Maliko 5:1-43

5  Kenako anafika kutsidya lina la nyanja, m’dera la Agerasa.+  Tsopano atangotsika m’ngalawa, anakumana ndi munthu wogwidwa ndi mzimu wonyansa akuchokera m’manda achikumbutso.+  Iye anali kukonda kukhala m’mandamo, ndipo n’kale lonse, kunalibe munthu ndi mmodzi yemwe, amene anatha kum’manga ngakhale ndi unyolo.  Izi zinali choncho chifukwa anamangidwapo mobwerezabwereza ndi matangadza ndiponso maunyolo, koma iye anali kudula maunyolowo ndi kuthyola matangadzawo. Chotero panalibe amene anatha kumugonjetsa.  Ndipo nthawi zonse, usiku ndi usana, anali kufuula m’manda ndi m’mapiri ndi kudzitematema ndi miyala.  Koma ataona Yesu chapatali ndithu, anam’thamangira ndi kum’chitira ulemu,  ndipo atafuula ndi mawu amphamvu,+ anati: “Kodi ndili nanu chiyani, Yesu, Mwana wa Mulungu Wam’mwambamwamba?+ Ndikukulumbiritsani+ pali Mulungu kuti musandizunze.”+  Pakuti Yesu anali kuuza mzimuwo kuti: “Tuluka mwa munthuyu, mzimu wonyansa iwe.”+  Ndiyeno anafunsa munthuyo kuti: “Dzina lako ndani?” Iye anayankha kuti: “Dzina langa ndine Khamu,+ chifukwa tilipo ambiri.”+ 10  Ndipo anam’chonderera mobwerezabwereza kuti asatumize mizimuyo kutali ndi deralo.+ 11  Tsopano chigulu cha nkhumba+ chinali kudya paphiri.+ 12  Chotero mizimuyo inam’chonderera kuti: “Titumizeni ku nkhumbazo, kuti tikalowe mwa zimenezo.” 13  Choncho iye anailola. Pamenepo mizimu yonyansayo inatuluka ndi kukalowa m’nkhumbazo, ndipo nkhumba zonsezo zinathamangira kuphedi ndi kulumphira m’nyanja. Nkhumbazo zinalipo pafupifupi 2,000, ndipo zinamira m’nyanjamo imodzi ndi imodzi.+ 14  Koma amene anali kuziyang’anira anathawa ndi kukanena zimenezi mumzinda ndi m’midzi, ndipo anthu anabwera kudzaona zimene zinachitikazo.+ 15  Choncho anafika kwa Yesu, ndipo anaona munthu wogwidwa ndi chiwanda uja ali chikhalire, atavala bwino komanso maganizo ake ali bwinobwino, inde munthu uja amene anali ndi khamu la mizimu yonyansa. Pamenepo iwo anachita mantha. 16  Komanso amene anaona zochitikazo, anawafotokozera mmene zinakhalira kwa munthu wogwidwa ziwanda uja ndiponso zimene zinachitikira nkhumba zija. 17  Chotero anthuwo anayamba kuchonderera Yesu kuti achoke m’madera akwawoko.+ 18  Tsopano pamene anali kukwera ngalawa, munthu amene anali ndi ziwanda uja anayamba kumuchonderera kuti aziyenda naye.+ 19  Komabe iye sanamulole, koma anamuuza kuti: “Pita kunyumba kwa achibale ako,+ ndipo ukawauze zonse zimene Yehova+ wakuchitira ndi chifundo+ chimene wakusonyeza.” 20  Chotero iye anachoka ndipo anayamba kufalitsa mu Dekapole+ zonse zimene Yesu anam’chitira, moti anthu onse anadabwa kwambiri.+ 21  Yesu atawolokanso pangalawa kubwerera kutsidya lina, khamu lalikulu la anthu linasonkhana kwa iye, ndipo iye anali m’mphepete mwa nyanja.