Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

 NKHANI YA PACHIKUTO

Zinthu Zitatu Zimene Sitingagule ndi Ndalama

Zinthu Zitatu Zimene Sitingagule ndi Ndalama

ANTHU ambiri masiku ano amakonda kugula zinthu. Ndipo n’zomvetsa chisoni kuti amachitabe zimenezi ngakhale kuti zingaike pangozi ntchito yawo komanso katundu wawo, kuphatikizapo nyumba.

Amalonda amakopa anthu ngati amenewa ndipo akamatsatsa malonda awo, amafuna kuti anthu aziona kuti ayenera kukhala ndi nyumba yaikulu, galimoto komanso zovala zapamwamba. Ndipo ngati alibe ndalama, amalondawo amawalimbikitsa kuti akhoza kugula zinthuzo pa ngongole. Anthu ambiri amalolera kuchita zimenezi n’cholinga choti azioneka ngati olemera, ngakhale atakhala kuti ali kale ndi ngongole zambiri.

Koma kenako amayamba kukumana ndi mavuto. Buku lina linanena kuti: “Munthu amene amagula katundu wapamwamba pa ngongole n’cholinga choti azioneka ngati wolemera, amafanana ndi munthu amene akusuta chamba n’cholinga choti asangalale. N’zoona kuti pogulapo akhoza kumaona ngati wagula zinthuzo motchipa komanso akhoza kuonekadi kuti ndi wolemera. Koma zimenezi sizichitika kwa nthawi yaitali chifukwa pamapeto pake amakhala wopanda ndalama komanso wosasangalala.”—The Narcissism Epidemic.

Baibulo limasonyeza kuti n’kupanda nzeru “kudzionetsera ndi zimene munthu ali nazo pa moyo wake.” (1 Yohane 2:16) Munthu akamakonda kwambiri kugula katundu, amalephera kupeza zinthu zomwe ndi zofunika kwambiri pa moyo wake, ndipo zinthu zimenezi ndi zoti sangagule ndi ndalama. Tiyeni tione zinthu zitatu zimene sitingagule ndi ndalama.

 1. BANJA LOGWIRIZANA

Mtsikana wina wa ku United States, dzina lake Brianne, * ananena kuti bambo ake amaona kuti ntchito yawo komanso ndalama zimene amapeza ndi zinthu zofunika kwambiri kuposa chilichonse. Iye anati: “Tili ndi chilichonse chimene timafunikira pa moyo wathu koma bambo anga sakhala pakhomo, amangokhalira kuyendayenda. Ndikudziwa kuti amachita zimenezi chifukwa cha ntchito yawo, komabe ndimaona kuti ayeneranso kumapeza nthawi yokhala ndi banja lawo.”

Zoti muganizire: Kodi mukuganiza kuti ndi zinthu ziti zimene zingadzachititse kuti bambo a Brianne adzanong’oneze bondo? Kodi kukonda kwambiri ndalama kungakhudze bwanji ubwenzi wawo ndi mwana wawoyo? Kodi bambowa angamachite chiyani kuti banja lawo lizisangalala?

Mfundo za m’Baibulo zofunika kuziganizira:

  • “Kukonda ndalama ndi muzu wa zopweteka za mtundu uliwonse, ndipo pokulitsa chikondi chimenechi, ena . . . adzibweretsera zopweteka zambiri pathupi lawo.”—1 Timoteyo 6:10.

  • “Ndi bwino kudya zamasamba koma pali chikondi, kusiyana ndi kudya nyama ya ng’ombe yamphongo yodyetsedwa bwino pali chidani.”—Miyambo 15:17.

Mfundo yofunika: Ndalama sizingapangitse kuti banja likhale logwirizana. Banja lingakhale logwirizana ngati onse m’banjamo amapeza nthawi yochezera limodzi komanso ngati amakondana.—Akolose 3:18-21.

 2. CHITETEZO CHENICHENI

Mtsikana wina wazaka 17, dzina lake Sarah ananena kuti: “Mayi anga amandiuza kuti ndidzakwatiwe ndi mwamuna wolemera komanso ndidzapeze ntchito yapamwamba kuti ndidzathe kudzisamalira kwa moyo wanga wonse. Nthawi zonse amangoganizira za mmene angapezere ndalama basi.”

Zoti muganizire: Mukamaganizira za tsogolo lanu, kodi ndi zinthu ziti zomwe zimakudetsani nkhawa kwambiri? Nanga munthu angadziwe bwanji kuti wayamba kudera nkhawa kwambiri za tsogolo lake? Kodi zimene mayi ake a Sarah ananena zinalidi zothandiza kwa mwana wawoyo?

Mfundo za m’Baibulo zofunika kuziganizira:

  • “Lekani kudziunjikira chuma padziko lapansi, pamene njenjete ndi dzimbiri zimawononga, ndiponso pamene mbala zimathyola ndi kuba.”—Mateyu 6:19.

  • “Simukudziwa kuti moyo wanu udzakhala wotani mawa.”—Yakobo 4:14.

Mfundo yofunika: Ndalama sizingapangitse kuti tikhale otetezeka chifukwa zikhoza kubedwa. Komanso sizingatiteteze ku matenda kapena imfa. (Mlaliki 7:12) Baibulo limasonyeza kuti munthu amakhala wotetezeka ngati amadziwa Mulungu komanso chifuniro chake.—Yohane 17:3.

 3. KUKHALA WOKHUTIRA

Mtsikana wina wazaka 24, dzina lake Tanya, ananena kuti: “Makolo anga anandiphunzitsa kukhala ndi moyo wosafuna zinthu zambiri. Nthawi zambiri ineyo ndi mkulu wanga tinkangokhala ndi zinthu monga zovala, zakudya ndi pogona, komabe tinkasangalala.”

Zoti muganizire: N’chifukwa chiyani zingakhale zovuta kuti munthu amene ali ndi zofunika pamoyo zokha akhale wokhutira? Kodi inuyo mumapereka chitsanzo chotani kwa banja lanu pa nkhani ya ndalama?

Mfundo za m’Baibulo zofunika kuziganizira:

  • “Pokhala ndi chakudya, zovala ndi pogona, tikhale okhutira ndi zinthu zimenezi.”—1 Timoteyo 6:8.

  • “Odala ndi anthu amene amazindikira zosowa zawo zauzimu.”—Mateyu 5:3.

Zoti muganizire: Tikhoza kukhala okhutira ngakhale titakhala kuti tilibe ndalama kapena katundu. Ndipotu Baibulo limati: “Ngakhale munthu atakhala ndi zochuluka chotani, moyo wake suchokera m’zinthu zimene ali nazo.” (Luka 12:15) Munthu angakhalenso wokhutira ngati atadziwa mayankho a mafunso ofunika otsatirawa:

  • N’chifukwa chiyani tili ndi moyo?

  • Kodi ndi zinthu zabwino ziti zimene zichitike kutsogoloku?

  • Kodi ndingatani kuti ndithetse njala yanga yauzimu?

A Mboni za Yehova, omwe amafalitsa magaziniyi, akhoza kukuthandizani kupeza mayankho a mafunso amenewa.  

^ ndime 8 Tasintha mayina m’nkhaniyi.