Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 ZIMENE BAIBULO LIMANENA

Ndalama

Ndalama

Kodi ndalama ndi zimene zimabweretsa mavuto onse?

“Kukonda ndalama ndi muzu wa zopweteka za mtundu uliwonse.”1 Timoteyo 6:10.

ZIMENE ENA AMANENA

Ndalama ndi zimene zimabweretsa mavuto onse.

ZIMENE BAIBULO LIMANENA

“Kukonda ndalama,” osati ndalama zenizenizo, n’kumene kumayambitsa mavuto a “mtundu uliwonse.” Baibulo limanena kuti Mfumu Solomo, amene anali wolemera, anatchula mavuto atatu amene anthu okonda ndalama amakumana nawo. Vuto loyamba: Amakhala ndi nkhawa. Lemba la Mlaliki 5:12 limati: “Zambiri zimene munthu wolemera amakhala nazo zimamulepheretsa kugona.” Vuto lachiwiri: Kusakhutitsidwa. Lemba la Mlaliki 5:10 limanena kuti: “Munthu wokonda siliva sakhutira ndi siliva, ndipo wokonda chuma sakhutira ndi phindu limene amapeza.” Vuto lachitatu: Zimakhala zosavuta kuti aphwanye malamulo. Lemba la Miyambo 28:20 limati: “Woyesetsa kuti apeze chuma mofulumira, sadzapitiriza kukhala wosalakwa.”

 Kodi ndalama zimathandiza bwanji?

‘Ndalama zimateteza.’Mlaliki 7:12.

ZIMENE ENA AMANENA

Ndalama zimateteza komanso zimapangitsa munthu kukhala wosangalala.

ZIMENE BAIBULO LIMANENA

Mfundo yoti ndalama zimapangitsa munthu kukhala wosangalala komanso wotetezeka ndi bodza lamkunkhuniza. (Maliko 4:19) Komabe ngakhale zili choncho, Baibulo limati “ndalama zimathandiza pa zinthu zonse” zofunika pa moyo. (Mlaliki 10:19) Mwachitsanzo, tingagwiritse ntchito ndalama kugula zinthu zimene zingatithandize kuti tikhale ndi moyo monga chakudya komanso mankhwala.—2 Atesalonika 3:12.

Mungagwiritsenso ntchito ndalama kusamalira banja lanu. Ndipotu Baibulo limati: “Ngati munthu sasamalira anthu amene ndi udindo wake kuwasamalira, makamaka a m’banja lake, wakana chikhulupiriro ndipo ndi woipa kuposa munthu wosakhulupirira.”—1 Timoteyo 5:8.

Kodi mungatani kuti muzigwiritsa ntchito bwino ndalama?

‘Muzikhala pansi n’kuwerengera ndalama zimene mungawononge.’Luka 14:28.

ZIMENE BAIBULO LIMANENA

Muzigwiritsa ntchito ndalama m’njira imene Mulungu amavomereza. (Luka 16:9) Ndi bwino kugwiritsa ntchito ndalama mwanzeru komanso mopanda chinyengo. (Aheberi 13:18) Kutsatira malangizo oti “moyo wanu ukhale wosakonda ndalama,” kungakuthandizeni kuti musamawononge ndalama zoposa zimene mumapeza.—Aheberi 13:5.

Ngakhale kuti Baibulo sililetsa ngongole, limatichenjeza kuti: “Wobwereka amakhala kapolo wa wobwereketsayo.” (Miyambo 22:7) Muzipewa kugula zinthu musanakonzekere, chifukwa “aliyense wopupuluma, ndithu adzasauka.” (Miyambo 21:5) M’malomwake, ‘muziika kenakake pambali kunyumba kwanu malinga ndi mmene zinthu zikuyendera pa moyo wanu.’—1 Akorinto 16:2.

Baibulo limatilimbikitsa kuti ‘tikhale opatsa.’ (Luka 6:38) Anthu amene amafuna kukondweretsa Mulungu amaona kuti ndi bwinodi kukhala owolowa manja chifukwa “Mulungu amakonda munthu wopereka mokondwera.” (2 Akorinto 9:7) Choncho, “musaiwale kuchita zabwino ndi kugawana zinthu ndi ena, pakuti nsembe zotero Mulungu amakondwera nazo.”—Aheberi 13:16.