Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Yehova Ndiye Mthandizi Wathu

Yehova Ndiye Mthandizi Wathu

Yehova Ndiye Mthandizi Wathu

“Thandizo langa lidzera kwa Yehova, Wakulenga zakumwamba ndi dziko lapansi.”​—SALMO 121:2.

1, 2. (a) N’chifukwa chiyani tinganene kuti tonsefe timafuna kuthandizidwa nthawi zina? (b) Kodi Yehova ndi Mthandizi wotani?

KODI ndani pakati pathupa amene safuna kuthandizidwa? Kunena zoona, tonsefe nthawi zina timafuna kuthandizidwa kuti tithe kupirira vuto lalikulu, imfa yopweteka ya munthu amene tinali kum’konda, ndiponso chiyeso chovuta kwambiri. Anthu akafuna thandizo, nthawi zambiri amapita kwa mnzawo amene amawaganizira. Vuto limapepuka tikafotokozerako munthu woteroyo za vutolo. Koma pali zina zimene munthu mnzathu sangathe kutithandiza. Komanso, ena sangathe kuti azitithandiza nthawi zonse tikafuna thandizo.

2 Komabe, pali Mthandizi amene ali ndi mphamvu zopanda malire ndiponso wopanda chinthu chimene chingamulake. Komanso, iye amatitsimikizira kuti sadzatisiya. Mthandizi ameneyu ndi amene wamasalmo anam’tchula pamene anafotokoza ndi chikhulupiriro chonse kuti: “Thandizo langa lidzera kwa Yehova.” (Salmo 121:2) N’chifukwa chiyani wamasalmoyu anali ndi chikhulupiriro chakuti Yehova adzam’thandiza? Kuti tiyankhe funso limeneli, tiyeni tione bwinobwino Salmo 121. Salmoli litithandiza kuona chifukwa chimene nafenso tingakhalire odalira Yehova kuti ndiye Mthandizi wathu.

Salephera Kuthandiza

3. Kodi n’kutheka kuti wamasalmo ankakweza maso ake ku mapiri ati, ndipo chifukwa chiyani?

3 Wamasalmoyu anayamba ndi kufotokoza kuti popeza Yehova analenga zonse, tili ndi chifukwa chomveka chom’khulupirira. Iye anati: “Ndikweza maso anga kumapiri: Thandizo langa lidzera kuti? Thandizo langa lidzera kwa Yehova, Wakulenga zakumwamba ndi dziko lapansi.” (Salmo 121:1, 2) Wamasalmoyu sikuti ankangokweza maso ku mapiri alionse. Pamene mawu amenewa ankalembedwa n’kuti kachisi wa Yehova ali ku Yerusalemu. Mzinda umenewu, womwe unali pamwamba m’mapiri a Yuda, unali malo amene Yehova ankakhalako mophiphiritsira. (Salmo 135:21) N’kutheka kuti wamasalmoyu ankakweza maso ake ku mapiri a Yerusalemu komwe anamangako kachisi wa Yehova. Ankatero posonyeza kuti akukhulupirira ndi mtima wonse kuti Yehova am’thandiza. N’chifukwa chiyani wamasalmoyu anali ndi chikhulupiriro choterechi choti Yehova angam’thandize? Chifukwa chakuti Iye ndiye “Wakulenga zakumwamba ndi dziko lapansi.” Tinganene kuti pamenepa, wamasalmoyu kwenikweni ankanena kuti: ‘Ndithudi, palibe chimene chingalepheretse Mlengi wamphamvuyonse kuti andithandize.’​—Yesaya 40:26.

4. Kodi wamasalmo anasonyeza motani kuti Yehova amakhala tcheru nthawi zonse kuona zimene anthu ake akufunikira, ndipo n’chifukwa chiyani mfundo imeneyi ili yolimbikitsa?

4 Kenako, wamasalmoyu anafotokoza kuti Yehova amakhala tcheru nthawi zonse kuona zimene atumiki ake akufunikira. Anati: “Sadzalola phazi lako literereke: Iye amene akusunga sadzawodzera. Taonani, wakusunga Israyeli sadzawodzera kapena kugona.” (Salmo 121:3, 4) N’zosatheka kuti Mulungu alole anthu amene amam’dalira ‘aterereke’ kapena kuti agwe moti sangathenso kudzuka. (Miyambo 24:16) Chifukwa? Chifukwa chakuti Yehova ali ngati mbusa wogalamuka amene akulondera nkhosa zake. Kodi izi sizolimbikitsa? Iye sangasiye m’pang’ono pomwe kuthandiza anthu ake pa zimene akufunikira. Amawalondera usana ndi usiku, mwatcheru kwambiri.

