Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Njira Yopezera Chimwemwe Chenicheni

Njira Yopezera Chimwemwe Chenicheni

Njira Yopezera Chimwemwe Chenicheni

KUTI mukhale ndi chakudya chokoma, pamafunika kukhala ndi munthu wodziwa kuphika komanso njira yabwino ya kaphikidwe. N’zofanananso ndi chimwemwe. Chimwemwe sichibwera ndi chinthu chimodzi chokha, koma pamafunika kukhala ndi zinthu zingapo pamoyo kuti munthu akhale wachimwemwe. Zinthu zake ndi monga ntchito, masewera, kuchitira zinthu limodzi ndi anthu a m’banja mwanu ndi anzanu, ndiponso zinthu zauzimu. Koma palinso zinthu zomwe sizionekera kwambiri, monga maganizo anu, zofuna zanu, ndi zolinga zanu pamoyo.

Mwayi wake ndi woti sitikufunikira kudzidziwira patokha zinthu zimene zingatibweretsere chimwemwe chenicheni. Chifukwa chiyani? Chifukwa choti Mlengi wathu watipatsa buku labwino kwambiri la malangizo. Bukuli ndi Baibulo, ndipo panopa likupezeka lonse kapena mbali zake m’zinenero 2,377, zomwe ndi zambiri kuposa za buku lina lililonse padziko lapansi.

Kuchuluka kwa zinenero za Baibulo kumeneku kukusonyeza zofuna za Mulungu kuti anthu onse akhale achimwemwe ndiponso akhale ndi moyo wabwino wauzimu. (Machitidwe 10:34, 35; 17:26, 27) Mulungu anati: “Ine ndine . . . amene ndikuphunzitsa kupindula.” Tikatsatira malamulo ake, akutilonjeza kuti tidzakhala ndi mtendere wa mumtima “ngati mtsinje.”—Yesaya 48:17, 18.

Lonjezo limeneli likutikumbutsa mawu a Yesu amene tawatchula mu nkhani yapita ija akuti: “Odala ali ozindikira kusowa kwawo kwauzimu.” (Mateyu 5:3) Kuzindikira kusowa kwauzimu kumene kwatchulidwa pano si kodzionetsera chabe. M’malo mwake kumakhudza chilichonse chimene timachita pa moyo wathu. Kumaonekera tikamakhala ofunitsitsa kumvera ndi kuphunzitsidwa ndi Mulungu chifukwa chozindikira kuti amatidziwa bwino kuposa mmene timadzidziwira eni akefe. Errol, munthu amene wakhala akuphunzira Baibulo kwa zaka zoposa 50, anati: “Chimene chimanditsimikizira ine kwambiri kuti Baibulo n’lochokeradi kwa Mulungu n’chakuti ukatsatira zimene limaphunzitsa, zimagwiradi ntchito.” Mwachitsanzo, taganizirani malangizo abwino kwambiri a m’Baibulo pa nkhani ya kufunafuna chuma ndi zosangalatsa.

Malangizo Anzeru Okhudza Ndalama

Yesu anati: “Moyo wake wa munthu sulingana ndi kuchuluka kwa zinthu zake ali nazo.” (Luka 12:15) Zoonadi, mtengo wanu weniweni ngati munthu, makamaka m’maso mwa Mulungu, sudalira pa kuchuluka kwa ndalama zimene muli nazo. Ndipotu, kufunafuna chuma nthawi zambiri kumabweretsa nkhawa, zimene zimamulanda munthu chimwemwe pamoyo wake ndiponso zimamudyera nthawi yomwe akanaigwiritsa ntchito pa zinthu zina zofunika kwambiri.—Marko 10:25; 1 Timoteo 6:10.

Malinga ndi zomwe ananena Richard Ryan, pulofesa wa maganizo a anthu ku United States, anthu akamayesetsa kupeza chimwemwe kuchokera ku chuma ndi katundu, m’pamenenso amapeza chimwemwe chochepa kuchokera ku zinthu zimenezi. Solomo, amene analemba nawo Baibulo, anafotokoza zimenezi motere: “Munthu wokonda ndalama sakhutitsidwa, ndipo munthu wokonda chuma chambiri sapeza phindu lililonse.” (Mlaliki 5:10, The New English Bible) Zimenezi tingazifanizire ndi pamalo pamene pakuyabwa chifukwa cholumidwa ndi udzudzu. Mukamakandapo kwambiri, naponso pamayabwa kwambiri, mpaka pamachita kachilonda.

Baibulo limatilimbikitsa kugwira ntchito mwakhama ndi kusangalala ndi zipatso za ntchito yathuyo. (Mlaliki 3:12, 13) Tikamachita zimenezi timadzisungira ulemu kwambiri, womwenso umathandiza kwambiri kuti munthu akhale wachimwemwe. Mwinanso tingakhale ndi mwayi wosangalala ndi zinthu zabwino m’moyo. Komabe, pali kusiyana pakati pa kusangalala ndi zinthu zimene munthu amatha kupeza chifukwa cha ndalama ndi kukhala ndi mtima wongofunafuna chuma.

