Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

NKHANI YA PACHIKUTO | KODI N’ZOTHEKA KUKHALA NDI BANJA LOSANGALALA?

Kodi N’chiyani Chimachititsa Kuti Anthu Azikangana M’banja?

Kodi N’chiyani Chimachititsa Kuti Anthu Azikangana M’banja?

A SARAH * ndi amuna awo a Jacob, amakhala ku Ghana ndipo akhala pa banja kwa zaka 17. Komabe nthawi zina amakangana. A Sarah anati: “Timakonda kukangana pa nkhani za ndalama. Zimandipweteka kwambiri chifukwa ndimayesetsa kusamalira banja lathu. Koma ndikangoyambitsa nkhani ya ndalama, mwamuna wanga amakwiya ndipo timasiya kuyankhulana.”

Nawonso a Jacob anavomereza zimenezi. Anati: “N’zoona kuti timakanganadi. Nthawi zina sitiyankhulana bwino ndipo zinthu zimatha kufika poipa ndithu. Ndimaona kuti zimenezi zimachitika chifukwa cha kusamvetsetsana ndiponso chifukwa choti aliyense amangopanga zake. Komanso tili ndi vuto loti timakonda kukoka nkhani, moti kankhani kang’onong’ono kamatha kupangitsa kuti tiyambane.”

A Nathan amakhala ku India, ndipo angokwatira kumene. Tsiku lina anakhumudwa kwambiri apongozi awo aamuna atawatsira mphepo. A Nathan anati: “Apongozi anga anakalipira kwambiri akazi awo atalakwitsa zinazake moti mayiwo anachoka pakhomo. Nditafunsa apongozi aamunawo chifukwa chimene anachitira zimenezi, anandipseranso mtima ineyo n’kuyamba kundikalipira.”

N’kutheka kuti nanunso mukudziwa kuti kusayankhula bwino kumayambitsa mavuto m’banja. Nthawi zina nkhani yabwinobwino imatha kusintha n’kupangitsa kuti anthu asemphane chichewa. Zimenezi zimachitika ngati ena atimva molakwika kapena ngati akuganiza kuti tayankhula mwadala zinthu zoti ziwapweteke. Komabe n’zotheka ndithu kumakhala mwamtendere ndi anthu a m’banja lathu.

Ndiye kodi mungatani ngati mwapsetsana mtima ndi anthu a m’banja lanu? N’chiyani chimene mungachite kuti muyambenso kugwirizana? Nanga mabanja angatani kuti azikhalabe mwamtendere? Werengani nkhani zotsatirazi kuti mudziwe mayankho a mafunso amenewa.

^ ndime 3 Tasintha mayina ena m’nkhanizi.