Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Munazionapo Zinsomba Zikuluzikulu Izi?

Kodi Munazionapo Zinsomba Zikuluzikulu Izi?

Chaka chilichonse, kungoyambira mwezi wa July, nsomba zina zikuluzikulu zotchedwa right whale (Eubalaena australis) zimakonda kubwera m’mbali mwa gombe la ku Santa Catarina m’dziko la Brazil. Nsombazi zimachokera kutali kwambiri ndipo zimabwera m’mbali mwa gombeli chifukwa si lakuya kwambiri ndipo sizivutika kusamalira ana awo. Ndiyeno zikabwera, anthu komanso alendo odzaona malo amasangalala kwambiri kuziona zikuyendayenda komanso zikudumphadumpha ndi ana awo. *

N’zazikulu Koma Zimadumpha Mochititsa Chidwi

Nsomba yaikazi imatha kukhala yaitali mamita 16 ndipo imalemera matani 80 (makilogalamu 72,575). Kukula kwake tingakuyerekeze ndi basi yaikulu. Nsombazi zimakhala zakuda ndipo zili ndi mawanga oyera pamimba pake. Zili ndi mitu ikuluikulu kwambiri komanso pakamwa papakulu. Nsomba zina za m’gulu la whale zimakhala ndi chipsepse pamsana, koma nsomba zimene tikunenazi sizikhala ndi chipsepsechi. Ndiye popeza zilibe chipsepsechi, kuti zisinthe kumene zikulowera, zimagwiritsa ntchito zipsepse zam’mbali. Zimene nsombazi zimachita n’zofanana ndi zimene ndege imachita ikamakhota. Koma kuti zipite kutsogolo zimakupiza chipsepse chake chakumbuyo pochipititsa m’mwamba komanso m’munsi.

Ngakhale kuti nsombazi zimakhala zazikulu kwambiri, zimatha kudzipinda komanso kudumpha mochititsa chidwi kwambiri. Nthawi zina zimayenda mothamanga pakati pa mafunde, zimatha kutulutsa chipsepse chake chakumbuyo kwa nthawi yaitali kenako n’kumenya madzi. Anthu amasangalala kwambiri nsombazi zikamachita zimenezo ndipo amatha kuziona zikuchita zimenezi ngakhale ali patali.

N’zosiyana Kwambiri Ndi Nsomba Zina

Pamutu komanso m’mbali mwa mutu wake muli khungu lolimba. Pa khunguli pamakhala tizilombo tina tokhala ngati nsabwe. Mtsogoleri wina wa bungwe loona za nsombazi ku Brazil, dzina lake Karina Groch, anati: “Nsomba zonse za gululi zimakhala ndi khungu lolimbali ndipo iliyonse imakhala ndi khungu losiyana ndi la inzake ngati mmene timakhalira timizere ta chala cha munthu. Ndiye kuti tithe kuzindikira nsombazi, timazijambula n’kusunga zithunzizo m’mafaelo athu.”

Akatswiri a sayansi amanena kuti n’zovuta kudziwa zaka zimene nsombazi zimakhala moyo chifukwa sizikhala ndi mano. Komabe akatswiriwa amanena kuti nsombazi zimatha kukhala ndi moyo zaka pafupifupi 65. *

Chakudya Chake

Nsombazi zimakonda kudya nkhanu komanso nkhono zing’onozing’ono. Zikamasaka zakudya zakezi, zimagwiritsa ntchito kamwa lake ngati ukonde. Ndiyeno zimatsegula kukamwa kwake moti chilichonse chimene chalowa m’kamwamo, chimatsakamira mu zinthu zinazake zokhala ngati sefa. Choncho tsiku likamatha, nsomba imodzi imatha kudya matani awiri a nkhanu komanso nkhono.

M’nyengo yoti sizikubereka, mwina mu January kapena February, nsomba zambiri za mtunduwu zimakonda kupita kunyanja ya Antarctic komwe kumapezeka zakudya zambiri. Zikakhala kumeneku, zimanenepa ndipo zimakhala ndi mafuta ambiri pafupi ndi khungu lawo. Mafutawa amathandiza kuti nsombazi zisamamve kuzizira zikakhala malo ozizira kwambiri. Komanso thupi lake limatha kusintha mafutawa n’kuwagwiritsa ntchito ngati chakudya zikamayenda maulendo ataliatali.

Nsombazi Zinkaphedwa Kwambiri

Kuyambira m’zaka za m’ma 1700, anthu ambiri ankakonda kupha nsombazi. Ankaona kuti n’zosavuta kugwira chifukwa sizithamanga kwambiri. Asodzi ankatha kuzigwira ngakhale pongogwiritsa ntchito mkondo. Kuwonjezera pamenepa, nsombazi zimayandama zikaphedwa. Zimenezi zinkathandiza anthu omwe apha nsombazi kuti asamavutike kuzikokera kumtunda.

Komanso pa nthawi imeneyo bizinezi ya mafuta komanso zipsepse za nsombazi inali yotentha kwambiri. Mafutawa ankawagwiritsa ntchito ngati mafuta a nyale komanso ngati girisi. Zipsepse zake ankapangira zovala za azimayi, tinthu topangira ma ambulera tooneka ngati tizitsulo komanso zokwapulira mahatchi. Ndipotu anthu amene ankachita bizinezi ya nsombazi ankagwira nsomba zambiri. Ankati akagulitsa zipsepse za nsomba imodzi yokha, ankapeza ndalama zokwanira kubweza ndalama zonse zomwe anawononga, moti ndalama zimene amagulitsa nsomba zinazo zinkangolowa m’matumba.

Koma chakumayambiriro kwa zaka za m’ma 1900, chiwerengero cha nsombazi chinatsika kwambiri moti bizineziyi inayamba kulowa pansi. Ku Brazil, malo omaliza omwe nsombazi zinkafikira zikaphedwa, anatsekedwa m’chaka cha 1973. Patapita nthawi, nsombazi zinayambanso kuchulukana komabe zikuoneka kuti mitundu ina ya nsombazi yangotsala pang’ono kutheratu.

Monga taonera, nsomba za right whale ndi zina mwa zinthu zambiri zochititsa chidwi zimene zili padzikoli. Nsombazi zimasonyeza kuti Yehova amene anazilenga ndi Mulungu wamphamvu komanso wanzeru zakuya.—Salimo 148:7.

^ ndime 2 Malo ena amene nsombazi zimapita kukaswa ana ake ndi m’mbali mwa nyanja zikuluzikulu ku Argentina, ku Australia, ku South Africa, ku Uruguay komanso kuzilumba za Auckland.

^ ndime 8 Asayansi anapeza kuti nsomba za right whale zilipo za mitundu itatu. Mitundu imeneyi ndi Eubalaena australis, Eubalaena glacialis komanso Eubalaena japonica. Nsomba za mtundu wa Eubalaena australis zimapezeka kum’mwera kwa dziko lapansi. Pomwe zamitundu inayo zimapezeka kumpoto kwa dziko lapansi.