Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

“Hema wa Oongoka Mtima Adzakula”

“Hema wa Oongoka Mtima Adzakula”

 “Hema wa Oongoka Mtima Adzakula”

NKHONDO ya Harmagedo ikadzaulika n’kuthetsa dongosolo la zinthu loipa la Satanali, “nyumba ya oipa idzapasuka.” Koma bwanji za “hema wa oongoka mtima”? M’dziko latsopano limene Mulungu adzabweretse, hema ameneyu “adzakula.”​—Miyambo 14:11.

Koma mpaka kufika panthawi imene ‘oipa adzalikhidwe m’dziko, achiwembu n’kuzulidwamo,’ anthu angwiro ayenera kukhalira limodzi ndi anthu oipa. (Miyambo 2:21, 22) Kodi anthu oongoka mtima zinthu zingawayendere bwino pamenepa? Mavesi 1 mpaka 11 a chaputala 14 cha buku la m’Baibulo la Miyambo amasonyeza kuti ngati tilola kuti nzeru itsogolere mawu ndi zochita zathu, tikhoza kukhala ndi moyo wabwino ndiponso wamtendere ngakhale panopa.

Nzeru Ikamanga Banja

Posonyeza mmene mkazi angakhudzire moyo wa banja lake, Mfumu Solomo ya ku Israyeli wakale inati: “Mkazi yense wanzeru amanga banja lake; koma wopusa alipasula ndi manja ake.” (Miyambo 14:1) Kodi mkazi wanzeru amamanga bwanji banja lake? Mkazi wanzeru amalemekeza lamulo la umutu limene Mulungu anakhazikitsa. (1 Akorinto 11:3) Satsatira mzimu wodziimira payekha umene wafala m’dziko la Satanali. (Aefeso 2:2) Amagonjera mwamuna wake ndipo amalankhula zabwino za iye, zimene zimachititsa kuti anthu ena azilemekeza mwamuna wakeyo kwambiri kuposa kale. Mkazi wanzeru amatenga nawo mbali pophunzitsa ana ake zinthu zauzimu ndi zinthu zina zowathandiza pamoyo wawo. Amagwira ntchito mwakhama kuti athandize banja lake, ndipo amakonza nyumba yake bwino kuti ikhale malo osangalatsa ndi abwino kwa banja lake kukhalamo. Amasamala ndalama akamayendetsa banja lake. Mkazi amene alidi wanzeru amachititsa banja lake kukhala ndi moyo wabwino ndiponso kukhala lolimba.

Mkazi wopusa salemekeza lamulo la umutu limene Mulungu anakhazikitsa. Sachita manyazi kulankhula zinthu zoipa za mwamuna wake. Pokhala wosadziwa kusunga ndalama, amawononga ndalama zimene banjalo linachita kupeza movutikira. Amawononganso nthawi. Chifukwa cha zimenezi, nyumba yake sikhala yosamalika ndipo ana ake amadwala matenda osiyanasiyana ndiponso amadwala mwauzimu. Zoonadi, munthu wopusa amapasula banja lake.

Koma kodi munthu amakhala wanzeru kapena wopusa chifukwa chiyani? Lemba la Miyambo 14:2 limati: “Woyenda moongoka mtima aopa Yehova; koma wokhota m’njira yake am’nyoza.” Munthu woongoka mtima amaopa Mulungu, ndipo “kumuopa Yehova ndiko chiyambi cha nzeru.” (Salmo 111:10) Munthu amene alidi wanzeru amadziwa kuti ndi udindo wake ‘kuopa Mulungu, ndi kusunga malamulo  ake.’ (Mlaliki 12:13) Koma munthu wopusa amachita zinthu zosemphana ndi miyezo ya Mulungu yachilungamo. Njira zake zimakhala zokhota. Munthu woteroyo amanyoza Mulungu, ndipo mumtima mwake amanena kuti “kulibe Mulungu.”​—Salmo 14:1.