Zosangalatsa Zili ndi Malo Ake

Kuona zinthu zauzimu kuti ndiye zofunika m’moyo kumatithandiza kupindula kwambiri ndi zosangalatsa zosiyanasiyana. Yesu ankakhala nawo pa chisangalalo pomwe pankakhala zakudya ndi zakumwa. (Luka 5:29; Yohane 2:1-10) Koma sikuti zinthu zimenezi ndizo zinali gwero lalikulu la chimwemwe m’moyo wake ayi. M’malo mwake, ankasangalala kwambiri kuchita zinthu zauzimu, zomwe zinaphatikizapo kuthandiza anthu kuphunzira za Mulungu ndiponso zolinga zake kwa anthu.—Yohane 4:34.

Mfumu Solomo inayesapo kuchita zosangalatsa pofuna kuona ngati ndizo zimapatsa munthu chimwemwe. Inati: “Ndisangalale koopsa.” Mfumu yolemerayi sikuti inasangalala moyerekeza ayi. Inasangalala koopsa! Koma kodi inamva motani pambuyo pake? “Izinso zinali zopanda pake,” inalemba motero mfumuyi.—Mlaliki 2:1, New English Bible.

Nthawi zambiri anthu amene amangofunafuna zosangalatsa sakhalanso okhutira. Ndipotu, ofufuza atayerekezera mtima wofunafuna zosangalatsa ndi zinthu monga kugwira ntchito yosangalatsa, kuchita zinthu zauzimu, ndiponso kucheza ndi banja, anapeza kuti mwa anthu amene anawagwiritsa ntchito pa kafukufukuyo, kufunafuna zosangalatsa kunali pomaliza penipeni pa zinthu zowathandiza kupeza chimwemwe.

Khalani Wopatsa ndi Woyamikira

M’malo mongochita zokomera iwo basi, anthu achimwemwe amakhala anthu opatsa ndiponso achidwi ndi ena. Yesu anati: “Kupatsa kutidalitsa koposa kulandira.” (Machitidwe 20:35) Kuwonjezera pa kukhala woolowa manja popereka katundu, tingagwiritsenso ntchito nthawi ndi nyonga zathu, zomwe mwina anthu makamaka a m’banja mwathu angayamikire kwambiri. Kuti ukwati ukhale wolimba ndi wosangalatsa, mwamuna ndi mkazi wake amafunika kupeza nthawi yocheza, ndipo makolo amafunika kupatula nthawi yokwanira yocheza ndi ana awo, imene angawasonyeze chikondi, ndiponso kuwaphunzitsa. Anthu m’banja akakhala opatsa pa zinthu monga zimenezi, zinthu zimawayendera bwino ndipo panyumba pawo pamakhala chimwemwe.

Komanso, anthu akakuchitirani zinthu moolowa manja, kaya pogwiritsa ntchito nthawi ndi nyonga zawo kapena mwa njira ina, kodi inuyo ‘mumakhala woyamikira’? (Akolose 3:15) Kutsatira mawu awiriwa m’moyo mwathu kungalimbikitse kwambiri ubwenzi wathu ndi anthu ena ndiponso kungatithandize kukhala achimwemwe kwambiri. Munthu akakuyamikirani mochokera pansi pa mtima, kodi inuyo simusangalala?

Kukhala woyamikira kumatithandizanso kuzindikira zinthu zabwino zomwe zikutichitikira. Pa kafukufuku wina amene anachita mosamala kwambiri, wofufuza wina wa pa yunivesite ya California, ku Riverside, m’dziko la United States, anapempha omwe anawagwiritsa ntchito pa kafukufukuyo kuti akhale ndi buku lolembamo zochitika za tsiku ndi tsiku zomwe iwo ankayamikira. N’zosadabwitsa kuti patatha milungu sikisi, anthuwo anali kuoneka osangalala kwambiri ndi moyo.

Kodi tikuphunzirapo chiyani? Mulimonse mmene zinthu zilili m’moyo wanu, phunzirani kumaganizira za zinthu zabwino zochitika pamoyo wanu. Ndipotu, izi n’zimene Baibulo limakulimbikitsani kuchita. Limati: “Kondwerani nthawi zonse. . . . M’zonse yamikani.” (1 Atesalonika 5:16, 18) Inde, kuti tithe kuchita zimenezi tifunika kuyesetsa kumakumbukira zinthu zabwino zomwe zikutichitikira. Bwanji osakhala ndi cholinga chochita zimenezi?

Chikondi ndi Chiyembekezo N’zofunika Kuti Munthu Akhale Wachimwemwe

Anthu salakwitsa akamanena kuti anthu kuyambira ali makanda mpaka kumwalira, amafuna kukondedwa. Popanda chikondi anthu sasangalala. Koma kodi chikondi n’chiyani kwenikweni? Ngakhale kuti masiku ano anthu akuwagwiritsa ntchito mwachisawawa mawu amenewa, Baibulo limawafotokoza bwino, kuti: “Chikondi chikhala chilezere.” Limapitiriza motere: “Chikondi sichidukidwa; chikondi sichidziwa kudzitamanda, sichidzikuza, sichichita zosayenera, sichitsata za mwini yekha, sichipsa mtima, sichilingirira zoipa; sichikondwera ndi chinyengo, koma chikondwera ndi choonadi; chikwirira zinthu zonse, chikhulupirira zinthu zonse, chiyembekeza zinthu zonse, chipirira zinthu zonse.”—1 Akorinto 13:4-8.