+ 22  Pamenepo mmodzi wa atsogoleri a sunagoge, dzina lake Yairo, anafika. Atamuona anagwada pamapazi ake+ 23  ndi kum’chonderera mobwerezabwereza, kuti: “Mwana wanga wamkazi akudwala mwakayakaya. Chonde tiyeni mukamuike manja+ kuti achire ndi kukhala ndi moyo.”+ 24  Pamenepo ananyamuka naye limodzi, ndipo khamu lalikulu la anthu linali kumutsatira ndi kumam’panikiza.+ 25  Tsopano panali mayi wina amene anali ndi nthenda yotaya magazi+ kwa zaka 12,+ 26  ndipo madokotala+ ambiri anam’chititsa kumva zopweteka zambiri. Iye anawononga chuma chake chonse koma osapindula kanthu, m’malomwake matendawo ankangokulirakulira. 27  Atamva zambiri zokhudza Yesu, anakalowa m’khamu la anthulo ndi kumudzera kumbuyo kwake, kenako anagwira+ malaya ake akunja. 28  Anachita zimenezi pakuti mumtima mwake anali kunena kuti: “Ndikangogwira malaya ake akunja okhawo, ndichira ndithu.”+ 29  Nthawi yomweyo kasupe wake wa magazi anauma, ndipo anamva m’thupi mwake kuti wachira nthenda yake yaikuluyo.+ 30  Nthawi yomweyonso, Yesu anamva m’thupi mwake kuti mphamvu+ yatulukamo. Pamenepo anatembenuka m’khamu la anthulo ndi kufunsa kuti: “Ndani wagwira malaya angawa?”+ 31  Koma ophunzira ake anayamba kumuuza kuti: “Inunso mukuona kuti anthu onsewa akukupanikizani,+ ndiye mungafunse bwanji kuti, ‘Ndani wandigwira?’” 32  Komabe iye anali kuyang’anayang’ana kuti aone mayi amene wachita zimenezi. 33  Koma mayiyo, anachita mantha ndi kuyamba kunjenjemera, podziwa zimene zam’chitikira. Ndipo anafika pafupi n’kugwada pamaso pake ndi kumuuza zoona zonse.+ 34  Iye anauza mayiyo kuti: “Mwanawe, chikhulupiriro chako chakuchiritsa. Pita mu mtendere,+ matenda ako aakuluwo atheretu.”+ 35  Ali mkati molankhula, panafika amuna ena ochokera kunyumba kwa mtsogoleri wa sunagoge uja ndipo anamuuza kuti: “Mwana wanu uja wamwalira! Musiyeni mphunzitsiyu musamuvutitse.”+ 36  Koma Yesu atamva zimene anali kunenazo, anauza mtsogoleri wa sunagogeyo kuti: “Usaope, ingokhala ndi chikhulupiriro basi.”+ 37  Pamenepo sanalolenso aliyense kumutsatira kupatulapo Petulo, Yakobo, ndi Yohane, m’bale wake wa Yakobo.+ 38  Choncho anafika kunyumba ya mtsogoleri wa sunagoge, ndipo anamva chiphokoso cha anthu akulira ndi kubuma kwambiri. 39  Atalowa mkati, anafunsa anthuwo kuti: “N’chifukwa chiyani mukubuma ndi kulira motere? Mwana wamng’onoyu sanamwalire ayi, koma akugona.”+ 40  Atanena zimenezi, anthuwo anayamba kum’seka monyodola. Koma atawatulutsa onsewo, anatenga bambo ndi mayi a mwanayo ndi amene anali naye aja, ndipo analowa kumene kunali mwanayo.+ 41  Ndiyeno anagwira dzanja la mwanayo ndi kunena kuti: “Talʹi·tha cuʹmi,” mawu amene powamasulira amatanthauza kuti: “Kamtsikana iwe, ndikunena ndi iwe, Dzuka!”+ 42  Nthawi yomweyo kamtsikanako kanadzuka ndi kuyamba kuyenda. Mwanayo anali ndi zaka 12. Pamenepo anthuwo anasangalala kwambiri.+ 43  Koma iye anawalamula mobwerezabwereza kuti asauze aliyense zimenezi.+ Kenako anawauza kuti apatse mtsikanayo chakudya.

Mawu a M'munsi