Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kondwerani M’chiyembekezo

Kondwerani M’chiyembekezo

Kondwerani M’chiyembekezo

JOE anali atadwala kwambiri matenda a khansa omwe sakanachira. Mkazi wake, Kirsten, ndi anzake angapo anali pambali pa bedi lake ndipo anali kulankhulana. Kirsten anayang’ana mwamuna wake ndipo anaona kuti misozi inali kuyenderera m’masaya mwake. Poyamba, Kirsten anaganiza kuti Joe akumva ululu. Mwina ankamvadi ululu, koma panthawiyi, anauza mkazi wakeyo kuti sankalira chifukwa cha ululu ayi.

“Panthawi yovuta imeneyi,” anatero Kirsten, “Joe anazunguliridwa ndi anzake apamtima, amene anabwera kudzakhala naye. Komanso, anali ndi chiyembekezo cha mtengo wapatali, chomwe panthawiyi, mosiyana ndi m’mbuyo monsemo sankakayikira m’pang’ono pomwe kuti chidzakwaniritsidwa, ndipo ankadziwa kuti palibe aliyense amene angamulande chiyembekezo chimenecho. Ananena kuti misozi yakeyo, inali misozi yachimwemwe. Pambuyo pake, usiku womwewo, Joe anamwalira.”

Kodi ndi chiyembekezo chotani chimene chinalimbikitsa Joe pamene anali kudwala? Linali lonjezo la Yehova Mulungu, la moyo wosatha umene udzakhala wa thanzi m’dziko lapansi la paradaiso. (Salmo 37:10, 11, 29) Lemba la Chivumbulutso 21:3, 4 limati: “Chihema cha Mulungu chili mwa anthu; . . . ndipo adzawapukutira misozi yonse kuichotsa pamaso pawo; ndipo sipadzakhalanso imfa; ndipo sipadzakhalanso maliro, kapena kulira, kapena chowawitsa; zoyambazo [kuphatikizapo mavuto ambiri omwe timakumana nawo lerowa] zapita.”

Chiyembekezo Ngakhale kwa Akufa

Kwa Joe, kukwaniritsidwa kwa chiyembekezo chake kudzatanthauza kuuka kuchokera kumanda. Inde, analimbikitsidwa ndi lonjezo la Yesu lakuti ‘onse amene ali m’manda,’ anthu akufa amene Mulungu akuwakumbukira, adzabwerera kuchokera ku tulo ta imfa. (Yohane 5:28, 29) Kodi ndinu wachisoni chifukwa choti winawake m’banja lanu kapena mnzanu anamwalira? Ngati ndi choncho, nanunso chiyembekezo cha kuuka kwa akufa chingakulimbikitseni. N’zoona kuti, chiyembekezo chimenechi sichimachotsa kutayikidwa kumene timakhala nako pamene munthu yemwe tinali kumukonda wamwalira. Yesu “analira” pamene mnzake, Lazaro anamwalira. Koma chiyembekezo chathuchi chimachepetsa ululu umene timakhala nawo.—Yohane 11:14, 34, 35; 1 Atesalonika 4:13.

“Joe atamwalira ndi khansa,” anatero Kirsten, “ndinkamva ngati kuti sindidzakhalanso wosangalala. Ngakhale panopo, pambuyo pa zaka zingapo, ndikudziwa kuti moyo wanga m’dongosolo lino la zinthu sudzakhalanso ngati mmene unalili kale. Palibe wina aliyense amene angalowe m’malo mwa Joe. Komabe, ndinganene moona mtima kuti ndapezanso mtendere wa m’maganizo ndiponso chimwemwe.”

Mawu a Kirsten akutikumbutsa kuti m’dongosolo lino la zinthu, sitingayembekezere kumasangalala kwambiri nthawi zonse. Moyo uli ndi zabwino komanso zoipa zake. Ndipo pali nthawi zimene tizikhala okhumudwa, pamene sikungakhale koyenera m’pang’ono pomwe kukhala osangalala. (Mlaliki 3:1, 4; 7:2-4) Komanso, n’kutheka kuti ena a ife tikulimbana ndi kuvutika maganizo, kobwera pa zifukwa zosiyanasiyana. Komabe, malonjezo a m’Baibulo ndi gwero lalikulu la chilimbikitso, ndipo nzeru zosayerekezereka zimene timapeza m’Baibulo zingatithandize kupewa mbuna zambiri zimene zimapangitsa kuti tisakhale achimwemwe. “Koma wondimvera ine,” Mulungu anatero, “adzakhala wosatekeseka, nadzakhala phe osaopa zoipa.”—Miyambo 1:33.

Inde, Yehova amatifunira zabwino kwambiri. Amafuna kuti tizikhala osangalala, osati pamaso pokha, koma m’kati mwenimweni ndiponso, osati kwa zaka zowerengeka chabe ayi, koma kosatha! Choncho, Mwana wake ananena mawu osasintha awa: “Odala ali ozindikira kusowa kwawo kwauzimu.” (Mateyu 5:3) N’chinthu chanzeru kutsatira zimene Yesu ananenazi.

[Bokosi/Chithunzi patsamba 9]

Zinthu Naini Zothandiza Kuti Mukhale Achimwemwe

1. Kuona zinthu zauzimu kuti ndiye zofunika m’moyo.​Mateyu 5:3.

2. Kukhala wokhutira ndi zimene muli nazo ndiponso kupewa “chikondi cha pa ndalama.”1 Timoteo 6:6-10.

3. Kuika zosangalatsa pamalo ake.​2 Timoteo 3:1, 4.

4. Kukhala woolowa manja ndiponso kuyesetsa kuchita zinthu zosangalatsa ena.​Machitidwe 20:35.

5. Kukhala woyamikira ndiponso kuganizira zinthu zabwino zimene zikukuchitikirani.​Akolose 3:15.

6. Kukhala ndi mtima wokhululukira ena.​Mateyu 6:14.

7. Kusankha mwanzeru anthu ocheza nawo.​Miyambo 13:20.

8. Kusamalira thupi lanu ndi kupewa zizolowezi zoipa.​2 Akorinto 7:1.

9. ‘Kukondwera ndi chiyembekezo’ chomwe mwapatsidwa m’Baibulo.​Aroma 12:12.

[Zithunzi pamasamba 8, 9]

Chiyembekezo cha m’Baibulo chodzakhala ndi moyo m’dziko latsopano ndi gwero la chilimbikitso chachikulu