Kunena zoona chikondi n’chopanda dyera! Poti “sichitsata za mwini yekha,” chikondi chimaika patsogolo chimwemwe cha anthu ena. N’zomvetsa chisoni kuti chikondi choterechi chikusowa kwambiri masiku ano. Ndipotu, mu ulosi wake waukulu wonena za mapeto a dongosolo lino la zinthu, Yesu ananena kuti “chikondano cha anthu aunyinji chidzazirala.”—Mateyu 24:3, 12; 2 Timoteo 3:1-5.

Koma sikuti zinthu zipitirira mmene zililimu mpaka muyaya ayi, chifukwa chimenechi ndi chipongwe kwa Mlengi, amene ndiye chitsanzo chachikulu cha chikondi! (1 Yohane 4:8) Posachedwapa, Mulungu adzachotsa padziko lonse anthu onse okonda udani kapena aumbombo. Adzasiya anthu okhawo amene akuyesetsa kukhala ndi chikondi chija chomwe tachifotokoza pamwambapa. Chotsatira chake chidzakhala mtendere ndi chimwemwe padziko lonse. Lonjezo la m’Baibulo ndi loti silingalephere kukwaniritsidwa: “Katsala kanthawi ndipo woipa adzatha psiti: Inde, udzayang’anira mbuto yake, nudzapeza palibe. Koma ofatsa adzalandira dziko lapansi; nadzakondwera nawo mtendere wochuluka.”—Salmo 37:10, 11.

Tayerekezerani kuti tsiku lililonse anthu akukhala ‘mokondwera’! Ndiye kodi n’zodabwitsa kuti Baibulo limati: “Kondwerani m’chiyembekezo”? (Aroma 12:12) Kodi mukufuna kudziwa zambiri pankhani ya zinthu zosangalatsa zimene Mulungu akulonjeza anthu omvera kuti aziyembekezera? Ndiyetu tikukupemphani kuti muwerenge nkhani yotsatirayi.

[Mawu Otsindika patsamba 7]

“Kupatsa kutidalitsa koposa kulandira.”—Machitidwe 20:3

[Bokosi/Chithunzi patsamba 5]

Kodi Nkhani za Anthu Omwe Zinthu Zinawayendera Bwino ndi Zoonadi?

Nthawi zina timamva nkhani zovuta kuzitsimikizira zonena za anthu amene anakulira moyo wovutika, koma anachita khama kwambiri mpaka kufika polemera kwambiri. “Nthawi zina anthu amagwiritsa ntchito nkhani zoterezi monga umboni wakuti iwo anayesetsa kulimbana ndi mavuto, ndipo zinthu zinawayendera bwino ngakhale kuti sanakulire m’moyo wabwino kapena kuti moyo wovutikawo ndiwo unawachititsa kukhala akhama kwambiri,” linatero lipoti lina lofotokoza za chimwemwe m’nyuzipepala ya San Francisco Chronicle. “Komano vuto ndi nkhani zoterezi n’lakuti, malinga ndi kafukufuku, n’kutheka kuti anthuwo sakhala achimwemwe ayi. Amangokhala olemera basi.”

[Bokosi/Chithunzi patsamba 6]

Chimwemwe Chimathandiza Munthu Kukhala Wathanzi Labwino

Kukhala wachimwemwe ndi mankhwala pakokha. “Zikuoneka kuti kukhala wachimwemwe kapena kukhala ndi chiyembekezo, kuganizira zabwino ndi kukhala wokhutira, zomwe ndi zogwirizana ndi kukhala wachimwemwe, zimathandiza kuti munthu asamadwale chisawawa kapena asamavutike kwambiri ndi matenda a mtima, mapapo, shuga, kuthamanga kwambiri kwa magazi, chimfine, ndiponso matenda a m’chifuwa,” linatero lipoti lina m’magazini ya Time. Komanso, pa kufufuza kwina komwe anachita pakati pa odwala achikulire ku Holland anapeza kuti panyengo ya zaka zoposa naini, kukhala wachimwemwe ndiponso woganizira zinthu zabwino kunachepetsa imfa ndi theka, zomwe ndi zochititsa chidwi kwambiri!

Mpaka pano sizinadziwikebe kuti pali kugwirizana kotani pakati pa mmene maganizo a munthu alili ndi thupi lake. Komabe, kafukufuku wasonyeza kuti m’matupi mwa anthu amene amaganizira zabwino simukhala timadzi tambiri timene timasokoneza mphamvu yoteteza thupi ku matenda.

[Chithunzi pamasamba 4, 5]

Monga mmene munthu angaphikire chakudya chokoma chifukwa chotsatira njira yabwino ya kaphikidwe, nakonso kutsatira malangizo a Mulungu kungathandize munthu kupeza chimwemwe