Nzeru Ikamatsogolera Milomo

Kodi tinganene chiyani za mawu a munthu amene amaopa Yehova ndi a munthu amene amanyoza Yehova? Mfumuyo inati: “M’kamwa mwa chitsiru muli nthyole ya kudzikuza; koma milomo ya anzeru idzawasunga.” (Miyambo 14:3) Popeza sakhala ndi nzeru yochokera kumwamba, munthu wopusa sakhala wokonda mtendere kapena womvetsa zinthu. Nzeru imene imatsogolera mapazi ake ndi yapadziko, ya chifuniro chachibadwidwe, ya ziwanda. Amanena mawu amtopola ndi odzikuza. Mawu ake odzitukumulawo amabweretsa mavuto ambiri kwa iyeyo ndi kwa anthu ena.​—Yakobo 3:13-18.

Milomo ya munthu wanzeru imamuteteza, zimene zimamuwonjezera chimwemwe pa moyo wake. Kodi zimenezi zimachitika bwanji? Malemba amati: “Alipo wonena mwansontho ngati kupyoza kwa lupanga; koma lilime la anzeru lilamitsa.” (Miyambo 12:18) Mawu a munthu wanzeru sakhala okhadzula kapena opweteka. Mtima wake umayamba waganizira kaye usanayankhe. (Miyambo 15:28) Mawu ake osamala amatsitsimula, ndiponso amalimbikitsa anthu amene akuvutika maganizo ndi amene akuzunzika. M’malo moputa anthu ena, mawu ake amalimbikitsa mtendere ndi bata.

Nzeru Ikamatsogolera Zochita za Anthu

Kenaka Solomo anafotokoza mwambi wochititsa chidwi kwambiri umene ukuoneka kuti ukunena za kufunika koganizira ubwino ndi kuipa kochita chinthu chinachake. Iye anati: “Popanda zoweta modyera muti see; koma mphamvu ya ng’ombe ichulukitsa phindu.”​Miyambo 14:4.

Ponena za tanthauzo la mwambi umenewu, buku lina linati: “Modyera mopanda kanthu mungasonyeze kuti kulibe ng’ombe zoti zidyetsedwe, choncho munthu sangavutikenso ndi kuyeretsamo ndi kusamalira nyamazo, motero angamawononge ndalama zochepa. Koma ‘ubwino’ umenewu sukhalaponso tikaganizira zimene zalembedwa mu [vesi] 4b: kupanda ng’ombe kungatanthauze kuti zokolola sizikhala zambiri.” Mlimiyo ayenera kusankha zochita zake mwanzeru.

Kodi sitingagwiritse ntchito mfundo ya mwambi umenewu tikamaganizira zosintha ntchito, kumanga nyumba, ndi kuchita zinthu zina zotero? Munthu wanzeru angaganizire ubwino ndi kuipa kochita zinthu zimenezo ndiyeno n’kuona ngati m’pofunikadi kuwononga mphamvu ndi ndalama zake kuchita zinthuzo.

Mboni Ikakhala Yanzeru

Solomo anapitiriza kuti: “Mboni yokhulupirika sidzanama; koma mboni yonyenga imalankhula zonama.” (Miyambo 14:5) Mabodza a mboni yonama angapweteke munthu kwambiri. Naboti wa ku Yezreeli anaponyedwa miyala mpaka kufa chifukwa chakuti anthu awiri oipa anamuchitira umboni wonama. (1 Mafumu 21:7-13) Ndiponso tisaiwale kuti zinali mboni zonama zimene zinanamizira Yesu kuti aphedwe. (Mateyu 26:59-61) Mboni zonama zinanamiziranso Stefano, wophunzira woyamba wa Yesu  kuphedwa chifukwa cha chikhulupiriro chake.​—Machitidwe 6:10, 11.

Munthu wonama akhoza kukhala wosaululika panopa, koma taganizirani za tsogolo lake. Baibulo limati Yehova amadana ndi “mboni yonama yonong’ona mabodza.” (Miyambo 6:16-19) Cholandira cha munthu woteroyo chidzakhala m’nyanja yotentha ndi moto ndi sulfure, imfa yachiwiri, limodzi ndi anthu ochita zoipa monga ambanda, achigololo, ndi olambira mafano.​—Chivumbulutso 21:8.

