Maliko 9:1-50

9  Ndiye anawauzanso kuti: “Ndithu ndikukuuzani, Pali ena mwa amene aimirira pano amene sadzalawa imfa m’pang’ono pomwe, kufikira choyamba ataona ufumu wa Mulungu utabwera ndi mphamvu zake.”+  Malinga ndi zimenezo, patapita masiku 6, Yesu anatenga Petulo, Yakobo ndi Yohane, n’kukwera nawo m’phiri lalitali, kwaokhaokha. Kumeneko iye anasandulika pamaso pawo,+  mwakuti malaya ake akunja ananyezimira, n’kuyera kwambiri kuposa mmene wochapa zovala aliyense padziko lapansi angayeretsere zovala.+  Komanso, Eliya ndi Mose anaonekera kwa iwo, ndipo anali kukambirana ndi Yesu.+  Petulo ataona zimenezi anauza Yesu kuti: “Rabi, ndi bwino ife tizikhala pano, choncho timange mahema atatu pano, limodzi lanu, limodzi la Mose, ndi lina la Eliya.”+  Petulo sanadziwe choti anene, chifukwa ophunzirawo anachita mantha kwambiri.  Pamenepo kunachita mtambo ndipo unawaphimba. Kenako mumtambomo munatuluka mawu+ akuti: “Uyu ndiye Mwana wanga+ wokondedwa, muzimumvera.”+  Pamenepo iwo anayang’ana uku ndi uku, ndipo anangoona kuti palibe wina aliyense, koma Yesu yekha basi.+  Pamene anali kutsika m’phirimo, Yesu anawalangiza mwamphamvu kuti asauze+ aliyense zimene anaonazo, kufikira Mwana wa munthu atauka kwa akufa.+ 10  Iwo anasungadi zimenezo mumtima, koma anayamba kukambirana tanthauzo la kuuka kwa akufa kumeneku. 11  Tsopano anayamba kumufunsa kuti: “N’chifukwa chiyani alembi amanena kuti Eliya+ ayenera kubwera choyamba?”+ 12  Iye anawayankha kuti: “Eliya adzabweradi choyamba ndi kubwezeretsa zinthu zonse.+ Koma n’chifukwa chiyani malemba amanena za Mwana wa munthu, kuti ayenera kukumana ndi mavuto ambiri,+ ndi kumuchita zinthu ngati munthu wopanda pake?+ 13  Kunena za kubwera kwa Eliya,+ ine ndikukuuzani kuti iye anabwera kale, ndipo anam’chitira zilizonse zimene anafuna, mmenedi Malemba amanenera za iye.”+ 14  Tsopano atayandikira kumene kunali ophunzira ena aja, iwo anaona khamu lalikulu la anthu litawazungulira, ndipo alembi anali kukangana nawo.+ 15  Koma khamu lonselo litamuona linadabwa, ndipo linam’thamangira ndi kuyamba kum’patsa moni. 16  Ndiyeno iye anawafunsa kuti: “Mukukangana nawo chiyani?” 17  Wina m’khamulo anamuyankha kuti: “Mphunzitsi, ine ndabweretsa mwana wanga wamwamuna kwa inu chifukwa ali ndi mzimu womulepheretsa kulankhula.+ 18  Mzimuwo umati ukamugwira, umamugwetsera pansi. Akatero amachita thovu ndi kukukuta mano, ndipo amatha mphamvu. Chotero, ndinauza ophunzira anu kuti autulutse, koma alephera.”+ 19  Poyankha iye anawauza kuti: “Inu a m’badwo wopanda chikhulupiriro,+ kodi ndikhala nanube mpaka liti? Ndipitirize kukupirirani mpaka liti? Bwera nayeni kuno.”+ 20  Pamenepo iwo anapita naye kwa Yesu. Koma mzimuwo utamuona, nthawi yomweyo unatsalimitsa mwanayo. Atagwa pansi anagubudukagubuduka ndi kuchita thovu.+ 21  Ndiyeno anafunsa bambo ake kuti: “Izi zakhala zikumuchitikira kwa nthawi yaitali bwanji?” Bamboyo anati: “Kuyambira ali mwana, 22  mwakuti nthawi zambiri wakhala ukum’gwetsera pamoto ndi m’madzi kuti umuwononge.+ Koma ngati mungathe kuchitapo kanthu, tichitireni chifundo ndi kutithandiza.” 23  Yesu anafunsa bamboyo kuti: “Mukuti, ‘Ngati mungathe’? Chilichonsetu n’chotheka kwa aliyense ngati iyeyo ali ndi chikhulupiriro.”+ 24  Nthawi yomweyo bambo wa mwanayo anafuula ndi kunena kuti: “Chikhulupiriro ndili nacho! Limbitsani chikhulupiriro changa!”