5. N’chifukwa chiyani akunena kuti Yehova ali ‘kudzanja lamanja’?

5 Pokhala ndi chikhulupiriro chakuti Yehova ndi Mtetezi wokhulupirika wa anthu ake, wamasalmoyu analemba kuti: “Yehova ndiye wakukusunga; Yehova ndiye mthunzi wako wa ku dzanja lako lamanja. Dzuwa silidzawamba usana, mwezi sudzakupanda usiku.” (Salmo 121:5, 6) Munthu amene akuyenda pansi m’chigawo chimene kumapezeka dziko la Israyeli angatetezedwe atakhala pamthunzi, kuusa dzuwa lotentha kwambiri. Yehova ali ngati mthunzi kwa anthu ake, ndipo amawateteza ku mavuto oopsa amene angawavulaze monga mmene limachitira dzuwa kukatentha. Onani kuti lembali likunena kuti Yehova ali ‘kudzanja lamanja.’ Pankhondo zakale, chishango ankachigwirira kumanzere motero sichinkateteza kwenikweni dzanja lamanja la msilikali. Bwenzi lokhulupirika linkatha kum’teteza msilikaliyo mwa kuima kudzanja lake lamanja ndi kumenya nkhondo litaima kudzanja lamanjalo. Mofanana ndi bwenzi loterolo, Yehova amaima nthawi zonse pambali pa anthu omwe amam’lambira, ndipo amakhala chire kuti awathandize.

6, 7. (a) Kodi wamasalmo akutitsimikizira motani kuti Yehova sadzasiya kuthandiza anthu ake? (b) N’chifukwa chiyani nafenso tingakhale ndi chikhulupiriro ngati chimene wamasalmo anali nacho?

6 Kodi Yehova adzasiya kuthandiza anthu ake? N’zosatheka m’pang’ono pomwe. Wamasalmoyu anamaliza motere: “Yehova adzakusunga kukuchotsera zoipa zili zonse; adzasunga moyo wako. Yehova adzasungira kutuluka kwako ndi kulowa kwako. Kuyambira tsopano kufikira nthawi zonse.” (Salmo 121:7, 8) Onani kuti mlembiyu wasiya kutsindika pa zinthu zochitika panopa ndipo wayamba kutsindika zam’tsogolo. Poyambirira, mu vesi 5, wamasalmoyu anati: ‘Yehova ndiye wakukusunga.’ Koma m’mavesi awa, wamasalmoyu analemba kuti: ‘Yehova adzakusunga.’ Motero olambira oona akuwatsimikizira kuti Yehova adzapitiriza kuwathandiza mpaka m’tsogolo. Zilibe kanthu kuti apita kuti, ndipo akukumana ndi vuto lotani, koma Yehova adzapitiriza kuwathandiza.​—Miyambo 12:21.

7 Zoonadi, amene analemba Salmo 121 anali ndi chikhulupiriro kuti Mlengi wamphamvuyonse amalondera bwino kwambiri atumiki ake, monga momwe mbusa wokonda ziweto zake amachitira, ndiponso amawalondera mwatcheru kwambiri ngati mmene amachitira mlonda wogalamuka. Tili ndi zifukwa zomveka zokhalira ndi chikhulupiriro ngati chomwe wamasalmoyu anali nacho, chifukwa chakuti Yehova sasintha. (Malaki 3:6) Kodi izi zikutanthauza kuti iye azititeteza ku mavuto athu alionsewo? Ayi, koma ngati tikum’dalira monga Mthandizi wathu, iye angatitchinjirize ku zinthu zonse zomwe zingativulaze mwauzimu. Ndiye m’pomveka kufunsa kuti, ‘Kodi Yehova amatithandiza motani?’ Tiyeni tione njira zinayi zimene iye amatithandizira. M’nkhani ino, tikambirana mmene iye ankathandizira atumiki ake m’nthawi za m’Baibulo. M’nkhani yotsatira, tiona mmene iye amathandizira anthu ake masiku ano.

Thandizo Lochokera kwa Angelo

8. Kodi n’chifukwa chiyani zili zosadabwitsa kuti angelo ali ndi chidwi kwambiri ndi zimene zimachitikira atumiki a Mulungu padziko lapansi pano?

