Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Zochitika Padzikoli

Zochitika Padzikoli

Spain

Akatswiri ena amakhulupirira kuti zochita za anthu n’zimene zinachititsa chivomezi chomwe chinachitika mu 2011 mumzinda wa Lorca, kum’mwera kwa dziko la Spain, chimene chinapha anthu 9 ndi kuvulaza anthu enanso ambirimbiri. Akatswiriwa anapeza kuti chivomezi choopsachi chinachitika kumadera amene anthu ankapopa madzi kuchokera m’nthaka pochita ulimi wothirira.

China

M’chaka cha 2012, anthu ochokera ku China okaona malo m’mayiko ena, anagwiritsa ntchito ndalama zokwana madola 102 biliyoni a ku America. Malinga ndi zimene linanena bungwe lina loona za anthu okaona malo, dziko la China ndi limene linagwiritsa ntchito ndalama zambiri kuposa dziko lina lililonse. Mayiko a Germany ndi America ndi omwe ali pa nambala 2 ndipo dziko lililonse pa awiriwa, linagwiritsa ntchito ndalama zokwana madola 84 biliyoni a ku America.

Japan

Magazini ina ya ku Britain inalemba zotsatira za kafukufuku wina amene anachitika pakati pa anthu pafupifupi 68,000 a ku Japan. Avereji ya zaka za anthuwa ndi 23. Kafukufukuyu anasonyeza kuti azimayi omwe anabadwa pakati pa 1920 ndi 1945 amene amayamba kusuta fodya asanakwanitse zaka 20, amachepetsa moyo wawo ndi zaka 10, poyerekeza ndi azimayi amene sasuta. Pomwe azibambo amene amasuta amachepetsa moyo wawo ndi zaka 8.

Mauritania

Boma la Mauritania laletsa kugula kuchokera kumayiko ena, kupanga komanso kugwiritsa ntchito mapepala apulasitiki. Bomali lachita izi pofuna kuteteza zamoyo za m’madzi komanso nyama zapamtunda zimene zimafa zikadya mapepalawa. Boma la Mauritania likulimbikitsa anthu kuti asamagwiritse ntchito mapepala apulasitiki, koma azigwiritsa ntchito zinthu zomwe zimawola chifukwa siziwononga chilengedwe.

Padziko Lonse

Makampani a inshulansi amawononga ndalama zokwana madola a ku America 50 biliyoni chaka chilichonse pa mavuto obwera chifukwa cha nyengo. Kuyambira m’ma 1980, chiwerengero cha ndalamazi chimawonjezeka kuposa kuwirikiza kawiri pa zaka 10 zilizonse. Izi zimachitika chifukwa cha kukwera mitengo wa zinthu.