Maliko 11:1-33

11  Tsopano pamene anali kuyandikira Yerusalemu, Betefage ndi Betaniya,+ ali paphiri la Maolivi, anatumiza ophunzira ake awiri+  ndi kuwauza kuti: “Pitani m’mudzi umene mukuuonawo. Mukakalowa mmenemo, mukapeza bulu wamng’ono wamphongo atam’mangirira, amene munthu sanakwerepo chiyambire. Mukam’masule ndi kubwera naye kuno.+  Wina akakakufunsani kuti, ‘N’chifukwa chiyani mukumumasula?’ Mukanene kuti, ‘Ambuye akumufuna, ndipo akangotha kum’gwiritsa ntchito am’bweza nthawi yomweyo.’”+  Choncho anapita ndipo anapeza bulu wamphongo atam’mangirira pakhomo, m’mphepete mwa msewu waung’ono. Chotero iwo anamasula buluyo.+  Koma ena mwa anthu amene anali ataimirira chapomwepo anayamba kuwafunsa kuti: “Cholinga chanu n’chiyani pomasula buluyu?”+  Iwo anawauza monga mmene Yesu ananenera ndipo anawalola kuti apite.+  Choncho anabweretsa bulu+ uja kwa Yesu. Kenako anayala malaya awo akunja pabuluyo, ndipo iye anakwerapo.+  Komanso, anthu ambiri anayala malaya awo akunja+ mumsewu, koma ena anadula zitsamba+ m’minda.+  Ndiyeno amene anali patsogolo ndi amene anali kubwera m’mbuyo anali kufuula kuti: “M’pulumutseni!+ Wodalitsidwa iye wobwera m’dzina la Yehova!+ 10  Wodalitsidwa ufumu ukubwerawo wa atate wathu Davide!+ M’pulumutseni kumwambamwambako!” 11  Pamenepo analowa mu Yerusalemu, ndi kufika m’kachisi. Ndiyeno anayang’anayang’ana zinthu zonse, koma popeza nthawi inali itatha kale, anapita ku Betaniya limodzi ndi ophunzira ake 12 aja.+ 12  Tsiku lotsatira, atatuluka mu Betaniya, anamva njala.+ 13  Ndipo ali chapatali ndithu, anaona mkuyu umene unali ndi masamba. Iye anapita pomwepo kuti akaone ngati angapezemo kanthu. Koma atafika pamtengowo, sanapezemo chilichonse koma masamba okha basi, pakuti sinali nyengo ya nkhuyu.+ 14  Choncho iye anauza mtengowo kuti: “Munthu sadzadyanso zipatso zako kwamuyaya.”+ Ndipo ophunzira ake anali kumvetsera. 15  Tsopano anafika ku Yerusalemu. Kumeneko analowa m’kachisi n’kuyamba kuthamangitsa ogula ndi ogulitsa m’kachisimo. Anagubuduza matebulo a osintha ndalama ndiponso mabenchi a ogulitsa nkhunda.+ 16  Iye sanalole aliyense kudutsa m’kachisimo atanyamula katundu. 17  Ndiyeno anayamba kuphunzitsa ndi kunena kuti: “Kodi Malemba sanena kuti, ‘Nyumba yanga idzatchedwa nyumba yopemphereramo+ mitundu yonse’?+ Koma inu mwaisandutsa phanga la achifwamba.”+ 18  Ansembe aakulu ndi alembi anamva zimenezo, ndipo anayamba kufunafuna njira yomuphera,+ chifukwa anali kumuopa, pakuti khamu lonse la anthu nthawi zonse linali kudabwa ndi zimene anali kuphunzitsa.+ 19  Tsopano chakumadzulo pa tsikulo, iwo anatuluka mumzindawo. 20  Koma pamene anali kudutsa m’mamawa, anaona mkuyu uja utafota kale ndi mizu yomwe.+ 21  Choncho Petulo, pokumbukira ananena kuti: “Rabi, onani! mkuyu umene munautemberera uja wafota.”+ 22  Poyankha Yesu anawauza kuti: “Khalani ndi chikhulupiriro mwa Mulungu. 23  Ndithu ndikukuuzani kuti aliyense wouza phiri ili kuti, ‘Nyamuka pano udziponye m’nyanja,’ ndipo sakukayika mumtima mwake, koma ali ndi chikhulupiriro kuti zimene wanena zichitikadi, zidzaterodi.+ 24  N’chifukwa chake ndikukuuzani kuti, Pa zinthu zonse zimene mukupempherera ndi kupempha, khalani ndi chikhulupiriro ngati kuti mwazilandira kale, ndipo mudzazilandiradi.+ 25  Ndipo mukaimirira n’kumapemphera,+ khululukani chilichonse chimene wina anakulakwirani kuti Atate wanu wakumwamba akukhululukireni machimo anunso.”+ 26 * —— 27  Kenako anafikanso ku Yerusalemu. Koma pamene anali kuyenda m’kachisi, ansembe aakulu, alembi ndi akulu anabwera kwa iye.+ 28  Iwo anayamba kum’funsa kuti: “Kodi muli ndi ulamuliro wochitira zinthu zimenezi? Kapena ndani anakupatsani ulamuliro umenewu?”+ 29  Yesu anawauza kuti: “Ndikufunsani funso limodzi. Mundiyankhe, ndipo inenso ndikuuzani ulamuliro umene ndimachitira zinthu zimenezi.+ 30  Kodi ubatizo+ wa Yohane unali wochokera kumwamba kapena kwa anthu? Ndiyankheni.”+ 31  Pamenepo iwo anayamba kukambirana kuti: “Tikanena kuti, ‘Unachokera kumwamba,’ iye anena kuti, ‘Nanga n’chifukwa chiyani simunamukhulupirire?’+ 32  Koma nanga tinganene kuti ‘Unachokera kwa anthu’ ngati?” . . . Anali kuopa khamu la anthu, chifukwa anthu onsewo anali kukhulupirira kuti Yohane analidi mneneri.+ 33  Ndiyeno poyankha kwa Yesu anangoti: “Sitikudziwa.” Nayenso Yesu anawauza kuti: “Inenso sindikuuzani ulamuliro umene ndimachitira zimenezi.”+

Mawu a M'munsi

Za mawu amene palibe, onani mawu a m’munsi pa Mt 17:21.