Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Mafunso Ochokera kwa Owerenga

Mafunso Ochokera kwa Owerenga

 Mafunso Ochokera kwa Owerenga

Popeza kuti Mfumu Solomo ya dziko lakale la Israyeli inakhala yosakhulupirika kwa Mulungu mu ukalamba wake, kodi tinganene kuti sidzauka kwa akufa?​—1 Mafumu 11:3-9.

Baibulo limatchula mayina a amuna ndi akazi ena achikhulupiriro amene mosakayikira adzauka kwa akufa. Koma silinena mwatchutchutchu kuti munthu aliyense amene dzina lake lili m’Baibulomo adzauka kapena ayi. (Ahebri 11:1-40) Koma za Solomo, tingathe kudziwa chiweruzo cha Mulungu kwa iye poyerekezera zimene zinachitika pa imfa yake ndi zimene zinachitika pa imfa za anthu ena okhulupirika.

Malemba amafotokoza zinthu ziwiri zokha zimene zingachitike kwa akufa. Malembawo amasonyeza kuti akufawo akhoza kudzakhalanso ndi moyo, kapena osadzakhalanso ndi moyo mpaka muyaya. Amene amaweruzidwa kuti n’ngosayenera kuuka kwa akufa, amaponyedwa “m’gehena,” kapena kuti “m’nyanja yamoto.” (Mateyu 5:22; Marko 9:47, 48; Chivumbulutso 20:14) Ena mwa iwo ndi anthu awiri oyambirira aja, Adamu ndi Hava, Yudasi Isikariote amene anapereka Yesu, ndi ena amene anaphedwa ndi chiweruzo cha Mulungu, monga anthu a m’nthawi ya Nowa ndi anthu a ku Sodomu ndi Gomora. * Amene ali oyenera kuuka kwa akufa, akamwalira amakhala kumanda kapena kuti ku Hade. Baibulo limanena za tsogolo la anthu amenewa kuti: “Nyanja inapereka akufawo anali momwemo, ndipo imfa ndi Hade zinapereka akufawo anali m’menemo; ndipo anaweruzidwa yense monga mwa ntchito zake.”​—Chivumbulutso 20:13.

Anthu okhulupirika amene Baibulo limawatchula pa Ahebri chaputala 11, ndiye kuti ali ku Hade, kuyembekezera kuuka kwa akufa. Ena mwa amenewa ndi atumiki a Mulungu okhulupirira monga Abrahamu, Mose ndi Davide. Tsopano taonani zimene Baibulo limanena kuti zinachitika pa imfa yawo. Yehova anauza Abrahamu kuti: “Ndipo iwe udzanka kwa makolo ako m’mtendere; nudzaikidwa ndi ukalamba wabwino.” (Genesis 15:15) Anauzanso Mose kuti: “Taona, udzagona tulo ndi makolo ako.” (Deuteronomo 31:16) Za Davide, bambo wake wa Solomo, Baibulo limati: “Davide anagona pamodzi ndi makolo ake, naikidwa m’mudzi wa Davide.” (1 Mafumu 2:10) Chotero, mawu akuti ‘kugona pamodzi ndi makolo ake,’ ndi njira ina yonenera kuti munthu ameneyo ali ku Hade kapena kuti kumanda.

Kodi Solomo chinam’chitikira n’chiyani atamwalira? Baibulo limayankha kuti: “Masiku amene Solomo anakhala mfumu ya Aisrayeli onse m’Yerusalemu anali zaka makumi anayi. Ndipo Solomo anagona ndi makolo ake, naikidwa m’mudzi wa Davide atate wake.” (1 Mafumu 11:42, 43) Choncho m’pomveka kunena kuti Solomo ali ku Hade, kapena kumanda, kuyembekezera kuuka kwa akufa.

Zimenezi zikusonyeza kuti anthu ambiri amene Malemba amati ‘anagona ndi makolo awo’ akhoza kudzauka kwa akufa. Ndipotu Baibulo limanenanso motero za mafumu ambiri amene analamulira pambuyo pa Solomo, ngakhale kuti anali osakhulupirika. Zimenezi si zodabwitsa ayi, pakuti “kudzakhala kuuka kwa olungama ndi osalungama.” (Machitidwe 24:15) Komabe, “onse ali m’manda” akadzauka, m’pamene tidzadziwe amene anali oyenerera kuuka kwa akufa. (Yohane 5:28, 29) Choncho, m’malo monena motsimikiza kuti munthu wina wake wakale adzauka kapena ayi, ndi bwino kungoyembekezera chiweruzo cholungama cha Yehova.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 4 Onani Nsanja ya Olonda ya June 1, 1988, tsamba 30 mpaka 31.