Maliko 6:1-56

6  Kenako anachoka kumeneko ndi kufika m’dera lakwawo, ndipo ophunzira ake anam’tsatira.+  Sabata itafika, iye anayamba kuphunzitsa m’sunagoge. Anthu ambiri amene anali kumvetsera, anadabwa ndipo anali kunena kuti: “Kodi munthu ameneyu anazitenga kuti zinthu zimenezi?+ Ndipo n’chifukwa chiyani nzeru zimenezi zinaperekedwa kwa munthu ameneyu, ndi kuti azitha kuchita ntchito zamphamvu zoterezi?  Kodi iyeyu si mmisiri wamatabwa,+ mwana wa Mariya,+ komanso m’bale wake wa Yakobo,+ Yosefe, Yudasi ndi Simoni?+ Ndipo alongo ake si awa omwe tili nawo pompano?” Choncho anayamba kukhumudwa naye.+  Koma Yesu anapitiriza kuwauza kuti: “Mneneri salemekezedwa kwawo,+ ngakhale ndi achibale ake, ngakhale m’nyumba mwake momwe, koma kwina.”+  Chotero sanathe kuchita ntchito zamphamvu zilizonse kumeneko, koma anangoika manja pa odwala owerengeka ndi kuwachiritsa.  Ndithudi, iye anadabwa kuona kuti anthuwo analibe chikhulupiriro. Ndipo anazungulira m’midzi yapafupi akuphunzitsa.+  Kenako anaitana ophunzira 12 aja, ndipo anayamba kuwatumiza awiriawiri,+ ndi kuwapatsa mphamvu pa mizimu yonyansa.+  Komanso, anawalangiza kuti asanyamule kanthu pa ulendowo kupatulapo ndodo yokha basi. Anawalangiza kuti asatenge mkate, thumba la chakudya,+ kapena ndalama m’zikwama zawo,+  koma kuti avale nsapato, ndi kuti asavale malaya awiri amkati.+ 10  Komanso anawauza kuti: “Mukafika pakhomo lililonse,+ khalani pamenepo mpaka nthawi yochoka kumeneko itakwana.+ 11  Kulikonse kumene sakakulandirani kapena kukumvetserani, pochoka kumeneko sansani fumbi kumapazi anu kuti ukhale umboni kwa iwo.”+ 12  Choncho anapita ndi kukalalikira kuti anthu alape.+ 13  Kumeneko anatulutsa ziwanda zambiri,+ ndi kudzoza mafuta anthu ambiri odwala+ ndi kuwachiritsa.+ 14  Tsopano izi zinamveka kwa Mfumu Herode,* chifukwa dzina la Yesu linamveka paliponse. Anthu anali kunena kuti: “Yohane m’batizi wauka kwa akufa, ndipo pa chifukwa chimenechi akuchita ntchito zamphamvu.”+ 15  Koma ena anali kunena kuti: “Ndi Eliya.”+ Ndipo ena anali kunena kuti: “Ndi mneneri monga analili aneneri ena.”+ 16  Koma Herode atamva zimenezo anayamba kunena kuti: “Ndithu Yohane amene ndinam’dula mutu uja waukitsidwadi.”+ 17  Pakuti Herodeyo anatumiza anthu kukagwira Yohane, kum’manga ndi kum’tsekera m’ndende, chifukwa Herode anakwatira Herodiya, mkazi wa m’bale wake Filipo.+ 18  Zinakhala choncho chifukwa Yohane anali kumuuza Herode mobwerezabwereza kuti: “N’kosaloleka kutenga mkazi wa m’bale wanu.”+ 19  Choncho Herodiya anam’sungira chidani mumtima+ ndipo anali kufuna kumupha, koma sanathe kutero.+ 20  Herode anali kulemekeza+ Yohane, pakuti anali kumudziwa kuti ndi munthu wolungama ndi woyera,+ choncho anali kumusunga bwino. Atamva+ zonena zake anathedwa nzeru, komabe anapitiriza kumumvetsera mokondwa. 21  Ndiyeno tsiku loyenera+ linafika pamene Herode anakonzera chakudya chamadzulo nduna zake, akuluakulu a asilikali ndi atsogoleri a mu Galileya, pa tsiku lokumbukira kubadwa kwake.+ 22  Ndipo mwana wamkazi wa Herodiya analowa ndi kuvina, moti anasangalatsa Herode ndi ena amene anali kudya+ naye limodzi. Tsopano mfumu inauza mtsikanayo kuti: “Upemphe kwa ine chilichonse chimene ukufuna, ndipo ndidzakupatsa.” 23  Ndithu, anachita kumulumbirira kuti: “Chilichonse chimene ungapemphe kwa ine, ndidzachipereka kwa iwe,+ ngakhale hafu ya ufumu wangawu.”+ 24  Choncho anatuluka n’kukafunsa mayi ake kuti: “Ndikapemphe chiyani?” Mayi akewo anamuuza kuti: “Kapemphe mutu wa Yohane m’batizi.”+ 25  Nthawi yomweyo anapita kwa mfumuyo mofulumira, ndi kupempha kuti: “Ndikufuna mundipatse mutu wa Yohane M’batizi m’mbale pompano.” 26  Ngakhale kuti mfumu inamva chisoni kwambiri, sinafune kumukanira poganizira lumbiro lake lija, komanso poganizira amene anali kudya nawo chakudya patebulopo.