Maliko 10:1-52

10  Atachoka kumeneko anakafika kumadera a kumalire kwa Yudeya kutsidya la Yorodano. Kumenekonso khamu la anthu linasonkhananso kwa iye, ndipo mwachizolowezi chake anayamba kuwaphunzitsa.+  Tsopano kunafika Afarisi. Pofuna kumuyesa, anayamba kumufunsa ngati n’kololeka kuti mwamuna asiye mkazi wake.+  Poyankha iye anawafunsa kuti: “Kodi Mose anakulamulani chiyani?”  Iwo anati: “Mose analola kuti munthu akafuna kusiya mkazi wake azilemba kalata yothetsa ukwati ndi kum’siya mkaziyo.”+  Koma Yesu anawauza kuti: “Iye anakulemberani lamulo limeneli chifukwa cha kuuma mtima kwanuku.+  Koma kuyambira pa chiyambi pa chilengedwe, ‘Mulungu anawalenga mwamuna ndi mkazi.+  Pa chifukwa chimenechi, mwamuna adzasiya bambo ake ndi mayi ake,  ndipo awiriwo adzakhala thupi limodzi,’+ moti salinso awiri, koma thupi limodzi.  Choncho chimene Mulungu wachimanga pamodzi, munthu asachilekanitse.”+ 10  Pamenenso anali m’nyumba,+ ophunzira anayamba kumufunsa za nkhani imeneyi. 11  Iye anawauza kuti: “Aliyense wosiya mkazi wake ndi kukwatira wina, wachita chigololo+ molakwira mkaziyo. 12  Ndipo ngati mkazi wasiya mwamuna wake, ndiyeno n’kukwatiwa ndi wina, wachita chigololo.”+ 13  Tsopano anthu anayamba kum’bweretsera ana aang’ono kuti awakhudze ndi manja ake, koma ophunzirawo anawakalipira.+ 14  Ataona zimenezi Yesu anakwiya ndipo anawauza kuti: “Alekeni anawo abwere kwa ine, musawaletse ayi. Pakuti ufumu wa Mulungu ndi wa anthu amene ali ngati ana amenewa.+ 15  Ndithu ndikukuuzani, Aliyense wosalandira ufumu wa Mulungu ngati mwana wamng’ono sadzalowa n’komwe mu ufumuwo.”+ 16  Ndiyeno anatenga anawo m’manja mwake ndi kuyamba kuwadalitsa, mwa kuika manja ake pa iwo.+ 17  Tsopano pamene anali kupita, mwamuna wina anam’thamangira ndi kugwada pamaso pake. Kenako anamufunsa kuti: “Mphunzitsi Wabwino, ndichite chiyani kuti ndikapeze moyo wosatha?”+ 18  Yesu anam’funsa kuti: “N’chifukwa chiyani ukunditchula kuti wabwino?+ Palibe wabwino, koma Mulungu yekha.+ 19  Iwe umadziwa malamulo akuti, ‘Usaphe munthu,*+ Usachite chigololo,+ Usabe,+ Usapereke umboni wonama,+ Usachite chinyengo+ ndiponso lakuti Uzilemekeza bambo ako ndi mayi ako.’”+ 20  Pamenepo munthuyo anayankha kuti: “Mphunzitsi, zonsezi ndakhala ndikuzitsatira kuyambira ndili wamng’ono.” 21  Yesu anamuyang’ana ndipo anam’konda. Kenako anamuuza kuti: “Chinthu chimodzi chikusowekabe mwa iwe: Pita kagulitse zilizonse zimene uli nazo ndipo ndalama zake upatse osauka. Ukatero udzakhala ndi chuma kumwamba, ndiyeno ubwere udzakhale wotsatira wanga.”+ 22  Koma iye anakhumudwa atamva mawuwo, ndipo anachoka ali wachisoni, chifukwa anali ndi katundu wambiri.+ 23  Yesu anayang’ana uku ndi uku, kenako anauza ophunzira akewo kuti: “Zidzakhalatu zovuta kwambiri kuti anthu andalama+ adzalowe mu ufumu wa Mulungu!”+ 24  Koma ophunzirawo anadabwa+ nawo mawu akewa. Poyankha Yesu anabwerezanso kuti: “Ana inu, kulowa mu ufumu wa Mulungu n’kovuta kwambiri! 25  N’chapafupi kuti ngamila ilowe padiso la singano kusiyana n’kuti munthu wolemera alowe mu ufumu wa Mulungu.”+ 26  Pamenepo iwo anadabwa kwambiri ndipo anamufunsa kuti: “Ndiye angapulumuke ndani?”+ 27  Yesu anawayang’ana ndi kuwauza kuti: “Kwa anthu n’zosathekadi, koma sizili choncho kwa Mulungu, pakuti zinthu zonse n’zotheka ndi Mulungu.”+ 28  Petulo anayamba kumuuza kuti: “Onani! Ife tinasiya zinthu zonse ndipo takhala tikukutsatirani.”