+ 25  Tsopano Yesu ataona kuti gulu la anthu likukhamukira kwa iwo, anakalipira+ mzimu wonyansawo kuti: “Mzimu wosalankhulitsa ndi wogonthetsa iwe, ndikukulamula, tuluka ndipo usadzalowenso mwa iye.” 26  Choncho mwanayo atafuula ndi kutsalima kwambiri, mzimuwo unatuluka.+ Iye anangokhala ngati wafa, mwakuti anthu ambiri anali kunena kuti: “Wamwalira!” 27  Koma Yesu anamugwira dzanja ndi kumudzutsa, ndipo anaimirira.+ 28  Tsopano atalowa m’nyumba, ophunzira ake anayamba kumufunsa paokha kuti: “N’chifukwa chiyani ife tinalephera kuutulutsa?”+ 29  Iye anawayankha kuti: “Mzimu wa mtundu umenewu sungathe kutuluka ndi chilichonse, koma pemphero basi.”+ 30  Atachoka kumeneko anapitiriza ulendo wawo kudutsa mu Galileya, koma iye sanafune kuti aliyense adziwe zoti ali kumeneko. 31  Pakuti anali kuphunzitsa ophunzira ake ndi kuwauza kuti: “Mwana wa munthu adzaperekedwa m’manja mwa anthu, ndipo adzamupha,+ koma ngakhale adzamuphe, adzauka patapita masiku atatu.”+ 32  Ophunzirawo sanali kumvetsa mawuwa, ndipo anali kuopa kumufunsa.+ 33  Kenako anafika ku Kaperenao. Ndiyeno pamene anali m’nyumba anawafunsa kuti: “Munali kukangana chiyani m’njira?”+ 34  Iwo anangokhala chete, pakuti m’njira anali kukangana za amene ali wamkulu pakati pawo.+ 35  Choncho anakhala pansi ndi kuitana ophunzira 12 aja ndi kuwauza kuti: “Ngati aliyense akufuna kukhala woyamba, ayenera kukhala wotsiriza pa onse, ndiponso mtumiki wa onse.”+ 36  Tsopano anatenga mwana wamng’ono n’kumuimika pakati pawo, ndi kumukumbatira, ndipo anawauza kuti:+ 37  “Aliyense wolandira mmodzi wa ana aang’ono oterewa m’dzina langa, walandiranso ine. Ndipo aliyense wolandira ine, salandira ine ndekha, koma amalandiranso iye amene anandituma.”+ 38  Kenako Yohane anauza Yesu kuti: “Mphunzitsi, ife taona munthu wina akutulutsa ziwanda m’dzina lanu, choncho tinamuletsa,+ chifukwa sanali kuyenda ndi ife.”+ 39  Koma Yesu anati: “Musamuletse, chifukwa palibe amene adzachita ntchito zamphamvu m’dzina langa, ndi kundinenera zachipongwe mwamsanga.+ 40  Pakuti amene sakutsutsana ndi ife ali kumbali yathu.+ 41  Chifukwa aliyense wokupatsani kapu+ ya madzi akumwa chifukwa chakuti ndinu ake a Khristu,+ ndithu ndikukuuzani, ameneyo mphoto yake sidzatayika ayi. 42  Koma aliyense wokhumudwitsa mmodzi wa tiana tokhulupirirati, zingakhale bwino kwambiri kuti amumangirire chimwala champhero m’khosi mwake, ngati chimene bulu amayendetsa, ndi kumuponya m’nyanja.+ 43  “Ndipo ngati dzanja lako limakuphunthwitsa, ulidule. Ndi bwino kuti ukapeze moyo ulibe chiwalo chimodzi, kusiyana n’kupita ku Gehena,* kumoto umene sungazimitsidwe, uli ndi manja onse awiri.+ 44 * —— 45  Ndipo ngati phazi lako limakupunthwitsa, ulidule. Ndi bwino kuti ukapeze moyo uli wolumala,+ kusiyana n’kuponyedwa m’Gehena uli ndi mapazi onse awiri.+ 46 * —— 47  Ngati diso lako limakuchimwitsa, ulitaye.+ Ndi bwino kuti ulowe mu ufumu wa Mulungu ndi diso limodzi, kusiyana n’kuponyedwa mu Gehena uli ndi maso onse awiri,+ 48  kumene mphutsi za mitembo sizifa ndipo moto wake suzima.+ 49  “Pakuti aliyense ayenera kuwazidwa mchere+ umene ukuimira moto. 50  Mchere ndi wabwino, koma mcherewo ukatha mphamvu, kodi mungaibwezeretse bwanji?+ Khalani ndi mchere+ mwa inu nokha, ndipo sungani mtendere+ pakati panu.”

Mawu a M'munsi

Onani Zakumapeto 9.
Za mawu amene palibe, onani mawu a m’munsi pa Mt 17:21.
Za mawu amene palibe, onani mawu a m’munsi pa Mt 17:21.