8 Yehova amalamulira angelo mamiliyoni ambirimbiri. (Danieli 7:9, 10) Ana auzimu amenewa amachita mokhulupirika zinthu zimene iye amafuna. (Salmo 103:20) Amadziwiratu kuti Yehova amawakonda kwambiri anthu amene amam’lambira ndiponso kuti amafuna kuwathandiza. Ndiye n’zosadabwitsa kuti angelo ali ndi chidwi kwambiri ndi zimene zimachitikira atumiki a Mulungu padziko lapansi pano. (Luka 15:10) Motero, angelowo ayenera kuti amasangalala Yehova akamawatuma kuti athandize anthu. Kodi Yehova ankawagwiritsira ntchito motani angelo kuthandiza anthu om’tumikira m’nthawi zakale?

9. Perekani chitsanzo cha mmene angelo anapatsidwira mphamvu ndi Mulungu zoti ateteze anthu okhulupirika.

9 Angelo anali kupatsidwa mphamvu ndi Mulungu kuti ateteze ndi kupulumutsa anthu okhulupirika. Angelo awiri anathandiza Loti ndi ana ake aakazi kuti apulumuke pamene Sodomu ndi Gomora anali kuwonongedwa. (Genesis 19:1, 15-17) Mngelo mmodzi anapha asilikali 185,000 a Asuri amene anali kuwopseza Yerusalemu. (2 Mafumu 19:35) Danieli ataponyedwa m’dzenje la mikango, Yehova ‘anatuma mthenga [kapena kuti mngelo] wake, natseka pakamwa pa mikango.’ (Danieli 6:21, 22) Mngelo wina anatulutsa mtumwi Petro m’ndende. (Machitidwe 12:6-11) Baibulo limatchula zitsanzo zinanso zambirimbiri za mmene angelo anatetezera anthu, zomwe zimatsimikizira kuti mawu a pa Salmo 34:7 ndi oona. Mawuwo amati: “Mngelo wa Yehova azinga kuwatchinjiriza iwo akuopa Iye, nawalanditsa iwo.”

10. Kodi Yehova anagwiritsira ntchito motani mngelo kuti alimbikitse mneneri Danieli?

10 Nthawi zina, Yehova ankagwiritsira ntchito angelo kuti alimbikitse ndi kupatsa mphamvu anthu okhulupirika. Chitsanzo chogwira mtima kwambiri cha zimenezi chili m’chaputala 10 cha buku la Danieli. N’kutheka kuti panthawiyi Danieli anali atatsala pang’ono kukwanitsa zaka 100. Mneneriyu analefulidwa kwambiri, mwina chifukwa chakuti Yerusalemu anali bwinja ndiponso chifukwa cha kuchedwa kwa ntchito yomanganso kachisi. Anasokonezedwanso maganizo ataona masomphenya ochititsa mantha kwambiri. (Danieli 10:2, 3, 8) Mwachikondi chake, Mulungu anatuma mngelo kuti am’limbikitse. Mngeloyo anakumbutsa Danieli maulendo angapo kuti Mulungu anali ‘kum’konda’ kwambiri. Kodi zotsatirapo zake zinali zotani? Mneneri wokalambayu anauza mngeloyo kuti: “Mwandilimbikitsa.”​—Danieli 10:11, 19.

11. Kodi chitsanzo chimodzi cha mmene angelo anagwiritsidwira ntchito kutsogolera ntchito yolalikira uthenga wabwino ndi chiti?

11 Yehova anagwiritsiranso ntchito angelo kutsogolera ntchito yolalikira uthenga wabwino. Mngelo anauza Filipo kuti alalikire za Kristu kwa mdindo wa ku Aitiopiya, amene pambuyo pake anabatizidwa. (Machitidwe 8:26, 27, 36, 38) Patapita nthawi yochepa chichitikireni zimenezi, Mulungu anali kufuna kuti uthenga wabwino ulalikidwe kwa anthu osadulidwa amene sanali Ayuda. M’masomphenya, mngelo anaonekera kwa Korneliyo, amene sanali Myuda koma ankaopa Mulungu, ndi kumuuza kuti aitanitse mtumwi Petro. Atam’peza Petro, anthu omwe Korneliyo anawatumawo anamuuza kuti: “Korneliyo . . . anachenjezedwa ndi mngelo woyera kuti atumize nakuitaneni mumuke ku nyumba yake, ndi kum’mvetsa mawu anu.” Petro anamvera zimenezi, ndipo chifukwa cha izi anthu a m’nyumba ya Korneliyo anakhala anthu oyambirira kulowa mpingo wachikristu amene sanali Ayuda ndiponso anali anthu osadulidwa. (Machitidwe 10:22, 44-48) Taganizani mmene mungamvere mutadziwa kuti mngelo wakuthandizani kupeza munthu wamtima woyenerera.

