zimene anthu ambiri kapena anthu otchuka amakhulupirira. Koma wochenjera amayamba kaye wafufuza mfundo zake. Amaganizira malemba monga, Aroma 1:20, ndi Ahebri 3:4. Pankhani zauzimu, munthu wanzeru samangovomereza zimene atsogoleri a zipembedzo amanena. Iye amayesa mawu onse kuona ngati ali ochokera kwa Mulungu.​—1 Yohane 4:1.

Ndi chinthu chanzerudi kutsatira langizo lakuti ‘tisamakhulupirire mawu aliwonse.’ Makamaka amene ali ndi udindo wopereka uphungu kwa ena mumpingo wachikristu ayenera kutsatiradi mawu amenewa. Wopereka uphungu ayenera kukhala ndi chithunzi chonse cha zimene zachitika. Ayenera kumvetsera bwinobwino ndi kupeza mfundo zonse kuchokera kumbali zonse kuti uphungu wake ukhale woyenera ndiponso wosakondera.​—Miyambo 18:13; 29:20.

“Munthu wa Ziwembu Adzadedwa”

Ponenanso kusiyana kwina kwa munthu wanzeru ndi wopusa, mfumu ya Israyeli inati: “Wanzeru amaopa nasiya zoipa; koma wopusa amanyada osatekeseka. Wokangaza kukwiya adzachita utsiru; ndipo munthu wa ziwembu adzadedwa.”​Miyambo 14:16, 17.

Munthu wanzeru amaopa zotsatira za njira yoipa. Choncho amakhala wosamala ndipo amayamikira uphungu uliwonse umene ungam’thandize kupewa kuchita zoipa. Koma wopusa alibe mantha amenewa. Pokhala wodzidalira, modzikuza amanyalanyaza uphungu umene ena angam’patse. Sachedwa kupsa mtima, choncho amachita mopusa. Koma kodi munthu wa ziwembu adzadedwa chifukwa chiyani?

M’chinenero choyambirira, mawu amene anawamasulira kuti “ziwembu” ali ndi matanthauzo awiri. Mawuwa angatanthauze kuzindikira kapena kuchenjera. (Miyambo 1:4; 2:11; 3:21) Mawuwa angatanthauzenso maganizo oipa kapena kuganizira za chiwembu.​—Salmo 37:7; Miyambo 12:2; 24:8.

Ngati m’chinenero choyambiriracho mawuwa akutanthauza “ziwembu,” n’kosavuta kuona chifukwa chake munthu wotero amadedwa. Koma ngati tanthauzo lake lili la wozindikira kapena wochenjera, kodi munthu wotero angamadedwe chifukwa chiyani? Kodi sizoona kuti munthu wozindikira angamadedwe ndi anthu osazindikira? Mwachitsanzo, amene mwanzeru amasankha ‘kusakhala a dziko lapansi,’ amadedwa ndi dziko. (Yohane 15:19) Achinyamata achikristu amene mwanzeru satengera zochita zosayenera za anzawo kuti apewe makhalidwe oipa amanyozedwa. Mfundo ndi yakuti opembedza oona amadedwa ndi dzikoli lomwe lili m’manja mwa Satana Mdyerekezi.​—1 Yohane 5:19.

Oipa Adzagwada

Anzeru kapena ochenjera amasiyana ndi achibwana mwa njira inanso. “Achibwana amalandira cholowa cha utsiru; koma ochenjera amavala nzeru ngati korona.” (Miyambo 14:18) Chifukwa chosowa nzeru, achibwana amasankha zopanda pake. Umenewu ndiwo umakhala moyo wawo. Koma nzeru imakongoletsa ochenjera monga mmene korona amapangitsira mfumu kukhala yolemekezeka.

Mfumu yanzeruyo inati: “Oipa amagwadira abwino, ndi ochimwa pa makomo a olungama.” (Miyambo 14:19) M’mawu ena, pamapeto pake abwino amaposa oipa. Taganizirani kuchuluka kwa anthu a Mulungu ndiponso moyo wabwino kwambiri umene ali nawo panopa. Poona madalitso amene atumiki a Yehova ali nawo, otsutsa ena angakakamizike ‘kugwadira’ mkazi wa Yehova wophiphiritsira wa kumwamba amene akuimiridwa ndi otsalira odzozedwa ndi mzimu amene akali padziko lapansi. Koma ngakhale asatero, pa Armagedo, otsutsawo adzakakamizika kuvomereza kuti gulu la Mulungu la padziko lapansi likuimiradi gulu la kumwamba.​—Yesaya 60:1, 14; Agalatiya 6:16; Chivumbulutso 16:14, 16.

