Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Kucheza ndi Anzanga a Ku Sukulu Kumapyola Malire Kukafika Pati?

Kodi Kucheza ndi Anzanga a Ku Sukulu Kumapyola Malire Kukafika Pati?

Zimene Achinyamata Amadzifunsa

Kodi Kucheza ndi Anzanga a Ku Sukulu Kumapyola Malire Kukafika Pati?

“Anzanga ku sukulu ankakamba za mmene asangalalira limodzi Loweruka ndi Lamlungu. Ndinkaona ngati akundisankha.”—Anatero Michelle. *

“Nthawi zina ndikaona gulu la ana ndinkati, ‘Koma ndiye amakondanatu. Nanenso ndimafuna n’takhala nawo pagulu limenelo.’”—Anatero Joe.

“Sindinkavutika kupeza anzanga ku sukulu. Zinali zophweka. Limeneli ndiye linali vuto langa.”—Anatero Maria.

NTHAWI yambiri masana imatha muli limodzi ndi anzanu ku sukulu. Mumakumana ndi zovuta zambiri zofanana, zokhumudwitsa zambiri zofanana, ndiponso pali zinthu zambiri zofanana zimene zimakuyenderani bwino. Mu zina, mungaone ngati kuti mumagwirizana pa zinthu zambiri ndi anthu amene muli nawo m’kalasi imodzi kusukuluwo kuposa makolo anu, achemwali kapena alongo anu, kapenanso Akristu anzanu. M’pomveka kuti mukhoza kukopeka nawo n’kukhala anzanu. Kodi zimenezo n’zolakwika? Kodi pali choopsa chilichonse? Ponena za anzanu ku sukulu, kodi mungadziwe bwanji kuti mukucheza nawo mopyola malire? Kodi ndi pati pomwe pangakhale malire?

Mumafunika Kukhala ndi Anzanu

Aliyense amafuna kukhala ndi anzake, anthu omwe angathe kumasuka nawo panthawi yosangalala ndiponso kuwadalira panthawi zovuta. Yesu anali ndi anzake amene ankasangalala kuchita nawo zinthu limodzi. (Yohane 15:15) Kenako, pamene anali kufa pa mtengo wozunzirapo, mnzake wa Yesu, Yohane, “wophunzira amene . . . anam’konda” kwambiri, anali naye pafupi. (Yohane 19:25-27; 21:20) Mumafunikira anzanu oterowo, anthu amene amakhala nanu limodzi pamtendere ngakhalenso pamavuto. Mwambi wina wa m’Baibulo umati: “Bwenzi limakonda nthawi zonse; ndipo mbale anabadwira kuti akuthandize pooneka tsoka.”—Miyambo 17:17.

Mwina mukuona kuti mwapeza munthu woteroyo ku sukulu, mmodzi mwa anthu a m’kalasi mwanu amene mumamvana naye zochita. Mumagwirizana pa zinthu zina ndiponso mumasangalala mukamacheza naye. N’zoonadi, munthuyo sangakhale wachikhulupiriro chofanana ndi chanu; komabe, inuyo mumaona kuti sangakhale m’gulu la anthu omwe ndi “mayanjano oipa.” (1 Akorinto 15:33) Kunena zoona, ena mwa achinyamata amene mumasiyana nawo zikhulupiriro za m’Baibulo, amakhala ndi makhalidwe abwino. (Aroma 2:14, 15) Koma kodi zimenezi zimatanthauza kuti iwo akhale anzanu apamtima?

Akristu Sadzipatula

Mwachionekere Akristu oona samazemba kucheza ndi anthu amene si Akristu ayi. Kuti akwanitse ntchito yomwe apatsidwa ‘yophunzitsa anthu a mitundu yonse,’ Akristu amalankhula ndi amuna ndi akazi a mafuko, zipembedzo, ndi zikhalidwe zonse. (Mateyu 28:19) Iwo sakhala onyada kwa anthu oyandikana nawo nyumba, anthu ogwira nawo ntchito, kapena anthu amene amaphunzira nawo limodzi ku sukulu, komanso sikuti amadzipatula ayi. M’malo mwake, Akristu amasonyeza chidwi chachikulu pa anthu ena.