Mboni yokhulupirika sinama ikalumbira kuti ipereka umboni woona. Umboni wake suphatikizapo mabodza. Komabe, zimenezi sizikutanthauza kuti ayenera kuulula zonse zomwe akudziwa kwa anthu amene angafune kupweteka anthu a Yehova m’njira inayake. Makolo akale Abrahamu ndi Isake sananene zinthu zina kwa anthu amene sankalambira Yehova. (Genesis 12:10-19; 20:1-18; 26:1-10) Rahabi wa ku Yeriko anasocheretsa amuna a mfumu. (Yoswa 2:1-7) Ngakhale Yesu Kristu mwiniwakeyo sanaulule zinthu zonse panthawi imene kuchita zimenezo kukanamupweteketsa. (Yohane 7:1-10) Iye anati: “Musamapatsa chopatulikacho kwa agalu.” Chifukwa chiyani? Kuti ‘potembenuka angang’ambe inu.’​—Mateyu 7:6.

Kuphunzira Kukakhala Kosavuta

Kodi ndi anthu onse amene ali ndi nzeru? Lemba la Miyambo 14:6 limati: “Wonyoza afunafuna nzeru osaipeza; koma wozindikira saona vuto m’kuphunzira.” Wonyoza angamafune nzeru, koma nzeru yeniyeni saipeza. Popeza munthu wodzitukumula amanyoza zinthu za Mulungu, amalephera kupeza chinthu chimene chimafunika kuti munthu akhale ndi nzeru, chimene chili kumudziwa Mulungu woona molondola. Kunyada ndi kudzitukumula kwake kumamulepheretsa kuphunzira za Mulungu ndi kupeza nzeru. (Miyambo 11:2) Ndiye n’chifukwa chiyani amadzivuta kufunafuna nzeru? Mwambiwu sunanene chifukwa chake, koma mwina amachita zimenezo kuti ena aziganiza kuti ali ndi nzeru.

“Wozindikira saona vuto m’kuphunzira.” Kuzindikira tingati kumatanthauza “kumvetsa zinthu.” Ndiyo mphamvu yotha kuona kugwirizana kwa mbali zosiyanasiyana za nkhani, n’kumvetsa bwino nkhani yonseyo osati mbali zake zokhazo. Mwambi umenewu ukunena kuti kuphunzira sikumuvuta munthu amene ali ndi mphamvu yotha kuchita zimenezi.

Pankhani imeneyi, taganizirani zimene zakuchitikirani inuyo pophunzira choonadi cha m’Malemba. Pamene munayamba kuphunzira Baibulo, zina mwa mfundo zoyambirira za choonadi zimene muyenera kuti munaphunzira zikuphatikizapo ziphunzitso zikuluzikulu zokhudza Mulungu, malonjezo ake, ndi Mwana wake. Kwa kanthawi, zimenezi munkaziona kuti zinali zinthu zosaoneka bwinobwino kugwirizana kwake. Koma pamene munapitiriza kuphunzira, mbali zosiyanasiyana zija zinayamba kugwirizana ndipo munayamba kuona bwinobwino mmene zimenezi zimagwirizanirana ndi cholinga chonse cha Yehova chokhudza anthu ndi dziko lapansi. Choonadi cha m’Baibulo chinayamba kumveka ndi kulumikizana bwino. Kenaka simunkavutikanso kuphunzira ndi kukumbukira zinthu zatsopano chifukwa munkatha  kuona mmene zikugwirizanirana ndi nkhani yonseyo.

Mfumu yanzeruyo inachenjeza za kumene nzeru sizingapezeke. Inati: “Pita pamaso pa munthu wopusa, sudzazindikira milomo yakudziwa.” (Miyambo 14:7) Munthu wopusa sakhala ndi nzeru zenizeni. Sakhala ndi milomo yolankhula za nzeru. Malangizo amene akuperekedwa apa ndi oti ndi bwino kumuchokera munthu woteroyo, ndipo n’chinthu chanzeru osapitanso kwa iyeyo. Aliyense amene ali “mnzawo wa opusa adzapwetekedwa.”​—Miyambo 13:20.

Solomo akupitiriza kuti: “Nzeru ya wochenjera ndiyo yakuti azindikire njira yake; koma utsiru wa opusa ndiwo chinyengo.” (Miyambo 14:8) Munthu wanzeru amaganiza kaye asanachite chilichonse. Amaganizira zinthu zosiyanasiyana zimene angachite ndiponso zotsatirapo zake. Amasankha zochita zake mwanzeru. Nanga bwanji munthu wopusa? Amasankha njira yopusa, pokhulupirira kuti akudziwa chomwe akuchita ndiponso kuti akusankha bwino kwambiri. Kupusa kwakeko kumamunyenga.