+ 29  Yesu anati: “Ndithu ndikukuuzani amuna inu, Palibe amene anasiya nyumba, abale, alongo, amayi, abambo, ana kapena minda chifukwa cha ine, ndi chifukwa cha uthenga wabwino,+ 30  amene panopa sadzapeza zochuluka kuwirikiza maulendo 100+ m’nthawi* ino. Iye adzapeza nyumba, abale, alongo, amayi, ana ndi minda, limodzi ndi mazunzo,+ ndipo m’nthawi imene ikubwerayo, adzapeza moyo wosatha. 31  Koma ambiri amene ali oyamba adzakhala omaliza, ndipo omaliza adzakhala oyamba.”+ 32  Tsopano anapitiriza ulendo wawo wopita ku Yerusalemu. Yesu anali patsogolo pawo, ndipo iwo anadabwa kwambiri. Anthu amene anali kum’tsatirawo anayamba kuchita mantha. Pamenepanso anatengera pambali ophunzira 12 aja ndi kuyamba kuwauza zinthu izi zimene zinali pafupi kum’chitikira:+ 33  “Tsopano kumene tikupitaku ndi ku Yerusalemu. Kumeneku Mwana wa munthu akaperekedwa kwa ansembe aakulu ndi alembi, ndipo akamuweruza kuti aphedwe, ndipo akam’pereka kwa anthu amitundu.+ 34  Iwo akam’chitira chipongwe, kum’lavulira, kum’kwapula ndi kumupha, koma patapita masiku atatu, adzauka.”+ 35  Koma Yakobo ndi Yohane, ana aamuna awiri a Zebedayo,+ anapita kwa iye ndi kumuuza kuti: “Mphunzitsi, tikufuna mutichitire chimene tikupempheni.”+ 36  Iye anawafunsa kuti: “Mukufuna ndikuchitireni chiyani?” 37  Iwo anamuyankha kuti: “Mutilole kuti mmodzi wa ife adzakhale kudzanja lanu lamanja, ndipo wina adzakhale kumanzere kwanu mu ulemerero wanu.”+ 38  Koma Yesu anawauza kuti: “Simukudziwa chimene mukupempha. Kodi mungathe kumwa zimene ine ndikumwa, kapena kubatizidwa ubatizo umene ine ndikubatizidwa nawo?”+ 39  Iwo anayankha kuti: “Tingathe.” Pamenepo Yesu anawauza kuti: “Zimene ine ndikumwa mudzamwadi, ndipo mudzabatizidwadi ndi ubatizo umene ine ndikubatizidwa nawo.+ 40  Koma kunena zokhala kudzanja langa lamanja kapena lamanzere, si ine wopereka mwayi umenewo,+ koma Atate wanga adzaupereka kwa anthu amene iwo anawakonzera.” 41  Tsopano ophunzira 10 ena aja atamva zimenezi, anakwiya kwambiri ndi Yakobo ndi Yohane.+ 42  Koma Yesu anawaitana, ndipo atafika kwa iye, anawauza kuti: “Inu mukudziwa kuti amene amaoneka ngati akulamulira anthu a mitundu ina amapondereza anthu awo ndipo akuluakulu awo amasonyeza mphamvu zawo pa iwo.+ 43  Sizili choncho pakati panu. Koma aliyense wofuna kukhala wamkulu pakati panu ayenera kukhala mtumiki wanu.+ 44  Amene akufuna kukhala woyamba pakati panu ayenera kukhala kapolo wa onse.+ 45  Pakuti ngakhale Mwana wa munthu sanabwere kudzatumikiridwa,+ koma kudzatumikira ndi kudzapereka moyo wake dipo+ kuwombola anthu ambiri.”+ 46  Kenako anafika mu Yeriko. Koma pamene iye ndi ophunzira ake ndi gulu lalikulu ndithu anali kutuluka mu Yeriko, Batimeyu, wopemphapempha komanso wakhungu (mwana wa Timeyu), anakhala pansi m’mphepete mwa msewu.+ 47  Pamene anamva kuti ndi Yesu Mnazareti, Batimeyu anayamba kufuula kuti: “Mwana wa Davide,+ Yesu, ndichitireni chifundo!”+ 48  Pamene ambiri anali kumuuza mwamphamvu kuti akhale chete, m’pamenenso iye anafuula kwambiri kuti: “Mwana wa Davide, ndichitireni chifundo!”+ 49  Choncho, Yesu anaima ndi kunena kuti: “Muitaneni.” Iwo anaitana wakhunguyo, ndi kumuuza kuti: “Limba mtima, nyamuka, akukuitana.”+ 50  Pamenepo anaponya uko malaya ake akunja, ndipo ananyamuka mofulumira kupita kwa Yesu. 51  Tsopano poyankha Yesu anamufunsa kuti: “Ukufuna kuti ndikuchitire chiyani?”+ Wakhunguyo anayankha kuti: “Rab·boʹni, ndithandizeni ndiyambe kuona.”+ 52  Yesu anamuuza kuti: “Pita, chikhulupiriro chako chakuchiritsa.”+ Nthawi yomweyo anayamba kuona,+ ndipo anayamba kutsatira Yesu mumsewu.+

Mawu a M'munsi

Kupha uku ndi kupha munthu mwachiwembu osati mwalamulo.
Onani Matanthauzo a Mawu Ena.