GALAMUKANI! March 2014 | Kodi Mukudziwa Mmene Mulungu Analengera Zinthu Zonsezi?

Pali kusiyana kwakukulu pakati pa zimene Baibulo limanena, zokhudza mmene chilengedwechi chinalengedwera ndi zimene anthu ambiri amadziwa.

Zochitika Padzikoli

Nkhani zake: chivomezi chifukwa chopopa madzi m’nthaka, dziko limene limagwiritsa ntchito ndalama zambiri pa maulendo okaona malo, ndi kuletsa mapepala apulasitiki.

NKHANI YAPACHIKUTO

Kodi Mukudziwa Mmene Mulungu Analengera Zinthu Zonsezi?

Kodi nkhani ya m’Baibulo yonena za mmene zinthu zinalengedwera imagwirizana ndi zimene Baibulo limanena?

ZIMENE BAIBULO LIMANENA

Ndalama

Kodi ndalama ndi zimene zimabweretsa mavuto onse?

ANTHU NDI MAYIKO

Dziko la El Salvador

Werengani nkhaniyi kuti mudziwe zambiri za anthu ansangala a ku El Salvador.”

Misozi Yathu Ndi Yodabwitsa Kwambiri

Anthu amatulutsa misozi ina yomwe nyama sizitulutsa. Kodi misozi yake ndi iti?

MFUNDO ZOTHANDIZA MABANJA

Ngati Banja Lanu Silikuyenda Bwino

Kodi simukondananso ndi mwamuna kapena mkazi wanu ndipo mumangomuona ngati munthu wokhala naye nyumba imodzi basi? Mfundo 5 zimene zingathandize kuti banja lanu liziyenda bwino.

KODI ZINANGOCHITIKA ZOKHA?

Khungu la Njoka

N’chiyani chimapangitsa kuti khungu la njoka likhale lolimba kwambiri moti njokayo imatha kukwera mtengo waminga komanso kuyenda pa mchenga ukuluukulu?

Zina zimene zili pawebusaiti

Kodi Ndingatani Kuti Ndisamachite Zinthu Mozengereza?

Werengani malangizo amene angakuthandizeni kuti musamachite zinthu mozengereza

Kodi Munthu Ameneyu Ndi Woyenera Kuti Ndimange Naye Banja?

Kodi n’chiyani chimene chingakuthandizeni kuti mudziwe makhalidwe enieni a mnzanuyo?

Zimene Achinyamata Amanena pa Nkhani ya Nkhanza Zokhudza Kugonana

Onani zimene achinyamata 5 ananena pa nkhani yochitiridwa nkhanza zokhudza kugonana komanso zimene mungachite wina akakuchitirani nkhanzazo.

Mafunso: Analankhula Izi Ndani? (Genesis 41-50)

Koperani nkhaniyi ndipo muyese kulumikiza mawuwo ndi munthu amene anawalankhula.