Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Bodza Loyamba: Pali Chinthu Chimene Chimakhalabe ndi Moyo Munthu Akafa

Bodza Loyamba: Pali Chinthu Chimene Chimakhalabe ndi Moyo Munthu Akafa

Kodi bodzali linayamba bwanji?

Buku lina limanena kuti Akhristu ena, omwenso anali akatswiri a maphunziro anzeru zapamwamba, anatengera chikhulupiriro cha Agiriki chakuti pali chinthu chinachake chimene sichimafa munthu akamwalira ndipo amati chinthu chimenechi chimaikidwa mwa munthu panthawi yake yobadwa.​—The New Encyclopædia Britannica (1988), Voliyumu 11, tsamba 25.

Kodi Baibulo limati chiyani?

Limanena kuti: “Mpweya wake uchoka, abwerera kumka ku nthaka yake; tsiku lomwelo zotsimikiza mtima zake zitayika.”​—Salmo 146:4.

Kodi anthu ali ndi chinthu chinachake, kapena kuti “mzimu,” chimene sichifa munthu akamwalira? Baibulo limaphunzitsa kuti Mulungu anaika mwa nyama ndiponso anthu mphamvu ya moyo, kapena kuti mzimu. Mphamvu imeneyi imakhalapo chifukwa chakuti nyama kapena munthuyo akupuma. Ndipo mphamvu imeneyi imathandiza kuti thupi likhale lamoyo. Komabe, nyama kapena munthu akasiya kupuma, mphamvu imeneyi imasiya kugwira ntchito ndipo amafa. Choncho, nyama ndiponso anthu akafa, sazindikira chilichonse.​—Genesis 3:19; Mlaliki 3:19-21; 9:5.

Kuyambira kale, chikhulupiriro chakuti chinthu china mwa munthu sichifa munthuyo akamwalira, chimayambitsa mafunso akuti: Kodi chinthu chimene sichifacho chimapita kuti munthuyo akamwalira? Kodi anthu oipa chimawachitikira n’chiyani akamwalira? Anthu amene ankati ndi Akhristu atayamba kukhulupirira bodza lakuti chinthu china chimakhalabe ndi moyo munthuyo akamwalira, anayambanso kukhulupirira bodza lina lakuti anthu oipa amakapsa kumoto.

Yerekezani ndi mavesi awa: Mlaliki 3:19; Mateyo 10:28; Machitidwe 3:23

ZOONA N’ZAKUTI:

Munthu akafa palibe chimene chimachoka mwa iye n’kupitiriza kukhalabe ndi moyo