+ 27  Choncho, nthawi yomweyo mfumu inatumiza msilikali ndi kumulamula kuti abweretse mutuwo. Iye anapita ndi kukamudula mutu m’ndendemo,+ 28  n’kuubweretsa m’mbale, ndi kuupereka kwa mtsikana uja. Ndiyeno mtsikanayo anakaupereka kwa mayi ake.+ 29  Ophunzira ake atamva zimenezo anabwera kudzatenga mtembo wake ndi kukauika m’manda achikumbutso.+ 30  Tsopano atumwi anasonkhana kwa Yesu ndi kumuuza zonse zimene iwo anachita ndi kuphunzitsa.+ 31  Iye anawauza kuti: “Inuyo bwerani kuno, tipite kwatokha kopanda anthu+ kuti mupumule pang’ono.”+ Pakuti ambiri anali kubwera ndi kupita, ndipo analibe nthawi yopuma, ngakhale yoti adye chakudya.+ 32  Choncho anakwera ngalawa, kupita kwaokhaokha kumalo opanda anthu.+ 33  Koma anthu anawaona akuchoka ndipo ambiri anadziwa zimenezo. Chotero kuchokera m’mizinda yonse, anthu anathamangira kumeneko wapansi, ndipo anthuwo ndi amene anayamba kukafika kumaloko.+ 34  Koma potsika, anaona khamu lalikulu la anthu, ndipo anawamvera chifundo,+ chifukwa anali ngati nkhosa zopanda m’busa.+ Choncho anayamba kuwaphunzitsa zinthu zambiri.+ 35  Tsopano kunja kunada, ndipo ophunzira ake anabwera kwa iye ndi kunena kuti: “Kuno n’kopanda anthu, ndipo nthawi yatha.+ 36  Auzeni anthuwa kuti anyamuke, apite m’midzi yapafupi ndi m’madera ozungulira kuti akagule okha chakudya.”+ 37  Koma iye anawayankha kuti: “Inuyo muwapatse chakudya.” Pamenepo iwo anafunsa Yesu kuti: “Kodi tipite kukagula mitanda ya mkate ya ndalama zokwana madinari 200 ndi kuipereka kwa anthuwa kuti adye?”+ 38  Powayankha iye anawafunsa kuti: “Muli ndi mitanda ingati ya mkate? Pitani mukaone!” Ataiona anati: “Ilipo isanu, ndi nsomba ziwiri.”+ 39  Kenako anauza anthuwo kuti akhale m’magulu+ pa udzu wobiriwira.+ 40  Ndipo anakhaladi m’magulu, ena anthu 100, ena anthu 50.+ 41  Tsopano anatenga mitanda ya mkate isanu ija ndi nsomba ziwiri zija n’kuyang’ana kumwamba ndi kupempha dalitso.+ Kenako ananyemanyema+ mitanda ya mkateyo ndi kuipereka kwa ophunzira ake kuti aipereke kwa anthuwo, ndiponso anaduladula nsomba ziwirizo ndi kugawira anthu onsewo. 42  Choncho, anthu onsewo anadya ndi kukhuta.+ 43  Kenako anatolera zotsala ndipo zinadzaza madengu 12, osawerengera nsombazo. 44  Ndipo onse amene anadya mkatewo anali amuna okwana 5,000.+ 45  Kenako mwamsanga, Yesu analimbikitsa ophunzira ake kuti akwere ngalawa ndi kutsogola kupita kutsidya lina loyang’anizana nalo cha ku Betsaida. Koma iye anatsalira akuuza anthuwo kuti azipita kwawo.+ 46  Ndipo atatsazikana ndi anthuwo, iye anachoka n’kupita m’phiri kukapemphera.+ 47  Madzulo mdima utagwa, ngalawa ija inali pakati pa nyanja, koma iye anali yekha kumtunda.+ 48  Kenako anaona ophunzirawo akupalasa movutika,+ chifukwa anali kulimbana ndi mphepo yamphamvu. Uwu unali m’bandakucha pafupifupi pa ulonda wachinayi,* ndipo iye anawalondola akuyenda panyanja. Koma ophunzirawo anaona ngati akufuna kuwapitirira. 49  Atamuona akuyenda panyanjapo, ophunzirawo anaganiza kuti: “Amenewa ndi masomphenya ndithu!” Ndipo anafuula mokweza.+ 50  Anachita zimenezi chifukwa onsewo anamuona ndipo anavutika mumtima. Koma nthawi yomweyo iye analankhula nawo, kuti: “Limbani mtima, ndine musachite mantha.”+ 51  Pamenepo Yesu anakwera nawo m’ngalawamo, ndipo mphepoyo inaleka. Ataona izi anadabwa kwambiri mumtima mwawo.+ 52  Popeza sanamvetse tanthauzo la mitanda ya mkate ija, mitima yawo inakhalabe yosazindikira.+ 53  Tsopano atawolokera kumtunda, anafika ku Genesarete ndi kuimika ngalawayo chapafupi.+ 54  Koma atangotsika m’ngalawamo, anthu anamuzindikira. 55  Choncho anthu am’dera lonselo anathamanga uku ndi uku ndi kunyamula odwala onse pamachira, kupita nawo kumene anamva kuti iye ali kumeneko. 56  Ndipo akangolowa m’midzi, kapena m’mizinda, kapena m’madera ozungulira alionse,+ anthu anali kukhazika odwala m’misika. Iwo anali kum’dandaulira kuti angogwira+ chabe ulusi wopota wa m’mphepete mwa malaya ake+ akunja. Ndipo anthu ambiri anaugwira ndi kuchira.+

Mawu a M'munsi

Onani mawu a m’munsi pa Mt 14:1.
Onani mawu a m’munsi pa Mt 14:25.