Thandizo Lodzera mwa Mzimu Woyera

12, 13. (a) N’chifukwa chiyani atumwi a Yesu anali ndi zifukwa zomveka zokhulupirira kuti mzimu woyera udzawathandiza? (b) Kodi Akristu a m’zaka 100 zoyambirira anapatsidwa motani mphamvu ndi mzimu woyera?

12 Yesu atatsala pang’ono kufa anatsimikizira atumwi ake kuti sadzakhala opanda thandizo. Atate adzawapatsa ‘nkhoswe [kapena kuti mthandizi], Mzimu Woyera.’ (Yohane 14:26) Atumwiwo anali ndi zifukwa zomveka zokhulupirira kuti mzimu woyera udzawathandiza. Ndipotu, Malemba ouziridwa ali ndi zitsanzo zambiri zosonyeza mmene Yehova anathandiza anthu ake ndi mzimu woyera, womwe ndi mphamvu yoposa mphamvu ina iliyonse.

13 Nthawi zambirimbiri, mzimu woyera unali kugwiritsidwa ntchito kuwapatsa mphamvu anthu kuti achite zimene Yehova akufuna. Mzimu woyera unawapatsa mphamvu Oweruza kuti apulumutse Israyeli. (Oweruza 3:9, 10; 6:34) Mzimu womwewo unapatsanso mphamvu Akristu a m’zaka 100 zoyambirira kuti apitirize kulalikira molimba mtima ngakhale kuti anthu anali kuwatsutsa m’njira zosiyanasiyana. (Machitidwe 1:8; 4:31) Umboni wamphamvu wosonyeza kuti mzimu woyera unali kugwira ntchito ndi wakuti utumiki wawo unayenda bwino kwambiri. Kodi tingati n’chiyaninso chinachititsa kuti anthu “osaphunzira ndi opulukira” athe kufalitsa uthenga wa Ufumu padziko lonse lomwe linkadziwika panthawiyo?​—Machitidwe 4:13; Akolose 1:23.

14. Kodi Yehova wagwiritsira ntchito motani mzimu wake woyera pothandiza anthu ake kumvetsa zinthu?

14 Yehova anagwiritsiranso ntchito mzimu woyera kuti anthu ake athandizidwe kumvetsa zinthu. Mothandizidwa ndi mzimu wa Mulungu, Yosefe anamasulira maloto aulosi a Farao. (Genesis 41:16, 38, 39) Ndi mzimu wake, Yehova anazindikiritsa zolinga zake kwa anthu odzichepetsa koma anazibisa kwa anthu onyada. (Mateyu 11:25) Motero, pofotokoza za zinthu zimene Yehova amapatsa “iwo akum’konda Iye,” mtumwi Paulo anati: “Kwa ife Mulungu anationetsera izi mwa Mzimu.” (1 Akorinto 2:7-10) Munthu angathe kumvetsa zomwe Mulungu amafuna chifukwa cha thandizo la mzimu woyera basi.

Thandizo Lochokera M’Mawu Ake

15, 16. Kodi Yoswa anauzidwa kuti azitani kuti azichita zinthu mwanzeru?

15 Mawu ouziridwa a Yehova ‘n’ngopindulitsa pa kuphunzitsa,’ ndipo amathandiza atumiki a Mulungu kukhala ‘oyenera, okonzeka kuchita ntchito iliyonse yabwino.’ (2 Timoteo 3:16, 17) M’Baibulo muli zitsanzo zambiri zosonyeza mmene anthu a Mulungu m’nthawi zakale anathandizidwira ndi zigawo za Mawu ake zomwe zinali zitalembedwa kale.

16 Malemba anathandiza kupereka malangizo abwino kwa olambira a Mulungu. Yoswa atapatsidwa ntchito yotsogolera Israyeli, anauzidwa kuti: “Buku ili la chilamulo [chimene chinali chitalembedwa ndi Mose] lisachoke pakamwa pako; koma ulingiriremo usana ndi usiku, kuti usamalire kuchita monga mwa zonse zolembedwamo; popeza ukatero udzakometsa njira yako, nudzachita mwanzeru.” Onani kuti Mulungu sanalonjeze Yoswa kuti am’patsa nzeru mozizwitsa. M’malo mwake, mwa kuwerenga ndi kusinkhasinkha ‘buku la chilamulo,’ Yoswa akanatha kuchita zinthu mwanzeru.​—Yoswa 1:8; Salmo 1:1-3.