Mtumwi Paulo anapereka chitsanzo chabwino kwambiri pankhaniyi. Iye ankadziwa mmene angalankhulire ndi “anthu onse,” ngakhale kuti anthuwo analibe chikhulupiriro chofanana ndi chake. Inde, cholinga cha Paulo sichinali chofuna kuchitira nawo zinthu limodzi. M’malo mwake iye anati: “Ndichita zonse chifukwa cha Uthenga Wabwino, kuti ndikakhale woyanjana nawo.”—1 Akorinto 9:22, 23.

Mungathe kutsatira chitsanzo cha Paulochi. Khalani waubwenzi ndi anzanu. Phunzirani kulankhula nawo bwino. Anzanu ena a ku sukulu angakhale akufunafuna chiyembekezo cha m’Baibulo chomwe inu muli nacho. Taonani za mtsikana wina wachikristu yemwe dzina lake ndi Janet. Iye ndi anzake a m’kalasi mwake anauzidwa kuti afotokoze mwachidule za wophunzira mnzawo aliyense, ndipo kenako, aliyense wa ophunzirawo anawerenga zimene zafotokozedwa ponena za iye. Mwa timapepala timene Janet analandira, panali kena kakuti: “Umaoneka wosangalala nthawi zonse. Chonde, tiuze chimene chimakuchititsa!”

Monga mmene chitsanzo cha Janet chikusonyezera, ena mwa anzanu a m’kalasi angafune kuphunzira zimene inu mumakhulupirira. Ndithudi, kukhala munthu waubwenzi ndi anthu oterowo n’kopindulitsa. N’zosakayikitsa kuti zimenezi zingakupatseni mwayi wofotokoza za chikhulupiriro chanu. Aloleni nawonso anzanu a m’kalasi mwanuwo kufotokoza maganizo awo, ndipo mvetserani moona mtima pamene akutero. Zimene mumaphunzira polankhula ndi anzanu zingadzakuthandizeni kwambiri mukadzayamba ntchito tsiku lina ndi kukumana ndi zochitika zofananazo. Kusukulu ndiponso kuntchito, khalidwe laubwenzi lingakuthandizeni ‘kukometsera chiphunzitso cha Mpulumutsi wathu Mulungu m’zinthu zonse.’—Tito 2:10.

‘Kumangidwa M’goli’ ndi Anzanu Olakwika

N’zoona kuti pali kusiyana pakati pa kukhala wansangala ndi mnzako wa m’kalasi ndi kukhala mnzake wapamtima. Paulo analemba kuti: “Musakhale omangidwa m’goli ndi osakhulupira osiyana.” (2 Akorinto 6:14) Kuti mukhale mnzake wapamtima wa munthu winawake, muyenera kukhala ndi makhalidwe ndiponso zolinga zofanana ndi zake. Zimenezo sizingatheke ndi munthu amene sakhulupirira ndiponso satsatira malamulo a m’Malemba mofanana ndi inuyo. Kumangidwa m’goli ndi anzanu a m’kalasi omwe ndi osakhulupirira, mwachionekere kungakukopeni kuchita nawo makhalidwe olakwika kapena kuwononga makhalidwe anu abwino.

Maria anaphunzira kuti zimenezi ndi zoona, pambuyo pokumana ndi mavuto. Chibadwa chake chochezeka chinam’pangitsa kukopa anzake mosavuta koma zinali zovuta kwa iye kudziwa mmene angachezere nawo mosapyola malire. “Ndinkasangalala kukondedwa, ndi atsikana ndiponso anyamata,” iye anatero. “Zotsatira zake zinali zakuti, ndinapezeka kuti ndili m’mavuto aakulu a m’dzikoli ovuta kuchokamo.”

Mofanana ndi Maria, kungakhale kovuta kudziwa pamene ubwenzi wanu ndi munthu amene ali ndi chikhulupiriro chosiyana ndi chanu wapyola malire. Komabe, mungathe kudziteteza kuti musalowe m’mavuto poika malire ooneka bwino pankhani ya amene mungalole kukhala anthu ongodziwana nawo ndi anthu amene mungasankhe kukhala anzanu apamtima. Kodi mungachite bwanji zimenezo?

