Maliko 12:1-44

12  Kenako, anayamba kulankhula nawo m’mafanizo kuti: “Munthu wina analima munda wa mpesa+ ndi kumanga mpanda kuzungulira mundawo. Komanso anakumba dzenje loponderamo mphesa, ndi kumanga nsanja.+ Atatero anausiya m’manja mwa alimi+ n’kupita kudziko lina.+  Tsopano nyengo ya zipatso itakwana, iye anatumiza kapolo wake kwa alimiwo kuti akam’patseko zina mwa zipatso za m’munda wa mpesawo.+  Koma iwo anam’gwira, n’kumumenya ndi kum’bweza chimanjamanja.+  Iye anatumizanso kapolo wina kwa iwo koma ameneyu anamutema m’mutu ndi kumuchitira zachipongwe.+  Anatumizanso wina, koma ameneyo anamupha. Ndiyeno anatumizanso akapolo ena ambiri. Ena mwa iwo anawamenya ndipo ena anawapha.  Tsopano anatsala ndi mmodzi yekha, mwana wake wokondedwa.+ Anatumizanso mwanayo kwa iwo ngati wotsirizira, n’kunena kuti, ‘Mwana wanga yekhayu akamulemekeza.’+  Koma alimiwo anayamba kukambirana kuti, ‘Eya, uyu ndiye wolandira cholowa.+ Bwerani, tiyeni timuphe, ndipo cholowacho chidzakhala chathu.’+  Choncho anamugwira n’kumupha,+ ndipo anamuponya kunja kwa munda wa mpesawo.+  Kodi mwinimunda wa mpesawo adzachita chiyani? Adzabwera ndi kupha alimiwo, ndipo munda wa mpesawo+ adzaupereka kwa ena.+ 10  Kodi simunawerengepo lemba limene limati, ‘Mwala+ umene omanga nyumba anaukana, umenewu wakhala mwala wapakona wofunika kwambiri’?+ 11  Kodi simunawerenge kuti ‘Umenewu wachokera kwa Yehova, ndipo ndi wodabwitsa m’maso mwathu’?”+ 12  Atamva zimenezo anayamba kufunafuna njira yomugwirira, koma anaopa khamu la anthu, pakuti iwo anazindikira kuti iye ananena fanizolo akuganiza za iwowo. Choncho anangomusiya n’kuchokapo.+ 13  Pambuyo pake anam’tumizira ena mwa Afarisi ndi a chipani cha Herode,+ kuti akam’kole m’mawu ake.+ 14  Atafika, iwo anamuuza kuti: “Mphunzitsi, tikudziwa kuti inu mumanena zoona ndipo simusamala kuti uyu ndani, chifukwa simuyang’ana maonekedwe a munthu, koma mumaphunzitsa njira ya Mulungu mogwirizana ndi choonadi:+ Kodi n’kololeka kupereka msonkho kwa Kaisara kapena ayi? 15  Kodi tizipereka kapena tisamapereke?”+ Pozindikira chinyengo chawo, Yesu anawafunsa kuti: “Bwanji mukundiyesa? Bweretsani khobidi la dinari kuno ndilione.”+ 16  Iwo anam’patsadi. Ndipo iye anawafunsa kuti: “Kodi chifaniziro ichi ndi mawu akewa n’zandani?” Iwo anayankha kuti: “Ndi za Kaisara.”+ 17  Pamenepo Yesu anati: “Perekani zinthu za Kaisara kwa Kaisara,+ koma zinthu za Mulungu muzizipereka kwa Mulungu.”+ Ndipo iwo anadabwa naye kwambiri.+ 18  Kenako Asaduki amene amanena kuti kulibe kuuka kwa akufa, anabwera kwa iye ndipo anam’funsa kuti:+ 19  “Mphunzitsi, Mose anatilembera kuti ngati munthu wamwalira ndi kusiya mkazi koma osasiya mwana, m’bale wake+ atenge mkazi wamasiyeyo ndi kuberekera m’bale wake uja ana mwa mkaziyo.+ 20  Tsopano panali amuna 7 apachibale. Woyamba anakwatira mkazi, koma pomwalira, sanasiye mwana aliyense.+ 21  Wachiwiri anatenga mkaziyo, koma nayenso anamwalira osasiya mwana. Zimenezi zinachitikanso chimodzimodzi kwa wachitatu. 22  Ndipo onse 7 aja sanasiye mwana. Pamapeto pake mkazi nayenso anamwalira.+ 23  Kodi pouka kwa akufa mkazi ameneyu adzakhala wa ndani? Popeza onse 7 anam’kwatira.”