17. Kodi Danieli ndiponso Mfumu Yosiya anathandizidwa motani ndi zigawo za Malemba zomwe zinalipo m’nthawi zawo?

17 Mawu olembedwa a Mulungu anathandizanso kudziwikitsa zofuna ndi zolinga zake. Mwachitsanzo, Danieli anazindikira kuchokera m’mabuku a Yeremiya kutalika kwa nthawi imene Yerusalemu adzakhale bwinja. (Yeremiya 25:11; Danieli 9:2) Komanso, taonani zomwe zinachitika panthawi ya ulamuliro wa Mfumu Yosiya ya Yuda. Panthawiyo, mtunduwo unali utam’siya Yehova, ndipo zikuoneka kuti mafumu analephera kudzilembera mabuku awo a Chilamulo ndi kuchitsatira. (Deuteronomo 17:18-20) Koma ntchito yokonzanso kachisi ili m’kati, ‘buku la chilamulo’ lomwe mwinamwake linalembedwa ndi Mose linapezeka. N’kutheka kuti ili linali buku loyambirira, lomwe linamalizidwa kulembedwa zaka zoposa 800 izi zisanachitike. Yosiya atamva zimene zinali m’bukulo, anazindikira kuti anthu aphonya kwambiri zofuna za Yehova, ndipo mfumuyo inatsimikiza kuchita zinthu zimene zinali m’bukumo. (2 Mafumu 22:8; 23:1-7) Kodi sizoonekeratu kuti anthu a Mulungu a m’nthawi zakale anathandizidwa ndi zigawo za Malemba Oyera zimene zinalipo panthawiyo?

Thandizo Lodzera mwa Okhulupirira Anzathu

18. N’chifukwa chiyani tinganene kuti Yehova ndiye amapereka thandizo nthawi iliyonse imene wolambira woona wathandiza mnzake?

18 Nthawi zambiri, thandizo limene Yehova amapereka limadzera kwa okhulupirira anzathu. Kunena zoona, wolambira woona akathandiza mnzake, thandizolo limakhala litachokera kwa Mulungu. N’chifukwa chiyani tinganene choncho? Tingatero pa zifukwa ziwiri. Chifukwa choyamba n’chakuti, kuchita izi kumakhudza mzimu woyera wa Mulungu. Mzimu umenewu umabala chipatso mwa anthu amene amayesetsa kuti uziwatsogolera, ndipo mwa zina, chipatsochi ndi chikondi ndi kukoma mtima. (Agalatiya 5:22, 23) Motero, ngati mtima wa mtumiki wa Mulungu wam’sonkhezera kuti athandize mtumiki mnzake, umenewo ndi umboni wakuti mzimu wa Yehova ukugwira ntchito. Chifukwa chachiwiri n’chakuti anthufe tinapangidwa m’chifanizo cha Mulungu. (Genesis 1:26) Izi zikutanthauza kuti tingathe kusonyeza makhalidwe ake, monga chifundo ndi kuchitirana chisoni. Motero, nthawi iliyonse yomwe mtumiki wa Yehova wathandiza mnzake, thandizo limenelo kwenikweni limakhala lochokera kwa mwiniwake wa makhalidwe amene munthuyo akusonyeza.

19. Malinga ndi zomwe zili m’Baibulo, kodi Yehova anawathandiza motani anthu kudzera mwa okhulupirira anzawo?

19 M’nthawi za m’Baibulo, kodi Yehova anali kuwathandiza motani anthu kudzera mwa okhulupirira anzawo? Nthawi zambiri Yehova ankachititsa kuti mmodzi wa atumiki ake alangize mnzake, monga momwe zinakhalira pamene Yeremiya anapatsa Baruki malangizo omwe anapulumutsa moyo wake. (Yeremiya 45:1-5) Nthawi ndi nthawi, olambira oona amasonkhezeredwa ndi mtima wawo kupereka thandizo la zinthu kwa okhulupirira anzawo, monga momwe zinakhalira pamene Akristu a ku Makedoniya ndi Akaya anasonyeza mtima wofuna kuthandiza abale awo ovutika ku Yerusalemu. Mtumwi Paulo anati mtima wowolowa manja umenewo unadzetsa “chiyamiko cha kwa Mulungu,” chifukwa ndiye alidi woyenerera kum’yamikira.​—2 Akorinto 9:11.