Nzeru Ikamatsogolera Ubwenzi Wathu ndi Ena

Munthu wotsogoleredwa ndi nzeru amakhala ndi ubwenzi wabwino ndi ena. Mfumu ya Israyeliyo inanena kuti: “Zitsiru zinyoza kupalamula; koma mwa oongoka mtima muli chiyanjano.” (Miyambo 14:9) Munthu woti n’chitsiru amaona kupalamula, kapena kuti kudziimba mlandu akalakwa, ngati kopanda ntchito. Sakhala ndi maubwenzi abwino kunyumba ndi kumalo kwina chifukwa “ndi wodzitukumula kwambiri moti safuna kukonzanso ubwenzi” ndi kukhazikitsanso mtendere ndi ena. (The New English Bible) Munthu woongoka mtima amalolera zolakwa za ena. Iyeyo akalakwa, amafulumira kupepesa ndi kukhazikitsanso ubwenzi wabwino ndi ena. Chifukwa choti amafuna mtendere, amakhala ndi maubwenzi abwino ndiponso olimba.​—Ahebri 12:14.

Kenaka Solomo anatchula chinthu chimene mabwenzi angathe kulephera kuchita. Iye anati: “Mtima udziwa kuwawa kwakekwake; mlendo sadudukira ndi chimwemwe chake.” (Miyambo 14:10) Kodi nthawi zonse tingathe kufotokoza kwa ena mmene tikumvera mumtima mwathu, kaya tili ndi chisoni kapena chimwemwe, n’kuwafotokozera ndendende zimene zikutichitikira? Ndipo kodi munthu nthawi zonse angamvetsetse mmene munthu wina akumvera mumtima mwake? Yankho la mafunso awiri onsewa n’loti ayi.

Mwachitsanzo, taganizirani za maganizo ofuna kudzipha. Munthu amene ali ndi maganizo oterowo nthawi zambiri sangafotokoze bwinobwino maganizo amenewa kwa wachibale kapena mnzake. Ndipo si nthawi zonse pamene anthu ena angathe kuona zizindikiro zoti mnzawo ali ndi maganizo ofuna kudzipha. Sitiyenera kudziimba mlandu tikalephera kuona zizindikiro zimenezi n’kuchitapo kanthu kuti timuthandize munthuyo. Mwambi umenewu ukutiphunzitsanso kuti ngakhale kuti timalimbikitsidwa tikamuululira zakukhosi mnzathu amene amatimvetsa, zimene anthu angathe kuchita kuti atilimbikitse n’zochepa. Tingafunike kudalira Yehova yekha basi tikamalimbana ndi mavuto enaake aakulu.

“M’nyumba Mwake Mudzakhala Akatundu ndi Chuma”

Mfumu ya Israyeliyo inati: “Nyumba ya oipa idzapasuka; koma hema wa oongoka mtima adzakula.” (Miyambo 14:11) Munthu woipa akhoza kulemera m’dongosolo lino la zinthu ndipo akhoza kumakhala m’nyumba yabwino, koma kodi zimenezo zidzamuthandiza bwanji akadzamwalira? (Salmo 37:10) Nyumba ya munthu woongoka mtima ikhoza kukhala yonyozeka. Ngakhale ndi choncho, Salmo 112:3 limati “m’nyumba mwake mudzakhala akatundu ndi chuma.” Kodi akatundu ndi chuma chimenechi zikutanthauza chiyani?

Mawu ndi zochita zathu zikamatsogoleredwa ndi nzeru, timakhala ndi “katundu ndi ulemu” zimene zimabwera chifukwa cha nzeru. (Miyambo 8:18) Zimenezi zimaphatikizapo ubwenzi wabwino ndi Mulungu ndi anthu anzathu, ndiponso moyo wabwino ndi wokhazikika. Zoonadi, “hema wa oongoka mtima” angakule ngakhale panopa.

[Chithunzi patsamba 27]

Mkazi wanzeru amamanga banja lake

[Chithunzi patsamba 28]

“Lilime la anzeru lilamitsa”