+ 24  Yesu anawayankha kuti: “Mukulakwitsa. Kodi kulakwitsa kumeneku si chifukwa chakuti simudziwa Malemba kapena mphamvu ya Mulungu?+ 25  Akadzauka kwa akufa, amuna sadzakwatira ndipo akazi sadzakwatiwa, koma adzakhala ngati angelo akumwamba.+ 26  Koma zakuti akufa amaukitsidwa, kodi inu simunawerenge m’buku la Mose, m’nkhani ya chitsamba chaminga, mmene Mulungu anamuuzira kuti, ‘Ine ndine Mulungu wa Abulahamu, Mulungu wa Isaki ndi Mulungu wa Yakobo’?+ 27  Iye ndi Mulungu wa anthu amoyo, osati akufa. Mukulakwitsa kwambiri anthu inu.”+ 28  Tsopano mmodzi wa alembi amene anafika ndi kuwamva akutsutsana, anadziwa kuti anawayankha bwino, ndipo anafunsa Yesu kuti: “Kodi lamulo loyamba ndi liti pa malamulo onse?”+ 29  Yesu anayankha kuti: “Loyamba n’lakuti, ‘Tamverani Aisiraeli inu, Yehova* Mulungu wathu ndi Yehova mmodzi.+ 30  Uzikonda Yehova Mulungu wako ndi mtima wako wonse, moyo wako wonse, maganizo ako onse ndi mphamvu zako zonse.’+ 31  Lachiwiri ndi ili, ‘Uzikonda mnzako mmene umadzikondera wekha.’+ Kulibe lamulo lina lalikulu kuposa amenewa.” 32  Mlembiyo ananena kuti: “Mphunzitsi, mwanena bwino mogwirizana ndi choonadi, ‘Iye ndi Mmodzi, ndipo palibenso wina, koma Iye yekha.’+ 33  Kunena za kukonda Mulungu ndi mtima wonse, maganizo onse, mphamvu zonse, komanso kukonda mnzako mmene umadzikondera wekha, n’zofunika kwambiri kuposa nsembe zonse zopsereza zathunthu ndi nsembe zina.”+ 34  Pamenepo Yesu, pozindikira kuti wayankha mwanzeru, anauza mlembiyo kuti: “Iwe suli kutali ndi ufumu wa Mulungu.” Ndipo panalibe amene analimba mtima kumufunsanso.+ 35  Koma pamene Yesu anali kuphunzitsa m’kachisi, anayankha zonse mwa kufunsa kuti: “N’chifukwa chiyani alembi amanena kuti Khristu ndi mwana wa Davide?+ 36  Mwa mzimu woyera,+ Davideyo ananena kuti, ‘Yehova anauza Ambuye wanga kuti: “Khala kudzanja langa lamanja kufikira nditaika adani ako kunsi kwa mapazi ako.”’+ 37  Davideyo anamutcha kuti ‘Ambuye,’ nanga zikutheka bwanji kuti alinso mwana wake?”+ Ndipo khamu lalikulu linali kumumvetsera mosangalala.+  38  Pophunzitsapo Yesu ananenanso kuti: “Chenjerani ndi alembi+ amene amakonda kuyendayenda atavala mikanjo ndi kupatsidwa moni m’misika. 39  Komanso amakonda kukhala m’mipando yakutsogolo m’masunagoge. Amakondanso malo olemekezeka kwambiri pa chakudya chamadzulo.+ 40  Iwo ndi amene amadyerera nyumba+ za akazi amasiye, ndipo mwachiphamaso amapereka mapemphero ataliatali. Anthu amenewa adzalandira chiweruzo champhamvu.”+ 41  Ndiyeno anakhala pansi moyang’anana ndi moponyamo zopereka+ ndipo anali kuona mmene khamu la anthu linali kuponyera ndalama moponya zoperekamo. Anthu ambiri olemera anali kuponyamo makobidi ambiri.+ 42  Kenako panafika mkazi wamasiye wosauka ndipo anaponyamo timakobidi tiwiri tating’ono.+ 43  Choncho Yesu anaitana ophunzira ake ndi kuwauza kuti: “Ndithu ndikukuuzani, mkazi wamasiye wosaukayu waponya zochuluka kuposa onse amene aponya ndalama moponya zoperekamo.+ 44  Zili choncho chifukwa onsewo aponya zimene atapa pa zochuluka zimene ali nazo, koma mayiyu, mu umphawi wake, waponya zonse zimene anali nazo, inde zonse zochirikizira moyo wake.”+

Mawu a M'munsi

Onani Zakumapeto 2.