‘Kuchitira Chifundo Osauka’

Ponenapo za chikhalidwe cha anthu, Solomo anati: “Waumphawi adedwa ndi anzake omwe; koma akukonda wolemera achuluka.” (Miyambo 14:20) Kodi izi si zimene anthu opanda ungwirofe timachita? Pokhala odzikonda mwachibadwa, anthu amakonda olemera kuposa osauka. Koma ngakhale kuti munthu wolemera amakhala ndi abwenzi ambiri, abwenzi akewo amakhala osakhalitsa ngati chuma chake chomwecho. Kodi sitiyenera kupewa kupanga abwenzi ndi ndalama kapena mwa kusyasyalika?

Nanga bwanji ngati ifeyo tadziunika bwinobwino n’kuona kuti timakonda kuchita zosyasyalika kapena kuti kusekerera olemera ndi kunyoza osauka? Tiyenera kudziwa kuti Baibulo limatsutsa kukondera kotero. Limati: “Wonyoza anzake achimwa; koma wochitira osauka chifundo adala.”​Miyambo 14:21.

Tiziwaganizira anzathu amene ali m’mavuto. (Yakobo 1:27) Kodi tingachite zimenezi motani? Mwa kuwapatsa “chuma cha dziko lapansi.” Zimenezi zikuphatikizapo ndalama, chakudya, malo ogona, zovala ndiponso kucheza nawo. (1 Yohane 3:17) Wokomera mtima anthu otero amakhala wachimwemwe chifukwa “kupatsa kutidalitsa koposa kulandira.”​—Machitidwe 20:35.

Kodi Zinthu Zimawayendera Motani Opusa ndi Ochenjera?

Mfundo yakuti “chimene munthu achifesa, chimenenso adzachituta,” imagwira ntchito kwa wochenjera ndi wopusa yemwe. (Agalatiya 6:7) Ochenjera amachita zabwino, pamene opusa amaganizira zoipa. “Kodi oganizira zoipa sasochera?” inafunsa motero mfumu yanzeru. Yankho ndi lakuti ‘amasochera.’ “Koma akuganizira zabwino adzalandira chifundo ndi ntheradi.” (Miyambo 14:22) Anthu ochita zabwino amalandira mafuno abwino kwa anzawo komanso Mulungu amawakomera mtima.

Solomo anasonyeza kuti kupambana n’kogwirizana ndi kugwira ntchito mwakhama, ndipo kulephera n’kogwirizana ndi kulankhulalankhula m’malo mogwira ntchito. Iye anati: “M’ntchito zonse muli phindu; koma kulankhulalankhula kungopatsa umphawi.” (Miyambo 14:23) Mfundo imeneyi imagwira ntchito kwambiri pa zochita zauzimu. Tikamachita mwakhama utumiki wathu wachikristu, timapindula ndi zotsatira za kuthandiza anthu ambiri kupeza choonadi chopulumutsa moyo cha m’Mawu a Mulungu. Tikamagwira mokhulupirika ntchito iliyonse yotumikira Mulungu imene tapatsidwa, tidzakhala achimwemwe ndi okhutira.

“Korona wa anzeru ndi chuma chawo; utsiru wa opusa ndiwo utsiru,” limatero Baibulo pa Miyambo 14:24. Izi zingatanthauze kuti nzeru zimene anzeru amayesetsa kukhala nazo ndizo chuma chawo, ndipo zili ngati korona wawo kapena kuti zimawakongoletsa. Koma opusa amangopeza utsiru. Buku lina limati mwambi umenewu ungatanthauzenso kuti “chuma chimakongoletsa anthu amene amachigwiritsa ntchito bwino . . . [pamene] opusa amangokhala ndi kupusa kwawo.” Kaya zilidi choncho kapena ayi, mfundo ndi yakuti munthu wanzeru zinthu zimamuyendera bwino kuposa wopusa.

Mfumu ya Israyeli inati: “Mboni yoona imalanditsa miyoyo; koma wolankhula zonama angonyenga.” (Miyambo 14:25) Ngakhale kuti izi n’zoonadi pa milandu, taganizirani mmene zikugwirira ntchito pa utumiki wathu. Ntchito yathu yolalikira Ufumu ndi kupanga ophunzira imaphatikizapo kuchitira umboni choonadi cha Mawu a Mulungu. Umboni umenewu umalanditsa anthu oona mtima ku chipembedzo chonyenga ndipo umapulumutsa miyoyo. Tikamadzipenyerera tokha ndiponso kusamala zimene timaphunzitsa, tidzadzipulumutsa tokha ndi amene amatimvetsera. (1 Timoteo 4:16) Popitiriza kuchita zimenezi, tiyeni tikhale tcheru kuti tikhale ochenjera m’mbali zonse za moyo wathu.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 11 Onani Galamukani! yachingelezi ya October 22, 1987, tsamba 11 mpaka 16.

[Chithunzi patsamba 18]

Kuti tizitha kusiyanitsa chabwino ndi choipa tiyenera kuphunzira mwakhama choonadi chozama

[Chithunzi patsamba 18]

Kodi moyo wokonda chuma umakhutiritsadi?