Mmene Mungasankhire Anzanu Abwino

Monga tanena kale, Yesu anali ndi anzake apamtima pamene anali padziko lapansi. Yesu anachita zimenezo pokhala woona mtima ndiponso polankhula zinthu zauzimu. Anthu akamatsatira zimene iye anali kuphunzitsa ndiponso mmene anali kukhalira, iye ankagwirizana nawo. (Yohane 15:14) Mwachitsanzo, atamva zimene Yesu analankhula, amuna anayi anakopeka mpaka “anasiya zonse, nam’tsata Iye.” Amuna amenewa—Petro, Andreya, Yakobo, ndi Yohane—anakhala anzake apamtima a Yesu.—Luka 5:1-11; Mateyu 4:18-22.

Zimene Yesu ankalankhula ndiponso zochita zake zinkasonyeza bwino lomwe kuti ankatanthauzadi zimene anali kukhulupirira ndipo sakanasintha ngakhale pang’ono. Anthu amene sanafune kutsatira zophunzitsa zake anamusiya, ndipo Yesu anawalola kupita.—Yohane 6:60-66.

Mwachitsanzo, kuona mtima kwa mwamuna wina kunamukhudza mtima kwambiri Yesu. Baibulo limati: “Yesu anam’yang’ana, nam’konda.” Koma mwamunayo atadziwa zimene anzake a Yesu ankafunikira kuchita, “anachoka.” Mwamunayo ankaoneka ngati munthu wabwino kwambiri. Indedi, Yesu ‘anam’konda.’ Komabe, panali zinanso zimene Yesu ankafuna kwa anzake. (Marko 10:17-22; Mateyu 19:16-22) Nanga bwanji inuyo?

Mungagwirizane ndi mnzanu wina wa ku sukulu. Koma muyenera kudzifunsa kuti: ‘Kodi munthu ameneyu akufuna kuchita zimene Yesu anatilamula? Kodi akufuna kuphunzira za Yehova, amene Yesu anatiuza kuti tizimulambira?’ (Mateyu 4:10) Mukamalankhula ndi anthu a m’kalasi mwanu ndiponso mukamatsatira miyezo ya m’Baibulo, mayankho a mafunso amenewa adzakhala oonekeratu.

N’koyenera kukhala munthu wochezeka kwa anzanu a m’kalasi, monga mmene Yesu anakhalira waubwenzi ndi anthu onse. Koma Yesu anaonetsetsa kuti anthu amene iye anasankha kukhala anzake apamtima ankakonda Atate wake wakumwamba, Yehova. Inunso mukhoza kuchita chimodzimodzi. ‘Mayendedwe anu akhale okoma’ kusukulu, ndipo mwanzeru lankhulani ndi ena za chikhulupiriro chanu. Koposa zonse, onetsetsani kuti mwasankha anzanu abwino kwambiri.—1 Petro 2:12.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 3 Maina ena tawasintha.

ZOTI MUGANIZIRE

▪ Kodi mungakumane ndi mavuto otani ngati mukhala limodzi ndi anzanu a m’kalasi amene ali osakhulupirira panthawi yanu yopuma mutaweruka ku sukulu? Kodi ndi nzeru kuchita zimenezi?

▪ Pambuyo powerenga nkhaniyi, kodi mukuona kuti ubwenzi ndi mnzanu wa m’kalasi wapyola malire? Ngati ndi choncho kodi mungachite chiyani?

[Bokosi/Zithunzi patsamba 18]

Kodi Ndingapeze Bwanji Anzanga Enieni?

Vidiyo iyi, yokonzedwa ndi Mboni za Yehova, ili ndi mfundo zosapita m’mbali zimene achinyamata a ku United States, Italy, France, ndi Spain anakamba. Ikupezeka mu zinenero zokwana 36.

[Chithunzi patsamba 18]

Ena mwa anthu a m’kalasi mwanu angasangalatsidwe ndi zimene inu mumakhulupirira