Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

ZIMENE BAIBULO LIMANENA

Imfa

Imfa

Anthu amakhala ndi maganizo osiyanasiyana pa nkhani imeneyi. Komabe Baibulo lingatithandize kudziwa zimene zimachitika munthu akamwalira.

Kodi n’zoona kuti pali chinachake chimene chimapitiriza kukhala ndi moyo munthu akamwalira?

ZIMENE ANTHU AMANENA

Ambiri amakhulupirira kuti munthu akamwalira, mzimu wake sufa ndipo umachoka n’kukakhala kwinakwake. Amati mzimuwo umapita kumwamba kapena kumoto. Ndipo ena amanena kuti munthu akafa, mzimuwo umakabadwanso kwinakwake.

ZIMENE BAIBULO LIMANENA

Baibulo silinena kuti pali chinachake chimene chimakhalabe ndi moyo munthu akamwalira. Koma limanena kuti munthu ndi “moyo.” Ndipo limanena kuti moyowo ndi umene umafa. Mwachitsanzo mneneri Ezekieli, yemwe analemba nawo Baibulo, ananena kuti “moyo” umafa. Komanso Baibulo likamanena za munthu amene wamwalira limanena kuti “munthu wakufa.” (Levitiko 21:11) Ndiye popeza “moyo” umafa, n’zomveka kunena kuti palibe chilichonse chimene chimachoka m’thupi la munthu n’kumapitirizabe kukhala ndi moyo munthuyo akamwalira.

“Moyo umene ukuchimwawo ndi umene udzafe.”Ezekieli 18:20.

Kodi chimachitika n’chiyani munthu akamwalira?

ZIMENE BAIBULO LIMANENA

Baibulo limanena kuti, “Kulibe kugwira ntchito, kuganiza zochita, kudziwa zinthu, kapena nzeru, ku Manda.” (Mlaliki 9:10) Choncho, munthu akamwalira “amabwerera kunthaka. Pa tsiku limenelo zonse zimene anali kuganiza zimatheratu.” (Salimo 146:4) Uwu ndi umboni wakuti munthu wakufa sangachite kapena kuganiza chilichonse. M’pake kuti Baibulo limayerekezera munthu amene wamwalira ndi amene ‘akugona’ tulo.—Mateyu 9:24.

N’CHIFUKWA CHIYANI KUDZIWA ZIMENEZI N’KOFUNIKA?

Anthu ambiri amene wachibale kapena mnzawo wamwalira amafuna atadziwa mayankho a mafunso otsatirawa: ‘Kodi wapita kuti? Kodi akhoza kutimva komanso kutiona? Kodi akuvutika?’ Ndiye popeza tadziwa kuti akufa sadziwa chilichonse, sitikhalanso ndi nkhawa chifukwa timadziwa kuti okondedwa athu sakuvutika. Komanso popeza palibe chilichonse chimene chimakhalabe ndi moyo munthu akafa, zimene Mulungu watilonjeza kuti adzaukitsa akufa zimakhala zomveka ndipo sitikayikira kuti adzachitadi zimenezi.—Yesaya 26:19.

“Akufa sadziwa chilichonse.”Mlaliki 9:5.