20, 21. Kodi mtumwi Paulo anakumana ndi zotani pamene abale a ku Roma anamulimbikitsa?

20 Nkhani zosonyeza mmene atumiki a Yehova anachitira khama kuti alimbikitsane zimatigwira mtima kwambiri. Taonani chitsanzo cha zimene zinachitikira mtumwi Paulo. Paulendo wopita ku Roma atamangidwa, Paulo anadutsa msewu wa ku Roma wa Apiyo. Ulendowu unali wosasangalatsa makamaka chakumapeto kwake, chifukwa chakuti anthuwo anadutsa m’zigwa zomwe zinali ndi zithaphwi zamadzi. * Abale a mumpingo wa ku Roma anadziwa kuti Paulo akubwera. Kodi akanachita chiyani? Kodi anakanangokhala mu mzindawo m’nyumba zawo zabwino, n’kumadikirira Paulo kuti afike ndiyeno akam’lonjere?

21 Luka, yemwe analemba nawo Baibulo, yemwenso anatsagana ndi Paulo paulendowu, anasimba zimene zinachitika. Iye anati: ‘Kuchokera kumeneko [ku Roma] abalewo, pakumva za ife, anadza kukomana nafe ku Bwalo la Apiyo, ndi ku Nyumba za Alendo Zitatu.’ Kodi mukutha kuona m’maganizo mwanu zomwe zinachitikazi? Podziwa kuti Paulo akubwera, gulu la abale linanyamuka ku Roma kupita kokam’chingamira. Abale ena pagulupo anam’dikirira ku Bwalo la Apiyo, malo otchuka kwambiri omwe anthu apaulendo anali kupumulirako, ndipo anali pa mtunda wa makilomita pafupifupi 74 kuchokera ku mzinda wa Roma. Abale enawo anali kum’dikirira pa Nyumba za Alendo Zitatu, malo opumulirapo omwe anali pa mtunda wa makilomita pafupifupi 58 kuchokera mu mzindawo. Kodi Paulo anatani ataona zoterezi? Luka anati: “Pamene Paulo anawaona, anayamika Mulungu, nalimbika mtima.” (Machitidwe 28:15) Tangoganizani mmene kungowaona abalewo, omwe anadzipereka kuyenda mtunda wonsewo, kunam’limbikitsira Paulo. Ndipo kodi Paulo anayamika ndani chifukwa cha thandizo lofunikali? Anayamika Yehova Mulungu, amene anapereka thandizolo.

22. Kodi lemba lathu la chaka cha 2005 ndi liti, ndipo kodi m’nkhani yotsatirayi tiona zotani?

22 N’zoonekeratu kuti nkhani zouziridwa za zimene Mulungu anachita zimasonyezeratu kuti iye ndi Mthandizi. Palibe wina amene angafanane naye. Mogwirizana ndi zimenezi, lemba la chaka cha 2005 la Mboni za Yehova lili ndi mawu a pa Salmo 121:2, akuti: “Thandizo langa lidzera kwa Yehova.” Koma kodi Yehova amatithandiza motani masiku ano? Tiona zimenezi m’nkhani yotsatirayi.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 20 Katswiri wina wolemba ndakatulo wachiroma, dzina lake Horace (yemwe anabadwa mu 65 ndi kumwalira m’chaka cha 8 B.C.E), amene anadutsapo msewu umenewo, anafotokozapo mavuto omwe anthu ankakumana nawo chakumapeto kwa ulendo wodutsa msewu umenewu. Horace ananena kuti Bwalo la Apiyo, lomwe kwenikweni linali msika, linali “lodzaza ndi oyendetsa mabwato ndiponso anthu oumira kwambiri omwe anali ndi nyumba za alendo.” Iye anadandaula za “tizilombo touluka toluma kwambiri ndiponso achule osowetsa mtendere” komanso za madzi ake “owawa.”

Kodi Mukukumbukira?

Kodi Yehova anawathandiza motani anthu​—

• pogwiritsira ntchito angelo?

• kudzera mwa mzimu wake woyera?

• pogwiritsira ntchito Mawu ake ouziridwa?

• kudzera mwa okhulupirira anzawo?

[Mafunso]

[Mawu Otsindika patsamba 15]

Lemba la chaka cha 2005 ndi lakuti: “Thandizo langa lidzera kwa Yehova.”​—Salmo 121:2.

[Chithunzi patsamba 16]

Paulo anayamika Mulungu chifukwa cha thandizo lomwe analandira kwa abale a ku Roma