Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 KODI ZINANGOCHITIKA ZOKHA?

Thupi Lathu Limatha Kudzichiza Lokha

Thupi Lathu Limatha Kudzichiza Lokha

M’THUPI lathu mumachitika zinthu zosiyanasiyana zimene zimathandiza kuti tizikhalabe ndi moyo. China mwa zinthu zimenezi n’choti limatha kudzichiza lokha tikavulala. Kodi zimenezi zimatheka bwanji?

Taganizirani izi: Tikangovulala, thupi limayamba kudzichiritsa lokha pochita zinthu zotsatirazi:

  • Magazi athu amakhala ndi maselo enaake omwe amapangitsa kuti tikavulala pabalapo pagwirane. Maselowa amachititsa kuti magazi aundane komanso amatseka mitsempha kuti magazi asiye kutuluka.

  • Nthawi zambiri malo amene tavulalawo amatupa. Zimenezi n’zothandiza kwambiri chifukwa pabalapo pamatsekeka ndipo sipalowa tizilombo toyambitsa matenda komanso zimathandiza kuti pakhale paukhondo.

  • Pakapita masiku angapo, thupi limayamba kubwezeretsa maselo omwe anawonongeka. Izi zimathandiza kuti malo omwe anatupa aja aphwe komanso kuti mitsempha ya magazi ilumikizane n’kuyambanso kugwira ntchito bwinobwino.

  • Pomaliza, thupi limalimbitsa khungu lomwe linali pomwe tinavulalapo n’kutsala chipsera.

Akatswiri ena akupanga zinthu zapulasitiki zoti zizitha kudzikonza zokha zikawonongeka potengera mmene thupi limachitira. Popanga mapulasitikiwa akumaika timapaipi momwe mukumakhala mankhwala enaake a mitundu iwiri. Ndiye pulasitikiyo ikawonongeka, timapaipito timaphulika n’kutulutsa mankhwala aja. Mankhwalawo akasakanikirana, akumakatseka malo amene anawonongekawo ndipo akumalimbitsa malowo n’kukhala ngati mmene analili poyamba. Katswiri wina yemwe anachita nawo zimenezi ananena kuti n’zotheka kupanga zipangizo zotha kudzikonza zokha zikawonongeka potengera mmene thupi la anthu komanso la nyama limachitira likavulala.

Kodi inuyo mukuganiza bwanji? Kodi zinangochitika zokha kuti thupi lathu lizitha kudzichiza lokha kapena pali winawake amene analilenga kuti lizichita zimenezi?